Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 26

Kodi Mungagwire Nawo Ntchito Yothandiza Anthu Kukhala Ophunzira a Yesu?

Kodi Mungagwire Nawo Ntchito Yothandiza Anthu Kukhala Ophunzira a Yesu?

“Mulungu . . . amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.”​—AFIL. 2:13.

NYIMBO NA. 64 Tizigwira Ntchito Yokolola Mosangalala

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yehova anakuchitirani zotani?

KODI munayamba bwanji choonadi? Choyamba munamva uthenga wabwino mwina kwa makolo anu, mnzanu wakuntchito kapena wakusukulu kapenanso kwa a Mboni ena omwe ankalalikira khomo ndi khomo. (Maliko 13:10) Kenako wa Mboni wina anachita khama kumaphunzira nanu Baibulo. Pa nthawi imene ankaphunzira nanu, munayamba kukonda Yehova ndipo munadziwa kuti iyenso amakukondani. Yehova anakuthandizani kudziwa choonadi ndipo panopa ndinu wophunzira wa Yesu Khristu komanso mukuyembekezera kudzapeza moyo wosatha. (Yoh. 6:44) Mosakayikira, mumayamikira Yehova kuti analimbikitsa munthu wina kuti akuphunzitseni choonadi komanso analola kuti mukhale mtumiki wake.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Tsopano popeza kuti tikudziwa choonadi, tili ndi mwayi wothandiza ena kuti nawonso aziyenda panjira yopita ku moyo wosatha. N’kutheka kuti sizimativuta kulalikira kunyumba ndi nyumba. Koma mwina zikhoza kumativuta kuti tiyambitse komanso kuchititsa maphunziro a m’Baibulo. Ngati inunso zimenezi zimakuchitikirani, mfundo za munkhaniyi zingakuthandizeni kwambiri. Tikambirananso zimene zimatilimbikitsa kuti tiziphunzitsa ena komanso zomwe tingachite polimbana ndi mavuto amene angatilepheretse kuchititsa maphunziro a Baibulo. Choyamba tiyeni tikambirane chifukwa chake sitiyenera kungokhala alaliki chabe, koma tiyenera kukhalanso aphunzitsi a uthenga wabwino.

YESU ANATILAMULA KUTI TIZILALIKIRA KOMANSO KUPHUNZITSA

3. Kodi n’chifukwa chiyani timalalikira?

3 Pamene Yesu anali padzikoli, anapatsa otsatira ake lamulo lomwe linali ndi mbali ziwiri. Choyamba iye anawauza kuti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndipo anawasonyeza mmene angachitire zimenezi. (Mat. 10:7; Luka 8:1) Mwachitsanzo, Yesu anauza ophunzira ake zimene angachite ngati anthu atakana kapena kumvetsera uthenga wa Ufumu. (Luke 9:2-5) Yesu ananeneratunso kuchuluka kwa ntchitoyi pomwe anauza otsatira ake kuti adzachitira “umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14; Mac. 1:8) Kaya anthu adzamvetsera kapena ayi, ophunzirawo ankafunika kuuza ena zokhudza Ufumu wa Mulungu komanso zimene udzachite.

4. Mogwirizana ndi Mateyu 28:18-20, n’chiyaninso chimene tiyenera kuchita kuwonjezera pa kulalikira za Ufumu?

4 Kodi mbali yachiwiri ya lamulo la Yesu inali yoti chiyani? Iye anauza otsatira ake kuti aziphunzitsa anthu kusunga zinthu zonse zimene analamula. Koma kodi ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa inaperekedwa kwa Akhristu oyambirira okha monga mmene ena amanenera? Ayi. Yesu anasonyeza kuti ntchito yofunikayi idzapitirizabe kuchitika mpaka mu nthawi yathu ino kapena kuti “mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Werengani Mateyu 28:18-20.) Zikuoneka kuti Yesu anapereka lamuloli pa nthawi imene anaonekera kwa ophunzira ake omwe analipo oposa 500. (1 Akor. 15:6) Komanso m’masomphenya amene anaonetsa Yohane, Yesu anasonyeza kuti amafuna kuti ophunzira ake onse azithandiza ena kudziwa zokhudza Yehova.​—Chiv. 22:17.

5. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 3:6-9, kodi Paulo anayerekezera ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa ndi chiyani?

5 Mtumwi Paulo anayerekezera ntchito yophunzitsa anthu ndi ulimi. Zimenezi zikusonyeza kuti pali zambiri zimene timayenera kuchita, osati kungodzala mbewu. Iye anakumbutsa Akhristu a ku Korinto kuti: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathirira . . . Inuyo ndinu munda wa Mulungu umene ukulimidwa.” (Werengani 1 Akorinto 3:6-9.) Popeza ndife antchito ‘m’munda wa Mulungu,’ sikuti timangodzala mbewu koma timazithirira pafupipafupi n’kumaona mmene zikukulira. (Yoh. 4:35) Komabe timazindikira kuti Mulungu ndi amene amakulitsa mbewuzo.

6. Kodi ntchito yothandiza ena imaphatikizapo kuchita chiyani?

6 Timafufuza anthu ‘omwe ali ndi maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’ (Mac. 13:48) Kuti anthu amenewa akhale ophunzira a Yesu, tiyenera kuwathandiza (1) kumvetsa, (2) kukhulupirira komanso (3) kugwiritsa ntchito zimene aphunzira m’Baibulo. (Yoh. 17:3; Akol. 2:6, 7; 1 Ates. 2:13) Aliyense mumpingo angathandize ophunzira Baibulo powasonyeza chikondi komanso kuwalandira ndi manja awiri akabwera kumisonkhano. (Yoh. 13:35) Mphunzitsiyo amafunika khama komanso nthawi yambiri kuti athandize wophunzirayo kusiya miyambo ndi zikhulupiriro zimene ‘zinazikika molimba’ mwa iye. (2 Akor. 10:4, 5) Pangadutse miyezi yambiri kuti munthu asinthe moyo wake n’kufika poyenerera kuti abatizidwe. Koma kusintha kumeneko n’kothandiza kwambiri.

CHIKONDI CHIMATICHITITSA KUTHANDIZA ENA KUKHALA OPHUNZIRA

7. Kodi n’chiyani chimatilimbikitsa kuti tizigwira nawo ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu?

7 N’chifukwa chiyani timagwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira? Chifukwa choyamba n’chakuti timakonda Yehova. Tikamayesetsa kumvera lamulo lakuti tizilalikira komanso kuthandiza ena kukhala ophunzira, timasonyeza kuti timakonda Mulungu. (1 Yoh. 5:3) Taganizirani izi: Chifukwa chakuti mumakonda Yehova, munayamba kugwira nawo ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba. Kodi zinali zophweka kumvera lamulo limeneli? Osati kwenikweni. Kodi mutafika kwa nthawi yoyamba pakhomo la munthu munkachita mantha? N’zosakayikitsa. Komabe munkadziwa kuti imeneyi ndi ntchito imene Yesu akufuna kuti muzigwira ndipo munamvera lamuloli. M’kupita kwa nthawi zinakhala zosavuta kuti muzigwira ntchito yolalikira. Koma kodi mumamva bwanji mukaganiza zochititsa phunziro la Baibulo? Kodi mumachita mantha? Mwina ndi choncho. Komabe mukam’pempha Yehova kuti akuthandizeni kuthetsa mantha, komanso kukulimbitsani mtima kuti muyambitse phunziro la Baibulo, iye adzachititsa kuti mukhale ndi mtima wofuna kuthandiza ena kuti akhale ophunzira a Yesu.

