Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 1

“Ofunafuna Yehova Sadzasowa Chilichonse Chabwino”

“Ofunafuna Yehova Sadzasowa Chilichonse Chabwino”

LEMBA LA CHAKA CHA 2022: “Ofunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.”​—SAL. 34:10.

NYIMBO NA. 4 “Yehova Ndi M’busa Wanga”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

Davide ankaona kuti ‘sankasowa chilichonse chabwino’ ngakhale pamene ankakumana ndi mavuto (Onani ndime 1-3) *

1. Kodi Davide anakumana ndi mavuto otani?

 DAVIDE ankathawa chifukwa moyo wake unali pangozi. Sauli, yemwe anali mfumu yamphamvu ya Isiraeli, anali atatsimikiza mtima kuti amuphe. Pa nthawi imene ankafuna chakudya, Davide anaima mumzinda wa Nobu ndipo anapempha mitanda 5 ya mkate. (1 Sam. 21:1, 3) Pambuyo pake, iye ndi amuna amene anali nawo, anakabisala kuphanga. (1 Sam. 22:1) Kodi chinachitika n’chiyani kuti zinthu zikhale chonchi pa moyo wa Davide?

2. Kodi Sauli anaika bwanji moyo wake pangozi? (1 Sam. 23:16, 17)

2 Sauli ankachitira nsanje Davide chifukwa choti anatchuka komanso anali atapambana pa nkhondo zambiri. Sauli ankadziwanso kuti kusamvera kwake kunachititsa kuti Yehova amukane ndiponso kuti anasankha Davide kuti akhale mfumu ya Isiraeli. (Werengani 1 Samueli 23:16, 17.) Koma monga mfumu ya Isiraeli, Sauli anali ndi gulu lalikulu la asilikali ndiponso anthu ambiri omwe anali kumbali yake. Choncho Davide anathawa kuti apulumutse moyo wake. Kodi Sauli ankaganiza kuti akanatha kulepheretsa cholinga cha Mulungu choti Davide akhale mfumu? (Yes. 55:11) Baibulo silinena koma chomwe tikudziwa n’chakuti Sauli ankaika moyo wake pangozi. Tikutero chifukwa nthawi zonse anthu amene amalimbana ndi Mulungu sapambana.

3. Kodi Davide ankamva bwanji ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto?

3 Davide anali wodzichepetsa kwambiri. Iye sanasankhe yekha kuti akhale mfumu ya Isiraeli. Koma Yehova ndi amene anamusankha. (1 Sam. 16:1, 12, 13) Sauli anayamba kuona Davide ngati mdani wake. Komatu Davide sanaimbe mlandu Yehova chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo. Ndipo sanadandaule kuti analibe chakudya kapenanso chifukwa choti ankabisala kuphanga. M’malomwake zikuoneka kuti pa nthawi imene ankabisala kuphangako ndi pamene analemba nyimbo yotamanda Mulungu imene ili ndi mawu a mulemba la chakali akuti: “Ofunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.”​—Sal. 34:10.

4. Kodi tikambirana mafunso ati, nanga n’chifukwa chiyani ali ofunika?

4 Masiku ano atumiki ambiri a Yehova sapeza chakudya chokwanira kapena zinthu zina zofunika pa moyo. * Izi ndi zimene zakhala zikuchitika makamaka pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Ndipo pamene “chisautso chachikulu” chikuyandikira, tikuyembekezera kuti tingakumane ndi mavuto enanso ambiri. (Mat. 24:21) Tili ndi mfundo zimenezi m’maganizo, tiyeni tipeze mayankho a mafunso 4 awa: Kodi Davide ‘sanasowe chilichonse chabwino’ m’njira yotani? N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira kukhala okhutira ndi zimene tili nazo? N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzatisamalira? Nanga kodi panopa tingakonzekere bwanji zimene tikumane nazo m’tsogolo?

