Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 3

NYIMBO NA. 35 “Muzitha Kusankha Zinthu Zimene Ndi Zofunikadi Kwambiri”

Muzisankha Zinthu Zimene Zingasangalatse Yehova

Muzisankha Zinthu Zimene Zingasangalatse Yehova

“Kuopa Yehova ndi chiyambi cha nzeru, ndipo ngati ungadziwe Mulungu, yemwe ndi Woyera Koposa, udzakhala womvetsa zinthu.”MIY. 9:10.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona mmene kudziwa zinthu, kumvetsa zinthu komanso kuzindikira kungatithandizire kuti tizisankha zinthu mwanzeru.

1. Kodi ndi vuto liti lomwe tonsefe timakumana nalo?

 TSIKU lililonse timafunika kusankha zochita. Zina zimakhala zosavuta monga kusankha zomwe tingadye m’mawa kapena nthawi imene tikufuna kukagona. Koma pali zina zomwe zimakhala zovuta chifukwa zimakhudza thanzi lathu, anthu amene timawakonda, kulambira kwathu komanso ngati tingakhale osangalala kapena ayi. Timafuna tizisankha zinthu zimene zingatithandize ifeyo komanso banja lathu. Koma chofunika kwambiri n’chakuti timafuna kuti zimene timasankha zizisangalatsa Yehova.—Aroma 12:1, 2.

2. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingatithandize kuti tizisankha zinthu mwanzeru?

2 Zinthu zotsatirazi, zingakuthandizeni kuti muzisankha bwino zochita: (1) kudziwa mfundo zonse, (2) kudziwa maganizo a Yehova pa nkhaniyo, komanso (3) kuyerekezera zotsatirapo zake. Tikambirana zinthu zitatuzi ndipo nkhaniyi itithandiza kuti tiziphunzitsa luso lathu lozindikira.—Miy. 2:11.

MUZIDZIWA MFUNDO ZONSE

3. Perekani chitsanzo chosonyeza kufunika kofufuza mfundo zonse musanasankhe zochita.

3 Chinthu choyamba kuti munthu asankhe bwino zochita ndi kudziwa mfundo zonse. N’chifukwa chiyani zimenezi ndi zofunika? Tiyerekeze kuti munthu ali ndi vuto lalikulu ndipo wapita kukakumana ndi dokotala. Kodi dokotalayo angapereke thandizo asanayeze kapena kufunsa mafunso wodwalayo? Ayi ndithu. Inunso musanasankhe zochita muzidziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

4. Mogwirizana ndi Miyambo 18:13, kodi mungatsimikize bwanji kuti mukudziwa mfundo zonse? (Onaninso chithunzi.)

4 Nthawi zambiri kufunsa mafunso kumatithandiza kuti tidziwe zinthu. Tiyerekeze kuti munthu wina wakuitanani kumacheza, kodi muyenera kupita? Ngati munthuyo simukumudziwa bwino komanso simukudziwa kuti macheza ake akakhala otani, mungamufunse mafunso awa: “Kodi machezawo akachitikira kuti, nanga akachitika nthawi yanji? Kodi kukakhala anthu ochuluka bwanji? Ndi ndani azikayang’anira machezawo? Ndi anthu ati amene aitanidwa? Nanga kukakhala zotani? Kodi kukakhala mowa?” Mayankho a mafunsowa angakuthandizeni kuti musankhe bwino zochita.—Werengani Miyambo 18:13.

Muzidzifunsa mafunso kuti mupeze mfundo zonse (Onani ndime 4) a


5. Kodi muyenera kuchita chiyani mukadziwa mfundo zonse?

5 Mukadziwa mfundozo muyenera kufufuzabe bwino kuti mudziwe nkhani yonse. Mwachitsanzo, kodi mungatani mutamva kuti kukakhalanso anthu ena omwe satsatira mfundo za m’Baibulo kapenanso kuti anthu azikamwa mowa popanda wowayang’anira? Kodi macheza amenewo sangasinthe n’kukhala phwando loipa? (1 Pet. 4:3) Kapena tiyerekeze kuti machezawo ali pa nthawi imene mumapita kumisonkhano kapena mu utumiki. Mukadziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo mukhoza kusankha bwino zochita. Koma palinso chinthu china chomwe muyenera kuchita. Pambuyo poti inuyo mwaidziwa bwino nkhaniyo, muyenera kuganizira mmene Yehova angaionere.—Miy. 2:6.

MUZIFUFUZA MAGANIZO A YEHOVA PA NKHANIYO

6. Mogwirizana ndi Yakobo 1:5, n’chifukwa chiyani tiyenera kupempha Yehova kuti atithandize?

6 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kudziwa maganizo ake. Yehova amatiuza kuti adzatipatsa nzeru zomwe zingatithandize kudziwa ngati zomwe tikufuna kuchita zingamusangalatse. Iye amapereka nzeru zimenezi “mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.”—Werengani Yakobo 1:5.

