Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 2

NYIMBO NA. 132 Tsopano Ndife Thupi Limodzi

Amuna, Muzilemekeza Akazi Anu

Amuna, Muzilemekeza Akazi Anu

“Inunso amuna, . . . muziwapatsa ulemu.”1 PET. 3:7.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tikambirana mmene mawu ndi zochita za mwamuna zingasonyezere kuti amalemekeza mkazi wake.

1. N’chifukwa chiyani Yehova anayambitsa ukwati?

 YEHOVA ndi “Mulungu wachimwemwe,” ndipo amafuna kuti ifenso tizisangalala. (1 Tim. 1:11) Watipatsa mphatso zambiri zotithandiza kuti tizisangalala. (Yak. 1:17) Imodzi mwa mphatso zimenezi ndi banja. Mwamuna ndi mkazi akakwatirana amalonjezana kuti azikondana, kulemekezana komanso kusamalirana. Iwo akamagwirizana amakhala osangalala kwambiri.—Miy. 5:18.

2. Kodi n’chiyani chikuchitika m’mabanja ambiri masiku ano?

2 Anthu ambiri amaiwala zimene analonjeza patsiku laukwati. Ndipo zotsatira zake ndi zoti sakhala osangalala. Lipoti laposachedwapa la Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linasonyeza kuti amuna ambiri amamenya akazi awo, kuwalankhula mawu achipongwe kapena kuwazunza m’njira zina. Amalemekeza akazi awo akakhala pagulu koma n’kumakawazunza akapita kunyumba. Mabanja ambiri sayendanso bwino ngati mwamuna amaonera zolaula.

3. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingachititse mwamuna kukhala wankhanza?

3 N’chifukwa chiyani amuna ena amazunza akazi awo? Mwina analeredwa ndi bambo wankhanza choncho amaganiza kuti palibe vuto kuchitira ena nkhanza. Ena amayendera chikhalidwe cholakwika choti mwamuna weniweni ayenera kusonyeza mphamvu kuti azilemekezedwa. Pomwe amuna ena sanaphunzitsidwe kudziletsa. Amuna ena amakhala ndi maganizo olakwika okhudza akazi komanso kugonana chifukwa choonera zolaula. Kuwonjezera pamenepa, malipoti akusonyeza kuti mliri wa COVID-19 wawonjezera mavuto amenewa. Komabe zimenezi si zifukwa zomveka zochititsa kuti amuna azichitira nkhanza akazi awo.

4. Kodi amuna a Chikhristu ayenera kupewa chiyani?

4 Akhristu ayenera kupewa maganizo olakwika okhudza akazi. a Chifukwa chiyani? Tikutero chifukwa zimene munthu amachita zimayamba ndi kuganiza. Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu odzozedwa ku Roma kuti ‘asamatengere nzeru za nthawi ino.’ (Aroma 12:1, 2) Pamene Paulo ankalemba kalatayi mpingo wa ku Roma unali utakhalapo kwa nthawi yaitali. Koma mawu a Paulowa akusonyeza kuti ena mumpingowo ankayendera maganizo komanso chikhalidwe cha m’dzikoli. N’chifukwa chake anawalimbikitsa kuti asinthe maganizo ndi khalidwe lawo. Malangizo amenewa ndi othandizanso kwa amuna a Chikhristu masiku ano. N’zomvetsa chisoni kuti ena atengera maganizo a m’dzikoli ndipo amachitira nkhanza akazi awo. b Koma kodi Yehova amafuna kuti amuna azichita bwanji zinthu ndi akazi awo? Tikupeza yankho la funso limeneli mulemba limene likutsogolera nkhaniyi.

5. Mogwirizana ndi 1 Petulo 3:7, kodi amuna ayenera kuchita zinthu bwanji ndi akazi awo?

5 Werengani 1 Petulo 3:7. Yehova amalamula amuna kuti azilemekeza akazi awo. Mwamuna amene amalekeza mkazi wake amachita naye zinthu mokoma mtima komanso mwachikondi. Munkhaniyi tikambirana zimene mwamuna angachite posonyeza kuti amalemekeza mkazi wake. Koma choyamba tiyeni tikambirane makhalidwe amene angasonyeze kuti mwamuna sakulemekeza mkazi wake.

