Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 1

NYIMBO NA. 2 ‘Dzina Lanu Ndi Yehova’

M’patseni Yehova Ulemerero

M’patseni Yehova Ulemerero

LEMBA LA CHAKA CHA 2025: “M’patseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.”SAL. 96:8.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tizipereka kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake.

1. Kodi anthu ambiri masiku ano amangoganizira za chiyani?

 MASIKU ano anthu ambiri amangoganizira za iwowo basi. Mwachitsanzo, ena amachita zambiri pa intaneti n’cholinga choti ena azichita nawo chidwi kapena adziwe zimene akuchita. Koma ndi anthu ochepa kwambiri amene amapereka ulemerero kwa Yehova Mulungu. Munkhaniyi tikambirana tanthauzo la kupereka ulemerero kwa Yehova komanso chimene chingatilimbikitse kuti tizichita zimenezo. Tionanso zimene tingachite kuti tizipereka kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake komanso mmene iyeyo adzalemekezere dzinalo m’tsogolo.

KODI KUPATSA YEHOVA ULEMERERO KUMATANTHAUZA CHIYANI?

2. Kodi Yehova anaonetsa bwanji ulemerero wake paphiri la Sinai? (Onaninso chithunzi)

2 M’Baibulo, mawu akuti “ulemerero” angatanthauze chilichonse chimene chingapangitse winawake kuti akhale wochititsa chidwi. Yehova anasonyeza ulemerero wake wodabwitsa Aisiraeli atangomasulidwa kumene ku ukapolo ku Iguputo. Yerekezerani kuti mukuona Aisiraeli ambirimbiri atasonkhana m’mbali mwa phiri la Sinai kuti akumane ndi Mulungu wawo. Mtambo wakuda waphimba phirilo. Kenako mwadzidzidzi chivomerezi champhamvu, chokhala ngati phiri likuphulika chikugwedeza pomwe iwo aima. Komanso pali kung’anima ndi kulira kwa mabingu ndiponso kulira kogonthetsa m’khutu kwa lipenga. (Eks. 19:16-18; 24:17; Sal. 68:8) Aisiraeli ayenera kuti anachita chidwi ndi mmene Yehova anasonyezera ulemerero wake.

Yehova anasonyeza mphamvu ndi ulemerero wake kwa Aisiraeli paphiri la Sinai (Onani ndime 2)


3. Kodi kupatsa Yehova ulemerero kumatanthauza chiyani?

3 Kodi anthufe tingapereke ulemerero kwa Yehova? Inde. Njira imodzi imene tingachitire zimenezo ndi kuuza anthu zokhudza mphamvu zake komanso makhalidwe ake abwino. Timaperekanso ulemerero kwa Mulungu tikamamulemekeza chifukwa cha zimene watithandiza kuchita. (Yes. 26:12) Mfumu Davide anali chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yolemekeza Yehova. M’pemphero limene Davide anapereka pagulu la Aisiraeli, iye anauza Mulungu kuti: “Inu Yehova, ukulu, mphamvu, kukongola, ulemerero ndi ulemu ndi zanu, chifukwa zinthu zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi ndi zanu.” Davide atamaliza kupereka pempheroli “anthu onsewo anayamba kutamanda Yehova.”—1 Mbiri 29:11, 20.

4. Kodi Yesu anapereka bwanji ulemerero kwa Yehova?

4 Yesu ali padzikoli, ankapereka ulemerero kwa Atate wake posonyeza kuti ndi amene ankamupatsa mphamvu kuti azichita zinthu zodabwitsa. (Maliko 5:18-20) Zimene Yesu ankalankhula zokhudza Atate wake komanso mmene ankachitira zinthu ndi ena, zinkapereka ulemerero kwa Yehova. Pa nthawi ina Yesu ankaphunzitsa ku sunagoge. Pagulu la anthu amene ankawaphunzitsawo panali mayi wina yemwe anali atavutitsidwa ndi chiwanda kwa zaka 18. Chiwandacho chinachititsa kuti apindike msana moti sankathanso kuweramuka. Zinalitu zomvetsa chisoni kwambiri. Yesu anamumvera chisoni ndipo anamuyandikira n’kumalankhula mokoma mtima kuti: “Mayi, mwamasuka ku matenda anu.” Kenako anamugwira ndipo mayiyo anaimirira moongoka “n’kuyamba kutamanda Mulungu,” Mayiyo anakhalanso wamphamvu. (Luka 13:10-13) Mofanana ndi mayiyu, tili ndi zifukwa zomveka zopatsira Yehova ulemerero.

N’CHIYANI CHIMATILIMBIKITSA KUTI TIZIPATSA YEHOVA ULEMERERO?

