Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 5

“Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi Yanu”

“Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi Yanu”

“Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”​—AEF. 5:15, 16.

NYIMBO NA. 8 Yehova Ndiye Pothawirapo Pathu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi timachita bwanji zinthu limodzi ndi Yehova?

 TIMASANGALALA kupeza nthawi yochita zinthu ndi anthu amene timawakonda. Mwamuna ndi mkazi wake amasangalalanso kwambiri kupeza nthawi yocheza limodzi. Nawonso achinyamata amamva bwino akamacheza ndi anzawo apamtima. Ndipo tonsefe timaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali tikamapeza nthawi yocheza ndi Akhristu anzathu. Koposa zonse, timasangalala kwambiri tikamapeza nthawi yochita zinthu ndi Mulungu wathu. Tingachite zimenezi popemphera kwa iye, powerenga Mawu ake komanso kuganizira cholinga chake ndi makhalidwe ake abwino. Nthawi imene timachita zinthu ndi Yehova ndi yamtengo wapatali.​—Sal. 139:17.

2. Kodi ndi vuto lotani limene timakumana nalo?

2 Ngakhale kuti timasangalala kupeza nthawi yochita zinthu ndi Yehova, pali vuto lina limene timakumana nalo. Timakhala otanganidwa zomwe zimachititsa kuti zizikhala zovuta kupeza nthawi yochita zinthu zokhudza kulambira. Ntchito, udindo wathu wosamalira banja komanso zinthu zina zofunika zimafuna nthawi yambiri moti tikhoza kumaona kuti sitingapeze nthawi yopemphera, kuphunzira komanso kuganizira za Yehova.

3. Kodi ndi chinthu china chiti chomwe chingachititse kuti tiziwononga nthawi yathu?

3 Palinso vuto lina losaonekera lomwe lingachititse kuti tiziwononga nthawi yathu. Ngati sitingasamale, zinthu zina zomwe timachita zomwe pazokha si zolakwika, zikhoza kuwononga nthawi yathu yoti tizilimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Mwachitsanzo, timafunika kupeza nthawi yopuma kapena kuchita zinthu zina zosangalatsa. Komatu ngakhale zosangalatsa zomwe si zolakwika zikhoza kuwononga nthawi yathu n’kufika poti sitingakhale ndi nthawi yokwanira yochita zinthu zokhudza kulambira. Choncho tizikumbukira kuti zosangalatsa siziyenera kukhala chinthu chofunika kwambiri.​—Miy. 25:27; 1 Tim. 4:8.

4. Kodi tsopano tikambirana chiyani?

4 Munkhaniyi, tikambirana chifukwa chake tiyenera kumaika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba. Tikambirananso zimene tingachite kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi imene timachita zinthu ndi Yehova komanso mmene kuchita zimenezi kungatithandizire.

MUZISANKHA ZOCHITA MWANZERU NDIPO MUZIONA KUTI ZOFUNIKA KWAMBIRI NDI ZITI

5. Kodi kuganizira malangizo a pa Aefeso 5:15-17, kungathandize bwanji wachinyamata kusankha moyo wabwino kwambiri?

5 Muzisankha moyo wabwino kwambiri. Nthawi zambiri achinyamata amaganizira zimene angachite kuti akhale ndi moyo wabwino. Aphunzitsi komanso achibale awo omwe si a Mboni, angamawalimbikitse kuti apite kuyunivesite n’cholinga choti adzagwire ntchito zapamwamba n’kumapeza ndalama zambiri. Komatu kuchita zimenezi kumafuna nthawi yochuluka. Makolo ndi anzawo mumpingo angamawalimbikitse kuti azichita zambiri potumikira Yehova. Ndiye kodi n’chiyani chingathandize wachinyamata yemwe amakonda Yehova kuti asankhe zochita mwanzeru? Iye angachite bwino kuwerenga komanso kuganizira mozama zimene zili pa Aefeso 5:15-17. (Werengani.) Pambuyo powerenga mavesiwa, wachinyamatayo angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi “chifuniro cha Yehova” n’chiyani? Kodi iye angasangalale kwambiri nditasankha ziti? Kodi ndi zosankha ziti zomwe zingachititse kuti ndizigwiritsa ntchito bwino nthawi?’ Kumbukirani kuti “masikuwa ndi oipa” ndipo dzikoli, lomwe wolamulira wake ndi Satana, liwonongedwa posachedwapa. Choncho ndi nzeru kugwiritsa ntchito moyo wathu m’njira imene ingatithandize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.

