Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 3

Zimene Tikuphunzira pa Misozi ya Yesu

Zimene Tikuphunzira pa Misozi ya Yesu

“Yesu anagwetsa misozi.”​—YOH. 11:35.

NYIMBO NA. 17 “Ndikufuna”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-3. Kodi ndi mavuto ati amene angachititse atumiki a Yehova kugwetsa misozi?

 KODI mukukumbukira ulendo womaliza umene munalira? Nthawi zina timagwetsa misozi chifukwa chosangalala. Koma nthawi zambiri timalira chifukwa chopwetekedwa mumtima. Mwachitsanzo, tikhoza kulira chifukwa choti munthu amene timamukonda wamwalira. Mlongo wina wa ku United States dzina lake Lorilei, analemba kuti: “Nthawi zina ululu umene ndinkamva chifukwa cha imfa ya mwana wanga wamkazi unkakhala waukulu moti ndinkangoona ngati palibe chimene chinganditonthoze. Pa nthawi zimenezi, ndinkangoona kuti sindingakwanitse kupirira.” *

2 Tingathenso kugwetsa misozi pazifukwa zina. Mpainiya wina wa ku Japan, dzina lake Hiromi, ananena kuti: “Nthawi zambiri ndimakhumudwa chifukwa anthu ambiri safuna kumvetsera ndikamawalalikira. Nthawi zina ndimapempha Yehova ndikugwetsa misozi kuti andithandize kupeza munthu wina yemwe akufunafuna choonadi.”

3 Kodi inunso munayamba mwamvapo ngati mmene ena aneneramu? Ambirife tinamvapo choncho. (1 Pet. 5:9) Timafuna kuti ‘tizitumikira Yehova mokondwera,’ koma mwina tingamamutumikire tikugwetsa misozi chifukwa choferedwa, zinthu zofooketsa kapenanso mavuto aakulu omwe angayese kukhulupirika kwathu kwa Yehova. (Sal. 6:6; 100:2) Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize tikamamva choncho?

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Tingaphunzirepo kanthu kuchokera pa chitsanzo cha Yesu. Nthawi zina iye ankakhudzidwa kwambiri mpaka kufika ‘pogwetsa misozi.’ (Yoh. 11:35; Luka 19:41; 22:44; Aheb. 5:7) Tiyeni tikambirane zimenezi ndipo tiona zimene tikuphunzirapo. Tikambirananso zimene tingachite ngati takumana ndi mavuto omwe achititsa kuti tigwetse misozi.

ANALIRA CHIFUKWA CHODERA NKHAWA ANZAKE

Muzithandiza amene aferedwa ngati mmene Yesu anachitira (Onani ndime 5-9) *

5. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yesu pa zimene zili pa Yohane 11:32-36?

5 Cha munyengo yozizira mu 32 C.E., Lazaro yemwe anali mnzake wapamtima wa Yesu anadwala n’kumwalira. (Yoh. 11:3, 14) Lazaro anali ndi azichemwali ake awiri, Mariya ndi Marita, ndipo Yesu ankakonda kwambiri banja limeneli. Akazi awiriwa anali ndi chisoni chachikulu chifukwa cha imfa ya mchimwene wawo. Lazaro atamwalira, Yesu anapita ku Betaniya kumene Mariya ndi Marita ankakhala. Marita atamva kuti Yesu akubwera, anathamanga kuti akakumane naye. Tangoganizani mmene iye ankamvera pamene anati: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.” (Yoh. 11:21) Pasanapite nthawi Yesu ataona Mariya ndi ena akulira, nayenso “anagwetsa misozi.”​—Werengani Yohane 11:32-36.

6. N’chifukwa chiyani Yesu analira Lazaro atamwalira?

6 N’chifukwa chiyani Yesu analira pa nthawiyi? Buku lina limayankha kuti: “‘Yesu anadzuma ndi kugwetsa misozi’ chifukwa cha imfa ya mnzake wapamtima Lazaro komanso chisoni chimene alongo ake a Lazaro anali nacho.” * Yesu ayenera kuti ankaganizira ululu umene mnzake wapamtimayo ankamva pamene ankadwala komanso mmene anamvera atazindikira kuti amwalira. Yesu ayeneranso kuti anagwetsa misozi poona mmene Mariya ndi Marita anakhudzidwira chifukwa cha imfa ya mlongo wawo. Ngati mnzanu wapamtima kapena wachibale wanu anamwalira, n’zosakayikitsa kuti inunso munamva chonchi. Tiyeni tione zinthu zitatu zimene tikuphunzirapo pa zimene zinachitikazi.

7. Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza Yehova pamene Yesu analira podera nkhawa anzake?

