Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 28

NYIMBO NA. 123 Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika

Kodi Mumatha Kuzindikira Choonadi?

Kodi Mumatha Kuzindikira Choonadi?

“Khalani olimba, mutamanga kwambiri choonadi mʼchiuno mwanu ngati lamba.”—AEF. 6:14.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona mmene tingadziphunzitsire kuti tizitha kusiyanitsa pakati pa choonadi chimene Yehova watiphunzitsa ndi mfundo zabodza zimene Satana ndi otsutsa amafalitsa.

1. Kodi timamva bwanji tikaganizira za choonadi chimene taphunzira?

 ANTHU a Yehova amakonda choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu. Zimene timawerenga m’mawu akewo zimalimbitsa chikhulupiriro chathu. (Aroma 10:17) Timakhulupirira kuti Yehova wakhazikitsa mpingo wa Chikhristu kuti ‘uzilimbikitsa ndi kuteteza choonadi.’ (1 Tim. 3:15) Timasangalalanso kugonjera ‘amene akutsogolera’ pakati pathu akamafotokoza choonadi cha m’Baibulo komanso kutipatsa malangizo ogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna.—Aheb. 13:17.

2. Mogwirizana ndi Yakobo 5:​19, kodi n’chiyani chingatichitikire pambuyo pophunzira choonadi?

2 Komabe, ngakhale kuti timadziwa choonadi komanso kufunika kotsatira malangizo a gulu la Mulungu, tikhoza kusocheretsedwa. (Werengani Yakobo 5:19.) Satana amafunitsitsa kuti tisiye kukhulupirira Baibulo komanso malangizo amene timalandira kuchokera ku gulu la Mulungu.—Aef. 4:14.

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsitsa choonadi? (Aefeso 6:​13, 14)

3 Werengani Aefeso 6:​13, 14. Posachedwapa, Mdyerekezi adzagwiritsa ntchito mabodza pofuna kusokoneza anthu a mitundu yonse kuti atsutsane ndi Yehova. (Chiv. 16:​13, 14) Tikudziwanso kuti Satana ayesetsa kwambiri kuti asokoneze anthu a Yehova. (Chiv. 12:9) Choncho tingachite bwino kudziphunzitsa kuti tizisiyanitsa choonadi ndi mfundo zabodza, n’kumamvera choonadicho. (Aroma 6:17; 1 Pet. 1:22) Kuchita zimenezi n’kumene kungathandize kuti tidzapulumuke pa chisautso chachikulu.

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Munkhaniyi tikambirana makhalidwe awiri amene angatithandize kuti tizizindikira choonadi chochokera m’Baibulo ndiponso kutsatira malangizo amene gulu la Mulungu limatipatsa. Kenako tikambirana zinthu zitatu zimene tingachite kuti tigwiritsitse choonadi.

MAKHALIDWE AMENE ANGATITHANDIZE KUTI TIZIZINDIKIRA CHOONADI

5. Kodi kuopa Yehova kumatithandiza bwanji kuzindikira choonadi?

5 Kuopa Yehova. Kuopa Yehova moyenera kumatithandiza kuti tizimukonda kwambiri moti sitingachite chilichonse chimene chingamukhumudwitse. Timafunitsitsa kuphunzira kuti tizitha kusiyanitsa pakati pa zoyenera ndi zosayenera ndiponso pakati pa choonadi ndi mfundo zabodza n’cholinga choti tizisangalatsa Yehova. (Miy. 2:​3-6; Aheb. 5:14) Sitiyenera kulola kuti tiziopa kwambiri anthu kuposa mmene timakondera Yehova chifukwa nthawi zambiri zimene anthu amakonda sizisangalatsa Mulungu.