6. Kodi Mariya anasankha zotani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti anasankha mwanzeru?

6 Muziika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba. Nthawi zina kuti tigwiritse ntchito nthawi yathu mwanzeru, timafunika kusankha pakati pa zinthu ziwiri zomwe si zolakwika pazokha. Timaona mfundo imeneyi tikaganizira zimene zinachitika Yesu atapita kunyumba kwa Mariya ndi Marita. N’zoonekeratu kuti posangalala kuti alandira Yesu monga mlendo wawo, Marita anaganiza zomuphikira chakudya chapamwamba. Koma pa nthawiyi, mchemwali wake Mariya anaona kuti ndi mwayi wake kuti akhale pafupi ndi Ambuye n’kumawamvetsera pamene ankaphunzitsa. N’zoona kuti Marita anali ndi zolinga zabwino pa zimene ankachitazi, koma Mariya anasankha “chinthu chabwino kwambiri.” (Luka 10:38-42) Ngakhale kuti patapita nthawi Mariya anaiwala chakudya chimene anadya pa tsikulo, tingakhale otsimikiza kuti iye sanaiwale zimene anaphunzira kwa Yesu. Mofanana ndi Mariya, yemwe anaona kuti nthawi yochepa yomwe ankamvetsera Yesu inali yamtengo wapatali, ifenso timaona kuti nthawi yomwe timachita zinthu zokhudza Yehova ndi yamtengo wapatali. Ndiye kodi tingatani kuti tiziigwiritsa ntchito bwino?

MUZIGWIRITSA NTCHITO BWINO NTHAWI YOCHITA ZINTHU ZOKHUDZA YEHOVA

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kumapeza nthawi yopemphera, kuphunzira komanso kuganizira kwambiri za Yehova?

7 Dziwani kuti pemphero, kuphunzira komanso kuganizira za Yehova ndi mbali ya kulambira kwathu. Tikamapemphera, timakhala tikulankhula ndi Atate wathu wakumwamba yemwe amatikonda kwambiri. (Sal. 5:7) Tikamaphunzira Baibulo ‘timamudziwadi Mulungu,’ yemwe ndi mwiniwake wa nzeru zonse. (Miy. 2:1-5) Kuganizira mozama kumatithandiza kuona makhalidwe ochititsa chidwi amene Yehova ali nawo komanso kumatikumbutsa zinthu zabwino zimene iye wakonzera anthu onse. Imeneyi ndi njira yabwino kwambiri yogwiritsira ntchito nthawi yathu. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi?

Muzipeza malo opanda phokoso mukamaphunzira Baibulo panokha (Onani ndime 8-9)

8. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Yesu pa nkhani ya mmene anagwiritsira ntchito nthawi yake m’chipululu?

8 Ngati n’zotheka, muzikhala pamalo opanda phokoso. Asanayambe utumiki wake wapadzikoli, Yesu anakhala m’chipululu masiku 40. (Luka 4:1, 2) Kumalo opanda phokoso amenewa anapemphera kwa Yehova komanso kuganizira mozama zimene Atate wake ankafuna kuti iye achite. Mosakayikira, kuchita zimenezi kunamuthandiza kukonzekera mayesero amene anakumana nawo pambuyo pake. Kodi kuganizira chitsanzo cha Yesu kungatithandize bwanji? Ngati m’banja lanu muli anthu ambiri, mwina zingakhale zovuta kuti mupeze malo opanda phokoso kunyumba. Choncho, mungachite bwino kukafufuza malo ena komwe sikungakhale phokoso. Izi ndi zimene Julie amachita akafuna kupeza nthawi yochita zinthu ndi Yehova popemphera kwa iye. Iye ndi mwamuna wake amakhala m’nyumba yaing’ono ku France ndipo zimakhala zovuta kuti akhale paokha popanda kusokonezedwa ndi anthu ena. Julie anafotokoza kuti: “Choncho ndimapita kukayenda kupaki tsiku lililonse. Kumeneko zimatheka kukhala ndekhandekha popanda kusokonezedwa ndipo ndimalankhula ndi Yehova momasuka.”