8. Mogwirizana ndi Maliko 6:34, kodi n’chiyaninso chimatichititsa kuti tiziphunzitsa ena?

8 Chachiwiri, kukonda anthu kumatichititsa kuti tiziphunzitsa ena choonadi. Pa nthawi ina Yesu ndi ophunzira ake anatopa kwambiri chifukwa choti analalikira kwa nthawi yaitali. Iwo ankafunika kupeza malo oti akapume, koma khamu la anthu linawatsatira komweko. Powamvera chifundo, Yesu anayamba kuwaphunzitsa “zinthu zambiri.” (Werengani Maliko 6:34.) Iye anachita zimenezi ngakhale kuti anali atatopa kwambiri. Chifukwa chiyani? Iye ankaganizira mmene anthuwo ankamvera. Ankafunitsitsa kuwathandiza chifukwa ankadziwa mavuto amene ankakumana nawo komanso kuti analibe chiyembekezo. Umunso ndi mmene anthu alili masiku ano. Sitiyenera kupusitsika ndi mmene amaonekera. Iwo ali ngati nkhosa zosochera zimene zilibe m’busa. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti anthu ngati amenewa sadziwa Mulungu ndipo alibe chiyembekezo. (Aef. 2:12) Iwo ali ‘pamsewu wopita kuchiwonongeko.’ (Mat. 7:13) Choncho tikamaganizira kuti umu ndi mmene anthu a m’gawo lathu alili, chikondi ndi chifundo zimatilimbikitsa kuti tiwathandize. Ndipo njira yabwino kwambiri imene tingawathandizire ndi kuphunzira nawo Baibulo.

9. Mogwirizana ndi Afilipi 2:13, kodi Yehova angakuthandizeni bwanji?

9 N’kutheka kuti mumazengereza kuyambitsa phunziro la Baibulo chifukwa mumaona kuti muzifunika nthawi yambiri yochititsa phunzirolo. Ngati zili choncho, muzimufotokozera Yehova mmene mukumvera. Muzimupempha kuti akuthandizeni kukhala ndi mtima wofuna kupeza komanso kuchititsa phunziro. (Werengani Afilipi 2:13.) Mtumwi Yohane anatitsimikizira kuti Mulungu adzayankha mapemphero athu omwe ndi ogwirizana ndi chifuniro chake. (1 Yoh. 5:14, 15) Choncho musamakayikire kuti Yehova adzakuthandizani kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza ena kuti akhale ophunzira a Yesu.

ZIMENE TINGACHITE POLIMBANA NDI MAVUTO ENA

10-11. N’chifukwa chiyani ena angazengereze kuchititsa phunziro la Baibulo?

10 Timaona kuti ntchito yophunzitsa ena ndi yofunika kwambiri ngakhale kuti timakumana ndi mavuto amene angatilepheretse kuchita zambiri pogwira ntchitoyi. Tiyeni tikambirane ena mwa mavuto amene timakumana nawo komanso zimene tingachite polimbana nawo.

11 Tikhoza kumaona kuti sitingachite zambiri. Mwachitsanzo, ofalitsa ena ndi achikulire kapena amadwaladwala. Kodi umu ndi mmene zilili ndi inu? Ngati ndi choncho, taganizirani zinthu zimene taphunzira pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Taona kuti n’zotheka kuchititsa maphunziro a Baibulo opita patsogolo pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono. Choncho mukhoza kuyambitsa komanso kumachititsa phunziro la Baibulo muli kunyumba kwanu. Komanso pali ubwino wina. Anthu ena amafuna kuphunzira Baibulo koma sapezeka panyumba pa nthawi imene abale akulalikira. Komabe mwina akhoza kupezeka panyumba m’mawa kwambiri kapena usiku. Kodi mungasinthe zinthu kuti muziphunzira ndi anthu pa nthawi ngati imeneyi? Yesu anaphunzitsa Nikodemo usiku, nthawi imene Nikodemoyo anaona kuti ndi yabwino kwa iye.​—Yoh. 3:1, 2.

12. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatithandize kuti tikhale aphunzitsi abwino?

