Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 5

“Chikondi Chimene Khristu Ali Nacho Chimatikakamiza”

“Chikondi Chimene Khristu Ali Nacho Chimatikakamiza”

“Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza . . . kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha.”—2 AKOR. 5:14, 15.

NYIMBO NA. 13 Khristu Ndi Chitsanzo Chathu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1-2. (a) Kodi tingamamve bwanji tikaganizira moyo wa Yesu komanso utumiki wake? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

 MUNTHU yemwe timamukonda akamwalira timamusowa kwambiri. Poyamba tingamamve chisoni tikaganizira zimene zinachitika atatsala pang’ono kumwalira, makamaka ngati anavutika kwambiri pa nthawiyo. Komabe n’kupita kwa nthawi tingayambe kusangalala tikamaganizira zinazake zomwe anatiphunzitsa, zimene anachita kapenanso zimene analankhula n’cholinga choti atilimbikitse kapena tisekerere.

2 Mofanana ndi zimenezi, timamva chisoni tikawerenga zokhudza kuvutika komanso imfa ya Yesu. Pa nyengo ya Chikumbutso timaganizira makamaka kufunika kwa nsembe yake ya dipo. (1 Akor. 11:24, 25) Komabe timasangalala kwambiri tikaganizira zonse zimene ananena komanso kuchita ali padzikoli. Timalimbikitsidwanso tikaganizira zimene akuchita panopa ndiponso zimene adzatichitire m’tsogolo. Kuganizira zimenezi komanso chikondi chake kwa ife kungatichititse kuyamikira m’njira zosiyanasiyana, monga mmene tionere munkhaniyi.

KUYAMIKIRA KUMATICHITITSA KUTI TIZITSANZIRA YESU

3. Kodi tili ndi zifukwa ziti zotichititsa kuyamikira dipo?

3 Timayamikira kwambiri tikaganizira moyo wa Yesu komanso imfa yake. Pa utumiki wake wonse ali padzikoli, Yesu ankaphunzitsa anthu zokhudza madalitso omwe Ufumu wa Mulungu udzabweretse. Timayamikira mfundo za choonadi zokhudza Ufumuzi. Timayamikiranso dipo chifukwa limatipatsa mwayi wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndi Yesu. Onse amene amakhulupirira Yesu alinso ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo mpaka kalekale komanso kudzaona okondedwa awo omwe anamwalira. (Yoh. 5:28, 29; Aroma 6:23) Palibe chomwe tinachita kuti tiyenerere madalitso amenewa, komanso sitingathe kubwezera Mulungu ndi Yesu pa zonse zomwe anatichitira. (Aroma 5:8, 20, 21) Komabe tingathe kuwasonyeza kuti timayamikira kwambiri. Motani?

Kodi kuganizira chitsanzo cha Mariya Mmagadala kungatilimbikitse bwanji kuti tizikhala oyamikira? (Onani ndime 4-5)

4. Kodi Mariya Mmagadala anasonyeza bwanji kuti ankayamikira zomwe Yesu anamuchitira? (Onani chithunzi.)

4 Taganizirani chitsanzo cha mayi wina wa Chiyuda dzina lake Mariya Mmagadala. Iye anali pamavuto aakulu chifukwa ankazunzidwa ndi ziwanda 7. N’kutheka kuti iye ankaganiza kuti mavuto akewa sangathe. Ndiye tangoganizani mmene anayamikirira Yesu atamutulutsa ziwandazo. Kuyamikiraku kunachititsa kuti iye akhale wotsatira wa Yesu komanso kuti azigwiritsa ntchito nthawi, mphamvu ndi zinthu zake pothandiza Yesu pa ntchito yolalikira. (Luka 8:1-3) Ngakhale kuti Mariya ankayamikira mochokera pansi pa mtima zimene Yesu anamuchitira, n’kutheka kuti sankadziwa kuti iye adzamupatsanso mphatso yaikulu m’tsogolo. Yesu anali kudzapereka moyo wake chifukwa cha anthu “kuti aliyense wokhulupirira iye” adzapeze moyo wosatha. (Yoh. 3:16) Komabe anasonyeza kuti ankayamikira Yesu pokhala wokhulupirika. Pamene Yesu ankavutika ndi ululu pamtengo wozunzikirapo, Mariya anaima chapafupi kuti alimbikitse Yesuyo ndi anthu ena. (Yoh. 19:25) Yesu atafa, Mariya ndi amayi ena awiri anabweretsa zonunkhira zoti apake thupi lake asanaliike m’manda. (Maliko 16:1, 2) Iye anadalitsidwa kwambiri chifukwa cha kukhulupirika kwake. Anali ndi mwayi wokumana ndi Yesu komanso kulankhula naye ataukitsidwa, mwayi womwe ophunzira ambiri analibe.​—Yoh. 20:11-18.

5. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova ndi Yesu pa zimene anatichitira?

5 Ifenso tingasonyeze kuti timayamikira Yehova ndi Yesu pa zimene anatichitira pogwiritsa ntchito nthawi, mphamvu ndi ndalama zathu popititsa patsogolo ntchito ya Ufumu. Mwachitsanzo, tingathandize nawo pa ntchito yomanga ndi kukonza malo amene timagwiritsa ntchito pa kulambira koona.

KUKONDA YEHOVA NDI YESU KUMATILIMBIKITSA KUTI TIZIKONDA ENA

6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti dipo ndi mphatso imene inaperekedwa kwa munthu aliyense payekha?

6 Tikaganizira mmene Yehova ndi Yesu anatisonyezera chikondi, timafunitsitsa kuti ifenso tiziwakonda. (1 Yoh. 4:10, 19) Timawakonda kwambiri tikazindikira kuti Yesu anatifera ifeyo aliyense payekha. Mtumwi Paulo ankadziwa mfundo imeneyi ndipo anasonyeza kuyamikira kwake pomwe analembera Akhristu a ku Galatiya kuti: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” (Agal. 2:20) Pogwiritsa ntchito dipo, Yehova anatikokera kwa iye kuti tikhale anzake. (Yoh. 6:44) Kodi simumasangalala kudziwa kuti Yehova anaona kanthu kenakake kabwino mwa inu ndiponso kuti anapereka mtengo wokwera n’cholinga choti mukhale mnzake? Kodi izi sizikuchititsani kuti muzikonda kwambiri Yehova ndi Yesu? Mungachite bwino kumadzifunsa kuti, ‘Kodi chikondi chimenechi chizindilimbikitsa kuchita chiyani?’

Kukonda Mulungu ndi Khristu kumatichititsa kuuza anthu a mitundu yonse uthenga wa Ufumu (Onani ndime 7)

7. Monga tikuonera pachithunzichi, kodi tonsefe tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova ndi Yesu? (2 Akorinto 5:14, 15; 6:1, 2)

7 Kukonda Mulungu ndi Khristu kumatichititsa kuti tizikondanso ena. (Werengani 2 Akorinto 5:14, 15; 6:1, 2.) Njira imodzi imene timasonyezera chikondicho ndi kugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira. Timalalikira kwa aliyense amene takumana naye. Sitimasankha munthu chifukwa cha mtundu wake, chikhalidwe, kapezedwe kake ka zinthu kapenanso maphunziro ake. Tikamachita zimenezi timakhala tikuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”​—1 Tim. 2:4.

8. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale ndi alongo athu?

8 Timasonyezanso kuti timakonda Mulungu ndi Khristu tikamakonda abale ndi alongo athu. (1 Yoh. 4:21) Timawaganizira ndipo timawathandiza akakumana ndi mayesero. Timawatonthoza akaferedwa, kukawaona akadwala komanso timachita zonse zomwe tingathe kuti tiwalimbikitse pamene afooka. (2 Akor. 1:3-7; 1 Ates. 5:11, 14) Timapitiriza kuwapempherera chifukwa timadziwa kuti “pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.”​—Yak. 5:16.

9. Kodi ndi njira ina iti yomwe tingasonyezere kuti timakonda abale ndi alongo athu?

9 Timasonyezanso kuti timakonda abale ndi alongo athu tikamayesetsa kukhala nawo mwamtendere. Timayesetsa kutengera chitsanzo cha Yehova pa nkhani yokhululukira ena. Ngati Yehova analolera kuti Mwana wake afe chifukwa cha machimo athu, kodi ifenso sitiyenera kukhala okonzeka kukhululukira abale ndi alongo athu akatilakwira? Sitingafune kukhala ngati kapolo woipa yemwe anatchulidwa m’fanizo lina la Yesu. Ngakhale kuti mbuye wake anamukhululukira ngongole yaikulu, iye analephera kukhululukira kapolo mnzake ngongole yaing’ono. (Mat. 18:23-35) Ngati munasemphana maganizo ndi munthu wina mumpingo, kodi mungayambepo kukhazikitsa mtendere isanafike nthawi ya Chikumbutso? (Mat. 5:23, 24) Kuchita zimenezo kungasonyeze kuti mumakonda kwambiri Yehova ndi Yesu.

