Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi a Mboni za Yehova ayenera kugwiritsa ntchito ma webusaiti othandiza munthu kupeza wokwatirana naye?

Yehova amafuna kuti anthu okwatirana azisangalala komanso azikondana kwa moyo wawo wonse. (Mat. 19:4-6) Ndiye ngati mukufuna kukwatira kapena kukwatiwa, kodi mungatani kuti mupeze munthu woyenerera? Yehova yemwe ndi mlengi wathu amadziwa zimene tingachite kuti tikhale ndi chibwenzi komanso banja labwino. Choncho ngati mungatsatire mfundo zimene amapereka, zinthu zingakuyendereni bwino. Tiyeni tione zina mwa mfundo zimenezi.

Choyamba tiyenera kumvetsa mfundo iyi yokhudza anthufe: “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.” (Yer. 17:9) Munthu akapeza mnzake amene akufuna kukwatirana naye, akhoza kukopeka komanso kutengeka mofulumira mpaka kufika polephera kuchita zinthu moganiza bwino. Nthawi zambiri anthu akasankha kukwatira pongotengera mmene akumvera mumtima mwawo, zinthu sizimawayendera bwino. (Miy. 28:26) N’chifukwa chake si bwino kuti anthu awiri amene akondana, azifulumira kutengeka maganizo kwambiri komanso kulonjezana zinthu kumayambiriro kwa chibwenzi chawo mpaka atadziwana bwino.

Lemba la Miyambo 22:3 limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.” Ndiye kodi kugwiritsa ntchito ma webusaiti othandiza anthu kupeza okwatirana nawo n’koopsa bwanji? N’zomvetsa chisoni kuti ena aphunzira nkhwangwa ili m’mutu kuti anthu osawadziwa amene ankacheza nawo pa intaneti, ankangofuna kuseweretsa maganizo awo. Komanso anthu achinyengo amadzibisa n’cholinga choti azibera anthu osazindikira. Ndipo nthawi zina anthu achinyengowa amanama kuti ndi a Mboni.

Taganiziraninso ngozi ina imene ingakhalepo. Ma webusaiti ena amagwiritsa ntchito mapulogalamu a pa kompyuta amene amati amathandiza munthu kudziwa woyenera kukwatirana naye. Komabe palibe umboni wosonyeza kuti zimenezi zimathandiza. Ndiye kodi ndi nzeru kudalira njira zopangidwa ndi anthu pa nkhani zofunika kwambiri monga kupeza munthu wokwatirana naye? Ndipo kodi mapulogalamu a pa kompyuta angakhale odalirika ngati mfundo za m’Baibulo?​—Miy. 1:7; 3:5-7.

Mfundo ya pa Miyambo 14:15 imati: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” Musanayambe kuona munthu wina kuti ndi woyenera kukwatirana naye, muyenera kumudziwa bwino kaye. Koma zingakhale zovuta kuchita zimenezi kudzera pa intaneti. Ngakhale kuti mumaona zinthu zina zokhudza munthuyo komanso kulankhula naye kwa nthawi yayitali pa intaneti, kodi munganene kuti mumamudziwadi? Anthu ena omwe ankaganiza kuti apeza munthu wabwino wokwatira naye, anakhumudwa atakumana ndi munthuyo pamasom’pamaso.

Wolemba masalimo anati: “Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu achinyengo. Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.” (Sal. 26:4) Anthu ena amaona kuti palibe vuto kunama kapena kubisa zinthu zina zokhudza iwowo n’cholinga chakuti aoneke abwino kwa ena. Akhoza kubisa komanso sangasonyeze makhalidwe ena oipa pofotokoza zokhudza iwowo. Popeza ena amanena kuti ndi a Mboni za Yehova, ndibwino kudzifunsa kuti, kodi munthuyu ndi wobatizidwa? Kodi ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova? Kodi anthu a mumpingo mwake amamulemekeza? Kapena kodi akhoza kukhala chitsanzo choipa ndiponso munthu wosafunika kugwirizana naye? (1 Akor. 15:33; 2 Tim. 2:20, 21) Kodi ali ndi ufulu wokwatira mogwirizana ndi Malemba? Muyenera kudziwa zinthu zimenezi koma zingakhale zovuta kudziwa ngati simunafunse a Mboni ena amene amamudziwa bwino munthuyo. (Miy. 15:22) Ndipotu mtumiki wokhulupirika wa Yehova sangafune ngakhale pang’ono ‘kumangidwa m’goli’ ndi osakhulupirira.​—2 Akor. 6:14; 1 Akor. 7:39.

Popeza kuti kugwiritsa ntchito ma webusaiti othandiza anthu kupeza okwatirana nawo n’koopsa, pali njira zina zabwino zofufuzira komanso kudziwira munthu woyenera kukwatirana naye zimene zingathandize kuti munthu adzakhale ndi banja labwino. Ndiye kodi mungatani kuti mupeze munthu woyenera kukwatirana naye? Panthawi imene kukumana m’magulu n’kololeka, a Mboni za Yehova amadziwana bwino akakumana pamisonkhano yampingo, yadera,yachigawo komanso pazochitika zina.

Mukamapeza nthawi yocheza limodzi, mungadziwe bwino ngati zolinga zanu komanso mfundo zimene mumayendera zili zofanana

Ngati zili zosatheka kukumana pamodzi m’magulu, mwachitsanzo panthawi ya mliri wa COVID-19, timagwiritsa ntchito zipangizo zamakono pochita misonkhano yampingo ndipo pamakhala mwayi wodziwana ndi a Mboni ena omwe sali pabanja. Mukhozanso kuona mmene amakambira nkhani komanso mmene amasonyezera chikhulupiriro chawo akamapereka ndemanga. (1 Tim. 6:11, 12) Pambuyo pamisonkhano mukhozanso kucheza nawo pambali yochezera ya pulogalamu imene mukugwiritsa ntchito pochitira misonkhanoyo. Mukamacheza ndi a Mboni ena pa zochitika zina pogwiritsa ntchito mapulogalamu a pa kompyuta, mukhoza kuona mmene amachitira zinthu ndi anthu ena ndipo zimenezi zingakuthandizeni kudziwa mmene alili. (1 Pet. 3:4) Pakapita nthawi mukhoza kudziwana bwino, kuona ngati muli ndi zolinga zofanana komanso ngati muli oyenerana.

Munthu akagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pofufuza wokwatirana naye, akhoza kuvomereza kuti mwambi uwu ndi woona: “Kodi munthu wapeza mkazi wabwino? Ndiye kuti wapeza chinthu chabwino, ndipo Yehova amakondwera naye.”​—Miy. 18:22.