Kodi Mukudziwa?
Kodi nduna ya ku Itiyopiya inakwera galeta lotani pamene inakumana ndi Filipo?
MAWU oyambirira amene anawamasulira kuti “galeta” mu Baibulo la Dziko Latsopano angatanthauze mitundu yosiyanasiyana ya magaleta. (Mac. 8:28, 29, 38) Koma zikuoneka kuti munthu wa ku Itiyopiyayu anakwera galeta lokulirapo kuposa lankhondo kapena lochitira mpikisano. N’chifukwa chiyani tikutero?
Munthu wa ku Itiyopiyayu anali waudindo waukulu ndipo anayenda ulendo wautali. Iye “anali ndi udindo waukulu ndipo ankathandiza Kandake, mfumukazi ya Itiyopiya. Ankayang’aniranso chuma chonse cha mfumukaziyo.” (Mac. 8:27) Dziko la Itiyopiya linkaphatikizapo dziko limene panopa limadziwika kuti Sudan komanso kum’mwera kwenikweni kwa dziko la Egypt. Ngakhale kuti mwina ndunayi sinayende pagaletali ulendo wonsewu, iyenera kuti inali ndi katundu chifukwa ulendowu unali wautali. Ena mwa magaleta omwe ankagwiritsidwa ntchito kalelo ponyamula anthu, ankakhala ndi denga komanso matayala 4. Buku lina linanena kuti “magaleta oterewa, ankakhala ndi malo okwanira oika katundu, ankatha kuyenda mtunda wautali komanso munthu ankakhala momasuka.”—Acts—An Exegetical Commentary.
Munthu wa ku Itiyopiyayu anali akuwerenga pamene Filipo anakumana naye. Nkhaniyo imati “Filipo anathamanga n’kumayenda m’mbali mwa galetalo ndipo anamumva akuwerenga mokweza ulosi wa mneneri Yesaya.” (Mac. 8:30) Magaleta okwera anthu sankathamanga kwambiri. Chifukwa chakuti galetalo linkayenda pang’onopang’ono, zinali zotheka kuti ndunayo iziwerenga komanso kuti Filipo athe kuyenda nalo n’kumamva zimene akuwerenga.
Munthu wa ku Itiyopiyayu “anapempha Filipo kuti akwere n’kukhala naye m’galetamo.” (Mac. 8:31) Mugaleta lampikisano, wokwera galetalo ankaimirira. Koma mugaleta lonyamula anthu munali malo oti Filipo komanso ndunayo akhoza kukhala pansi.
Mogwirizana ndi zimene timawerenga m’buku la Machitidwe chaputala 8 komanso umboni wopezeka m’mabuku a mbiri yakale, mabuku athu akhala akusonyeza zithunzi zosonyeza nduna ya ku Itiyopiya itakwera galeta lalikulu kuposa lankhondo kapena lampikisano.