Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 29

Kodi Mwakonzekera Chisautso Chachikulu?

Kodi Mwakonzekera Chisautso Chachikulu?

“Khalani okonzeka.”​—MAT. 24:44.

NYIMBO NA. 150 Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. N’chifukwa chiyani ndi nzeru kukonzekera ngozi zam’chilengedwe kapena mavuto ena aakulu?

 KUKONZEKERA kumathandiza kuti anthu apulumuke. Ngozi zam’chilengedwe kapena mavuto enaake aakulu akachitika, nthawi zambiri anthu amene anakonzekera amapulumuka, ndipo amathanso kuthandiza anzawo. Bungwe lina lothandiza anthu la ku Europe linanena kuti: “Kukonzekera kumathandiza kwambiri.”

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera chisautso chachikulu? (Mateyu 24:44)

2 “Chisautso chachikulu” chidzayamba modzidzimutsa. (Mat. 24:21) Komabe, mosiyana ndi ngozi zina zadzidzidzi, si anthu onse omwe adzadzidzimuke ndi kuyambika kwa chisautso chachikulu. Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Yesu anachenjeza otsatira ake kuti azikonzekera za nthawiyi. (Werengani Mateyu 24:44.) Tikakhala okonzeka, zidzakhala zosavuta kupirira pa nthawiyo komanso kuthandiza ena kuti azipirira.​—Luka 21:36.

3. Kodi kupirira, chifundo komanso chikondi zingatithandize bwanji kukonzekera chisautso chachikulu?

3 Taganizirani makhalidwe atatu omwe angatithandize kukonzekera chisautso chachikulu. Kodi tidzatani ngati titauzidwa kuti tilengeze uthenga wamphamvu wachiweruzo koma anthu osakhulupirira akutitsutsa? (Chiv. 16:21) Tidzafunika kupirira kuti timvere Yehova n’kumakhulupirira kuti atiteteza. Nanga tidzatani ngati abale athu atataya zinthu zina kapena katundu wawo yense? (Hab. 3:17, 18) Tidzafunika kukhala achifundo kuti tiwapatse zimene akufunikira. Kodi tidzatani ngati mgwirizano wa mayiko utatiukira ndipo tikufunika kukhala ndi abale ndi alongo athu m’kanyumba kakang’ono kwakanthawi? (Ezek. 38:10-12) Tidzafunika kuwasonyeza chikondi chachikulu kuti tidzapirire pa nthawi yovutayo.

4. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti tiyenera kuyesetsa kukhala opirira, achifundo komanso achikondi?

4 Baibulo limatilimbikitsa kuti tipitirize kukhala opirira, achifundo komanso achikondi. Pa Luka 21:19 pamati: “Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.” Pa Akolose 3:12 pamati: “Valani chifundo.” Ndipo pa 1 Atesalonika 4:9, 10 pamati: “Mulungu amakuphunzitsani kukondana. . . . Koma tikukudandaulirani abale kuti mupitirize kutero mowonjezereka.” Mavesi onsewa analembera ophunzira omwe anali atasonyeza kale kuti anali opirira, achifundo komanso achikondi. Komabe, iwo ankafunika kupitiriza kusonyeza makhalidwewa. Ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. Kuti tithe kuchita zimenezi, tikambirana mmene Akhristu oyambirira anasonyezera lililonse la makhalidwe amenewa. Kenako tiona mmene tingawatsanzirire, zomwe zingasonyeze kuti takonzekera chisautso chachikulu.

PITIRIZANI KUKHALA OPIRIRA

5. Kodi Akhristu oyambirira ankatani kuti azipirira mayesero omwe ankakumana nawo?

5 Akhristu oyambirira ankafunika kuti azipirira. (Aheb. 10:36) Kuwonjezera pa mavuto a tsiku ndi tsiku omwe anthu onse ankakumana nawo, iwo ankakumananso ndi mayesero. Ambiri mwa Akhristuwa ankazunzidwa, osati ndi atsogoleri a Chiyuda kapena olamulira a Chiroma okha, koma ankazunzidwanso ndi achibale awo. (Mat. 10:21) Komanso nthawi zina ankafunika kulimbana ndi ziphunzitso za anthu ampatuko omwe ankafuna kugawanitsa mpingo. (Mac. 20:29, 30) Komabe Akhristuwo anapirira. (Chiv. 2:3) Kodi n’chiyani chinawathandiza? Iwo ankaganizira zitsanzo zopezeka m’Malemba za anthu omwe anapirira, monga Yobu. (Yak. 5:10, 11) Ankapempha Yehova kuti awapatse mphamvu. (Mac. 4:29-31) Komanso ankaganizira zotsatirapo zabwino zomwe akanapeza chifukwa chopirira.​—Mac. 5:41.

6. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Merita yemwe anapirira pamene ankatsutsidwa?

6 Ifenso tingathe kupirira ngati nthawi zonse titamaphunzira komanso kuganizira zitsanzo zotchulidwa m’Mawu a Mulungu ndiponso m’mabuku athu za anthu omwe anapirira. Kuchita zimenezi kunathandiza mlongo wina wa ku Albania dzina lake Merita, yemwe ankazunzidwa kwambiri ndi achibale ake. Iye anati: “Ndinalimbikitsidwa kwambiri nditaphunzira nkhani ya Yobu m’Baibulo. Yobu anavutika kwambiri. Koma ngakhale kuti sankadziwa chomwe chinkayambitsa mavuto ake, ananena kuti: ‘Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.’ (Yobu 27:5) Ndinayerekezera mayesero amene ndinkakumana nawo ndi mavuto a Yobu. Koma mosiyana ndi iye, ine ndinkadziwa yemwe ankachititsa mavuto anga.”

7. Ngati sitikukumana ndi mayesero aakulu, kodi tiyenera kuphunzira kuchita chiyani panopa?

7 Tingathenso kupitiriza kukhala opirira ngati nthawi zonse timapemphera mochokera pansi pa mtima komanso kufotokozera Yehova nkhawa zathu. (Afil. 4:6; 1 Ates. 5:17) N’kutheka kuti panopa simukukumana ndi mayesero aakulu. Komabe, kodi mumapempha Yehova kuti akutsogolereni nthawi iliyonse imene mwakhumudwa, kusokonezeka maganizo kapena kupanikizika? Ngati nthawi zonse mumapempha Mulungu kuti akuthandizeni pa mavuto alionse, simudzazengereza kumupempha kuti akuthandizeni mukadzakumana ndi mavuto aakulu m’tsogolo. Komanso simudzakayikira kuti Yehova akudziwa bwino nthawi imene angakuthandizireni ndiponso mmene angachitire zimenezi.​—Sal. 27:1, 3.

KUPIRIRA

Kupirira mayesero alionse omwe takumana nawo kungatithandize kuti tidzathenso kupirira mayesero otsatira (Onani ndime 8)

8. Kodi chitsanzo cha Mira chikusonyeza bwanji kuti kupirira mayesero panopa kungatithandize kuti tidzapirirenso m’tsogolo? (Yakobo 1:2-4) (Onaninso chithunzi.)

8 Zingadzakhale zosavuta kupirira chisautso chachikulu ngati timapirira mayesero panopa. (Aroma 5:3) N’chifukwa chiyani tikutero? Abale ambiri amaona kuti kupirira mayesero omwe anakumana nawo, kunawathandiza kuti apirirenso mayesero otsatira. Izi zawathandiza kuti azikhulupirira kwambiri kuti Yehova ndi wokonzeka kuwathandiza. Zotsatira zake n’zakuti chikhulupirirocho chimawathandiza kuti azitha kupirira mayesero otsatira. (Werengani Yakobo 1:2-4.) Mpainiya wina wa ku Albania, dzina lake Mira, anaona kuti zimene anapirira m’mbuyomu zinamuthandiza kuti azitha kupirira mayesero amene amakumana nawo panopa. Mira anavomereza kuti nthawi zina amaona ngati iye yekha ndi amene akukumana ndi mavuto ambiri. Komabe amakumbukira mmene Yehova wakhala akumuthandizira pa zaka 20 zapitazi ndipo amadziuza kuti, ‘Pitiriza kukhala wokhulupirika. Usalole kuti zonse zimene wakwanitsa kuchita pogonjetsa mavuto onse mothandizidwa ndi Yehova pa zaka zonsezi zipite pachabe.’ Inunso mungachite bwino kumaganizira mmene Yehova wakhala akukuthandizirani kupirira. Musamakayikire kuti iye amaona nthawi iliyonse imene mwapirira mayesero enaake, ndipo adzakudalitsani. (Mat. 5:10-12) Chisautso chachikulu chikamadzayamba, mudzakhala mutaphunzira kupirira ndipo mudzatsimikiza mtima kuti mupitiriza kutero.