10-11. Kodi akulu angasonyeze bwanji kuti amakonda Yehova ndi Yesu? (1 Petulo 5:1, 2)

10 Kodi akulu angasonyeze bwanji kuti amakonda Yehova ndi Yesu? Njira yofunika kwambiri yomwe angachitire zimenezi ndi kusamalira nkhosa za Yesu. (Werengani 1 Petulo 5:1, 2.) Yesu anasonyeza bwino mfundo imeneyi pamene ankalankhula ndi mtumwi Petulo. Pambuyo pokana Yesu maulendo atatu, Petulo ayenera kuti ankafunitsitsa kuti asonyeze Yesu kuti amamukonda. Ataukitsidwa, Yesu anafunsa Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda?” Sitikukayikira kuti Petulo akanachita chilichonse pofuna kusonyeza kuti amakonda Mbuye wake. Yesu anauza Petulo kuti: “Weta ana a nkhosa anga.” (Yoh. 21:15-17) Kwa moyo wake wonse Petulo ankasamalira mwachikondi nkhosa za Ambuye posonyeza kuti amawakonda.

11 Akulu, kodi mungasonyeze bwanji pa nyengo ya Chikumbutso kuti mawu amene Yesu anauza Petulo ndi ofunikanso kwa inu? Mungasonyeze kuti mumakonda Yehova ndi Yesu poyesetsa kuti nthawi zonse muzipeza nthawi yolimbikitsa abale ndi alongo, komanso pochita khama kuthandiza amene anafooka kuti abwerere kwa Yehova. (Ezek. 34:11, 12) Muzichitanso chidwi ndi amene akuphunzira Baibulo komanso amene afika ku Chikumbutso kwa nthawi yoyamba kuti azidzimva kukhala olandiridwa. Muzikumbukira kuti iwowa angathe kudzakhala ophunzira a Yesu.

KUKONDA KHRISTU KUMATICHITITSA KUKHALA OLIMBA MTIMA

12. N’chifukwa chiyani kuganizira mawu amene Yesu analankhula pa usiku wake womaliza kungatithandize kukhala olimba mtima? (Yohane 16:32, 33)

12 Pa usiku wake womaliza Yesu anauza ophunzira ake kuti: “M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.” (Werengani Yohane 16:32, 33) Kodi n’chiyani chinathandiza Yesu kuti alimbe mtima kukumana ndi adani ake komanso kukhalabe wokhulupirika mpaka imfa? Iye ankadalira Yehova. Podziwa kuti otsatira ake adzakumananso ndi mayesero ngati amenewa, Yesu anapempha Yehova kuti aziwayang’anira. (Yoh. 17:11) N’chifukwa chiyani zimenezi zimatithandiza kukhala olimba mtima? Chifukwa Yehova ndi wamphamvu kuposa adani athu. (1 Yoh. 4:4) Iye amaona chilichonse. Timakhulupirira kuti tikamamudalira, angatithandize kuti tisamaope ndiponso tikhale olimba mtima.

13. Kodi Yosefe wa ku Arimateya anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima?

13 Taganizirani chitsanzo cha Yosefe wa ku Arimateya. Iye ankalemekezedwa kwambiri ndi Ayuda anzake. Yosefe anali mmodzi wa oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda lotchedwa Sanihedirini. Koma pamene Yesu ankachita utumiki wake padzikoli, Yosefe sanali wolimba mtima. Yohane ananena kuti iye anali “wophunzira wa Yesu koma wamseri chifukwa anali kuopa Ayuda.” (Yoh. 19:38) Ngakhale kuti Yosefe ankachita chidwi ndi uthenga wa Ufumu, sanauze ena kuti ankakhulupirira Yesu. Mosakayikira, iye ankaopa kuti ataya udindo wake wapamwamba. Koma Baibulo limatiuza kuti Yesu atafa, pamapeto pake Yosefe “anapita kwa Pilato molimba mtima kukapempha mtembo wa Yesu.” (Maliko 15:42, 43) Apa Yosefe sanadzibisenso kuti anali wophunzira wa Yesu.

14. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mumaopa anthu?

14 Kodi nanunso munayamba mwachitapo mantha ngati mmene anachitira Yosefe? Mukakhala kusukulu kapena kuntchito, kodi nthawi zina mumachita manyazi kuuza ena kuti ndinu wa Mboni za Yehova? Kodi mumazengereza kukhala wofalitsa kapena kubatizidwa chifukwa choopa zimene ena aziganiza zokhudza inuyo? Musamalole zimenezi kukulepheretsani kuchita zimene mukudziwa kuti n’zoyenera. Muzipemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. Muzimupempha kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima kuti muchite chifuniro chake. Mukamaona mmene Yehova akuyankhira mapemphero anu, mudzakhala amphamvu komanso olimba mtima kwambiri.​—Yes. 41:10, 13.