7 Yehova amamvetsa mmene tikumvera. Yesu ndi “chithunzi chenicheni” cha Atate wake. (Aheb. 1:3) Iye atagwetsa misozi, anasonyeza mmene Yehova amamvera. (Yoh. 14:9) Ngati muli ndi chisoni chifukwa cha imfa ya munthu amene munkamukonda, mungakhale otsimikiza kuti sikuti Yehova amangoona zimenezo, koma amakhudzidwanso chifukwa cha mmene mukumvera. Iye amafuna kukutonthozani.​—Sal. 34:18; 147:3.

8. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yesu adzaukitsa okondedwa athu?

8 Yesu amafunitsitsa kudzaukitsa okondedwa anu. Asanalire, Yesu anatsimikizira Marita kuti: “Mlongo wako adzauka.” Marita anakhulupirira zimenezi. (Yoh. 11:23-27) Monga mtumiki wokhulupirika wa Yehova, Marita ayenera kuti ankadziwa kuti zaka zambiri m’mbuyomo, mneneri Eliya komanso Elisa anaukitsapo anthu. (1 Maf. 17:17-24; 2 Maf. 4:32-37) N’kuthekanso kuti anamvapo za anthu amene Yesu anawaukitsa. (Luka 7:11-15; 8:41, 42, 49-56) Inunso mungakhale otsimikiza kuti mudzaonanso okondedwa anu amene anamwalira. Kulira kwa Yesu pamene ankatonthoza anzake omwe anali ndi chisoni ndi umboni woti Yesu amafunitsitsa kudzaukitsa akufa.

9. Mofanana ndi Yesu, kodi mungathandize bwanji amene ali ndi chisoni chifukwa choferedwa? Perekani chitsanzo.

9 Mungathe kuthandiza amene aferedwa. Kuwonjezera pa kulira ndi Marita ndi Mariya, Yesu ankawamvetsera komanso kuwatonthoza. Ifenso tingachite zimenezi kwa amene ali ndi chisoni chifukwa choferedwa. Dan, yemwe amakhala ku Australia, ananena kuti: “Mkazi wanga atamwalira, ndinkafunika kuthandizidwa. Mabanja angapo ankakhala nane nthawi zonse ndipo ankandimvetsera ndikamalankhula. Iwo sankandiletsa kusonyeza chisoni changa ndipo sankakhumudwa ndikamalira. Ankandithandizanso m’njira zina monga kunditsukira galimoto, kukandigulira zinthu komanso kundiphikira ngati ndikulephera kuchita zinthu zimenezi ndekha. Ankapempheranso nane pafupipafupi. Iwo anasonyeza kuti anali anzanga enieni ndiponso m’bale amene ‘anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.’”​—Miy. 17:17.

ANALIRA CHIFUKWA CHODERA NKHAWA ANTHU ENA

10. Fotokozani zochitika zomwe zili pa Luka 19:36-40.

10 Yesu anafika ku Yerusalemu pa Nisani 9, mu 33 C.E. Pamene ankayandikira mzindawo, khamu lalikulu la anthu linayala zovala zawo mumsewu povomereza kuti iye ndi Mfumu yawo. Imeneyitu inali nthawi yosangalatsa. (Werengani Luka 19:36-40.) Mwina ophunzira ake sanayembekezere zimene zinachitika pambuyo pake. “[Yesu] atayandikira mzinda wa Yerusalemu, anaona mzindawo n’kuyamba kuulirira.” Misozi ili m’maso, iye ananeneratu zinthu zoopsa zimene zidzachitikire anthu a mu Yerusalemu.​—Luka 19:41-44.

11. N’chifukwa chiyani Yesu analirira anthu a mu Yerusalemu?

11 Ngakhale kuti Yesu analandiridwa bwino pa tsikuli, iye anamva kupweteka mumtima chifukwa Ayuda ambiri anali atasonyeza kuti sankafuna kumvetsera uthenga wa Ufumu. Chifukwa cha zimenezi, mzinda wa Yerusalemu ukanawonongedwa ndipo Ayuda omwe akanapulumuka akanatengedwa kupita ku ukapolo. (Luka 21:20-24) N’zomvetsa chisoni kuti monga mmene iye ananenera, anthu ambiri anamukanadi. Kodi anthu ambiri kudera limene mumakhala amamvetsera uthenga wa Ufumu? Ngati ndi anthu ochepa amene amamvetsera mukamayesetsa kuwaphunzitsa choonadi, kodi mungaphunzire chiyani pa misozi ya Yesu? Taganizirani zinthu zitatu zinanso zimene tikuphunzirapo.