5. Kodi tili ndi zifukwa ziti zotichititsa kulemekeza Yehova?

5 Timapereka ulemerero kwa Yehova chifukwa chakuti timamulemekeza kwambiri. Tili ndi zifukwa zambiri zomulemekezera. Yehova ndi wamphamvu yonse, kutanthauza kuti ali ndi mphamvu zopanda malire. (Sal. 96:4-7) Timaona nzeru zake mu zinthu zimene analenga. Ndi amene anatipatsa moyo komanso zonse zimene zimatithandiza kuti tikhalebe ndi moyo. (Chiv. 4:11) Yehova ndi wokhulupirikanso. (Chiv. 15:4) Chilichonse chimene amachita chimayenda bwino ndipo nthawi zonse amakwaniritsa zimene walonjeza. (Yos. 23:14) N’zomveka kuti mneneri Yeremiya anafotokoza za Yehova kuti: “Pakati pa anzeru onse a m’mitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse, palibiretu aliyense wofanana ndi inu.” (Yer. 10:6, 7) Choncho tili ndi zifukwa zabwino zolemekezera Atate wathu wakumwamba. Sikuti timangolemekeza Yehova, koma timamukondanso kwambiri.

6. N’chifukwa chiyani timakonda Yehova?

6 Timapereka ulemerero kwa Yehova chifukwa timamukonda kwambiri. Taganizirani makhalidwe abwino a Yehova omwe amachititsa kuti tizimukonda. Iye ndi wachifundo. (Sal. 103:13; Yes. 49:15) Amaganizira ena ndipo tikamamva ululu nayenso zimamupweteka. (Zek. 2:8) Iye amaonetsetsa kuti tikhale anzake. (Sal. 25:14; Mac. 17:27) Yehova ndi wodzichepetsa ndipo “amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi. Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa m’fumbi.” (Sal. 113:6, 7) Tonsefe timafuna kupereka ulemerero kwa Mulungu wathu wamkulu?—Sal. 86:12.

7. Kodi tili ndi mwayi wochita chiyani?

7 Timapereka ulemerero kwa Yehova chifukwa timafuna kuti ena amudziwe. Anthu ambiri samudziwa bwinobwino Yehova. Zili choncho chifukwa chakuti Satana wawachititsa khungu pofalitsa mabodza okhudza Mulungu. (2 Akor. 4:4) Iye wachititsa anthu kukhulupirira kuti Yehova ndi wankhanza, sasamala za anthu komanso ndi amene amachititsa mavuto ambiri m’dzikoli. Koma ife timadziwa zoona zokhudza Mulungu wathu. Tili ndi mwayi wothandiza ena kudziwa zokhudza iye komanso kumupatsa ulemerero. (Yes. 43:10) Chaputala 96 cha Masalimo chimafotokoza zokhudza kulemekeza Yehova. Tikamakambirana mawu ouziridwa a mu Salimoli, muziganizira njira zimene mungaperekere ulemerero kwa Yehova.

KODI TINGATANI KUTI TIZIPATSA YEHOVA ULEMERERO UMENE AMAFUNIKA KULANDIRA?

8. Kodi ndi njira imodzi iti yomwe tingalemekezere Yehova? (Salimo 96:1-3)

8 Werengani Salimo 96:1-3. Zimene tingalankhule zokhudza Yehova, zingachititse kuti alandire ulemerero. Musalimoli tikulimbikitsidwa ‘kuimbira Yehova,’ ‘kutamanda dzina lake,’ ‘kulengeza uthenga wabwino wa chipulumutso chake’ komanso ‘kulengeza ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina.’ Zimenezi ndi njira zimene tingaperekere ulemerero kwa Atate wathu wakumwamba. Ayuda okhulupirika komanso Akhristu oyambirira, ankauza ena zinthu zabwino zimene Yehova ankawachitira komanso makhalidwe ake abwino. (Dan. 3:16-18; Mac. 4:29) Kodi ifeyo tingachite bwanji zimenezi?

9-10. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Angelena? (Onaninso chithunzi.)

9 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku United States dzina lake Angelena. a Iye anafotokoza molimba mtima zinthu zabwino zokhudza Yehova kuntchito kwake. Atangolembedwa kumene ntchito, Angelena anaitanidwa kumsonkhano wa pakampanipo komwe aliyense ankafunika kufotokozera anzake zokhudza mbiri yake. Angelena anakonza kavidiyo ka zithunzi kosonyeza kuti ankasangalala kukhala wa Mboni za Yehova. Nthawi yake itatsala pang’ono, munthu wina anafotokoza kuti analeredwa m’banja la Mboni ndipo anayamba kunyoza zimene timakhulupirira. Angelena anati: “Mtima wanga unayamba kugunda kwambiri. Koma ndinadziuza kuti, ‘Koma zoona ndilole kuti munthu wina anene mabodza okhudza Yehova? Ndilimba mtima n’kulankhula zabwino zokhudza iye.’”