7. Kodi tingadziwe bwanji maganizo a Yehova? Perekani chitsanzo.

7 Mukapemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni, muzichita chidwi kuti muone mmene akuyankhira pemphero lanulo. Tiyerekeze kuti muli pa ulendo ndipo mwasochera ndipo mukufunsa munthu wina wa kuderalo kuti akuthandizeni. Kodi munganyamuke asanakuyankheni? Ayi simungachite zimenezo. Mudzamvetsera mwachidwi akamakufotokozerani mmene mungayendere. Mofanana ndi zimenezi, mukapempha Yehova kuti akupatseni nzeru, muzifufuza malamulo ndi mfundo za m’Baibulo zomwe zikugwirizana ndi nkhaniyo. Mwachitsanzo, poganizira ngati mungapite kumacheza amene tatchula kale aja, mungaganizire zimene Baibulo limanena pa nkhani ya maphwando oipa, kugwirizana ndi anthu oipa komanso kufunika koika zinthu za Ufumu pa malo oyamba m’malo mwa zofuna zathu.—Mat. 6:33; Aroma 13:13; 1 Akor. 15:33.

8. Kodi mungatani kuti mupeze mfundo zomwe zingakuthandizeni? (Onaninso chithunzi.)

8 Komabe nthawi zina mungafunike kuti wina akuthandizeni kuti mupeze zimene mukufufuza. M’bale kapena mlongo wodziwa zambiri akhoza kukuthandizani pa nkhaniyi. Komabe mungapindulenso kwambiri mukamafufuza panokha. Mungapeze mfundo zabwino zambiri m’zinthu zothandiza pophunzira monga Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani komanso Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu. Kumbukirani kuti cholinga chanu ndi choti muzitha kusankha zinthu zomwe zingasangalatse Yehova.

Muziganizira mmene Yehova akuionera nkhaniyo (Onani ndime 8) b


9. Kodi tingadziwe bwanji ngati zomwe tasankha zingasangalatse Yehova? (Aefeso 5:17)

9 Kodi tingatsimikize bwanji ngati zimene tasankha zingasangalatse Yehova? Choyamba tiyenera kumudziwa bwino. Baibulo limati: “Ngati ungadziwe Mulungu, yemwe ndi Woyera Koposa, udzakhala womvetsa zinthu.” (Miy. 9:10) Choncho kuti munthu akhale womvetsa zinthu, ayenera kudziwa bwino makhalidwe a Yehova, cholinga chake komanso zimene amakonda ndi zimene amadana nazo. Dzifunseni kuti, ‘Mogwirizana ndi zomwe ndikudziwa zokhudza Yehova, kodi ndingasankhe kuchita zinthu ziti zomwe zingamusangalatse?’—Werengani Aefeso 5:17.

10. N’chifukwa chiyani mfundo za m’Baibulo n’zofunika kwambiri kuposa miyambo kapena chikhalidwe chathu?

10 Kuti tisangalatse Yehova, nthawi zina timafunika kusankha zinthu zomwe zingakhumudwitse anthu omwe amatikonda. Mwachitsanzo, makolo angalimbikitse mwana wawo kuti akwatiwe ndi mwamuna wopeza bwino kapena amene akuona kuti angawapatse ndalama zambiri zolowolera ngakhale kuti mwamunayo sali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. N’zoona kuti iwo amafuna kuti mwana wawo azisamalidwa bwino koma ndi ndani amene adzamuthandize kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova? Kodi Yehova amaiona bwanji nkhaniyi? Tingapeze yankho la funso limeneli pa Mateyu 6:33. Palembali, Akhristu amalimbikitsidwa kuti ‘aziika Ufumu pamalo oyamba pa moyo wawo.’ Ngakhale kuti timalemekeza makolo komanso anthu a m’dera lathu, chofunika kwambiri kwa ife ndi kusangalatsa Yehova.

KUYEREKEZERA ZOTSATIRAPO ZAKE

11. Kodi ndi khalidwe liti lotchulidwa pa Afilipi 1:9, 10, lomwe lingatithandize kuyerekezera zomwe tasankha?

11 Mukafufuza mfundo za m’Baibulo zogwirizana ndi nkhani imene mukufuna kusankha, muziganizira bwino zotsatirapo zake. (Werengani Afilipi 1:9, 10.) Kuzindikira kudzakuthandizani kuti muziganizira zotsatirapo zonse za zimene mungasankhe. Nthawi zina zimakhala zosavuta kusankha zochita koma nthawi zina zimakhala zovuta. Kuzindikira kungakuthandizeni kuti musankhe zochita mwanzeru ngakhale pa nkhani zomwe ndi zovuta kwambiri.

12-13. Kodi kuzindikira kungatithandize bwanji kuti tisankhe mwanzeru pa nkhani ya ntchito?

