Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’zoona Kuti Yesu Anandifera Ineyo?

Kodi N’zoona Kuti Yesu Anandifera Ineyo?

M’Baibulo muli mawu ambiri ochokera pansi pa mtima amene ananenedwa ndi anthu “monga ife tomwe.” (Yak. 5:17) Mwachitsanzo, timatha kumvetsa mmene Paulo ankamvera pamene ananena mawu opezeka pa Aroma 7:21-24. Iye anati: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine. . . . Munthu wovutika ine!” Zimene Paulo ananenazi zimatilimbikitsa nafenso tikamalephera kuchita zabwino chifukwa choti si ife angwiro.

Paulo ananenanso mawu ena ochokera pansi pa mtima. Mwachitsanzo, pa Agalatiya 2:20, iye ananena motsimikiza kuti Yesu “anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” Kodi ifenso timaona kuti Yesu anatifera ifeyo? Mwina nthawi zina timakayikira.

Tikayamba kudziona kuti ndife osafunika chifukwa cha machimo amene tinachita, nthawi zina zimakhala zovuta kuti tivomereze kuti Yehova amatikonda, anatikhululukira komanso kuti nsembe ya dipo ndi mphatso imene inaperekedwa kwa ifeyo. Koma kodi ndi zoona kuti Yesu amafuna kuti tiziona nsembe yake ngati mphatso yathuyathu? Kodi n’chiyani chingatithandize kuona kuti nsembe ya dipo imatikhudza patokha? Tiyeni tikambirane mafunso awiriwa.

KODI YESU AMAONA BWANJI NSEMBE YAKE?

Yesu amafuna kuti aliyense aziona nsembe ya dipo ngati mphatso yakeyake. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Taganizirani za nkhani ya pa Luka 23:39-43. Munthu wina anapachikidwa pafupi ndi Yesu. Iye anavomereza kuti anapachikidwa chifukwa cha zoipa zimene anachita. Ayenera kuti anapalamula zazikulu chifukwa chilango chimene analandirachi chinkaperekedwa kwa anthu ochita zoipa kwambiri. Munthuyo ankada nkhawa kwambiri ndipo anapempha Yesu kuti: “Mukandikumbukire mukakalowa mu Ufumu wanu.”

Kodi Yesu anatani? Tayerekezerani kuti mukumuona akutembenuza mutu wake movutikira kuti amuyang’ane. Ngakhale kuti akumva ululu, Yesu akuyesetsa kumwetulira kenako akuuza munthuyo kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” Yesu akanatha kungouza munthuyo kuti: “Mwana wa munthu [anabwera] . . . kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mat. 20:28) Koma iye anathandiza munthuyo kuzindikira kuti nsembe yake inkamukhudza iyeyo payekha. Yesu analankhula ndi munthuyo ngati mnzake pogwiritsa ntchito mawu akuti “iwe” komanso “ine.” Ndipo anauza munthuyo kuti adzakhala m’Paradaiso padziko lapansi.

N’zoonekeratu kuti Yesu ankafuna kuti munthuyo aziona kuti nsembe ya Khristu inali mphatso yakeyake. Ngati Yesu ankafuna kuti munthuyu aziona nsembe motere ngakhale kuti anali chigawenga, ndipo analibe mpata wotumikira Mulungu, kuli bwanji Mkhristu wobatizidwa yemwe akutumikira Mulungu? Ndiye n’chiyani chingatithandize kuti tiziona kuti nsembe ya Yesu ingatithandize ifeyo ngakhale kuti tinachitapo machimo m’mbuyomu?

ZIMENE ZINATHANDIZA PAULO

Utumiki umene Paulo anapatsidwa unkamuthandiza kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya nsembe ya Yesu. Tikutero chifukwa iye ananena kuti: “Ndikuyamika Khristu Yesu Ambuye wathu amene anandipatsa mphamvu poona kuti ndine wokhulupirika, ndipo anandipatsa utumiki. Anatero ngakhale kuti kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe.” (1 Tim. 1:12-14) Utumiki wa Paulo unamutsimikizira kuti Yesu anamuchitira chifundo, ankamukonda komanso kumudalira. Ifenso Yesu anatipatsa utumiki. (Mat. 28:19, 20) Kodi utumiki wathu ungatithandizenso kuzindikira kuti Yesu anatifera?

Albert, amene anabwezeretsedwa chaposachedwapa pambuyo pokhala kunja kwa zaka pafupifupi 34, ananena kuti: “Nthawi zonse ndimakumbukira zimene ndinalakwitsa. Koma ndikakhala mu utumiki, ndimaona kuti Yesu anandipatsa utumiki ngati mmene zinalili ndi mtumwi Paulo. Zimenezi zimandilimbikitsa kwambiri. Zimandithandiza kukhala wosangalala ndiponso kuzindikira kuti si ine wachabechabe koma ndili ndi tsogolo labwino.”​—Sal. 51:3.

Mukamaphunzira ndi anthu, muziwatsimikizira kuti Yesu amawakonda komanso kuwachitira chifundo

Allan, yemwe anali chigawenga asanaphunzire choonadi ananena kuti: “Ndimakumbukirabe zinthu zoipa zimene ndinkachitira anthu. Nthawi zina ndimakhumudwa kwambiri. Koma ndimayamikira kuti Yehova amalola munthu wochimwa ngati ine kuti ndizilalikira uthenga wabwino kwa anthu ena. Ndikamaona anthu akulandira uthenga wabwino zimandikumbutsa kuti Yehova ndi wabwino komanso wachikondi. Ndimaona kuti akundigwiritsa ntchito kuti ndithandize anthu amene anachitanso zoipa ngati ineyo.”

Utumiki umatithandiza kuti tizichita zinthu zoyenera komanso kuganizira zabwino zokhazokha. Umatitsimikizira kuti Yesu ndi wachifundo, amatikonda komanso amatikhulupirira.

YEHOVA NDI WAMKULU KUPOSA MITIMA YATHU

M’dziko la Satanali, mitima yathu ingapitirize kutitsutsa chifukwa cha zolakwa zimene tinachita m’mbuyomu. Kodi tingathane bwanji ndi vuto limeneli?

Jean, yemwe nthawi zina amadziimba mlandu chifukwa cha zoipa zimene ankachita ali wachinyamata, ananena kuti: “Ndimasangalala kuti ‘Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.’” (1 Yoh. 3:19, 20) Mtima wathu ukhoza kukhala m’malo tikamakumbukira kuti Yehova ndi Yesu amamvetsa kwambiri mavuto amene tili nawo chifukwa cha uchimo kuposa ifeyo. Paja iwo anapereka dipo chifukwa cha anthu ochimwa amene alapa osati chifukwa cha anthu angwiro.​—1 Tim. 1:15.

Tiyeni tiziganizira mozama mmene Yesu ankachitira zinthu ndi anthu ochimwa. Tizichitanso zonse zimene tingathe pa utumiki wathu. Tikamatero tidzatsimikizira m’mitima yathu kuti dipo ndi mphatso yathuyathu. Ndipo mofanana ndi Paulo, tikhoza kunena kuti Yesu “anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.”