MUZISONYEZA CHIFUNDO

9. Kodi Akhristu a ku Antiokeya wa ku Siriya anasonyeza bwanji chifundo?

9 Taganizirani zomwe zinachitikira Akhristu pa nthawi yomwe ku Yudeya kunali njala yaikulu. Akhristu a mumpingo wa ku Antiokeya wa ku Siriya atamva za njalayo, mosakayikira anamvera chisoni abale a ku Yudeya. Koma kenako anachitapo kanthu powasonyeza chifundo. Iwo “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo lililonse limene akanatha kwa abale okhala ku Yudeya.” (Mac. 11:27-30) Ngakhale kuti Akhristu omwe anakhudzidwa ndi njalayi ankakhala kutali, Akhristu a ku Antiokeya anali atatsimikiza mtima kuti awathandize.​—1 Yoh. 3:17, 18.

CHIFUNDO

Ngozi zam’chilengedwe zimatipatsa mwayi woti tisonyeze ena chifundo (Onani ndime 10)

10. Kodi tingasonyeze bwanji chifundo kwa Akhristu anzathu omwe akhudzidwa ndi mavuto aakulu? (Onaninso chithunzi.)

10 Ifenso masiku ano tingasonyeze chifundo ngati Akhristu anzathu akhudzidwa ndi ngozi zam’chilengedwe kapena mavuto ena aakulu. Tingachitepo kanthu mofulumira, mwina pofunsa akulu ngati tingagwire nawo ntchito yopereka thandizo, popereka ndalama zothandiza pa ntchito yapadziko lonse kapenanso popempherera amene akhudzidwa. b (Miy. 17:17) Mwachitsanzo, mu 2020, Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi oposa 950 anakhazikitsidwa padziko lonse kuti athandize anthu omwe anakhudzidwa ndi mliri wa COVID-19. Timayamikira kwambiri abale amene amatumikira m’makomiti amenewa. Chifundo chimawalimbikitsa kuti azithandiza abale ndi alongo awo powapatsa zimene akufunikira, kuwalimbikitsa mwauzimu komanso nthawi zina kuwakonzera kapena kuwamangira nyumba zawo ndi malo olambirira.​—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 8:1-4.

11. Kodi kuchitira ena chifundo kumasonyeza bwanji kuti timalemekeza Atate wathu wakumwamba?

11 Tikamasonyeza chifundo Akhristu anzathu pakachitika ngozi inayake, anthu ena amaona kudzipereka kwathu. Mwachitsanzo, mu 2019, mphepo yamphamvu yotchedwa Dorian inawononga Nyumba ya Ufumu ku Bahamas. Pamene abale ankamanganso Nyumba ya Ufumuyo, anafunsa munthu wina wogwira ntchito zomangamanga yemwe si wa Mboni kuti awauze ndalama zomwe zinkafunikira kuti awathandize ntchito inayake. Iye anawauza kuti: “Ndingakonde kupereka zipangizo . . . komanso kukugwirirani ntchitoyi kwaulere. Ndikungofuna kuchitira zimenezi gulu lanuli. Ndimachita chidwi ndi chifundo chimene mumasonyeza anzanu.” Anthu ambiri m’dzikoli sadziwa Yehova. Komabe, ambiri amaona zimene a Mboni za Yehova amachita. Ndi mwayi wamtengo wapatali kudziwa kuti zimene timachita posonyezana chifundo, zingachititse ena kuti afune kuphunzira zambiri zokhudza Yehova, amene ndi “wachifundo chochuluka.”​—Aef. 2:4.

12. Kodi kuyesetsa kukhala achifundo kungatithandize bwanji kukonzekera chisautso chachikulu? (Chivumbulutso 13:16, 17)

12 N’chifukwa chiyani tidzafunika kumasonyeza chifundo pa chisautso chachikulu? Baibulo limasonyeza kuti amene satenga nawo mbali pa nkhani zandale, azikumana ndi mavuto panopa komanso pa nthawi ya chisautso chachikulu. (Werengani Chivumbulutso 13:16, 17.) Tidzafunika kuthandiza abale ndi alongo athu kupeza zofunikira pa moyo. Choncho tiyeni tiyesetse kuti pamene Mfumu yathu, Khristu Yesu, adzabwere kudzapereka chiweruzo, adzatipeze tikusonyeza chifundo ndipo adzatiuze kuti ‘tilowe mu Ufumu.’​—Mat. 25:34-40.

