Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 27

Tizikonzekera Kuti Tidzathe Kupirira Pozunzidwa

Tizikonzekera Kuti Tidzathe Kupirira Pozunzidwa

“Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.”​2 TIM. 3:12.

NYIMBO NA. 129 Tipitirizabe Kupirira

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera kuzunzidwa?

USIKU woti aphedwa mawa lake, Yesu ananena kuti anthu onse omutsatira adzadedwa. (Yoh. 17:14) Mpaka pano, Akhristu okhulupirika amazunzidwa ndi anthu amene amadana ndi kulambira koona. (2 Tim. 3:12) Ndipo pamene mapeto akuyandikira, adani athu azititsutsa kwambiri.​—Mat. 24:9.

2-3. (a) Kodi tiyenera kudziwa zotani zokhudza mantha? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Ndiye kodi tingakonzekere bwanji panopa? Si bwino kuyesa kuganizira zinthu zoipa zimene zingatichitikire. Tikutero chifukwa chakuti zikhoza kutichititsa mantha kapena kutidetsa nkhawa kwambiri. Ndiyeno tikhoza kugonjeratu mayesero enieni asanafike. (Miy. 12:25; 17:22) Mantha ndi chida champhamvu chimene ‘mdani wathu Mdyerekezi’ amagwiritsa ntchito pofuna kutisokoneza. (1 Pet. 5:8, 9) Ndiye tingatani kuti tikonzekere?

3 Munkhaniyi, tikambirana zimene tingachite kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova komanso chifukwa chake tiyenera kuchita zimenezi panopa. Tikambirananso zimene zingatithandize kuti tikhale olimba mtima. Pomaliza, tikambirana zimene tingachite ngati anthu ena akudana nafe.

KODI TINGALIMBITSE BWANJI UBWENZI WATHU NDI YEHOVA?

4. Mogwirizana ndi Aheberi 13:5, 6, kodi sitiyenera kukayikira chiyani? Perekani chifukwa.

4 Musamakayikire kuti Yehova amakukondani ndipo sadzakusiyani. (Werengani Aheberi 13:5, 6.) Zaka zambiri zapitazo, Nsanja ya Olonda ina inati: “Munthu amene amadziwa bwino Mulungu amamudalira kwambiri akakumana ndi mayesero.” Mfundo imeneyi ndi yoona. Kuti tipirire tikamazunzidwa, tiyenera kukonda ndiponso kudalira Yehova ndi mtima wonse popanda kukayikira ngakhale pang’ono kuti nayenso amatikonda.​—Mat. 22:36-38; Yak. 5:11.

5. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuzindikira kuti Yehova amakukondani?

5 Muziwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku n’cholinga choti muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. (Yak. 4:8) Mukamawerenga Baibulo muziganizira kwambiri makhalidwe abwino a Yehova. Muziona mmene mawu ake komanso zochita zake zimasonyezera kuti amakukondani. (Eks. 34:6) Anthu ena amavutika kukhulupirira kuti Mulungu amawakonda chifukwa sanakondedwepo ndi anthu ena. Ngati zili choncho ndi inu, muziyesetsa tsiku lililonse kulemba zimene Yehova wachita pokusonyezani chifundo komanso kukoma mtima. (Sal. 78:38, 39; Aroma 8:32) Mukamaganizira zimene zakuchitikirani komanso zimene mwawerenga m’Baibulo, mudzatha kulemba zinthu zambiri zimene Yehova wakuchitirani. Mukamayamikira kwambiri zimene Yehova amachita, ubwenzi wanu ndi iye udzalimba.​—Sal. 116:1, 2.

6. Malinga ndi Salimo 94:17-19, kodi kupemphera mochokera mumtima kungakuthandizeni bwanji?

6 Muzikonda kupemphera. Taganizirani za mwana amene wakumbatiridwa ndi bambo ake. Mwanayo akumva kuti ndi wotetezeka kwambiri moti akumasuka n’kuuza bambo akewo zinthu zabwino komanso zoipa zimene zamuchitikira tsikulo. Umu ndi mmene inuyonso mungamvere mukamapemphera kwa Yehova tsiku lililonse. (Werengani Salimo 94:17-19.) Mukamapemphera, muyenera ‘kukhuthula mtima wanu ngati madzi’ n’kuuza Atate wanu wachikondi zonse zimene zikukuchititsani mantha kapena kukudetsani nkhawa. (Maliro 2:19) Kodi n’chiyani chidzachitike mukamachita zimenezi? Baibulo limanena kuti mudzapeza “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afil. 4:6, 7) Mukamakonda kupemphera chonchi, ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimba kwambiri.​—Aroma 8:38, 39.

