NKHANI YOPHUNZIRA 2
Zimene Tingaphunzire Kwa “Wophunzira Amene Yesu Anali Kumukonda Kwambiri”
“Tiyeni tipitirize kukondana, chifukwa chikondi chimachokera kwa Mulungu.”—1 YOH. 4:7.
NYIMBO NA. 105 “Mulungu Ndiye Chikondi”
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi chikondi cha Mulungu chimatithandiza bwanji?
MTUMWI Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8) Mawu amenewa amatikumbutsa mfundo yofunika kwambiri ya choonadi yakuti: Mulungu ndi amene analenga moyo komanso ndi mwiniwake wa chikondi. Yehova amatikonda kwambiri ndipo zimenezi zimatithandiza kuti tiziona kuti ndife otetezeka, tizikhala osangalala komanso okhutira.
2. Mogwirizana ndi Mateyu 22:37-40, kodi malamulo awiri aakulu kwambiri ndi ati, nanga n’chifukwa chiyani zingativute kumvera lamulo lachiwirili?
2 Akhristu sachita kusankha kuti asonyeze chikondi kapena ayi chifukwa limeneli ndi lamulo. (Werengani Mateyu 22:37-40.) Tikamudziwa bwino Yehova, ndi pamene zimakhala zosavuta kumvera lamulo loyamba. Izi zili choncho chifukwa choti Yehova ndi wangwiro, amatiganizira komanso amachita nafe zinthu mokoma mtima. Koma mwina zingativute kumvera lamulo lachiwiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa abale ndi alongo athu, omwe ali m’gulu la anzathu amene tiyenera kuwakonda, si angwiro. Nthawi zina akhoza kulankhula kapena kuchita zinthu m’njira yosonyeza kuti sanatiganizire. Yehova ankadziwa kuti tidzakumana ndi mavuto ngati amenewa, choncho anauzira anthu ena kuti alembe malangizo ofotokoza chifukwa chake tiyenera kusonyezana chikondi komanso mmene tingachisonyezere. Ndipo mmodzi wa anthuwa anali Yohane.—1 Yoh. 3:11, 12.
3. Kodi Yohane anafotokoza chiyani pa nkhani ya chikondi?
3 Yohane analemba mobwerezabwereza kuti Akhristu ayenera kumasonyeza chikondi. Mwachitsanzo, pofotokoza za moyo wa Yesu, Yohane anagwiritsa ntchito kwambiri mawu akuti “chikondi” kuposa anzake atatu amene analembanso Uthenga Wabwino. 1 Yoh. 4:10, 11) Komabe, zinamutengera nthawi Yohane kuti azindikire mfundo imeneyi.
Yohane anali ndi zaka pafupifupi 100 pamene ankalemba buku lake la Uthenga Wabwino komanso makalata ake atatu. Mabuku a m’Baibulo amenewa amatithandiza kudziwa kuti Akhristu ayenera kusonyeza chikondi pa zochita zawo zonse. (4. Kodi Yohane ankasonyeza chikondi nthawi zonse?
4 Pamene Yohane anali wachinyamata, nthawi zina zinkamuvuta kusonyeza chikondi. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Yesu ndi ophunzira ake ankapita ku Yerusalemu ndipo anadutsa ku Samariya. Anthu a m’mudzi wina wa ku Samariyako sanawalandire bwino. Ndiye kodi Yohane anachita chiyani? Iye anauza Yesu kuti apemphe moto kuti utsike kuchokera kumwamba ndi kuwononga anthu onse a m’mudzi umenewo. (Luka 9:52-56) Pa nthawi inanso, Yohane analephera kusonyeza chikondi kwa atumwi anzake. Iye ndi m’bale wake Yakobo ananyengerera mayi awo kuti akapemphe Yesu kuti adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu wake. Atumwi enawo atadziwa zimene Yakobo ndi Yohane anachita, anakwiya kwambiri. (Mat. 20:20, 21, 24) Koma ngakhale kuti Yohane ankalakwitsa zinthu zina, Yesu ankamukondabe.—Yoh. 21:7.
5. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
5 Munkhaniyi, tikambirana za chitsanzo cha Yohane komanso zinthu zina zomwe analemba zokhudza chikondi. Tikamakambirana zimenezi, tiona mmene tingasonyezere chikondi kwa abale ndi alongo athu. Tikambirananso njira ina yofunika yomwe mwamuna, yemwe ndi mutu wa banja angasonyezere kuti amakonda banja lake.
TIMASONYEZA CHIKONDI MWA ZOCHITA ZATHU
6. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amatikonda?
6 Nthawi zambiri anthufe timaganiza kuti tingasonyeze kuti timakonda munthu pomuuza mawu abwino. Komatu zochita zathu ndi zimene zingasonyeze kuti timamukondadi. (Yerekezerani ndi Yakobo 2:17, 26.) Mwachitsanzo, Yehova amatikonda. (1 Yoh. 4:19) Ndipo amatiuza zimenezi kudzera m’Mawu ake Baibulo. (Sal. 25:10; Aroma 8:38, 39) Komabe, timadziwa kuti Mulungu amatikonda osati chabe chifukwa cha mawu amene amatiuzawo, koma chifukwa cha zimene amatichitira. Yohane analemba kuti: “Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye.” (1 Yoh. 4:9) Yehova analola kuti Mwana wake wokondedwa avutike komanso kufa chifukwa cha ife. (Yoh. 3:16) Ndiye kodi pamenepa tingakayikirenso kuti Yehova amatikonda kwambiri?
7. Kodi Yesu anachita chiyani posonyeza kuti amatikonda?
7 Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti ankawakonda kwambiri. (Yoh. 13:1; 15:15) Iye anasonyeza kuti amakonda ophunzira ake kuphatikizapo ifeyo osati ndi mawu okha, komanso ndi zochita zake. Iye anati: “Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.” (Yoh. 15:13) Ndiye tikamaganizira zimene Yehova komanso Yesu anatichitirazi, kodi tiyenera kuchita chiyani?
8. Kodi lemba la 1 Yohane 3:18, limanena kuti tiyenera kuchita chiyani?
8 Timasonyeza kuti timakonda Yehova komanso Yesu tikamawamvera. (Yoh. 14:15; 1 Yoh. 5:3) Ndipotu Yesu anatilamula kuti tizikondana. (Yoh. 13:34, 35) Tisamangosonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu ndi mawu okha. M’malomwake, tizisonyeza kuti timawakonda ndi zochita zathu. (Werengani 1 Yohane 3:18.) Kodi ndi zinthu ziti zimene tingachite posonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu?
TIZIKONDA ABALE NDI ALONGO ATHU
9. Kodi chikondi chinathandiza Yohane kuchita chiyani?
9 Yohane akanatha kusankha kukhalabe ndi bambo ake ndi kumapeza ndalama zambiri popanga bizinezi yawo yopha nsomba. Koma m’malomwake, iye anagwiritsa ntchito nthawi yotsala ya moyo wake pothandiza ena kuti adziwe choonadi chonena za Yehova ndi Yesu. Moyo umene anasankhawu, sunali wophweka. Iye anazunzidwa ndipo chakumapeto kwa nthawi ya atumwi anathamangitsidwa m’dera lakwawo, apa n’kuti ali wokalamba. (Mac. 3:1; 4:1-3; 5:18; Chiv. 1:9) Ngakhale kuti iye anamangidwa chifukwa cholalikira za Yesu, Yohane anasonyeza kuti ankakonda anthu ena. Mwachitsanzo, ali pachilumba cha Patimo iye analemba buku la Chivumbulutso n’kulitumiza kumipingo n’cholinga choti Akhristu anzake adziwe ‘zinthu zimene zimayenera kuchitika posachedwapa.’ (Chiv. 1:1) Kenako Yohane analemba Uthenga Wabwino wonena za moyo wa Yesu ndi utumiki wake. Pa nthawiyi ayenera kuti anali atatulutsidwa m’ndende pachilumba cha Patimo. Iye analembanso makalata atatu n’cholinga chofuna kulimbikitsa abale ndi alongo ake. Kodi tingatsanzire bwanji Yohane yemwe anasonyeza kuti anali ndi moyo wodzimana?