10 Mnzakeyo atangomaliza kulankhula, Angelena anapemphera mwachidule chamumtima. Kenako anamulankhula mwaulemu kuti: “Mbiri yanga ndi yofanana ndi yanu. Inenso ndinaleredwa m’banja la Mboni za Yehova. Ndipo ndinebe wa Mboni.” Zinali zovuta kwambiri koma Angelena sanatekeseke. Iye anaonetsa anthu zithunzi za misonkhano imene anapezekapo ndipo analankhula mosamala poikira kumbuyo zinthu zimene timakhulupirira. (1 Pet. 3:15) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Pamene Angelena ankamaliza kulankhula, munthuyo anali atasinthiratu maganizo ake. Iye anafotokoza kuti panali zinthu zina zabwino zimene zinkachitika pamene ankaleredwa m’banja la Mboni. Angelena anati: “Tiyenera kuikira kumbuyo Yehova. Ndi mwayi waukulu kulankhula zokhudza dzina lake.” Ifenso tapatsidwa mwayi wotamanda Yehova komanso kumupatsa ulemerero ngakhale pamene ena sakumulemekeza.

Tingalemekeze Yehova ndi zolankhula zathu, zinthu zathu, komanso khalidwe lathu (Onani ndime 9-10) b


11. Kodi atumiki a Yehova akhala akutsatira bwanji mfundo ya pa Salimo 96:8?

11 Werengani Salimo 96:8. Tikhoza kupatsa Yehova ulemerero popereka zinthu zathu zamtengo wapatali. Kuyambira kale, atumiki a Yehova akhala akumupatsa ulemerero m’njira imeneyi. (Miy. 3:9) Mwachitsanzo, Aisiraeli ankapereka zinthu zawo kuti zithandize pa ntchito yomanga ndi kusamalira kachisi. (2 Maf. 12:4, 5; 1 Mbiri 29:3-9) Ophunzira ena a Yesu, ‘ankagwiritsa ntchito chuma chawo’ pothandiza iyeyo ndi atumwi ake. (Luka 8:1-3) Akhristu oyambirira ankaperekanso chithandizo kwa abale ndi alongo awo. (Mac. 11:27-29) Ifenso masiku ano tikhoza kulemekeza Yehova popereka zinthu zathu.

12. Kodi zopereka zathu zingalemekeze bwanji Yehova? (Onaninso chithunzi.)

12 Tiyeni tikambirane chitsanzo chimodzi chosonyeza kuti zopereka zathu zimathandiza kuti Yehova alemekezedwe. Lipoti lina la mu 2020 linasonyeza kuti ku Zimbabwe kunali mavuto aakulu chifukwa cha chilala chomwe chinatenga nthawi yaitali. Anthu ambiri analibe chakudya, kuphatikizapo mlongo wina dzina lake Prisca. Ngakhale kuti panali mavutowa, Prisca anapitirizabe kulalikira Lachitatu ndi Lachisanu. Iye ankachitabe zimenezi ngakhale pa nthawi yolima. Anthu ena ankamunyoza chifukwa chopita kukalalikira m’malo mopita kumunda ndipo ankanena kuti , “Iwetu ufa ndi njala.” Prisca ankawayankha mtima uli m’malo kuti, “Yehova sanayambe wasiyapo atumiki ake.” Pasanapite nthawi yaitali, iye analandira zinthu zimene gulu lathu linkapereka. Zinthu zimenezi zinapezeka chifukwa cha zopereka za abale ndi alongo. Anthu ena aja anachita chidwi ndipo anamuuza kuti, “Mulungu sanakusiyepo, ndiye tikufuna tiphunzire zambiri zokhudza Mulungu ameneyo.” Anthu okwana 7 anayamba kupezeka pamisonkhano.

Tingalemekeze Yehova ndi zolankhula zathu (Onani ndime 12) c


13. Kodi khalidwe lathu lingapereke bwanji ulemerero kwa Yehova? (Salimo 96:9)

13 Werengani Salimo 96:9. Tikhoza kupereka ulemerero kwa Yehova pokhala ndi khalidwe labwino. Ansembe omwe ankatumikira Yehova pakachisi, ankafunika kusamba komanso kuchapa kuti akhale oyera. (Eks. 40:30-32) Koma chofunika kwambiri n’chakuti ankafunika kukhala ndi khalidwe labwino. (Sal. 24:3, 4; 1 Pet. 1:15, 16) Ifenso tiyenera kuyesetsa kuvula “umunthu wathu wakale” womwe ndi makhalidwe oipa, n’kuvala “umunthu watsopano” kutanthauza kuti tiyenera kuganiza komanso kuchita zinthu motsanzira makhalidwe a Yehova. (Akol. 3:9, 10) Yehova akhoza kuthandiza ngakhale munthu wamakhalidwe oipa komanso wachiwawa kwambiri kuti asinthe n’kuvala umunthu watsopano.

14. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Jack? (Onaninso chithunzi.)

14 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Jack, yemwe anali wachiwawa komanso woopsa ndipo ankangomutchula kuti chiwanda. Chifukwa cha milandu imene anapalamula, Jack analamulidwa kuti ayenera kuphedwa. Akuyembekezera tsiku lophedwa, Jack anayamba kuphunzira Baibulo ndi m’bale wina yemwe anafika kundendeko. Ngakhale kuti poyamba anali ndi khalidwe loipa, Jack anasinthiratu ndipo pambuyo pake anayenerera kubatizidwa. Jack anasintha kwambiri moti tsiku limene ankakaphedwa asilikali omwe ankamuyang’anira anayamba kulira potsanzikana naye. Msilikali wina yemwe ankagwira ntchito pandendepo ananena kuti: “Jack anali mkaidi woipa kwambiri. Koma tsopano ndi mmodzi mwa akaidi abwino kwambiri.” Jack ataphedwa, mlungu wotsatira abale anapita kundendeko kukachititsa misonkhano ndipo anaona mkaidi wina yemwe kanali koyamba kufika pamisonkhanopo. Mkaidiyo anayamba kufika pamisonkhanopo ataona mmene Jack anasinthira ndipo ankafuna kudziwa zimene angachite kuti azilambira Yehova. Apa zikuonekeratu kuti khalidwe lathu likhoza kupereka ulemerero kwa Atate wathu wakumwamba.—1 Pet. 2:12.

Tingalemekeze Yehova ndi khalidwe lathu (Onani ndime 14) d


KODI YEHOVA ADZALEMEKEZA BWANJI DZINA LAKE M’TSOGOLOMU?

15. Kodi Yehova adzalemekeza bwanji dzina lake posachedwapa? (Salimo 96:10-13)

15 Werengani Salimo 96:10-13. Mavesi omaliza a mu Salimo 96 amafotokoza kuti Yehova ndi Woweruza wachilungamo komanso Mfumu. Kodi Yehova adzalemekeza bwanji dzina lake posachedwapa? Posachedwapa Yehova adzalemekeza dzina lake popereka chiweruzo. Iye adzawononga Babulo Wamkulu chifukwa chonyoza dzina lake loyera. (Chiv. 17:5, 16; 19:1, 2) Anthu ena omwe adzaone Babulo Wamkulu akuwonongedwa, adzayamba kulambira nafe Mulungu. Ndipo pa Aramagedo, Yehova adzawononga dziko lonse la Satanali n’kuchotsa anthu onse omwe amamutsutsa komanso kunyoza dzina lake. Koma adzapulumutsa anthu onse omwe amamukonda, kumumvera ndiponso kumupatsa ulemerero. (Maliko 8:38; 2 Ates. 1:6-10) Pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu komanso mayesero omaliza, Yehova adzakhala atayeretseratu dzina lake. (Chiv. 20:7-10) Pa nthawiyo “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa ulemerero wa Yehova, ngati mmene madzi amadzazira nyanja.”—Hab. 2:14.

16. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani? (Onaninso chithunzi.)

16 Zidzakhala zosangalatsa kwambiri pa nthawiyo, chifukwa aliyense amene adzakhale moyo, azidzapereka kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake. Pamene tikuyembekezera nthawiyi, tiyeni tiziyesetsa kupereka ulemerero kwa Yehova pa mpata uliwonse umene wapezeka. Pofuna kutsindika mfundo imeneyi, Bungwe Lolamulira lasankha kuti lemba Salimo 96:8 likhale lemba la chaka cha 2025. Lembali limati: “Mʼpatseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.”

Aliyense amene adzakhale ndi moyo, azidzapatsa Yehova ulemerero woyenera dzina lake (Onani ndime 16)

NYIMBO NA. 12 Yehova Mulungu Wamkulu

a Mayina ena asinthidwa.

b MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI : Chithunzi choyerekezera cha zimene zinachitikira Angelena.

c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Chithunzi choyerekezera cha zimene zinachitikira Prisca.

d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Chithunzi choyerekezera cha zimene zinachitikira Jack.