Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA

Kujambula Kumathandiza Kuti Tizikumbukira Zinthu

Kujambula Kumathandiza Kuti Tizikumbukira Zinthu

Mwina inunso mumavutika kukumbukira zimene mwaphunzira. Koma kodi munaona kuti zimakhala zosavuta kukumbukira mafanizo a Yesu? Zili choncho chifukwa mumatha kuona m’maganizo mwanu zimene ananena ndipo zimenezi zimathandiza kuti muzizikumbukira. Muthanso kumakumbukira zimene mumawerenga ngati mumaziona m’maganizo mwanu. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Muzijambula zithunzi pamene mukuphunzira.

Anthu amene amajambula zinthu zatsopano zimene aphunzira saziiwala. Kuchita zimenezi kumawathandiza kuti azikumbukira mawu komanso mfundo zikuluzikulu zimene aphunzira. Iwo amangojambula zinthu zosavuta osati zaluso kwambiri. Ndipo zikuoneka kuti anthu achikulire angapindule kwambiri ndi njira imeneyi.

Ulendo wina mukamadzaphunzira, mudzayese kujambula zithunzi za zimene mwaphunzirazo. Mudzadabwa kuti mudzakumbukira zinthu zambiri.