Munthu amalimba mtima ngati amakhulupirira Yehova ndi Ufumu wake

Kudziwa bwino za Ufumu wa Mulungu kunathandiza kwambiri Stanely Jones (Onani ndime 7)

7. N’chifukwa chiyani muyenera kukhulupirira ndi mtima wonse kuti malonjezo a Mulungu okhudza Ufumu wake adzakwaniritsidwa?

7 Musamakayikire madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse. (Num. 23:19) Ngati simukhulupirira malonjezo a Mulungu ndi mtima wonse, Satana ndi anthu ake sangavutike kukuchititsani mantha. (Miy. 24:10; Aheb. 2:15) Ndiye kodi mungatani kuti muzikhulupirira kwambiri Ufumu wa Mulungu? Mungachite bwino kupeza nthawi yofufuza ndi kuganizira malonjezo a Mulungu okhudza Ufumu komanso zimene zimakutsimikizirani kuti malonjezowo adzakwaniritsidwa. Kodi zimenezi zingakuthandizeni bwanji? Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Stanley Jones, yemwe anali m’ndende kwa zaka 7 chifukwa cha chikhulupiriro chake. * N’chiyani chinamuthandiza kupirira n’kukhalabe wokhulupirika? Iye anati: “Kudziwa bwino za Ufumu wa Mulungu ndiponso kuukhulupirira ndi mtima wonse n’kumene kunandithandiza kuti ndikhalebe wokhulupirika.” Ngati inunso mumakhulupirira malonjezo a Mulungu ndi mtima wonse, mudzakhala naye pa ubwenzi wolimba ndipo simungachite mantha.​—Miy. 3:25, 26.

8. Kodi zimene timachita panopa pa nkhani ya misonkhano zimasonyeza chiyani? Fotokozani.

8 Muzikonda kupezeka pamisonkhano. Misonkhano imatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Zimene timachita panopa pa nkhani ya misonkhano zingasonyeze zimene tidzachite tikamadzazunzidwa m’tsogolo. (Aheb. 10:24, 25) N’chifukwa chiyani tikutero? Ngati panopa timalola zinthu zing’onozing’ono kutilepheretsa kusonkhana, kodi m’tsogolo tidzatha kuika moyo wathu pa ngozi kuti tizisonkhana? Koma ngati panopa timayesetsa kufika kumisonkhano zivute zitani, ndiye kuti sitidzalola kuti adani athu atiletse kuchita zimenezi m’tsogolo. Panopa ndi nthawi yoti tiyambe kukonda kwambiri misonkhano yathu. Tikamakonda kwambiri kusonkhana sitingasiye kumvera Mulungu pa nkhaniyi ngakhale adani atatitsutsa kapena boma litatiletsa.​—Mac. 5:29.

Kuloweza malemba ndi nyimbo za Ufumu kungadzakuthandizeni pa nthawi imene mukuzunzidwa (Onani ndime 9) *

9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuloweza malemba kungatithandize pokonzekera kuzunzidwa?

9 Muziloweza malemba amene amakusangalatsani. (Mat. 13:52) Mwina mumavutika kukumbukira zinthu koma Yehova angagwiritse ntchito mzimu wake woyera pokuthandizani kukumbukira malemba. (Yoh. 14:26) M’bale wina amene anali mundende ku East Germany ndipo anatsekeredwa m’chipinda chayekha ananena kuti: “Ndinasangalala kwambiri kuti ndinali nditaloweza malemba mahandiredi angapo. Zinandithandiza kukhala ndi nkhani zambiri za m’Baibulo zoti ndiziganizira pa nthawi imene ndinali ndekhandekha.” Malembawo anathandiza m’bale wathuyu kuti akhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova komanso akhalebe wokhulupirika.

(Onani ndime 10) *

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kuloweza nyimbo?

10 Muziloweza nyimbo zotamanda Yehova. Paulo ndi Sila atatsekeredwa mundende ku Filipi, anaimba nyimbo zauzimu zomwe anaziloweza. (Mac. 16:25) Kodi n’chiyani chinathandizanso abale a ku Soviet Union amene anathamangitsidwa n’kupita ku Siberia? Mlongo wina dzina lake Mariya Fedun anati: “Tinkaimba nyimbo zonse zam’buku lathu la nyimbo zomwe tinaloweza.” Iye ananena kuti nyimbozo zinkawalimbikitsa kwambiri ndipo zinawathandiza kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. Kodi inuyo mumalimbikitsidwa mukamaimba nyimbo zauzimu zimene zimakusangalatsani? Ngati zili choncho, muyenera kuloweza panopa nyimbo zimenezo.​—Onani bokosi lakuti “ Ndithandizeni Ndikhale Wolimba Mtima.”

