Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 32

Muzitsanzira Yehova pa Nkhani Yololera

Muzitsanzira Yehova pa Nkhani Yololera

“Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera. Ambuye ali pafupi.”—AFIL. 4:5.

NYIMBO NA. 89 Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso

ZIMENE TIPHUNZIRE a

Kodi mungakonde kukhala ngati mtengo uti? (Onani ndime 1)

1. Kodi Mkhristu ayenera kukhala ngati mtengo m’njira iti? (Onaninso chithunzi.)

 MWAMBI wina umati, “Mphepo sithyola mtengo umene umapindika.” Mwambiwu ukusonyeza kuti kulolera ndi chinthu chofunika kwambiri kuti mtengo usathyoke. Kuti tipitirize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, Akhristufe tiyenera kukhala ololera. Tingachite zimenezi povomereza zinthu zikasintha pa moyo wathu komanso kulemekeza maganizo a ena ndiponso zimene asankha.

2. Kodi ndi makhalidwe ati omwe angatithandize zinthu zikasintha pa moyo wathu, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Monga atumiki a Yehova timafuna kukhala ololera. Timafunanso kukhala odzichepetsa komanso oona mtima. Munkhaniyi tiona mmene makhalidwe amenewa anathandizira Akhristu ena kuzolowera kusintha komwe kunachitika pa moyo wawo. Tionanso mmene angatithandizire ifeyo. Koma choyamba, tiyeni tiphunzire zokhudza Yehova ndi Yesu, omwe ndi zitsanzo zabwino kwambiri pa nkhani yololera.

YEHOVA NDI YESU NDI OLOLERA

3. Kodi tili ndi umboni wotani wosonyeza kuti Yehova ndi wololera?

3 Yehova amatchulidwa kuti “Thanthwe” chifukwa choti ndi wosasunthika. (Deut. 32:4) Komabe iye ndi wololera. Pamene zinthu zikusintha m’dzikoli, Mulungu wathu nayenso akupitiriza kusintha mmene amachitira zinthu kuti akwaniritse cholinga chake. Yehova analenga anthu m’chifaniziro chake, choncho nawonso amatha kusintha zinthu zikasintha. Iye anatipatsa mfundo za m’Baibulo zomveka bwino zomwe zimatithandiza kuti tizisankha zochita mwanzeru, kaya tikukumana ndi mavuto otani. Chitsanzo chimene Yehova amatipatsa komanso mfundo zake ndi umboni wakuti ngakhale kuti iye ndi “Thanthwe,” ndi wololera.

4. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova ndi wololera. (Levitiko 5:7, 11)

4 Zonse zimene Yehova amachita zimasonyeza kuti ndi wololera komanso amazichita m’njira yabwino. Iye sakhwimitsa zinthu akamachita zinthu ndi anthu. Taganizirani mmene anasonyezera kuti ndi wololera pochita zinthu ndi Aisiraeli. Sankayembekezera kuti anthu azipereka nsembe zofanana, kaya anthuwo ndi olemera kapena osauka. Nthawi zina ankalola kuti munthu apereke nsembe mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wake.​—Werengani Levitiko 5:7, 11.

5. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova ndi wodzichepetsa komanso wokoma mtima.

5 Kudzichepetsa komanso kukoma mtima kumachititsa Yehova kuti akhale wololera. Mwachitsanzo Yehova anasonyeza kuti ndi wodzichepetsa pamene ankafuna kuwononga anthu oipa ku Sodomu. Pogwiritsa ntchito angelo ake, Yehova anauza Loti kuti athawire kudera lamapiri. Koma Loti ankachita mantha kupita kumeneko. Choncho anachonderera Yehova kuti iye ndi banja lake athawire ku Zowari, tauni yaing’ono imene inkafunikanso kuwonongedwa. Yehova akanatha kuuza Loti kuti atsatirebe malangizo amene anamupatsa. M’malomwake anavomereza zimene Loti anapempha ngakhale kuti zimenezi zinachititsa kuti asawononge mzinda wa Zowari. (Gen. 19:18-22) Patapita zaka zambiri, Yehova anasonyezanso chifundo kwa anthu a mumzinda wa Nineve. Iye anatumiza Yona kuti akalengeze kuti mzinda woipa wa Nineve uwonongedwa. Koma ataona kuti anthu a mumzindawo alapa, anawamvera chisoni ndipo sanawawononge.​—Yona 3:1, 10; 4:10, 11.

6. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene Yesu ankatsanzirira Yehova pa nkhani yololera.

6 Yesu ankatsanzira Yehova pa nkhani yololera. Iye anatumizidwa padziko lapansili kuti akalalikire kwa “nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” Komabe iye anasonyeza kuti ndi wololera pamene ankachita utumiki wake. Pa nthawi ina, mayi wina yemwe sanali wa Chiisiraeli anamupempha kuti achiritse mwana wake wamkazi, yemwe anali atagwidwa ndi “chiwanda chochititsa mantha.” Mwachifundo Yesu anachita zomwe mayiyo anamupempha ndipo anamuchiritsira mwana wakeyo. (Mat. 15:21-28) Taganiziraninso chitsanzo china. Chakumayambiriro kwa utumiki wake, Yesu ananena kuti:“Aliyense wondikana . . . , inenso ndidzamukana.” (Mat. 10:33) Komatu Yesu sanamusiye Petulo ngakhale kuti Petuloyo anali atamukana maulendo angapo. Ankadziwa kuti Petulo anali atalapa komanso anali wokhulupirika. Ataukitsidwa, iye anaonekera kwa Petulo ndipo mwachidziwikire anamutsimikizira kuti anamukhululukira komanso kuti amamukonda.​—Luka 24:33, 34.

7. Mogwirizana ndi Afilipi 4:5, kodi timafuna kukhala ndi mbiri yotani?

7 Taona kuti Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu ndi ololera. Nanga bwanji ifeyo? Yehova amayembekezera kuti ifenso tizikhala ololera. (Werengani Afilipi 4:5.) M’Baibulo lina anamasulira vesili kuti: “Muzidziwika ndi mbiri yoti ndinu ololera.” Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi anthu amaona kuti ndine wololera kapena amandiona kuti ndine wokhwimitsa zinthu, wovuta kapena womva zake zokha? Kodi ndimakakamiza ena kuti azingoyendera maganizo anga? Kapena kodi ndimamvetsera maganizo a ena komanso kuchita zimene akufuna ngati zili zoyenera kutero?’ Zimene timachita pa nkhani ya kulolera zingasonyeze ngati timatsanzira kwambiri Yehova ndi Yesu kapena ayi. Tsopano tikambirana mbali ziwiri zimene timafunika kukhala ololera: Pamene zinthu zasintha pa moyo wathu ndiponso pamene ena akuona komanso kusankha zinthu mosiyana ndi ifeyo.

MUZIKHALA OLOLERA ZINTHU ZIKASINTHA

8. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala ololera zinthu zikasintha pa moyo wathu? (Onaninso mawu a m’munsi.)

8 Kulolera kumaphatikizapo kukhala okonzeka kusintha zinthu zikasintha pa moyo wathu. Nthawi zina kusintha kungachititse kuti tikumane ndi mavuto osayembekezereka. Mwadzidzidzi, tingakumane ndi mavuto okhudza thanzi lathu. Mwinanso kusintha pa nkhani zachuma kapena zandale kungasokoneze kwambiri moyo wathu. (Mlal. 9:11; 1 Akor. 7:31) Chikhulupiriro chathu chingayesedwenso pamene utumiki wathu wasintha. Kaya takumana ndi mavuto otani, tikhoza kuzolowera kusintha komwe kwachitika ngati titachita zinthu 4 zotsatirazi: (1) kuvomereza mmene zinthu zilili, (2) kuganizira za m’tsogolo, (3) kuganizira zabwino zimene zikuchitika komanso (4) kuthandiza ena. b Tiyeni tione zimene zinachitikira anthu ena, zomwe zikusonyeza kuti kutsatira mfundozi n’kothandiza.