10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda anthu ena?
10 Tingasonyeze kuti timakonda anthu ena ndi zimene timasankha kuchita pa moyo wathu. Dziko la Satanali limafuna kuti tizithera nthawi yathu komanso mphamvu zathu zonse pochita zofuna zathu zokha. Monga ngati kufunafuna ndalama kapena kutchuka. Koma Akhristu padziko lonse, amasonyeza mtima wodzimana ndipo amathera nthawi yawo yambiri polalikira uthenga wabwino komanso kuthandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. Ndiponso ena amasankha kugwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu nthawi zonse.
11. Kodi Akhristu ambiri okhulupirika amasonyeza bwanji kuti amakonda Yehova komanso abale ndi alongo awo?
11 Akhristu ambiri okhulupirika amayenera kugwira ntchito kuti azipeza zofunika pa moyo wawo komanso azisamalira mabanja awo. Komabe, iwo amachita zonse zimene angathe pothandiza gulu la Mulungu. Mwachitsanzo, ena amagwira nawo ntchito yothandiza pakachitika ngozi, ena pa ntchito zomangamanga ndipo aliyense ali ndi mwayi wopereka ndalama zothandiza pa Ntchito Yapadziko Lonse. Akhristuwa amachita zimenezi chifukwa amakonda Mulungu komanso anthu ena. Mlungu uliwonse, timasonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu tikamayesetsa kupezeka komanso kuyankha pamisonkhano. Ndipotu timayankha ngakhale pamene tili ndi mantha. Timayesetsanso kuchita zimenezi ngakhale kuti nthawi zina timakhala titatopa. Ngakhale kuti tonsefe tili ndi mavuto athu, timalimbikitsa ena misonkhano isanayambe komanso pambuyo pamisonkhano. (Aheb. 10:24, 25) Timayamikira kwambiri zimene abale ndi alongo athu okondedwawa amachita.
12. Kodi ndi njira inanso iti imene Yohane anasonyezera kuti ankakonda abale ndi alongo ake?
1 Yoh. 1:8–2:1, 13, 14) Ifenso tiyenera kumayamikira abale ndi alongo athu pa zabwino zimene amachita. Koma ngati wina wayamba kuchita makhalidwe oipa, tingasonyeze kuti timamukonda pomupatsa malangizo mokoma mtima. Pamafunika kulimba mtima kuti tipereke malangizo kwa anzathu ndipotu Baibulo limanena kuti anthu amene amakondana amapatsana malangizo.—Miy. 27:17.
12 Yohane anasonyezanso kuti ankakonda abale ndi alongo ake, osati pongowayamikira akachita bwino, koma powapatsanso malangizo. Mwachitsanzo, m’makalata ake, iye anayamikira abale ndi alongo chifukwa cha chikhulupiriro chawo komanso ntchito zawo zabwino. Koma anawapatsanso malangizo osapita m’mbali pa nkhani yokhudza kuchita machimo. (13. Kodi tiyenera kumapewa kuchita chiyani?