CHIMWEMWE CHIMATILIMBIKITSA KUTI TIZITUMIKIRA YEHOVA MWAKHAMA

15. Pambuyo poti Yesu waonekera kwa ophunzira ake, kodi chimwemwe chawo chinawalimbikitsa kuchita chiyani? (Luka 24:52, 53)

15 Pamene Yesu anaphedwa, ophunzira ake anakhumudwa kwambiri. Taganizirani mmene inunso mukanamvera mukanakhalapo pa nthawiyo. Sikuti iwo ankangoona kuti ataya mnzawo wapamtima koma ankaonanso kuti alibe chiyembekezo. (Luka 24:17-21) Komabe ataonekera kwa iwo, Yesu anawathandiza kumvetsa mmene zomwe zinamuchitikira zinakwaniritsira ulosi wa m’Baibulo. Anawapatsanso ntchito yofunika kwambiri yoti agwire. (Luka 24:26, 27, 45-48) Pamene Yesu ankakwera kumwamba pambuyo pa masiku 40, chisoni cha ophunzirawo chinasanduka chimwemwe chachikulu. Kudziwa kuti Mbuye wawo ali moyo komanso ndi wokonzeka kuwathandiza pantchito yatsopano imene anawapatsa, kunawathandiza kukhala osangalala. Chimwemwe chimene anali nacho chinawathandiza kuti azitamanda Yehova mwakhama.​—Werengani Luka 24:52, 53; Mac. 5:42.

16. Kodi tingatsanzire bwanji ophunzira a Yesu?

16 Kodi tingatsanzire bwanji ophunzira a Yesu? Tingapeze chimwemwe polambira Yehova osati pa nyengo ya Chikumbutso yokha koma chaka chonse. Zimenezi zimafuna kuti tiziika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba. Mwachitsanzo, ambiri asintha mmene amagwirira ntchito zawo kuti azigwira nawo ntchito yolalikira, kupezeka pamisonkhano komanso azichita kulambira kwa pabanja nthawi zonse. Enanso afika mpaka pololera kusakhala ndi zinthu zomwe anthu ena amaona kuti n’zofunika kwambiri n’cholinga choti azichita zambiri mumpingo kapena akatumikire kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Ngakhale kuti timafunika kupirira kuti tipitirize kutumikira Yehova, iye amalonjeza kuti adzatidalitsa kwambiri tikamaika zokhudza Ufumu pamalo oyamba.​—Miy. 10:22; Mat. 6:32, 33.

Pa nyengo ya Chikumbutso, muzipeza nthawi yoganizira zimene Yehova ndi Yesu akuchitirani inuyo panokha (Onani ndime 17)

17. Kodi mwatsimikiza kuchita chiyani pa nyengo ya Chikumbutsoyi? (Onani chithunzi.)

17 Tikuyembekezera mwachidwi kudzachita Chikumbutso Lachiwiri pa 4 April. Komabe sitikufunika kuchita kuyembekezera nthawi imeneyo kuti tidzaganizire za moyo wa Yesu ndi imfa yake komanso chikondi chimene iye ndi Atate wake anatisonyeza. Tidzagwiritse ntchito mwayi uliwonse umene wapezeka kuti tichite zimenezi pa nyengo yonse ya Chikumbutso. Mwachitsanzo, tingakonze zoti tidzawerenge komanso kuganizira zochitika zomwe zili pa tchati chakuti “Wiki Yomaliza ya Moyo wa Yesu Padziko Lapansi,” mu Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu, mutu 16. Pamene mukuwerenga muziona mfundo za m’Baibulo zokuthandizani kukhala oyamikira, achikondi, olimba mtima ndiponso achimwemwe. Kenako muziganizira njira zomwe mungasonyezere kuyamikira mochokera pansi pa mtima. Mungakhale otsimikiza kuti Yesu adzayamikira zonse zomwe mudzachite pomukumbukira pa nyengo ya Chikumbutsoyi.​—Chiv. 2:19.

NYIMBO NA. 17 “Ndikufuna”

a Pa nyengo ya Chikumbutso timalimbikitsidwa kuti tiziganizira moyo wa Yesu ndi imfa yake komanso chikondi chimene iye ndi Atate wake anatisonyeza. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tiziwayamikira. Nkhaniyi isonyeza njira zimene tingasonyezere kuti timayamikira dipo komanso kuti timakonda Yehova ndi Yesu. Tionanso mmene zimenezi zingatilimbikitsire kuti tizikonda abale ndi alongo athu, tizikhala olimba mtima ndiponso tizisangalala ndi utumiki wathu.