9. Kodi banja lina lomwe likuchita umishonale linatani litakumana ndi mavuto osayembekezereka?

9 Muzivomereza mmene zinthu zilili. Emanuele ndi Francesca anatumizidwa kukachita umishonale kudziko lina. Atangoyamba kuphunzira chilankhulo china komanso kusonkhana ndi mpingo wawo watsopano, mliri wa COVID-19 unayamba. Chifukwa cha izi, iwo ankafunika kumakhala kwaokha. Mwadzidzidzi, amayi a Francesca anamwalira. Iye ankafunitsitsa kukhala limodzi ndi achibale awo pamalirowo, koma chifukwa cha mliriwu sakanakwanitsa kupita. Ndiye kodi anatani atakumana ndi zofooketsazi? Choyamba, Emanuele ndi Francesca monga banja, anapemphera kwa Yehova kuti awapatse nzeru kuti tsiku lililonse azitha kupirira komanso asamade nkhawa kwambiri. Yehova anayankha pemphero lawo powapatsa malangizo a pa nthawi yake kudzera m’gulu lake. Iwo analimbikitsidwa ndi zimene m’bale wina ananena muvidiyo ina, kuti: “Tikavomereza mwamsanga kuti zinthu zasintha, m’pamenenso timakhala osangalala kwinaku tikugwiritsira ntchito mpata umenewu potumikira Yehova ndi kuthandiza ena ngakhale kuti zinthu zasintha.” c Chachiwiri, anaganiza zowonjezere luso lawo pa nkhani yolalikira pafoni, mpaka anayambitsa phunziro la Baibulo. Chachitatu, iwo ankavomera kulimbikitsidwa ndi kuthandizidwa ndi abale ndi alongo awo ndipo ankayamikira. Tsiku lililonse kwa chaka chonse, mlongo wina ankawatumizira meseji yokhala ndi mfundo ya m’Baibulo. Mofanana ndi zimenezi, ifenso tikamavomereza mmene zinthu zilili pa moyo wathu, tidzakhala osangalala chifukwa cha zimene tikukwanitsa kuchita.

10. Kodi mlongo wina anatani kuti azolowere kusintha kwakukulu komwe kunachitika pa moyo wake?

10 Muziganizira kwambiri zam’tsogolo komanso zabwino zimene zikuchitika. Mlongo wina wa ku Romania dzina lake Christina, yemwe akukhala ku Japan, anakhumudwa mpingo wa Chingelezi womwe ankasonkhana utathetsedwa. Komabe, iye sankangoganizira zomwe zinachitikazo. M’malomwake, anasankha kuti azichita zonse zomwe angathe mumpingo wa Chijapanizi womwe anayamba kusonkhana, polalikira nawo mwakhama m’gawo la mpingowu. Iye anapempha mayi wina yemwe poyamba ankagwira naye ntchito kuti amuthandize kuphunzira Chijapanizi. Mayiyo anavomera kumagwiritsa ntchito Baibulo ndiponso kabuku ka Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale pophunzitsa Christina chilankhulochi. Sikuti Christina anangowonjezera luso lake lolankhula Chijapanizi, koma mayiyo anayambanso kuchita chidwi ndi mfundo za choonadi. Tikamaganizira zam’tsogolo komanso kuona zinthu moyenera, zinthu zomwe zasintha mwadzidzidzi zingabweretse madalitso omwe sitimawayembekezera.

11. Kodi banja lina linatani kuti lipirire litakumana ndi mavuto a zachuma?

11 Muzithandiza ena. Banja lina lomwe likukhala m’dziko limene ntchito yathu ndi yoletsedwa linasiya kupeza ndalama zokwanira dziko lawo litakumana ndi mavuto a zachuma. Ndiye kodi banjali linatani kuti lizolowere kusinthaku? Choyamba, iwo anayamba kukhala moyo wosalira zambiri. Kenako, m’malo momangoganizira za mavuto awo, iwo anayamba kuthandiza ena pochita khama pa ntchito yolalikira. (Mac. 20:35) Bambo wa banjalo anati: “Kuchita zambiri pa ntchito yolalikira kunatithandiza kuti tisamaganizire kwambiri zofooketsa, koma tiziganizira kwambiri zochita chifuniro cha Mulungu.” Zinthu zikasintha pa moyo wathu, tiyenera kukumbukira kuti chofunika kwambiri ndi kuthandiza ena, makamaka pogwira nawo ntchito yolalikira.