“SINDIDZASOWA KANTHU”

5-6. Kodi Salimo 23:1-6, limatithandiza bwanji kumvetsa zimene Davide ankatanthauza pomwe anati atumiki a Mulungu “sadzasowa chilichonse chabwino”?

5 Kodi Davide ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti atumiki a Yehova “sadzasowa chilichonse chabwino”? Tingapeze yankho lake tikaganizira mawu ofanana ndi amenewa omwe ali mu Salimo 23. (Werengani Salimo 23:1-6.) Davide anayamba Salimoli ndi mawu akuti: “Yehova ndi M’busa wanga. Sindidzasowa kanthu.” M’mavesi ena onse mu Salimoli, Davide anatchula zinthu zimene ndi zofunika kwambiri monga madalitso amene Yehova ankamupatsa chifukwa anali M’busa wake. Iye ananena kuti Yehova ankamutsogolera “m’tinjira tachilungamo” ndiponso kumuthandiza mokhulupirika pa nthawi imene zinthu zinali bwino komanso pa mavuto. Iye ankadziwa kuti kukhala “m’mabusa a msipu wambiri” a Yehova, sikunkatanthauza kuti sazikumana ndi mavuto. Ankadziwanso kuti nthawi zina angakumane ndi zofooketsa, zomwe anaziyerekezera ndi kuyenda “m’chigwa cha mdima wandiweyani,” ndiponso kuti adzakhala ndi adani. Koma popeza Yehova anali M’busa wake, Davide ‘sakanaopa kanthu.’

6 Choncho apa tapeza yankho la funso lakuti, kodi Davide ‘sanasowe chilichonse chabwino’ m’njira yotani? Iye anali ndi chilichonse chimene chikanamuthandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Kuti akhale wosangalala sizinkadalira kuti akhale ndi zinthu zambiri. Davide ankakhutira ndi zimene Yehova ankamupatsa. Chofunika kwambiri kwa iye chinali madalitso komanso chitetezo zochokera kwa Mulungu.

7. Mogwirizana ndi Luka 21:20-24, kodi Akhristu a ku Yudeya anakumana ndi vuto lotani?

7 Kuchokera pa mawu a Davidewa tingaone kufunika koona moyenera zinthu zimene tingakhale nazo. Tikhoza kumasangalala ndi zinthu zilizonse zimene tingakhale nazo koma sitiyenera kuziona kuti ndi zofunika kwambiri pa moyo wathu. Imeneyi inali mfundo ya choonadi yofunika kwambiri imene Akhristu a ku Yudeya ankafunika kuimvetsa. (Werengani Luka 21:20-24.) Yesu anali atawachenjezeratu kuti pa nthawi ina ‘magulu a nkhondo adzazungulira’ Yerusalemu. Iwo ankafunika kuti akadzaona zimenezi “adzayambe kuthawira kumapiri.” Kuthawako kukanachititsa kuti apulumuke, komabe ankafunika kusiya zinthu zambiri. Nsanja ya Olonda ina m’mbuyomu inanena kuti: “Iwo anasiya minda, nyumba ndipo sanatenge ngakhale katundu wa m’nyumba zawo. Ankakhulupirira kuti Yehova adzawateteza komanso kuwathandiza ndipo ankaona kuti kumulambira n’kofunika kwambiri kuposa china chilichonse.”

8. Kodi ndi phunziro lofunika liti limene tingapeze pa zimene zinachitikira Akhristu a ku Yudeya?

8 Kodi ndi phunziro lofunika kwambiri liti limene tikupeza pa zimene zinachitikira Akhristu omwe ankakhala ku Yudeya? Nsanja ya Olonda ija inanenanso kuti: “M’tsogolomu tingadzakumane ndi mayesero okhudza mmene timaonera zinthu zimene tili nazo. Kodi timaona kuti zinthu zimenezi ndi zofunika kwambiri? Kapena timaona kuti chofunika kwambiri ndi kupulumuka kwa anthu onse omwe ali kumbali ya Mulungu? Mapeto akadzafika tingadzakumane ndi mavuto ndipo mwinanso tingadzafunike kusiya zinthu zina. Mofanana ndi Akhristu anzathu omwe anathawa ku Yudeya, tidzayenera kukhala okonzeka kuchita chilichonse chimene chingafunike kuti tipulumuke.” *

