Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 5

NYIMBO NA. 108 Chikondi Chokhulupirika cha Mulungu

Madalitso Amene Timapeza Chifukwa cha Chikondi cha Yehova

Madalitso Amene Timapeza Chifukwa cha Chikondi cha Yehova

“Khristu Yesu anabwera mʼdziko kudzapulumutsa ochimwa.”​—1 TIM. 1:15.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tikambirana madalitso amene timapeza chifukwa cha dipo komanso mmene tingasonyezere kuti timayamikira Yehova.

1. Kodi tingatani kuti tizisangalatsa Yehova?

 TIYEREKEZE kuti mwapatsa munthu wina amene mumamukonda mphatso yokongola komanso yothandiza. Kodi mungamve bwanji ngati atangoiponya penapake osaiganiziranso? Kunena zoona, mukhoza kusangalala ngati atamaigwiritsa ntchito komanso kusonyeza kuyamikira. Mofanana ndi zimenezi, Yehova amasangalala tikamasonyeza kuti timayamikira mphatso ya dipo komanso chikondi chimene anatisonyeza potipatsa mphatso yamtengo wapataliyi.—Yoh. 3:16; Aroma 5:7, 8.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Koma nthawi ikamapita, tikhoza kuyamba kuona mopepuka mphatso imeneyi. Zingakhale ngati tatenga mphatso ya Mulungu n’kungoiponya penapake. Zili ngati timasangalala nayo koma sitifuna kuti izikhala poonekera. Kuti zimenezi zisatichitikire tiyenera kumaganizira nthawi zonse zimene Mulungu ndi Khristu anatichitira. Nkhaniyi itithandiza kuti tizichita zimenezi. Tiona mmene dipo limatithandizira panopa komanso mmene lidzatithandizire m’tsogolo. Tikambirananso zimene tingachite posonyeza kuti timayamikira chikondi cha Yehova makamaka panyengo ya Chikumbutsoyi.

MADALITSO AMENE TIMAPEZA PANOPA CHIFUKWA CHA DIPO

3. Kodi ndi madalitso ati amene timapeza panopa chifukwa cha dipo?

3 Pali madalitso amene timapeza panopa chifukwa cha nsembe ya Khristu. Mwachitsanzo, Yehova amatikhululukira machimo athu chifukwa cha nsembeyi. Ife si oyenera kutikhululukira koma iye amafuna kuchita zimenezo. Wolemba masalimo, yemwe ankasonyeza kuyamikira, anaimba kuti: “Inu Yehova ndinu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.”—Sal. 86:5; 103:3, 10-13.

4. Kodi Yehova anapereka dipo kuti lithandize ndani? (Luka 5:32; 1 Timoteyo 1:15)

4 Anthu ena amadziona kuti ndi osayenera kukhululukidwa ndi Yehova. Zoona n’zakuti tonsefe si oyenera kukhululukidwa. Mtumwi Paulo anazindikira kuti iye sanali “woyenera kutchedwa mtumwi.” Koma ananenanso kuti: “Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili mmene ndililimu.” (1 Akor. 15:9, 10) Tikalapa machimo athu Yehova amatikhululukira. Sikuti amachita zimenezo chifukwa chakuti ndife oyenera kukhululukidwa, koma chifukwa chakuti amatikonda. Mukayamba kudziona ngati achabechabe, muzikumbukira kuti Yehova anapereka dipo kuti lithandize anthu ochimwa omwe alapa, osati anthu amene sachimwa.—Werengani Luka 5:32; 1 Timoteyo 1:15.

5. Kodi pali munthu aliyense amene anganene kuti ndi woyenera kulandira chifundo cha Yehova? Fotokozani.

5 Palibe aliyense amene ayenera kudziona kuti ndi woyenera kuchitiridwa chifundo ndi Yehova ngakhale atakhala kuti wamutumikira kwa zaka zambiri. Ngakhale zili choncho, Yehova amayamikira kukhulupirika kwathu. (Aheb. 6:10) Iye anapereka Mwana wake ngati mphatso yaulere osati ngati malipiro a zimene timachita pomutumikira. Tikamaganiza kuti ndife oyenera kuchitiridwa chifundo kapenanso kuti ndife oyenera kuganiziridwa mwapadera, zingakhale ngati tikunena kuti Khristu sanafunike kutifera.—Yerekezerani ndi Agalatiya 2:21.

6. N’chifukwa chiyani Paulo ankachita khama potumikira Yehova?

6 Paulo ankadziwa kuti iye si woyenera kuchitiridwa chifundo ndi Mulungu. Ndiye n’chifukwa chiyani ankachita khama kutumikira Yehova? Ankachita zimenezo pofuna kusonyeza kuti amayamikira kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova, osati chifukwa chakuti ankayenera kuchitiridwa chifundo. (Aef. 3:7) Mofanana ndi Paulo, timapitiriza kutumikira mwakhama pofuna kusonyeza kuyamikira, osati pofuna kusonyeza kuti ndife oyenera kuchitiridwa chifundo.