MUZIPEWA MAKHALIDWE AMENE ANGASONYEZE KUTI SIMULEMEKEZA MKAZI WANU

6. Kodi Yehova amamva bwanji amuna akamazunza akazi awo? (Akolose 3:19)

6 Kumenya mkazi wanu. Yehova amadana ndi munthu aliyense wachiwawa. (Sal. 11:5) Iye amadana kwambiri ndi mwamuna amene amazunza mkazi wake. (Mal. 2:16; werengani Akolose 3:19.) Mogwirizana ndi lemba lotsogolera nkhaniyi la 1 Petulo 3:7, ngati mwamuna amazunza mkazi wake amasokoneza ubwenzi wake ndi Mulungu. Yehova sangayankhe mapemphero ake.

7. Mogwirizana ndi Aefeso 4:31, 32, kodi amuna ayenera kupewa kalankhulidwe kati? (Onaninso “Tanthauzo la Mawu Ena.”)

7 Kulankhula mawu achipongwe. Amuna ena amazunza akazi awo powalankhula mawu achipongwe komanso mwaukali. Koma Yehova amadana ndi ‘kupsa mtima, mkwiyo, kulalata komanso mawu achipongwe.’ c (Werengani Aefeso 4:​31, 32.) Iye amamva zonse zimene timalankhula. Ndipo amakhudzidwa ndi mmene mwamuna amalankhulira ndi mkazi wake ngakhale ali kwa okha. Mwamuna amene amalankhula mwachipongwe ndi mkazi wake amasokoneza banja lake komanso ubwenzi wake ndi Mulungu.—Yak. 1:26.

8. Kodi Yehova amamva bwanji anthu akamaonera zolaula, nanga n’chifukwa chiyani?

8 Kuonera zolaula. Yehova amadana kwambiri ndi zolaula. Choncho mwamuna amene amaonera zolaula amasokoneza ubwenzi wake ndi Yehova komanso salemekeza mkazi wake. d Yehova amayembekezera kuti zochita komanso zoganiza za mwamuna zizisonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa mkazi wake. Yesu ananena kuti mwamuna amene amayang’ana mkazi wina momusirira wachita naye kale chigololo “mumtima mwake.” eMat. 5:28, 29.

9. N’chifukwa chiyani Yehova sasangalala mwamuna akamazunza mkazi wake pa nkhani zokhudza kugonana?

9 Kuchita zosayenera pa nkhani yokhudza kugonana. Amuna ena amakakamiza akazi awo kuti agonane m’njira imene ingachititse mkazi kumva kuti ndi wodetsedwa kapena kuti sakondedwa. Yehova amadana ndi khalidwe lodzikonda komanso losaganizira ena limeneli. Iye amafuna kuti mwamuna azikonda, kusamalira komanso kulemekeza mkazi wake. (Aef. 5:28, 29) Ndiye kodi Mkhristu angatani ngati salemekeza mkazi wake, amamuchitira nkhanza kapena amaonera zolaula? Kodi angatani kuti asinthe maganizo komanso zochita zake?

ZIMENE MWAMUNA ANGACHITE NGATI SAMALEMEKEZA MKAZI WAKE

10. Kodi chitsanzo cha Yesu chingathandize bwanji amuna?

10 N’chiyani chingathandize mwamuna kuti asiye kuchitira nkhanza mkazi wake? Iye ayenera kuyesetsa kutsanzira Yesu. N’zoona kuti Yesu sanakwatire koma amuna akhoza kuphunzirapo kanthu akaganizira mmene iye ankachitira zinthu ndi ophunzira ake. (Aef. 5:25) Mwachitsanzo, kodi Yesu ankachita bwanji zinthu ndi ophunzira ake nanga ankawalankhula bwanji? Kodi amuna angaphunzirepo chiyani?

11. Kodi Yesu ankachita bwanji zinthu ndi atumwi ake?

11 Yesu ankasonyeza ulemu komanso kukoma mtima kwa atumwi ake. Iye sanali wankhanza kapena wopondereza. Ngakhale kuti iye anali Mbuye wawo, sanagwiritse ntchito mphamvu kuti azimuopa. M’malomwake, ankawatumikira modzichepetsa. (Yoh. 13:12-17) Iye anauza ophunzira ake kuti: “Lolani kuti ndikuphunzitseni, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mat. 11:28-30) Onani kuti Yesu anali wofatsa. Munthu wofatsa si wofooka, koma amakhala ndi mphamvu zotha kudziletsa. Akaputidwa amakhala wodekha ndipo amadziletsa.