9. Kodi malangizo a Paulo opita kwa Akhristu a Chiheberi angakulimbikitseni bwanji?

9 Taganizirani mmene zinalili zovuta kwa Akhristu amenewa kusiya chilichonse n’kukayambanso moyo watsopano. Iwo ankafunika kukhala ndi chikhulupiriro n’kumadalira kuti Yehova aziwathandiza kupeza zofunika pa moyo. Koma palinso china chimene chikanawathandiza. Kutatsala zaka 5 kuti Aroma azungulire mzinda wa Yerusalemu, mtumwi Paulo anapatsa Akhristu a Chiheberi malangizo ofunika awa: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’ Moti tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?’” (Aheb. 13:5, 6) N’zosachita kufunsa kuti onse amene anatsatira malangizo a Paulo, Aroma asanaukire mzindawu, sizinawavute kukhala okhutira ndi zochepa zimene anali nazo kumene anathawirako. Sankakayikira kuti Yehova aziwapatsa zimene ankafunikira. Mawu a Paulowa akutitsimikizira kuti ifenso tingamadalire Yehova.

“TIKHALE OKHUTIRA NDI ZINTHU ZIMENEZI”

10. Kodi Paulo anatifotokozera “chinsinsi” chotani?

10 Paulo anapereka malangizo ofanana ndi amenewa kwa Timoteyo ndipo amagwiranso ntchito kwa ife. Iye analemba kuti: “Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.” (1 Tim. 6:8) Kodi izi zikutanthauza kuti sitiyenera kudya chakudya chabwino, kukhala ndi nyumba yabwino kapenanso kumagula zovala zatsopano? Zimenezi si zomwe Paulo ankatanthauza. Apa iye ankangotanthauza kuti tiyenera kukhala okhutira ndi zilizonse zimene tili nazo. (Afil. 4:12) Chimenechi ndiye chinali “chinsinsi” cha Paulo. Chinthu chofunika kwambiri ndi ubwenzi wathu ndi Mulungu osati zinthu zimene tingakhale nazo.​—Hab. 3:17, 18.

Aisiraeli ‘sanasowe kanthu’ pa zaka 40 zomwe anali m’chipululu. Kodi ifeyo timakhutira ndi zimene tili nazo panopa? (Onani ndime 11) *

11. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yokhala okhutira kuchokera pa zimene Mose anauza Aisiraeli?

11 Pangakhale kusiyana pakati pa mmene ifeyo timaonera zomwe timafunikira ndi mmene Yehova amaonera. Taganizirani zimene Mose anauza Aisiraeli atayenda m’chipululu kwa zaka 40. Iye anati: “Yehova Mulungu wanu wakudalitsani pa chilichonse chimene dzanja lanu likuchita. Iye akudziwa za kuyenda kwanu kudutsa m’chipululu chachikulu ichi. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu zaka 40 zimenezi, ndipo simunasowe kanthu.” (Deut. 2:7) Pa zaka 40 zimenezo, Yehova anapatsa Aisiraeli mana kuti azidya. Komanso zovala zawo zomwe anachoka nazo ku Iguputo sizinang’ambike. (Deut. 8:3, 4) Ngakhale kuti ena akanaona kuti zimenezi n’zosakwanira, Mose anakumbutsa Aisiraeliwo kuti anali ndi zonse zomwe ankafunika. Yehova angasangalale kwambiri ngati ataona kuti timakhala okhutira n’kumayamikira ngakhale zochepa zimene watipatsa komanso kumaziona monga madalitso.