9. Ngakhale kuti ankatanganidwa kwambiri, kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi wofunika?

9 Yesu ankakhala wotanganidwa kwambiri. Pamene ankachita utumiki wake, anthu ambiri ankangomutsatira kulikonse ndipo onsewo ankafuna kuti awathandize. Pa nthawi ina, ‘anthu onse amumzinda anasonkhana pakhomo’ limene anali kuti adzamuone. Ngakhale zinali choncho, iye anapeza nthawi yolimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova. Tsiku lotsatira m’mawa kusanache, iye anapita “kumalo kopanda anthu” kuti akapemphere kwa Atate wake.​—Maliko 1:32-35.

10-11. Mogwirizana ndi Mateyu 26:40, 41, kodi ndi malangizo a panthawi yake ati amene Yesu anapatsa ophunzira ake m’munda wa Getsemane, koma chinachitika n’chiyani?

10 Pa usiku wake womaliza padzikoli, pamene utumiki wake unkapita kumapeto, Yesu anapitanso kumalo opanda phokoso kuti akaganizire kwambiri za Yehova komanso kupemphera. Malo opanda phokosowa anawapeza m’munda wa Getsemane. (Mat. 26:36) Pa nthawiyi, Yesu anapatsa ophunzira ake malangizo a panthawi yake okhudza kupemphera.

11 Taganizirani zimene zinachitika. Pamene ankafika m’munda wa Getsemane, unali usiku kwambiri, mwinanso kudutsa pakati pa usiku. Iye anauza atumwi kuti ‘akhale maso’ ndipo kenako anapita kukapemphera. (Mat. 26:37-39) Koma pamene iye ankapemphera, atumwiwo anagona. Atawapeza akugona, Yesu anawauzanso kachiwiri kuti ‘akhale maso ndi kupemphera mosalekeza.’ (Werengani Mateyu 26:40, 41.) Iye anadziwa kuti iwo anali ndi nkhawa kwambiri ndiponso anali atatopa. Mwachifundo Yesu anavomereza kuti “thupi ndi lofooka.” Ngakhale zinali choncho, Yesu anapita maulendo ena awiri kukapemphera ndipo ulendo uliwonse akabwera ankapeza ophunzirawo akugona m’malo mopemphera.​—Mat. 26:42-45.

Muzipemphera kwa Yehova pa nthawi imene simunatope kwambiri (Onani ndime 12)

12. Kodi tingatani ngati nthawi zina tikuona kuti tikulephera kupemphera chifukwa cha nkhawa kapena kutopa kwambiri?

12 Muzisankha nthawi yabwino. Nthawi zina tingamalephere kupemphera chifukwa cha nkhawa kapenanso kutopa kwambiri. Ngati zimenezi zinakuchitikiranipo, dziwani kuti si inu nokha. Ndiye kodi mungatani? Anthu ena omwe anazolowera kupemphera kwa Yehova madzulo, anaona kuti n’zothandiza kumapemphera kusanade kwambiri pomwe amakhala asanatope. Enanso amaona kuti kukhala moyenera popemphera kumathandiza kwambiri. Koma bwanji ngati mukuona kuti simungakwanitse kupemphera chifukwa cha nkhawa kapena kutopa kwambiri? Muzimuuza Yehova mmene mukumvera ndipo mungakhale wotsimikiza kuti Atate wathu yemwe ndi wachifundo akukumvetsani.​—Sal. 139:4.