7. Kodi ndi madalitso enanso ati amene timapeza panopa chifukwa cha dipo? (Aroma 5:1; Yakobo 2:23)

7 Madalitso ena omwe timapeza panopa chifukwa cha dipo ndi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. a Mogwirizana ndi zimene takambirana munkhani yapita ija, anthufe sitimabadwa tili pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Koma chifukwa cha dipo, tingathe kukhala “pa mtendere ndi Mulungu” ndipo akhoza kukhala mnzathu wapamtima.—Werengani Aroma 5:1; Yakobo 2:23.

8. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira Yehova chifukwa cha mwayi wa pemphero?

8 Popeza tili pa ubwenzi wabwino ndi Yehova timatha kupemphera kwa iye. Sikuti Yehova amangomva mapemphero apagulu a atumiki ake akasonkhana, koma amamvanso pemphero la aliyense payekha. Pemphero limatithandiza kuti mtima wathu ukhale m’malo komanso maganizo athu akhazikike. Komatu pemphero limatithandizanso m’njira zina. Limathandiza kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ukhale wolimba. (Sal. 65:2; Yak. 4:8; 1 Yoh. 5:14) Yesu ali padzikoli ankakonda kupemphera. Iye ankadziwa kuti Yehova amamva mapemphero komanso kuti pemphero lingathandize kuti ubwenzi wake ndi Atate wake ukhale wolimba. (Luka 5:16) Timayamikira kuti nsembe ya Yesu imatithandiza kuti tikhale anzake a Yehova komanso kuti tizilankhula naye m’pemphero.

MADALITSO AMENE TIDZAPEZE M’TSOGOLO

9. Kodi ndi madalitso ati omwe anthu okhulupirika adzapeze m’tsogolo chifukwa cha dipo?

9 Kodi ndi madalitso ati omwe atumiki okhulupirika a Yehova adzapeze m’tsogolo? Iwo adzapatsidwa moyo wosatha. Anthu ambiri amaganiza kuti zimenezi n’zosatheka chifukwa anthu akhala akufa kwa zaka zambiri. Koma cholinga choyambirira cha Yehova chinali choti anthu adzakhale ndi moyo mpaka kalekale. Adamu akanapanda kuchimwa, palibe aliyense amene akanakayikira za moyo wosatha. N’zoona kuti panopa zikhoza kutivuta kukhulupirira kuti tingadzakhale ndi moyo mpaka kalekale. Koma sitimakayikira zimenezi chifukwa timadziwa kuti Yehova anapereka malipiro apamwamba kwambiri omwe ndi moyo wa Mwana wake.—Aroma 8:32.

10. Kodi odzozedwa komanso a nkhosa zina akuyembekezera chiyani?

10 Ngakhale kuti moyo wosatha tidzaulandira kutsogolo, Yehova amafuna kuti tiziuganizirabe panopa. Odzozedwa amaganizira za moyo wabwino kwambiri umene adzalandire kumwamba pomwe azidzalamulira ndi Khristu. (Chiv. 20:6) A nkhosa zina amaganizira za moyo wopanda mavuto umene adzakhale nawo m’paradaiso padziko lapansi. (Chiv. 21:3, 4) Kodi muli m’gulu la nkhosa zina ndipo mukuyembekezera moyo wosatha padziko lapansi? Sikuti mphoto imeneyi ndi yotsika tikayerekezera ndi moyo wakumwamba. Anthufe tinalengedwa kuti tizikhala padzikoli ndipo moyo wa padzikoli udzakhala wosangalatsa kwambiri.

11-12. Kodi ndi madalitso ati omwe tikuyembekezera m’dziko latsopano? (Onaninso zithunzi.)

11 Taganizirani mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso. Simudzadanso nkhawa chifukwa cha matenda kapena imfa. (Yes. 25:8; 33:24) Yehova adzakupatsani zinthu zonse zoyenera zimene mumalakalaka. Kodi inuyo mudzafuna kuphunzira zinthu ziti? Za sayansi, nyimbo kapena zojambula? N’zoonekeratu kuti padzafunika akatswiri oona za mapulani ndi zomangamanga komanso a zaulimi. Padzafunikanso anthu ogwira ntchito zina monga kukonza zoonongeka, kuphika, kupanga zipangizo zogwirira ntchito komanso kudzala maluwa. (Yes. 35:1; 65:21) Popeza kuti tidzakhala ndi moyo wosatha, tidzatha kuphunzira luso lililonse lomwe tingadzafune.

12 Zidzakhalatu zosangalatsa kulandira anthu amene adzaukitsidwe. (Mac. 24:15) Tidzasangalalanso kuphunzira zambiri zokhudza Yehova kudzera m’zinthu zimene analenga. (Sal. 104:24; Yes. 11:9) Chosangalatsa kwambiri n’chakuti tizidzalambira Yehova popanda kudziimba mlandu chifukwa chakuti talakwitsa zinazake. Kodi mungalolere kutaya zonsezi chifukwa chongofuna ‘kusangalala kwa nthawi yochepa pochita machimo’? (Aheb. 11:25) Simungafune kuchita zimenezo. Tingalolere kutaya chilichonse panopa kuti tidzapeze madalitso amenewa. Kumbukirani kuti zimene tikuyembekezera m’Paradaiso tsiku lina zidzachitikadi. Tizidzatere tili m’Paradaiso. Zimenezi sizikanatheka Yehova akanapanda kutikonda n’kupereka mphatso ya Mwana wake.