12 Tingamadzikayikire kuti sitingathe kuchititsa phunziro la Baibulo. Mwina mumaona kuti muyenera kudziwa zambiri kapena kukhala ndi luso lophunzitsa musanayambe kuphunzira Baibulo ndi winawake. Ngati umu ndi mmene mumamvera, taganizirani zinthu zitatu izi zomwe zingakuthandizeni kuti musamadzikayikire. Choyamba, Yehova amaona kuti ndinu woyenerera kuphunzitsa ena. (2 Akor. 3:5) Chachiwiri, Yesu yemwe ali ndi ‘ulamuliro wonse kumwamba ndi padziko lapansi,’ wakulamulani kuti muziphunzitsa. (Mat. 28:18) Ndipo chachitatu, mukhoza kupempha ena kuti akuthandizeni. Yesu ankadalira zimene Atate wake anamuphunzitsa, inunso mungachite zomwezo. (Yoh. 8:28; 12:49) Mukhoza kupempha woyang’anira gulu lanu la utumiki, mpainiya kapena wofalitsa waluso kuti akuthandizeni kuyambitsa phunziro la Baibulo. Njira imodzi imene ingakuthandizeni kuti musamadzikayikire ndi kupita limodzi ndi ofalitsa ngati amenewa ku maphunziro awo a Baibulo.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kuzolowera njira zatsopano zophunzitsira?

13 Tingamavutike kuzolowera kugwiritsa ntchito njira komanso zinthu zatsopano. Njira imene timagwiritsa ntchito pochititsa maphunziro a Baibulo yasintha. Buku logwiritsa ntchito pophunzira Baibulo ndi anthu lakuti Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale, limafuna kuti tizikonzekera bwino komanso kuphunzitsa m’njira yosiyana ndi mmene tinkachitira m’mbuyomu. Tiziwerenga ndime zochepa n’kukhala ndi nthawi yambiri yokambirana ndi wophunzirayo. Tizigwiritsa ntchito kwambiri mavidiyo komanso zinthu zapazipangizo zamakono monga JW Library®. Ngati mungamavutike kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi, mungapemphe munthu wina kuti akuthandizeni. Mwachibadwa anthufe timakonda kuchita zinthu zimene tinazolowera. Sizophweka kuzolowera njira zatsopano zochitira zinthu. Koma Yehova ndi anthu ena angatithandize ndipo tikhoza kuona kuti n’zosavuta kusintha komanso tikhoza kumasangalala tikamaphunzira Baibulo ndi anthu. Monga mmene mpainiya wina ananenera, njira imeneyi yophunzirira, ndi “yosangalatsa kwa wophunzira komanso mphunzitsi wake.”

14. Kodi tizikumbukira chiyani ngati gawo limene timalalikira ndi lovuta, nanga lemba la 1 Akorinto 3:6, 7, lingatilimbikitse bwanji?

14 Tikhoza kumakhala m’dera limene n’zovuta kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Mwina anthu sangamachite chidwi ndi uthenga wathu ndipo akhoza kumatitsutsa. N’chiyani chingatithandize kuti tizipitirizabe kuona moyenera anthu a m’gawo ngati limeneli? Tizikumbukira kuti zinthu zikhoza kusintha mwadzidzidzi pa moyo wa anthu m’dziko loipali, ndipo anthu amene poyamba analibe chidwi akhoza kuzindikira kuti amafunika Mulungu kuti aziwatsogolera. (Mat. 5:3) Anthu ena omwe ankakana mabuku athu, patapita nthawi anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Tizikumbukiranso kuti Yehova ndiye Mwiniwake wa zokolola. (Mat. 9:38) Amafuna kuti tizipitiriza kudzala komanso kuthirira koma iye ndi amene amakulitsa. (1 Akor. 3:6, 7) Komanso ndi zolimbikitsa kudziwa kuti ngakhale kuti tilibe phunziro la Baibulo, Yehova amatidalitsa chifukwa cha khama lathu osati chifukwa cha kuchuluka kwa mabuku amene timagawira kapena maphunziro amene tili nawo. *

MUZISANGALALA POTHANDIZA ANTHU KUTI AKHALE OPHUNZIRA A YESU

Onani mmene ntchito yathu yolalikira komanso kuphunzitsa ingathandizire munthu (Onani ndime 15-17) *