13 Nthawi zina tingasonyeze kuti timakonda abale ndi alongo athu chifukwa cha zimene sitichita. Mwachitsanzo, tingasonyeze kuti timawakonda ngati sitikhumudwa msanga chifukwa cha zimene alankhula. Taganizirani zimene zinachitika pa nthawi ina, chakumapeto kwa moyo wa Yesu ali padziko lapansili. Iye anauza ophunzira ake kuti angapeze moyo ngati atadya mnofu wake komanso kumwa magazi ake. (Yoh. 6:53-57) Zimene ananenazi zinakhumudwitsa ophunzira ake ambiri ndipo anasiya kumutsatira. Koma anzake a pamtima kuphatikizapo Yohane, sanamusiye koma anapitirizabe kumutsatira mokhulupirika. Nawonso sanamvetse zimene Yesu ankatanthauza ndipo ayenera kuti anadabwa ndi mawu amenewa. Koma anzake a Yesu okhulupirikawa sanaganize kuti zimene Yesu ananenazi ndi zolakwika ndipo sanakhumudwe nazo. M’malomwake, iwo anamukhulupirira chifukwa ankadziwa kuti nthawi zonse ankalankhula zoona. (Yoh. 6:60, 66-69) Choncho ndi bwino kuti ifenso tisamafulumire kukhumudwa ndi zimene anzathu alankhula. Koma tiziwalola kuti atifotokozere zomwe akutanthauza.—Miy. 18:13; Mlal. 7:9.
14. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudana ndi abale ndi alongo athu?
14 Yohane anatilimbikitsanso kuti tisamadane ndi abale ndi alongo athu. Ngati sitingatsatire malangizo amenewa, zingachititse kuti Satana azitigwiritsa ntchito. (1 Yoh. 2:11; 3:15) Zimenezi ndi zomwe zinachitikiranso ena chakumapeto kwa nthawi ya atumwi. Satana anayesetsa kuchita zonse zomwe angathe kuti atumiki a Mulungu azidana komanso kuti agawikane. Pa nthawi imene Yohane ankalemba makalata ake, anthu ena amene ankachita zinthu ngati Satana, anali atalowa mumpingo. Mwachitsanzo, mumpingo wina, Diotirefe anachititsa kuti anthu asamagwirizane. (3 Yoh. 9, 10) Iye sankalemekeza akulu omwe bungwe lolamulira linkawatumiza kuti aziyendera mipingo. Anafika mpaka pochotsa mumpingo aliyense amene ankalandira anthu amene iye ankadana nawo. Zimenezitu zinali zoipa kwambiri. Masiku anonso Satana akuyesetsa kuchititsa atumiki a Mulungu kuti asamagwirizane. Choncho, tisalole kuti tizidana ndi abale athu kapena kusiya kuwathandiza.
MUZIKONDA BANJA LANU
15. Kodi mwamuna yemwe ndi mutu wa banja, ayenera kukumbukira chiyani?
15 Njira imodzi imene mwamuna yemwe ndi mutu wa banja angasonyezere kuti amakonda anthu a m’banja lake, ndi kuwapezera zinthu zofunika pa moyo. (1 Tim. 5:8) Koma iye ayenera kukumbukira kuti chofunika kwambiri ndi kuwathandiza kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Mat. 5:3) Taganizirani chitsanzo chabwino chimene Yesu anapereka kwa mitu ya mabanja. Mogwirizana ndi Uthenga Wabwino wa Yohane, Yesu ali pamtengo wozunzikirapo ankaganizirabe anthu a m’banja lake. Pa nthawiyi, Yohane anali ataima pafupi ndi Mariya, mayi ake a Yesu. Ngakhale kuti Yesu anali mu ululu waukulu, anapempha Yohane kuti azisamalira mayi akewo. (Yoh. 19:26, 27) Yesu anali ndi achibale ake omwe akanatha kupezera Mariya zofunika pa moyo. Koma zikuoneka kuti pa nthawiyi panalibe ngakhale mmodzi amene anali wophunzira wake. Choncho Yesu ankafuna kuonetsetsa kuti pali munthu amene azisamalira mayi akewo komanso kuwalimbikitsa kuti apitirize kutumikira Yehova.