12. Kodi tingaphunzire chiyani zokhudza Yehova pa zimene Yesu anachita polirira anthu ena?

12 Yehova amadera nkhawa anthu. Misozi ya Yesu imatikumbutsa kuti Yehova amaganizira kwambiri anthu. “Safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Masiku ano timasonyeza kuti timakonda anthu ena poyesetsa kuwathandiza kuti amve uthenga wabwino wa Ufumu.​—Mat. 22:39. *

Muzisintha nthawi yolalikirira ngati mmene Yesu anachitira (Onani ndime 13-14) *

13-14. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankachitira anthu chifundo, nanga tingatani kuti tikhale ndi khalidwe limeneli?

13 Yesu ankachita khama pa ntchito yolalikira. Iye anasonyeza kuti ankakonda anthu powaphunzitsa pa mpata uliwonse umene wapezeka. (Luka 19:47, 48) N’chiyani chinkamuchititsa zimenezi? Ankawachitira chifundo. Nthawi zambiri anthu ankafuna kumvetsera mawu ake ndipo iye limodzi ndi ophunzira ake ‘sankatha n’komwe kudya chakudya.’ (Maliko 3:20) Pa nthawi ina Yesu anaphunzitsa munthu wina usiku, nthawi yomwe inali yabwino kwa munthuyo. (Yoh. 3:1, 2) Anthu ambiri omwe poyamba anamvetsera uthenga wake, sanakhale ophunzira ake. Koma onse omwe anamumvetsera, Yesu anawachitira umboni mokwanira. Masiku ano timafunika kuthandiza aliyense kuti amve uthenga wabwino. (Mac. 10:42) Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, mwina tingafunike kusintha zinthu zina pa nkhani yolalikira.

14 Muzikhala okonzeka kusintha. Ngati sitingasinthe nthawi yolalikirira, mwina sitingakwanitse kulalikira anthu amene angamvetsere uthenga wabwino. Mpainiya wina dzina lake Matilda ananena kuti: “Ine ndi mwamuna wanga timayesetsa kulalikira anthu pa nthawi zosiyanasiyana. Kum’mawa timakalalikira kumalo azamalonda. Masana pamene anthu ambiri amapezeka mumsewu, timalalikira pogwiritsa ntchito timashelefu. Chakumadzulo timaona kuti zimakhala bwino kukalalikira anthu kunyumba zawo.” M’malo molalikira pa nthawi yomwe ndi yabwino kwa ife, tizikhala okonzeka kusintha n’cholinga choti tizilalikira pa nthawi imene tingakumane ndi anthu. Tikamachita zimenezi, tikhoza kukhala otsimikiza kuti Yehova akusangalala nafe.

ANALIRA CHIFUKWA CHODERA NKHAWA DZINA LA ATATE WAKE

Muzipemphera mopembedzera kwa Yehova mukamada nkhawa ngati mmene Yesu anachitira (Onani ndime 15-17) *

15. Mogwirizana ndi Luka 22:39-44, kodi n’chiyani chinachitika pa usiku womaliza wa moyo wa Yesu?

15 Usiku pa Nisani 14, 33 C.E., Yesu anapita kumunda wa Getsemane. Kumeneko iye anayamba kupemphera kwambiri kwa Yehova. (Werengani Luka 22:39-44.) Ndi pa nthawi yovuta imeneyi pamene Yesu “anapereka mapemphero opembedzera, . . . mofuula komanso akugwetsa misozi.” (Aheb. 5:7) Kodi n’chiyani chimene Yesu ankapempherera pa usiku wake womaliza asanaphedwe? Iye anapempha Yehova kuti amupatse mphamvu n’cholinga choti akhalebe wokhulupirika komanso achite chifuniro chake. Yehova anamva pemphero lochokera pansi pamtima la Mwana wakeyu ndipo anatumiza mngelo kuti adzamulimbikitse.

16. N’chifukwa chiyani Yesu anavutika mumtima pamene ankapemphera m’munda wa Getsemane?

16 N’zosakayikitsa kuti Yesu analira pamene ankapemphera m’munda wa Getsemane chifukwa chovutika ndi maganizo oti azionedwa monga wonyoza Mulungu. Iye ankadziwanso kuti anali ndi udindo waukulu kwambiri woyeretsa dzina la Atate wake. Ngati mukukumana ndi zinthu zodetsa nkhawa zomwe zikuyesa kukhulupirika kwanu kwa Yehova, kodi mungaphunzire chiyani pa zimene Yesu anachita pogwetsa misozi? Taganizirani mfundo zina zitatu zomwe tikuphunzirapo.

17. Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza Yehova pamene anayankha mapemphero a Yesu ochokera pansi pamtima?