12 Taganizirani chitsanzo ichi. Mukufufuza ntchito yomwe ingakuthandizeni kuti muzisamalira banja lanu. Ndiye papezeka ntchito ziwiri. Mukuganizira mfundo zonse monga mtundu wa ntchitoyo, nthawi yomwe muziigwira komanso mtunda umene mungamayende ndi zina. Ntchito zonsezo ndi zoti Mkhristu angagwire. Komabe inuyo mukukonda ntchito imodzi chifukwa cha mtundu wake komanso malipiro ake. Ngakhale zili choncho, pali mfundo zinanso zimene muyenera kuziganizira musanasankhe zochita.

13 Mwachitsanzo, kodi ntchitoyo iziwombana ndi nthawi yanu ya kumisonkhano? Kodi izikutherani nthawi yomwe mumafunikira kucheza ndi banja lanu ndiponso kulithandiza kuti likhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova? Kuganizira mafunso amenewa kungakuthandizeni kudziwa kuti “zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri,” ndi zokhudza kulambira kwanu komanso kusamalira banja lanu kuposa kupeza ndalama zambiri. Mukatero mungasankhe zochita zimene zingachititse kuti Yehova akudalitseni.

14. Kodi kuzindikira komanso kukonda ena kungatithandize bwanji kuti tizipewa kuwakhumudwitsa?

14 Kuzindikira kungatithandize kuti tiziganizira mmene zomwe tingasankhe zingakhudzire ena n’cholinga choti tizipewa ‘kuwakhumudwitsa.’ (Afil. 1:10) Zimenezi ndi zofunika kwambiri tikamasankha pa nkhani zokhudza kuvala ndi kudzikongoletsa. Mwachitsanzo, ifeyo tingakonde masitayilo enaake a zovala kapena kudzikongoletsa mwa njira inayake. Koma bwanji ngati abale ndi alongo komanso anthu ena angakhumudwe ndi zimene tasankha? Kuzindikira kudzatithandiza kuti tizilemekeza mmene ena angamvere. Kukonda ena kudzatilimbikitsa kuti tiziganizira “zopindulitsanso ena” komanso tikhale odzichepetsa. (1 Akor. 10:23, 24, 32; 1 Tim. 2:9, 10) Tikatero tidzasankha zinthu zomwe zimasonyeza kuti timakonda komanso kulemekeza ena.

15. Kodi tiyenera kuganizira chiyani tisanasankhe zochita pa nkhani zofunika kwambiri?

15 Mukamasankha zochita pa nkhani zofunika kwambiri, muziganiziranso zomwe mungachite kuti muzikwaniritse. Yesu anatiphunzitsa kuti ‘tiziwerengera’ mtengo wake. (Luka 14:28) Choncho muziganizira kuchuluka kwa nthawi komanso zinthu zina zomwe zingafunikire kuti zimene mwasankhazo zitheke. Nthawi zina mungafunike kukambirana ndi banja lanu kuti mudziwe mmene aliyense angathandizirepo pa zimene mwasankhazo. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika? Zingakuthandizeni kudziwa ngati zimene mwasankhazo zikufunika kukonza pena ndi pena kapenanso ngati pali njira ina yabwino kwambiri. Ndiponso mukamakambirana ndi anthu a m’banja lanu n’kumamvetsera maganizo awo, iwo amakhala okonzeka kukuthandizani kuti zimene mwasankha ziyende bwino.—Miy. 15:22.

MUZISANKHA ZINTHU ZIMENE ZINGATHEKE

16. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingakuthandizeni kuti musankhe zochita mwanzeru? (Onaninso bokosi lakuti “ Zimene Mungachite Kuti Musankhe Zochita Mwanzeru.”)

16 Ngati mwatsatira zonse zimene takambirana munkhaniyi, ndinu okonzeka kusankha zochita mwanzeru. Mwapeza mfundo zimene zingakuthandizeni kuti musankhe zochita zomwe zingasangalatse Yehova. Tsopano mungapemphe Yehova kuti akuthandizeni kuti zimene mwasankhazo ziyende bwino.

17. Kodi chofunika kwambiri n’chiyani kuti tisankhe zochita mwanzeru?

17 Ngakhale kuti kambirimbiri m’mbuyomo mwasankhapo zochita mwanzeru, muzikumbukira kuti chimene chingakuthandizeni kuti musankhe bwino si kudalira nzeru kapena luso lanu koma nzeru yochokera kwa Yehova. Iye yekha ndi amene angakuthandizeni kudziwa zinthu, kumvetsa komanso kuzindikira, zomwe ndi mbali zikuluzikulu za nzeru imeneyi. (Miy. 2:1-5) Yehova angakuthandizeni kusankha zochita zimene zimamusangalatsa.—Sal. 23:2, 3.

NYIMBO NA. 28 Tikhale pa Ubwenzi Ndi Yehova

a MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Abale ndi alongo achinyamata akukambirana za uthenga womwe alandira pa mafoni awo wowaitanira kuphwando.

b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale mmodzi akufufuza kaye asanasankhe kupita kuphwandolo.