16. Kodi Yohane anali ndi maudindo otani?
16 Yohane anali ndi maudindo ambiri. Monga mtumwi, anali ndi udindo wotsogolera pa ntchito yolalikira. Ayeneranso kuti anali ndi banja ndipo anali ndi udindo wopezera anthu a m’banja lake zofunika pa moyo komanso kuwathandiza kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (1 Akor. 9:5) Kodi amuna omwe ndi mitu ya mabanja akuphunzirapo chiyani masiku ano?
17. N’chifukwa chiyani mwamuna ayenera kuthandiza anthu a m’banja lake kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova?
17 M’bale yemwe ndi mutu wa banja, amakhala ndi maudindo ambiri. Mwachitsanzo, ngati amagwira ntchito yolembedwa, amayesetsa kugwira ntchitoyo mwakhama n’cholinga choti khalidwe lake lizilemekezetsa dzina la Yehova. (Aef. 6:5, 6; Tito 2:9, 10) Iye angakhalenso ndi maudindo ena mumpingo, monga kulimbikitsa abale ndi alongo komanso kutsogolera pa ntchito yolalikira. Kuwonjezera pamenepo, amafunikanso kuti nthawi zonse aziphunzira Baibulo ndi mkazi wake komanso ana ake. Anthu a m’banja lake amamuyamikira chifukwa chowathandiza kuti akhale a thanzi, azisangalala komanso azipitirizabe kutumikira Yehova.—Aef. 5:28, 29; 6:4.
“MUDZAKHALABE M’CHIKONDI CHANGA”
18. Kodi Yohane sankakayikira chiyani?
18 Yohane anakhala ndi moyo zaka zambiri ndipo pa moyo wake anakumana ndi zinthu zambiri zosangalatsa. Anakumananso ndi mavuto ambiri omwe akanatha kufooketsa chikhulupiriro chake. Koma nthawi zonse iye ankayesetsa kutsatira malamulo a Yesu kuphatikizapo lamulo loti azikonda abale ndi alongo ake. Chifukwa cha zimenezi, Yohane sankakayikira kuti Yehova komanso Yesu amamukonda ndiponso kuti azimupatsa mphamvu kuti athe kupirira mayesero aliwonse amene angakumane nawo. (Yoh. 14:15-17; 15:10; 1 Yoh. 4:16) Palibe chimene Satana kapena dziko lakeli, akanachita chomwe chikanalepheretsa Yohane kusonyeza kuti amakonda abale ndi alongo ake mwa zochita ndi zolankhula zake.
19. Kodi lemba la 1 Yohane 4:7, limatilimbikitsa kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
19 Mofanana ndi Yohane, ifenso tikukhala m’dziko limene wolamulira wake ndi Satana, yemwe alibe chikondi. (1 Yoh. 3:1, 10) Ngakhale kuti iye amafuna kuti tisiye kukonda abale ndi alongo athu, sizingatheke, pokhapokha ngati ifeyo titalola zimenezo. Tiyeni tipitirize kukonda abale ndi alongo athu ndipo tizisonyeza zimenezi mwa zolankhula komanso zochita zathu. Tikatero, tidzasangalala kukhala m’banja la Yehova ndipo moyo wathu udzakhala wabwino kwambiri.—Werengani 1 Yohane 4:7.
NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu
^ ndime 5 Mtumwi Yohane ayenera kuti ndi “wophunzira amene Yesu anali kumukonda kwambiri.” (Yoh. 21:7) Choncho ngakhale kuti iye anali wachinyamata, ayenera kuti anali ndi makhalidwe ambiri abwino. Patapita nthawi, ali wachikulire, Yehova anamugwiritsa ntchito kulemba zambiri zokhudza chikondi. Munkhaniyi, tikambirana zina zimene iye analemba komanso zomwe tingaphunzire pa chitsanzo chake.
^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mwamuna yemwe ndi mutu wa banja komanso amakhala wotanganidwa, akugwira nawo ntchito yothandiza pakachitika ngozi, akupereka ndalama zothandiza pa Ntchito Yapadziko Lonse komanso waitana ena kuti adzakhale nawo pa kulambira kwawo kwa pabanja.