Muzipewa kuyankha mameseji ndi maimelo mukakhala pamisonkhano (Onani ndime 13-14)

13. Kodi zipangizo zamakono zingatisokoneze bwanji tikamachita zinthu zokhudza Yehova?

13 Muzipewa zosokoneza mukamaphunzira. Pemphero si njira yokhayo imene ingatithandize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kupezeka pamisonkhano kungatithandizenso kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Kodi pali zina zimene mungachite kuti muzigwiritsa ntchito bwino nthawi imene mumaphunzira panokha komanso kupezeka pamisonkhano yampingo? Dzifunseni kuti, ‘Kodi n’chiyani chimandisokoneza ndikakhala pamisonkhano yampingo kapena ndikamaphunzira pandekha?’ Kodi ndi kuimbiridwa foni, kulandira imelo kapena uthenga pafoni kapena chipangizo china chamakono? Masiku ano anthu ambiri ali ndi zipangizo zoterezi. Ofufuza ena amanena kuti ngati tikufuna kuika maganizo athu onse pa zimene tikuchita koma tili ndi foni pafupi, ikhoza kutisokoneza. Katswiri wina woona za kaganizidwe ananena kuti: “Maganizo ako sakhala pa zimene ukuchita, m’malomwake amakhala kwina.” Nthawi zambiri msonkhano wadera kapena wachigawo usanayambe, timauzidwa kuti titchere zipangizo zathu zamakono m’njira yoti zisasokoneze ena. Kodi tingachitenso chimodzimodzi ndi zipangizo zathu zamakono kuti zisatisokoneze ifeyo tikakhala patokha pochita zinthu zokhudza Yehova?

14. Mogwirizana ndi Afilipi 4:6, 7, kodi Yehova adzatithandiza bwanji kuti tisamasokonezeke?

14 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuti musasokonezedwe. Mukaona kuti maganizo anu akuyendayenda mukamaphunzira panokha kapena mukakhala pamisonkhano, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Ngati mwakhumudwa kapena muli ndi nkhawa, sizingakhale zophweka kuti muike maganizo anu onse pa zinthu zokhudza kulambira. Koma ndi zimene muyenera kuchita. Muzipempha Mulungu kuti akupatseni mtendere umene kuwonjezera pa kuteteza mtima wanu, udzatetezanso “maganizo anu.”​—Werengani Afilipi 4:6, 7.

KUPEZA NTHAWI YOCHITA ZINTHU ZOKHUDZA YEHOVA N’KOTHANDIZA

15. Kodi ndi phindu lina liti limene tingapeze tikamachita zinthu ndi Yehova?

15 Mungapindule kwambiri mukamapeza nthawi yoti muzilankhula, kumvetsera komanso kuganizira za Yehova. Motani? Choyamba, muzisankha zochita mwanzeru. Baibulo limatitsimikizira kuti “munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.” (Miy. 13:20) Choncho mukamapeza nthawi yochita zinthu ndi Yehova, yemwe ndi mwiniwake nzeru, mudzakhala wanzeru. Mudzadziwa zimene mungachite kuti muzimusangalatsa komanso kupewa zimene zingamukhumudwitse.

16. Kodi kuchita zinthu limodzi ndi Yehova kumatithandiza bwanji kuti tiziphunzitsa bwino?

16 Chachiwiri, mukhoza kukhala mphunzitsi wabwino. Tikamaphunzira Baibulo ndi munthu, chimodzi mwa zolinga zathu zikuluzikulu ndi kumuthandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Tikamayesetsa kupemphera komanso kuphunzira za Atate wathu wakumwamba m’pamenenso timayamba kumukonda kwambiri. Izi zimachititsa kuti tikhale okonzeka mokwanira kuthandiza amene tikuphunzira naye Baibulo kuti nayenso ayambe kukonda Yehova. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yesu. Iye ankafotokoza zokhudza Atate wake mokoma mtima komanso mwachikondi moti otsatira ake okhulupirika sakanachitira mwina koma nawonso kuyamba kukonda Yehova.​—Yoh. 17:25, 26.

17. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kupemphera komanso kuphunzira patokha kumatithandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu?