MUZIKONDA KWAMBIRI ABALE NDI ALONGO ANU

13. Monga mmene lemba la Aroma 15:7 likusonyezera, n’chiyani chinathandiza Akhristu oyambirira kuti azikondana kwambiri?

13 Chikondi ndi chimene chinkadziwikitsa Akhristu oyambirira. Koma kodi zinali zophweka kuti azisonyezana chikondi? Taganizirani za anthu osiyanasiyana omwe anali mumpingo wa ku Roma. Sikuti mumpingowu munali Ayuda okhaokha, omwe makolo awo anawaphunzitsa kuti azitsatira Chilamulo cha Mose. Koma munalinso anthu amitundu ina omwe anali osiyana kwambiri ndi Ayuda. N’kutheka kuti ena anali akapolo pomwe ena ayi, ndipo mwina enanso anali ndi akapolo. Ndiye kodi Akhristuwo akanatani kuti azikondana kwambiri ngakhale kuti anali osiyana chonchi? Mtumwi Paulo anawalimbikitsa kuti ‘azilandirana.’ (Werengani Aroma 15:7.) Kodi ankatanthauza chiyani pamenepa? Mawu amene anawamasulira kuti “landira,” amatanthauza kuchitira winawake zinthu mokoma mtima kapena kumuchereza, monga kumuitanira kunyumba kapena pakati pa anzathu. Mwachitsanzo, Paulo anauza Filimoni kuti alandire kapolo wake Onesimo yemwe anathawa, ndipo anati: “Umulandire ndi manja awiri.” (Filim. 17) Komanso Purisikila ndi Akula analandira Apolo yemwe ankadziwa mfundo zochepa zokhudza Chikhristu poyerekeza ndi iwowo ndipo “anamutenga.” (Mac. 18:26) Choncho Akhristuwa sanalole kuti kusiyana pa zinthu zina kuwagawanitse ndipo ankalandirana.

CHIKONDI

Timafunikira chikondi cha abale ndi alongo athu (Onani ndime 15)

14. Kodi Anna ndi mwamuna wake anasonyeza bwanji chikondi?

14 Ifenso tingasonyeze kuti timakonda abale ndi alongo athu powalola kuti akhale anzathu. Nthawi zambiri zimenezi zimachititsa kuti nawonso ayambe kutikonda. (2 Akor. 6:11-13) Taganizirani zimene zinachitikira Anna ndi mwamuna wake. Patangopita kanthawi kochepa kuchokera pomwe anapita ku West Africa monga amishonale, mliri wa COVID-19 unayamba. Ngakhale kuti anali atangofika kumene, iwo sakanatha kukumana ndi abale ndi alongo a mumpingo wawo. Ndiye kodi banjali likanasonyeza bwanji chikondi? Iwo ankacheza ndi abale ndi alongowo kudzera pavidiyokomfelensi n’kumawauza kuti ankafunitsitsa kwambiri kuti awadziwe. Zimenezi zinakhudza kwambiri mabanja omwe ankacheza nawo, moti ankawaimbira mafoni komanso kuwalembera mameseji pafupipafupi. N’chifukwa chiyani Anna ndi mwamuna wake ankayesetsa kuti adziwe abale ndi alongowo? Anna anati: “Sindidzaiwala zimene abale ndi alongo ankachita posonyeza chikondi banja lathu pa mavuto ndi pa mtendere, ndipo zimenezi zinandilimbikitsa kuti ndizisonyezanso chikondi kwa ena.”

15. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Vanessa pa nkhani yokonda abale ndi alongo athu? (Onaninso chithunzi.)