12. Kodi Yesu ankalankhula bwanji ndi anthu ena?

12 Yesu ankalankhula mawu olimbikitsa komanso otsitsimula kwa ena. Iye sankalankhula mwaukali kwa ophunzira ake. (Luka 8:47, 48) Ngakhale otsutsa ankamunyoza komanso kumuputa, “iye sanabwezere zachipongwe.” (1 Pet. 2:21-23) Nthawi zina Yesu ankakhala chete osayankha chilichonse. (Mat. 27:12-14) Apatu iye anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa amuna a Chikhristu.

13. Mogwirizana ndi Mateyu 19:4-6, kodi mwamuna angatani kuti ‘adziphatike kwa mkazi wake’? (Onaninso chithunzi.)

13 Yesu analangiza amuna kuti azikhala okhulupirika kwa akazi awo. Iye anagwiritsa ntchito mawu amene Atate wake ananena akuti mwamuna ayenera ‘kudziphatika kwa mkazi wake.’ (Werengani Mateyu 19:4-6.) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kudziphatika” angatanthauze “kumata ndi guluu.” Choncho mwamuna ndi mkazi, ayenera kumagwirizana kwambiri ngati amatidwa pamodzi ndi guluu. Ngati iwo atasiyanitsidwa, awiri onsewa adzamva kupweteka. Mwamuna amene amagwirizana chonchi ndi mkazi wake sangaonere zolaula zilizonse. Iye amatembenuka mwamsanga kuti ‘asayang’ane zopanda pake.’ (Sal. 119:37) Zimakhala ngati wapangana ndi maso ake kuti asayang’ane mosirira akazi ena.—Yobu 31:1.

Mwamuna wokhulupirika akupewa kuona zolaula (Onani ndime 13) g


14. Kodi mwamuna yemwe amazunza mkazi wake, angatani kuti akonze ubwenzi wake ndi Yehova komanso ndi mkazi wakeyo?

14 Mwamuna amene amazunza kapena kulankhula mwachipongwe mkazi wake ayenera kuchita zinthu zina kuti akonze ubwenzi wake ndi Yehova komanso ndi mkaziyo. Kodi ndi zinthu ziti zimene ayenera kuchita. Choyamba, iye ayenera kuzindikira kuti ali ndi vuto lalikulu. Palibe chilichonse chimene chimabisika kwa Yehova. (Sal. 44:21; Mlal. 12:14; Aheb. 4:13) Chachiwiri, iye ayenera kusiya kuzunza mkazi wake ndiponso kusinthiratu khalidwe lake. (Miy. 28:13) Chachitatu, ayenera kupepesa mkazi wake komanso kupempha Yehova kuti amukhululukire. (Mac. 3:19) Ayeneranso kupempha Yehova kuti amuthandize kukhala ndi mtima wofuna kusintha komanso kuti akhale wodziletsa pa zimene amaganiza, kulankhula ndiponso kuchita. (Sal. 51:10-12; 2 Akor. 10:5; Afil. 2:13) Cha 4, iye ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi mapemphero ake podana ndi zachiwawa zilizonse komanso mawu achipongwe. (Sal. 97:10) Cha 5, ayenera kupempha thandizo kwa abusa achikondi mumpingo. (Yak. 5:14-16) Cha 6, iye ayenera kukhala ndi pulani yomuthandiza kuti asadzayambirenso khalidwe loipalo. Mwamuna yemwe amaonera zolaula ayeneranso kuchita zinthu zonse zimenezi ndipo Yehova adzamuthandiza kuti asinthe khalidwe lake. (Sal. 37:5) Koma kungopewa zinthu zimene zingakhumudwitse mkazi wake si kokwanira. Iye ayenera kuphunzira kulemekeza mkazi wake. Kodi angachite bwanji zimenezi?

KODI MWAMUNA ANGALEMEKEZE BWANJI MKAZI WAKE?