TIZIKHULUPIRIRA KUTI YEHOVA ADZATISAMALIRA

12. N’chiyani chikusonyeza kuti Davide sankadzidalira koma ankadalira Yehova?

12 Davide ankadziwa kuti Yehova ndi wokhulupirika ndipo amasamalira kwambiri onse amene amamukonda. Ngakhale kuti pamene ankalemba Salimo 34, moyo wake unali pangozi, mwachikhulupiriro Davide ankaona kuti “mngelo wa Yehova” wamanga msasa ‘kumuzungulira.’ (Sal. 34:7) N’kutheka kuti iye ankayerekezera mngelo wa Yehova ndi msilikali amene ali kunkhondo yemwe nthawi zonse amakhala tcheru kuti aone kumene kungachokera mdani. Ngakhale kuti anali msilikali wodziwa kumenya nkhondo komanso Yehova anamulonjeza kuti adzamupatsa ufumu, Davide sanadalire luso lake loponya mwala ndi gulaye kapenanso logwiritsa ntchito lupanga pogonjetsa adani ake. (1 Sam. 16:13; 24:12) Iye ankadalira Mulungu ndipo ankakhulupirira kuti mngelo wa Yehova ‘amapulumutsa onse omuopa.’ N’zoona kuti masiku ano sitiyembekezera kuti Yehova azititeteza modabwitsa. Koma tikudziwa kuti onse amene amadalira Yehova, ngakhale panopa atamwalira, adzalandira moyo wosatha.

Pa nthawi ya chisautso chachikulu, Gogi wa ku Magogi adzayesa kutiukira m’nyumba zathu. Koma sitidzachita mantha podziwa kuti Yesu ndi angelo ake akuona zomwe zikuchitika ndipo atiteteza (Onani ndime 13)

13. Kodi Gogi wa ku Magogi akamadzaukira, n’chifukwa chiyani tidzaoneke ngati osatetezeka, koma n’chiyani chidzatithandize kuti tisakhale ndi mantha? (Onani chithunzi chapachikuto.)

13 Posachedwapa m’tsogolomu tidzayesedwa ngati timakhulupirira kuti Yehova angatiteteze. Pamene Gogi wa ku Magogi, amene ndi mgwirizano wa mayiko, azidzaukira anthu a Mulungu, miyoyo yathu idzaoneka ngati ili pangozi. Tidzafunika kukhulupirira kuti Yehova angathe kutipulumutsa ndipo atipulumutsadi. Mitundu ya anthu izidzationa ngati nkhosa zosatetezeka. (Ezek. 38:10-12) Tidzakhala opanda zida komanso osadziwa nkhondo. Mayiko azidzaona kuti n’zosavuta kutigonjetsa. Iwo sadzadziwa kuti angelo a Mulungu atizungulira kuti atiteteze koma ife tidzadziwa zimenezi chifukwa cha chikhulupiriro. Mayiko amenewa sadzadziwa chifukwa sakhulupirira Mulungu. Iwotu adzadabwa kwambiri kuona magulu a angelo akumenya nkhondo kuti atipulumutse.​—Chiv. 19:11, 14, 15.

TIZIKONZEKERA ZAM’TSOGOLO PANOPA

14. Kodi tingatani panopa pokonzekera zam’tsogolo?

14 Kodi tingatani kuti panopa tizikonzekera zam’tsogolo? Choyamba tiziona moyenera zinthu zimene tili nazo n’kumakumbukira kuti tsiku lina tidzazisiya. Tiyeneranso kumakhala okhutira ndipo tizisangalala kwambiri chifukwa cha ubwenzi wabwino umene tili nawo ndi Yehova. Tikamamudziwa bwino Mulungu wathu, m’pamenenso tingadzakhulupirire kwambiri kuti adzatiteteza Gogi wa ku Magogi akamadzatiukira.