12. Kodi chitsanzo cha mtumwi Paulo chingatithandize bwanji kuti tizikhala okonzeka kusintha tikamalalikira?

12 Tikamagwira ntchito yolalikira, tiyenera kukhala okonzeka kusintha. Timakumana ndi anthu osiyana zikhulupiriro, kochokera komanso mmene amaonera zinthu. Mtumwi Paulo ankatha kusintha akamalalikira ndipo tingaphunzirepo kanthu pa chitsanzo chake. Yesu anasankha Paulo kukhala ‘mtumwi wotumidwa kwa mitundu ina.’ (Aroma 11:13) Pa utumiki wakewu, iye ankalalikira Ayuda, Agiriki, anthu ophunzira, alimi, anthu olemekezeka ndiponso mafumu. Kuti aziwafika pa mtima, Paulo ankakhala “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana.” (1 Akor. 9:19-23) Iye ankachita chidwi ndi zikhalidwe, kochokera ndiponso zikhulupiriro za anthuwo, ndipo ankasintha mmene ankalalikirira kuti zigwirizane ndi zimenezo. Ifenso zinthu zingamatiyendere bwino mu utumiki ngati timachita chidwi ndi anthu n’kumasintha mmene timalalikirira kuti zigwirizane ndi mmene zinthu zilili pa moyo wawo.

MUZILEMEKEZA MAGANIZO A ENA

Ngati ndife ololera, timalemekeza maganizo a ena (Onani ndime 13)

13. Kodi tingapewe mavuto ati otchulidwa pa 1 Akorinto 8:9 ngati timalemekeza maganizo a anthu ena?

13 Kukhala ololera kumatithandizanso kuti tizilemekeza maganizo a anthu ena. Mwachitsanzo, alongo athu ena amakonda kuphoda, pomwe ena ayi. Akhristu ena amasangalala kumwako mowa pang’ono, pomwe ena amasankha kuti asamamwe n’komwe. Akhristu onse amafuna kukhala ndi thanzi labwino koma amasankha zinthu mosiyana pa nkhani yosamalira thanzi lawo. Ngati timaona kuti zimene timasankha pa nkhani inayake ndiye zabwino kwambiri n’kumalimbikitsa Akhristu anzathu kuti azichita zomwezo, tikhoza kukhumudwitsa ena komanso kugawanitsa mpingo. Ndipotu sitingafune kuchita zimenezi ngakhale pang’ono. (Werengani 1 Akorinto 8:9; 10:23, 24) Tiyeni tikambirane zitsanzo ziwiri zosonyeza kuti kugwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba kungatithandize kuti tiziona zinthu moyenera komanso kuti tipitirize kukhala pamtendere.

Ngati ndife ololera, timalemekeza maganizo a ena (Onani ndime 14)

14. Kodi Tiyenera kutsatira mfundo ziti za m’Baibulo pa nkhani ya kuvala ndi kudzikongoletsa?

14 Kuvala ndi kudzikongoletsa. M’malo motiikira malamulo pa nkhani ya zimene tiyenera kuvala, Yehova anatipatsa mfundo zoti tizitsatira. Tiyenera kuvala moyenera monga atumiki a Mulungu, n’kumasonyeza kuti ndife oganiza bwino, odzichepetsa komanso “anzeru.” (1 Tim. 2:9, 10; 1 Pet. 3:3) Choncho sitichititsa anthu kuti azingoganizira za ifeyo chifukwa cha mmene tavalira. Mfundo za m’Baibulo zingathandizenso akulu kuti asamaike malamulo awoawo pa nkhani ya zovala komanso masitayilo a tsitsi. Mwachitsanzo, akulu mumpingo wina ankafuna kuthandiza abale achinyamata omwe ankatengera sitayilo ina yomwe inali yofala, yosunga tsitsi lalifupi koma losapesa. Kodi akuluwa akanathandiza bwanji achinyamatawa popanda kuwaikira malamulo? Woyang’anira dera anawauza malangizo oti akapatse abalewa kuti, “Ngati mukukamba nkhani papulatifomu ndiye abale ndi alongo akuchita chidwi kwambiri ndi mmene mukuonekera, osati zimene mukunena, ndiye kuti pali vuto ndi mmene mwavalira ndi kudzikongoletsera.” Kufotokoza zinthu mwanjira imeneyi kunathandiza kuthetsa nkhaniyo popanda kupanga lamulo. d

Ngati ndife ololera, timalemekeza maganizo a ena (Onani ndime 15)