Kodi ndi madalitso ati amene mukufunitsitsa kudzawaona m’dziko latsopano? (Onani ndime 11-12)


TIZIYAMIKIRA CHIKONDI CHA YEHOVA

13. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira chikondi cha Yehova? (2 Akorinto 6:1)

13 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova chifukwa chotipatsa dipo? Tingatero poika ntchito yake pamalo oyamba pa moyo wathu. (Mat. 6:33) Paja Yesu anafa kuti ‘onse amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera nʼkuukitsidwa.’ (2 Akor. 5:15) Sitikufuna kuphonya cholinga cha kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova.—Werengani 2 Akorinto 6:1.

14. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira malangizo a Yehova?

14 Tingasonyezenso kuti timayamikira chikondi cha Yehova pokhulupirira malangizo ake. Mwachitsanzo, tiziganizira zimene Yehova angafune tikafuna kusankha zochita pa nkhani monga zokhudza maphunziro ndi ntchito. (1 Akor. 10:31; 2 Akor. 5:7) Pali zinthu zina zosangalatsa zimene zimachitika tikamakhulupirira malangizo a Yehova posankha zochita. Timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, chikhulupiriro chathu chimalimba komanso chiyembekezo chathu chimakhala champhamvu.—Aroma 5:3-5; Yak. 2:21, 22.

15. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira kwathu pa nyengo ya Chikumbutso?

15 Palinso chinthu china chomwe tingachite posonyeza kuyamikira chikondi cha Yehova. Chinthu chake ndi kugwiritsa ntchito bwino nyengo ya Chikumbutsoyi. Kuwonjezera pa kukonzekera kuti tidzapezekepo, tingaitanirenso anthu ena. (1 Tim. 2:4) Poitana anthuwo tingachite bwino kuwauza zimene zikachitike pamwambowo. Tingachitenso bwino kuwaonetsa mavidiyo a pa jw.org monga akuti N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa? komanso Tizikumbukira Imfa ya Yesu. Akulu ayeneranso kuitana anthu amene anafooka. Kumwamba kungakhale chisangalalo chachikulu kwambiri ngati nkhosa imodzi yotayika itabwerera m’gulu. (Luka 15:4-7) Pa tsiku la Chikumbutso, tidzayesetse kupereka moni kwa abale ndi alongo, koma makamaka atsopano ndi amene anasiya kusonkhana. Tiyeni tidzawachititse kuti akhale omasuka.—Aroma 12:13.

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuwonjezera zochita pa ntchito yolalikira pa nyengo ya Chikumbutso?

16 Kodi mungawonjezere zochita pa ntchito yolalikira pa nyengo ya Chikumbutso? Kuchita zimenezo kungasonyeze kuti tikuyamikira zimene Mulungu ndi Khristu anatichitira. Tikamachita zambiri potumikira Yehova m’pamenenso timaona kuti akutithandiza kwambiri ndipo timayambanso kumukhulupirira kwambiri. (1 Akor. 3:9) Mudzayesetsenso kutsatira ndandanda yowerengera Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso yomwe imapezeka mu kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku kapenanso mu Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu. Mungathenso kugwiritsa ntchito machaputala amenewa pophunzira Baibulo panokha.

17. Kodi Yehova amasangalala ndi chiyani? (Onaninso bokosi lakuti “ Mmene Tingasonyezere Kuti Timayamikira Chikondi cha Yehova.”)

17 Koma mwina chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wanu, simungakwanitse kutsatira zonse zimene zanenedwa munkhaniyi. Kumbukirani kuti Yehova amaona zimene zili mumtima mwanu ndipo sayerekezera zimene mumachita ndi zimene ena amachita. Iye amasangalala akamaona kuti mumayamikira mphatso ya dipo kuchokera pansi pa mtima.—1 Sam. 16:7; Maliko 12:41-44.

18. N’chifukwa chiyani timayamikira Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu?

18 Mphatso ya dipo ndi imene imachititsa kuti tikhululukidwe machimo, tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso tiziyembekezera moyo wosatha. Tiyeni tiziyamikira chikondi cha Yehova yemwe anachititsa kuti tipeze madalitso onsewa. (1 Yoh. 4:19) Tizisonyezanso kuti timayamikira Yesu yemwe anapereka moyo wake chifukwa chotikonda.—Yoh. 15:13.

NYIMBO NA. 154 Chikondi Sichitha

a Yehova ankakhululukira atumiki ake Khristu asanapereke dipo. Iye ankachita zimenezi chifukwa sankakayikira kuti Mwana wake adzakhala wokhulupirika mpaka imfa. Choncho kwa Mulungu zinali ngati dipo laperekedwa kale.—Aroma 3:25.