15. Kodi Davide anakumana ndi zotani ali mnyamata, zomwe zinamuthandiza kudziwa kuti Yehova sangamugwiritse mwala?

15 Taganizirani chinanso chimene chinathandiza Davide chomwe chingatithandizenso ifeyo kukonzekera mayesero amene tingakumane nawo. Iye anati: “Anthu inu, talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa iye.” (Sal. 34:8) Mawu amenewa akusonyeza chifukwa chake Davide ankakhulupirira kuti Yehova angamuthandize. Nthawi zonse ankadalira Yehova ndipo sanamugwiritsepo mwala. Iye ali mnyamata, atakumana ndi Goliyati yemwe anali Mfilisiti wodziwa kumenya nkhondo anamuuza kuti: “Lero Yehova akupereka m’manja mwanga.” (1 Sam. 17:46) Pa nthawi inanso Davide ankatumikira Mfumu Sauli, yemwe mobwerezabwereza ankafuna kumupha. Koma “Yehova anali ndi Davideyo.” (1 Sam. 18:12) Choncho popeza Davide anali ataona Yehova akumuthandiza m’mbuyomu, ankakhulupirira kuti amuthandizanso pa mavuto amene ankakumana nawo.

16. Kodi ‘tingalawe’ ubwino wa Yehova m’njira ziti?

16 Tikamadalira kwambiri Yehova kuti azititsogolera panopa, tidzamudaliranso kwambiri m’tsogolo kuti adzatipulumutsa. Pamafunika chikhulupiriro komanso mtima wofunitsitsa kuti tidalire Yehova kuti tipemphe abwana athu kuti atilole kukapezeka kumsonkhano wadera kapena wachigawo, kapenanso kuwapempha kuti atichepetsere nthawi yogwira ntchito n’cholinga choti tizipezeka pamisonkhano komanso kumagwira nawo mokwanira ntchito yolalikira. Tiyerekeze kuti abwana athuwo akana zimene tawapempha ndipo atichotsa ntchito, kodi timakhulupirira kuti Yehova sangatisiye ndiponso kuti nthawi zonse azitipatsa zimene timafunikira? (Aheb. 13:5) Atumiki a nthawi zonse ambiri angatifotokozere zimene zinawachitikira, zomwe zimasonyeza mmene Yehova anawathandizira pa nthawi imene ankafunika kwambiri kuthandizidwa. Yehova ndi wokhulupirika.

17. Kodi lemba la chaka cha 2022 ndi liti, nanga n’chifukwa chiyani lili loyenera?

17 Popeza Yehova ali kumbali yathu, palibe chifukwa choopera zimene tikumane nazo m’tsogolo. Ngati timaika zimene Mulungu amafuna pamalo oyamba pa moyo wathu, iye sadzatisiya. Pofuna kutikumbutsa kufunika kokonzekera panopa mavuto amene tingadzakumane nawo, komanso kuti Yehova sadzatisiya, Bungwe Lolamulira lasankha Salimo 34:10, kuti likhale lemba la chaka cha 2022. Lembali limati: “Ofunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.”

NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa

^ ndime 5 Lemba la chaka cha 2022, lachokera pa Salimo 34:10. Lembali limati: “Ofunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.” Atumiki ambiri a Yehova alibe katundu kapena ndalama zambiri. Ndiye n’chifukwa chiyani tingati iwo ‘sasowa chilichonse chabwino’? Nanga kodi kumvetsa tanthauzo la vesi limeneli kungatithandize bwanji kukonzekera mavuto amene tingakumane nawo m’tsogolo?

^ ndime 4 Onani nkhani yakuti, “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2014.

^ ndime 8 Onani Nsanja ya Olonda ya May 1, 1999, tsamba 19.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Ngakhale pamene ankabisala kuphanga pothawa Mfumu Sauli, Davide ankayamikira zimene Yehova ankamupatsa.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Aisiraeli atachoka ku Iguputo, Yehova anawapatsa mana kuti azidya ndipo anachititsa kuti zovala zawo zisang’ambike.