15 Ambirife tili m’mipingo imene muli abale ndi alongo omwe ndi osiyana pa zinthu zambiri komanso makhalidwe. Kuganizira makhalidwe awo abwino kungatithandize kuti tiziwakonda kwambiri. Mlongo wina yemwe akutumikira ku New Zealand, dzina lake Vanessa, zinkamuvuta kuti azigwirizana ndi ena mumpingo. M’malo mosiya kucheza ndi anthu amene anali ndi makhalidwe omwe samusangalatsa, iye anaganiza zoti azipeza nthawi yambiri yochita nawo zinthu limodzi. Kuchita zimenezi kunamuthandiza kuti adziwe zinthu zimene zimachititsa kuti Yehova aziwakonda. Iye anati: “Kungochokera pamene mwamuna wanga anakhala woyang’anira dera, timapeza nthawi yochita zinthu ndi abale ndi alongo ambiri omwe ndi osiyana makhalidwe, ndipo zimakhala zosavuta kuti tizigwirizana nawo. Panopa ndimakonda anthu onse. N’zoonekeratu kuti nayenso Yehova amasangalala ndi zimenezi chifukwa anatikokera m’gulu limene muli anthu osiyanasiyana.” Tikamaphunzira kuona anthu mmene Yehova amawaonera, timasonyeza kuti timawakonda.​—2 Akor. 8:24.

Pa nthawi ya chisautso chachikulu, Yehova adzatiteteza monga mmene analonjezera tikadzapitiriza kuchita zinthu mogwirizana ndi abale ndi alongo (Onani ndime 16)

16. N’chifukwa chiyani chikondi chidzakhala chofunika kwambiri pa chisautso chachikulu? (Onaninso chithunzi.)

16 Chikondi chidzakhala chofunika kwambiri pa chisautso chachikulu. Kodi n’kuti komwe tidzapeze chitetezo chisautsochi chikadzayamba? Taganizirani malangizo amene Yehova anapereka kwa anthu ake pamene Ababulo ankawaukira. Iye anati: “Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Zikuoneka kuti malangizo amenewa akugwiranso ntchito kwa ife amene tikuyembekezera chisautso chachikulu. ‘Zipinda zamkati’ zingatanthauze mipingo yathu. Pa nthawi ya chisautso chachikulu, Yehova adzatiteteza monga mmene analonjezera ngati tidzapitirize kuchita zinthu mogwirizana ndi abale ndi alongo athu. Choncho panopa tiyenera kuyesetsa kuti kuwonjezera pa kulola kuchita zinthu ndi abale ndi alongo athu, tiziwakondanso. Zimenezi ndi zofunika kwambiri kuti tidzapulumuke.

TIZIKONZEKERA PANOPA

17. Ngati titakonzekera panopa, kodi tidzakwanitsa kuchita chiyani pa chisautso chachikulu?

17 “Tsiku lalikulu la Yehova” lidzakhala loopsa kwa anthu onse. (Zef. 1:14, 15) Nawonso atumiki a Yehova adzakumana ndi mavuto. Ngati titakonzekereratu panopa tidzatha kukhala mosatekeseka komanso kuthandiza ena. Tidzatha kupirira mavuto alionse omwe tingakumane nawo. Abale ndi alongo athu akamadzavutika, tidzachita zomwe tingathe powasonyeza chifundo komanso kuwapatsa zimene akufunikira. Ndipo tidzagwirizana ndi abale ndi alongo athu omwe tinali titayamba kale kuwakonda. Kenako Yehova adzatidalitsa potipatsa moyo wosatha m’dziko limene simudzakhalanso mavuto alionse.​—Yes. 65:17.

NYIMBO NA. 144 Yang’ananibe Pamphoto

a Chisautso chachikulu chiyamba posachedwapa. Makhalidwe monga kupirira, chifundo komanso chikondi adzatithandiza pa nthawi yovuta kwambiriyi, yomwe sinachitikepo ndi kale lonse. Munkhaniyi, tiona zimene Akhristu oyambirira anachita kuti akhale ndi makhalidwewa, mmene ifenso tingachitire zimenezo masiku ano komanso mmene makhalidwewa angatithandizire kukonzekera chisautso chachikulu.

b Amene angafune kugwira nawo ntchito yopereka chithandizo, choyamba ayenera kulemba Fomu ya Ofuna Kutumikira Mongodzipereka M’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga (DC-50) kapena Fomu ya Amene Akufuna Utumiki Wongodzipereka (A-19) kenako n’kudikira kuti adzaitanidwe kukathandiza pa ntchito inayake.