15. Kodi ndi malamulo komanso mfundo ziti zomwe timatsatira tikamasankha thandizo la chipatala? (Aroma 14:5)

15 Thandizo lachipatala. Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha zochita pa nkhani yosamalira thanzi lake. (Agal. 6:5) Koma pa nkhaniyi, m’Baibulo muli malamulo ochepa achindunji, monga lamulo lokhudza kupewa magazi ndiponso zamizimu, ndipo izi zimakhudza thandizo lamankhwala lomwe Mkhristu angasankhe kulandira. (Mac. 15:20; Agal. 5:19, 20) Koma pa nkhani zina munthu amasankha yekha. Ena amasankha kulandira thandizo lamankhwala kuchipatala kokha, pamene ena amasankha njira zina zosamalira thanzi lawo. Kaya timaona kuti njira inayake yosamalira thanzi lathu ndi yabwino kwambiri, tiyenera kulemekeza ufulu wa abale ndi alongo athu wosankha njira imene akuona kuti ndi yabwino kwa iwowo. Pa nkhaniyi, nthawi zonse tiyenera kumakumbukira mfundo zotsatirazi: (1) Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetseretu matenda onse. (Yes. 33:24) (2) Mkhristu aliyense ayenera kukhala “wotsimikiza ndi mtima wonse” za chimene chingamuthandize kwambiri. (Werengani Aroma 14:5.) (3) Sitiyenera kuweruza ena kapena kuwakhumudwitsa. (Aroma 14:13) (4) Akhristu amasonyeza chikondi ndipo amaona kuti kukhala ogwirizana mumpingo n’kofunika kwambiri kuposa ufulu wawo wosankha zochita. (Aroma 14:15, 19, 20) Ngati titamakumbukira mfundozi, tidzapitiriza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi abale ndi alongo athu ndiponso tidzalimbikitsa mtendere mumpingo.

Ngati ndife ololera, timalemekeza maganizo a ena (Onani ndime 16)

16. Kodi mkulu angasonyeze bwanji kuti ndi wololera akamachita zinthu ndi akulu anzake? (Onaninso zithunzi.)

16 Akulu ayenera kukhala chitsanzo chabwino pa nkhani yololera. (1 Tim. 3:2, 3) Mwachitsanzo, mkulu sayenera kuyembekezera kuti maganizo ake azitsatiridwa nthawi zonse, chabe chifukwa chakuti iyeyo ndi wamkulu kuposa akulu ena. Iye amadziwa kuti mzimu wa Yehova ungachititse mkulu aliyense pabungwe lawo kunena zinthu zomwe zingathandize bungwelo kusankha zochita mwanzeru. Ndipo ngati sizikusemphana ndi mfundo za m’Baibulo, akulu ololera amavomereza mofunitsitsa zimene akulu ambiri pabungwe lawo asankha, ngakhale kuti si zimene iwowo akanasankha.

UBWINO WOKHALA WOLOLERA

17. Kodi Akhristu ololera amapeza madalitso ati?

17 Akhristu amapeza madalitso ambiri chifukwa chokhala ololera. Timakhala pa ubwenzi wabwino ndi abale ndi alongo athu ndipo mumpingo mumakhala mtendere. M’banja la Yehova lomwe ndi logwirizana muli anthu osiyana zochita ndi zikhalidwe ndipo izi zimatisangalatsa. Koposa zonse, timasangalala kudziwa kuti tikutsanzira Mulungu wathu Yehova, yemwe ndi wololera.

NYIMBO NA. 90 Tizilimbikitsana

a Yehova ndi Yesu ndi ololera ndipo amafuna kuti ifenso tikhale ololera. Ngati ndife ololera, zidzakhala zosavuta kuvomereza zinthu zikasintha pa moyo wathu, monga pa nkhani yokhudza thanzi lathu kapena zachuma. Tidzalimbikitsanso mtendere ndi mgwirizano mumpingo.

b Onani nkhani yakuti “Zimene Mungachite Zinthu Zikasintha” mu Galamukani! Na. 4 2016.

c Onerani vidiyo yakuti Kucheza ndi M’bale Dmitriy Mikhaylov, yomwe ili mu nkhani yakuti “Yehova Amasintha Chizunzo Kukhala Mwayi Wolalikira,” mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ka March-April 2021.

d Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya kuvala ndi kudzikongoletsa, onani phunziro 52 m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.