KODI TINGATANI KUTI TIKHALE OLIMBA MTIMA?

11-12. (a) Malinga ndi 1 Samueli 17:37, 45-47, kodi n’chiyani chinathandiza Davide kuti akhale wolimba mtima? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Davide?

11 Munthu amafunika kukhala wolimba mtima kuti apirire pozunzidwa. Kodi mungatani ngati mumaona kuti si inu olimba mtima? Kumbukirani kuti munthu sakhala wolimba mtima chifukwa cha msinkhu wake, mphamvu zake kapena luso lake. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Davide pa nthawi imene ankafuna kumenyana ndi Goliyati. Tikamuyerekezera ndi Goliyati, Davide ankaoneka wamng’ono, wopanda mphamvu komanso analibe zida zamphamvu. Iye analibe ndi lupanga lomwe koma anali wolimba mtima kwambiri. Davide anathamanga molimba mtima n’kukamenyana ndi chimphona chokula mtimacho.

12 N’chifukwa chiyani Davide analimba mtima? Iye sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova ali naye. (Werengani 1 Samueli 17:37, 45-47.) Davide sankaganizira zoti Goliyati ndi wamkulu kwambiri kuposa iyeyo. Koma ankaona kuti Goliyatiyo ndi wamng’ono kwambiri kuyerekezera ndi Yehova. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tikhoza kukhala olimba mtima ngati sitikayikira zoti Yehova ali nafe komanso tikamakumbukira kuti adani athu ndi aang’ono kwambiri poyerekezera ndi Mulungu Wamphamvuyonse. (2 Mbiri 20:15; Sal. 16:8) Ndiye kodi tingatani kuti tikhale olimba mtima panopa, tisanayambe kuzunzidwa?

13. Kodi tingatani kuti tikhale olimba mtima? Fotokozani.

13 Kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu kungatithandize kuti tikhale olimba mtima. N’chifukwa chiyani tikutero? Ntchito yolalikira imatithandiza kuti tisamaope anthu koma tizidalira Yehova. (Miy. 29:25) Thupi la munthu limakhala lolimba akamachita masewera olimbitsa thupi. Mofanana ndi zimenezi, tikamalalikira kunyumba ndi nyumba, kumalo opezeka anthu ambiri, kumaofesi ndi m’mashopu komanso kwa anthu amene timakumana nawo, timakhala olimba mtima. Ndipo tikamalimba mtima n’kumalalikira panopa, tidzakhalanso olimba mtima n’kumalalikira ngakhale ntchito yathu italetsedwa.​—1 Ates. 2:1, 2.

Nancy Yuen sanalole kuti asiye kulalikira uthenga wabwino(Onani ndime 14)

14-15. Kodi tikuphunzira chiyani kwa alongo awiri otchulidwa m’ndimezi?

14 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi alongo awiri okhulupirika amene anali olimba mtima kwambiri. Mmodzi mwa alongowa ndi Nancy Yuen. Iye anali wopanda mantha ngakhale kuti anali wamfupi mamita 1.5. * Mlongoyu sanalole kuletsedwa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Izi zinachititsa kuti akhale kundende ya ku China kwa zaka 20. Akuluakulu a boma amene ankamufunsa mafunso ananena kuti iye anali “munthu wamakani kwambiri” m’dziko lonse la China.

Valentina Garnovskaya sankakayikira zoti Yehova ali naye (Onani ndime 15)

15 Chitsanzo china ndi cha Mlongo Valentina Garnovskaya. Iye anamangidwa maulendo atatu ku Soviet Union ndipo tikaphatikiza zaka zonse zimene anali kundende zikukwana 21. * N’chifukwa chiyani anamangidwa? Iye sankafuna kusiya kulalikira moti akuluakulu a boma ananena kuti anali “chigawenga choopsa kwambiri.” Koma kodi n’chiyani chinathandiza alongo awiriwa kuti akhale olimba mtima? Iwo sankakayikira ngakhale pang’ono zoti Yehova ali nawo.

16. N’chiyani chingatithandize kuti tikhale olimba mtima?

16 Malinga ndi zimene takambirana, kuti tikhale olimba mtima sitiyenera kuganizira za mphamvu zathu kapena luso lathu. Koma tiyenera kukhulupirira kuti Yehova ali nafe ndipo akutimenyera nkhondo. (Deut. 1:29, 30; Zek. 4:6) Zimenezi n’zimene zingatithandize kuti tikhale olimba mtima.

KODI TINGATANI NGATI ANTHU AKUDANA NAFE?

17-18. Kodi Yesu anapereka chenjezo liti pa Yohane 15:18-21? Fotokozani.