17 Chachitatu, chikhulupiriro chanu chidzalimba kwambiri. Taganizirani zimene zimachitika mukapempha Mulungu kuti akutsogolereni, akulimbikitseni kapena akuthandizeni. Nthawi iliyonse imene Yehova wayankha pemphero lanu, mumayamba kumukhulupirira kwambiri. (1 Yoh. 5:15) Kodi chinanso n’chiyani chimene chingakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu? Kuphunzira Baibulo panokha. Ndipotu paja “munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.” (Aroma 10:17) Komabe, kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu, pamafunika zambiri osati kungophunzira chabe. Ndiye kodi timayenera kuchitanso chiyani?

18. Perekani chitsanzo chosonyeza kufunika koganizira zimene timaphunzira.

18 Tiyenera kumaganizira mozama zimene tikuphunzira. Taganizirani zimene zinachitikira yemwe analemba Salimo 77. Wolemba salimoyu ankada nkhawa chifukwa choganiza kuti iyeyo limodzi ndi Aisiraeli anzake sankakondedwanso ndi Yehova. Maganizo amenewa anamuchititsa kuti azilephera kugona usiku. (Vesi 2-8) Ndiye kodi anatani? Iye anauza Yehova kuti: “Ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zonse, ndipo ndiziganizira zochita zanu.” (Vesi 12) N’zoona kuti wolemba salimoyu ankadziwa zinthu zimene Yehova anali atachitira anthu ake m’mbuyomo. Komabe anadzifunsa kuti: “Kodi Mulungu waiwala kukhala wokoma mtima, kapena watsekereza chifundo chake mwaukali?” (Vesi 9) Iye anaganizira ntchito za Yehova komanso mfundo yakuti Mulungu anali atasonyeza chifundo ndiponso kukoma mtima kwa anthu ake m’mbuyomo. (Vesi 11) Ndiye kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Wolemba masalimoyo anakhala wotsimikiza kuti Yehova sangasiye anthu ake. (Vesi 15) Mofanana ndi zimenezi, chikhulupiriro chanu chingalimbe kwambiri mukamaganizira zimene Yehova wachitira anthu ake komanso zimene wakuchitirani inuyo panokha.

19. Kodi kuchita zinthu ndi Yehova kungatithandizenso bwanji?

19 Chanambala 4 komanso chofunika kwambiri ndi chakuti, mudzayamba kukonda kwambiri Yehova. Kuposa makhalidwe ena onse, chikondi chingakuthandizeni kuti muzimvera Yehova, kulolera kusiya zinthu zina kuti mumusangalatse komanso kupirira mayesero alionse. (Mat. 22:37-39; 1 Akor. 13:4, 7; 1 Yoh. 5:3) Palibe chinthu china chofunika kwambiri kuposa kukonda komanso kukhala pa ubwenzi ndi Yehova.​—Sal. 63:1-8.

20. Kodi mwakonza zotani kuti muzipeza nthawi yochita zinthu ndi Yehova?

20 Muzikumbukira kuti kupemphera, kuphunzira komanso kuganizira mozama zimene tikuphunzirazo ndi mbali ya kulambira kwathu. Mofanana ndi Yesu, muzipeza malo opanda phokoso kuti muchite zinthu ndi Yehova. Muzipewa zilizonse zimene zingakusokonezeni. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuika maganizo anu onse pa zinthu zokhudza kulambira zomwe mukuchita. Mukamagwiritsa ntchito bwino nthawi yanu panopa, Yehova adzakudalitsani ndipo mudzakhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu mpaka kalekale.​—Maliko 4:24.

NYIMBO NA. 28 Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova

^ ndime 5 Yehova ndi mnzathu wapamtima. Timaona kuti ubwenzi wathu ndi iye ndi wamtengo wapatali ndipo timafunitsitsa kuti timudziwe bwino. Pamatenga nthawi yaitali kuti tidziwane bwino ndi winawake. Choncho pangafunike nthawi yokwanira kuti tipitirize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Popeza kuti masiku ano timakhala otanganidwa kwambiri, kodi tingatani kuti tizipeza nthawi yolimbitsa ubwenzi wathu ndi Atate wathu wakumwamba? Nanga kuchita zimenezi kungatithandize bwanji?