15. Kodi Yehova amamva bwanji munthu akavomera kuphunzira Baibulo n’kumagwiritsa ntchito zimene akuphunzirazo?

15 Yehova amasangalala munthu akaphunzira choonadi cha m’Baibulo n’kumauzako ena zimene waphunzirazo. (Miy. 23:15, 16) Iye ayenera kuti amasangalala kwambiri akaona zimene zikuchitika masiku ano. Mwachitsanzo, ngakhale kuti m’chaka chautumiki cha 2020 padziko lonse panali mliri, tinachititsa maphunziro a Baibulo  7,705,765 zomwe zinathandiza kuti anthu 241,994 adzipereke kwa Yehova n’kubatizidwa. Ophunzira atsopanowa, nawonso azichititsa maphunziro a Baibulo kuti anthu enanso ambiri akhale ophunzira a Yesu. (Luka 6:40) N’zosakayikitsa kuti timasangalatsa mtima wa Yehova tikamagwira nawo ntchito yothandiza anthu kuti akhale ophunzira.

16. Kodi ndi cholinga chabwino chiti chimene tiyenera kukhala nacho?

16 Kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira kumafuna khama. Koma Yehova angatithandize kuphunzitsa atsopano amenewa kuti azikonda Atate wathu wakumwamba. Bwanji osakhala ndi cholinga choyambitsa komanso kuchititsa phunziro la Baibulo, ngakhale limodzi lokha? Tikhoza kudabwa ndi zimene zingachitike ngati titamagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene wapezeka kupempha munthu kuti tiziphunzira naye Baibulo. Sitikukayikira kuti Yehova adzadalitsa khama lathu.

17. Kodi tingamamve bwanji ngati titamakwanitsa kuchititsa phunziro la Baibulo?

17 Ndi mwayitu waukulu kwambiri kugwira nawo ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu choonadi. Ntchito imeneyi imatithandiza kuti tizisangalala kwambiri. Mtumwi Paulo, yemwe anathandiza anthu ambiri a ku Tesalonika kuti akhale ophunzira, anafotokoza mmene ankamvera, ndipo anati: “Kodi chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe chathu n’chiyani? Inde, mphoto yathu yoinyadira pamaso pa Ambuye wathu Yesu, pa nthawi ya kukhalapo kwake n’chiyani? Si inu amene kodi? Ndithudi, inu ndinudi ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.” (1 Ates. 2:19, 20; Mac. 17:1-4) Abale ndi alongo ambiri amamvanso chimodzimodzi masiku ano. Mlongo wina dzina lake Stéphanie ndi mwamuna wake athandiza anthu ambiri kufika pobatizidwa ndipo anati: “Palibenso chinthu china chosangalatsa kwambiri kuposa kuthandiza anthu kuti adzipereke kwa Yehova.”

NYIMBO NA. 57 Tizilalikira kwa Anthu a Mitundu Yonse

^ ndime 5 Yehova watipatsa mwayi, osati wogwira ntchito yolalikira yokha, koma kutinso tiziphunzitsa anthu kusunga zinthu zonse zimene Yesu analamula. Ndiye n’chiyani chimatilimbikitsa kuti tiziphunzitsa ena? Kodi ndi mavuto otani amene timakumana nawo tikamalikira komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale otsatira a Yesu? Nanga tingatani kuti mavutowo asatilepheretse kugwira ntchitoyi? Munkhaniyi, tikambirana mayankho a mafunso amenewa.

^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani yokhudza zimene aliyense angachite pothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu, onani nkhani yakuti, “Aliyense Mumpingo Angathandize Ophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe,” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya March 2021.

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Onani mmene kuphunzira Baibulo kungathandizire munthu kusintha moyo wake: Poyamba munthuyu akuona kuti moyo wake ulibe cholinga chifukwa sadziwa Yehova. Kenako wakumana ndi a Mboni omwe akulalikira ndipo wavomera kuti aziphunzira Baibulo. Zimene waphunzira zamuthandiza kuti adzipereke kwa Yehova ndipo akubatizidwa. M’kupita kwa nthawi nayenso akuthandiza ena kuti akhale ophunzira a Yesu. Pamapeto pake onse akusangalala m’Paradaiso.