17 Tonsefe timafuna kulemekezedwa ndi anthu. Koma sitiyenera kuganiza kuti ndife opanda pake ngati anthu ena sasangalala nafe. Paja Yesu ananena kuti: “Ndinu odala anthu akamadana nanu, kukusalani, kukunyozani ndi kukana dzina lanu n’kumanena kuti ndi loipa, chifukwa cha Mwana wa munthu.” (Luka 6:22) Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamenepa?

18 Yesu sankatanthauza kuti Akhristu azisangalala akamadedwa. Koma ankangofotokoza mmene zinthu zizikhalira. Akhristufe sitili mbali ya dziko. Timatsatira mfundo zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo timalalikira uthenga umene iye ankalalikira. Izi zimachititsa kuti anthu m’dzikoli azidana nafe. (Werengani Yohane 15:18-21.) Koma chomwe ife timafuna n’kusangalatsa Yehova basi. Ndiye kaya anthu ena azidana nafe chifukwa choti timakonda Atate athu, zimenezo ndi zawo.

19. Kodi tingatsanzire bwanji atumwi?

19 Tisalole kuti zolankhula kapena zochita za anthu zitisokoneze mpaka kufika pochita manyazi kuti ndife a Mboni za Yehova. (Mika 4:5) Kuganizira zimene atumwi anachita ku Yerusalemu pambuyo poti Yesu waphedwa kungatithandize kuti tisamaope anthu. Iwo ankadziwa kuti atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankadana nawo kwambiri. (Mac. 5:17, 18, 27, 28) Koma tsiku lililonse ankapita kukachisi ndipo ankasonyeza kuti ndi otsatira a Yesu. (Mac. 5:42) Iwo sanafooke chifukwa cha mantha. Kuti nafenso tikhale opanda mantha, tiyenera kusonyeza kuti ndife a Mboni za Yehova, kaya tili kuntchito, kusukulu kapena m’dera limene timakhala.​—Mac. 4:29; Aroma 1:16.

20. N’chifukwa chiyani atumwi ankasangalala ngakhale kuti ankadedwa?

20 N’chifukwa chiyani atumwi ankasangalala? Iwo ankadziwa chimene chinkachititsa kuti anthu azidana nawo. Ndipo ankaona kuti ndi mwayi waukulu kuzunzidwa chifukwa chochita zimene Yehova amafuna. (Luka 6:23; Mac. 5:41) Patapita nthawi, mtumwi Petulo analemba kuti: “Ngakhale mutavutika chifukwa cha chilungamo, mudzakhalabe odala.” (1 Pet. 2:19-21; 3:14) Tikazindikira kuti anthu akudana nafe chifukwa chakuti tikuchita zinthu zoyenera, sitidzalola kuti tifooke chifukwa choopa anthuwo.

KUKONZEKERA KUDZATITHANDIZA KWAMBIRI

21-22. (a) Kodi inuyo muchita zotani pokonzekera kuzunzidwa? (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

21 Sitikudziwa kuti ndi liti pamene tingazunzidwe kapena kuletsedwa kulambira Yehova. Koma chomwe tikudziwa n’chakuti tikhoza kukonzekera panopa. Tingakonzekere polimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova, kuyesetsa kuti tikhale olimba mtima komanso kudziwa zochita ngati anthu akudana nafe. Kukonzekera panopa kungatithandize kuti tisadzasiye kutumikira Yehova m’tsogolo.

22 Koma kodi tingatani ngati boma litatiletsa kulambira Yehova? Munkhani yotsatira, tidzakambirana mfundo zimene zingatithandize kuti tizilambirabe Yehova ngati zimenezi zitachitika.

NYIMBO NA. 118 “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

^ ndime 5 Anthufe sitifuna kuti anthu azidana nafe. Ngakhale zili choncho, tsiku lina aliyense wa ife adzazunzidwa. Ndiyeno nkhaniyi itithandiza kuti tidzalimbe mtima pa nthawi imene tikuzunzidwa.

^ ndime 7 Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya December 15, 1965, tsamba 756-767.

^ ndime 14 Onani vidiyo ya pa JW Broadcasting® ya mutu wakuti Anthu Adzadziwa Dzina la Yehova. Pitani pamene alemba kuti ZOCHITIKA PA MOYO WA ANTHU ENA. Onaninso Nsanja ya Olonda yachingelezi ya July 15, 1979, tsamba 4-7.

^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Makolo akugwiritsa ntchito makadi pothandiza ana awo kuti aloweze malemba pa nthawi ya kulambira kwa pabanja.

^ ndime 70 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Banja likupita kumisonkhano pa galimoto ndipo likuimba nyimbo za Ufumu.