15. Kodi mwamuna angasonyeze bwanji chikondi kwa mkazi wake?

15 Muzisonyeza chikondi. Amuna ena omwe akusangalala m’banja lawo amayesetsa kuti tsiku lililonse azichita chinachake chomwe chingasonyeze kuti amakonda akazi wawo. (1 Yoh. 3:18) Mwamuna akhoza kusonyeza kuti amakonda mkazi wake m’njira zing’onozing’ono monga kumugwira dzanja kapena kumuhaga. Atha kumutumizira uthenga monga wakuti, “Ndakusowa” kapena kumufunsa kuti, “Zikuyenda?” Nthawi zinanso akhoza kumulembera mawu osankhidwa bwino pakhadi. Mwamuna akamachita zinthu ngati zimenezi amalemekeza mkazi wake ndipo banja lawo limakhala lolimba.

16. N’chifukwa chiyani mwamuna ayenera kuyamikira mkazi wake?

16 Muziyamikira mkazi wanu. Mwamuna amene amalemekeza mkazi wake amamulimbikitsa. Njira ina yolimbikitsira mkazi ndi kumuyamikira pa zonse zomwe amachita. (Akol. 3:15) Mwamuna akamayamikira mkazi wake kuchokera pansi pa mtima, mkaziyo amamva bwino. Amamva kuti ndi wotetezeka, amakondedwa komanso amalemekezedwa.—Miy. 31:28.

17. Kodi mwamuna angasonyeze bwanji kuti amalemekeza mkazi wake?

17 Muzichita zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu. Mwamuna amene amakonda mkazi wake amaona kuti iye ndi wamtengo wapatali. Amamuona kuti ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova. (Miy. 18:22; 31:10) Choncho amachita naye zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu ngakhale pa nkhani yokhudza kugonana. Iye sakakamiza mkazi wake kuti azigonana m’njira imene ingachititse kuti asamamve bwino, azidzimva kuti ndi wachabechabe kapenanso chikumbumtima chake chizimuvutitsa. f Mwamunayo amayesetsanso kuti azichita zinthu zimene zingathandize kuti akhale ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Yehova.—Mac. 24:16.

18. Kodi amuna ayenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani? (Onani bokosi lakuti “ Njira 4 Zothandiza Kuti Mukhale Mwamuna Waulemu.”)

18 Amuna, dziwani kuti Yehova amaona komanso kuyamikira zimene mumachita polemekeza mkazi wanu. Pitirizani kulemekeza mkazi wanu popewa khalidwe loipa komanso popitiriza kuchita naye zinthu mokoma mtima, mwaulemu ndiponso mwachikondi. Mukamachita zimenezo mudzasonyeza kuti mumamukonda komanso ndi wamtengo wapatali. Mukamalemekeza mkazi wanu, mudzateteza chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanu, chomwe ndi ubwenzi wanu ndi Yehova.—Sal. 25:14.

NYIMBO NA. 131 “Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”

a Amuna angachite bwino kuwerenga nkhani yamutu wakuti “Kodi Mumaona Akazi Ngati Mmene Yehova Amawaonera?” mu Nsanja ya Olonda ya January 2024.

b Anthu amene amazunzidwa pakhomo angachite bwino kuwerenga nkhani yakuti “Mfundo Zothandiza Anthu Omwe Achitiridwa Nkhanza Zosiyanasiyana” pagawo lakuti “Nkhani Zina” pa jw.org komanso JW Library®.

c TANTHAUZO LA MAWU ENA: “Mawu achipongwe” angatanthauze kutchula mayina onyoza, kulankhula mwaukali komanso kumangokhalira kuimba winawake mlandu.

d Onani pa jw.org komanso pa JW Library nkhani yakuti “Kuonera Zolaula Kungasokoneze Banja Lanu.”

e Mkazi yemwe mwamuna wake amaonera zolaula angachite bwino kuwerenga nkhani yakuti “Ngati Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Amaonera Zolaula” mu Nsanja ya Olonda ya August 2023.

f Baibulo silitchula zonse zokhudza kugonana koyenera kapena kosayenera kwa pakati pa mwamuna ndi mkazi wake. Banja la Chikhristu liyenera kusankha lokha zochita pa nkhaniyi zomwe zingasonyeze kuti limalemekeza Yehova, limafunika kukhala ndi chikumbumtima chabwino komanso limachita zinthu moganizirana. Kunena zoona, banja siliyenera kukambirana ndi aliyense nkhani zawo zokhudza kugonana.

g MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akuitanidwa ndi anzake a kuntchito kuti aone mabuku a zinthu zolaula.