17 Yehova amamvetsera mapemphero anu opembedzera. Iye anamvetsera pamene Yesu ankapemphera mochokera pansi pamtima. Chifukwa chiyani? Chifukwa Yesu ankadera nkhawa kwambiri zokhudza kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova komanso kuyeretsa dzina lake. Ngati timadera nkhawa kwambiri zokhudza kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova komanso kuyeretsa dzina lake, iye adzayankha mapemphero athu.​—Sal. 145:18, 19.

18. Kodi Yesu ali ngati mnzathu amene amatimvetsa m’njira iti?

18 Yesu amamvetsa mmene timamvera. Tikapanikizika ndi nkhawa, timayamikira mnzathu amene amatimvetsa akatitonthoza, makamaka ngati mnzathuyo anakumanapo ndi mavuto ngati amene ifenso takumana nawo. Yesu ndi mnzathu ameneyu. Iye amadziwa mmene zimakhalira ukafooka komanso ukamafuna kuti ena akuthandize. Amadziwa zofooka zathu ndipo adzaonetsetsa kuti tathandizidwa “pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheb. 4:15, 16) Mofanana ndi Yesu yemwe anavomera kuthandizidwa ndi mngelo m’munda wa Getsemane, ifenso tiyenera kukhala okonzeka kulandira thandizo lomwe Yehova angatipatse kudzera m’mabuku athu, mavidiyo, nkhani kapenanso kudzera mwa mkulu, m’bale kapena mlongo yemwe wabwera kudzatilimbikitsa.

19. Kodi tingatani kuti tipezenso mphamvu ngati takumana ndi mavuto omwe angachititse kuti tisakhale okhulupirika kwa Mulungu? Perekani chitsanzo.

19 Yehova adzatipatsa “mtendere” wake. Kodi Yehova amatilimbikitsa bwanji? Tikamapemphera, iye amatipatsa “mtendere [wake] umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afil. 4:6, 7) Mtendere umene Yehova amatipatsa umatithandiza kuti mtima wathu ukhale pansi komanso kuti tiziganiza bwino. Zimenezi ndi zomwe zinachitikira mlongo wina dzina lake Luz. Iye anati: “Nthawi zambiri ndimavutika ndi maganizo odziona kuti ndili ndekhandekha. Nthawi zina maganizo amenewa amandichititsa kuona ngati Yehova sandikonda. Koma ndikangoyamba kukhala ndi maganizo amenewa, nthawi yomweyo ndimafotokozera Yehova mmene ndikumvera. Pemphero limandithandiza kuti ndiyambenso kuganiza bwino.” Zimene zinachitikira mlongoyu zikusonyeza kuti tingapeze mtendere tikamapemphera.

20. Kodi taphunzira chiyani pa zimene Yesu anachita pogwetsa misozi?

20 Tingaphunzire mfundo zolimbikitsa komanso zothandiza kuchokera pa zimene Yesu anachita pogwetsa misozi. Taona kuti tifunika kuthandiza mnzathu amene ali ndi chisoni chifukwa choferedwa komanso kumakhulupirira kuti Yehova ndi Yesu angatithandize ngati munthu amene timamukonda wamwalira. Taonanso kuti chifundo chizitichititsa kulalikira ndi kuphunzitsa anthu chifukwa Mulungu ndi Yesu Khristu amasonyeza khalidwe labwinoli. Timalimbikitsidwanso kudziwa kuti Yehova ndi Mwana wake wokondedwa amamvetsa mmene timamvera, amatichitira chifundo pa zofooka zathu komanso amafuna kutithandiza kuti tipirire. Tiyeni tipitirize kutsatira zimene taphunzira mpaka tsiku limene Yehova adzakwaniritse lonjezo lake losangalatsa lakuti “adzapukuta misozi yonse m’maso [mwathu].”​—Chiv. 21:4.

NYIMBO NA. 120 Tikhale Ofatsa Ngati Khristu

^ ndime 5 Nthawi zina Yesu ankakhudzidwa kwambiri moti ankagwetsa misozi. Munkhaniyi tikambirana zochitika zitatu pamene zimenezi zinamuchitikira ndiponso zomwe tingaphunzirepo.

^ ndime 1 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 6 Onani buku lachingelezi lakuti Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 69.

^ ndime 12 Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “mnzako” pa Mateyu 22:39, sikuti amangonena za munthu amene timakhala moyandikana naye. Mawuwa anganenenso za munthu amene timachita naye zinthu.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Yesu anatonthoza Mariya ndi Marita. Ifenso tingachite zimenezi kwa amene aferedwa.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mofunitsitsa Yesu anaphunzitsa Nikodemo usiku. Tiziphunzira Baibulo ndi anthu pa nthawi yomwe ndi yabwino kwa iwowo.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Yesu anapempha Yehova kuti amupatse mphamvu n’cholinga choti akhalebe wokhulupirika. Ifenso tiyenera kuchita zimenezi tikamayesedwa.