6. Kodi kuopa anthu kunachititsa bwanji atsogoleri 10 a Aisiraeli kupotoza choonadi?

6 Tikamaopa kwambiri anthu kuposa Mulungu tikhoza kupatutsidwa pa choonadi. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi atsogoleri amafuko 12 amene anapita kukaona dziko limene Mulungu analonjeza kuti adzapereka kwa Aisiraeli. Atsogoleri 10 ankaopa kwambiri Akanani kuposa mmene ankakondera Yehova. Iwo anauza Aisiraeli anzawo kuti: “Sitingathe kukalimbana nawo anthuwo, chifukwa ndi amphamvu kuposa ifeyo.” (Num. 13:​27-31) N’zoona kuti malinga n’kuona kwa anthu, Akanani anali amphamvu kuposa Aisiraeli. Koma ponena kuti Aisiraeli sakanatha kugonjetsa adani awo ndiye kuti sankaganizira za Yehova. Atsogoleri 10 amenewa anafunika kuganizira zimene Yehova ankafuna kuti Aisiraeli achite. Ankafunikanso kuganizira zimene iye anali atangowachitira kumene. Ndiyeno akanazindikira kuti mphamvu za Akanani zinali zochepa kwambiri poyerekezera ndi mphamvu za Yehova zopanda malire. Mosiyana ndi atsogoleri opanda chikhulupirirowo, Yoswa ndi Kalebe ankafuna kusangalatsa Yehova. Iwo anauza anthuwo kuti: “Ngati Yehova akusangalala nafe, adzatilowetsadi mʼdzikolo nʼkulipereka kwa ife.”—Num. 14:​6-9.

7. Kodi tingatani kuti tiziopa kwambiri Yehova? (Onaninso chithunzi.)

7 Kuti tiziopa kwambiri Yehova, tiyenera kukhala ofunitsitsa kuti tizimusangalatsa pa chilichonse chomwe timasankha kuchita. (Sal. 16:8) Mukamawerenga nkhani za m’Baibulo muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikanakhalapo, ndikanasankha kuchita chiyani?’ Mwachitsanzo, yerekezerani kuti munkamva pamene atsogoleri amafuko 10 a Aisiraeli ankalankhula zinthu zosalimbikitsa. Kodi mukanakhulupirira zimene ankanena n’kuyamba kuopa anthu, kapena kukonda kwanu Yehova kukanakuchititsani kuchita zinthu zomusangalatsa? Aisiraeli onse sanakhulupirire choonadi chimene Yoswa ndi Kalebe ankalankhula. Zotsatira zake n’zakuti onse anataya mwayi wokalowa m’Dziko Lolonjezedwa.—Num. 14:​10, 22, 23.

Kodi mukanakhulupirira ndani? (Onani ndime 7)


8. Kodi tiyenera kuyesetsa kukhala ndi khalidwe liti, ndipo n’chifukwa chiyani?

8 Kudzichepetsa. Yehova amaulula choonadi chake kwa anthu odzichepetsa. (Mat. 11:25) Ifeyo tinadzichepetsa n’kulola kuti tiphunzitsidwe choonadi. (Mac. 8:​30, 31) Koma tiyenera kukhala osamala kuti tisayambe kudzikuza. Kunyada kungatichititse kuona kuti maganizo athu ndi anzeru kuposa mfundo za m’Malemba komanso malangizo amene gulu la Yehova limatipatsa.

9. Kodi tingatani kuti tikhalebe odzichepetsa?

9 Kuti tikhalebe odzichepetsa tiyenera kukumbukira kuti ndife ang’ono kwambiri poyerekezera ndi Yehova. (Sal. 8:​3, 4) Tiyeneranso kupemphera kuti tikhale ndi mtima wodzichepetsa komanso wophunzitsika. Yehova adzatithandiza kuti tiziona kuti maganizo ake, omwe timawaphunzira kuchokera m’Baibulo komanso m’gulu lake, ndi ofunika kwambiri kuposa maganizo athu. Mukamawerenga Baibulo, muzipeza umboni wotsimikizira kuti Yehova amakonda anthu odzichepetsa osati onyada kapena odzikuza. Tiyenera kuyesetsa kuti tikhalebe odzichepetsa tikalandira utumiki umene umatichititsa kuti tizionekera kwambiri kwa anthu.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIGWIRITSITSE CHOONADI

10. Kodi Yehova wakhala akugwiritsa ntchito ndani kuti apereke malangizo kwa anthu ake?

10 Muzikhulupirira malangizo ochokera kugulu la Mulungu. Kale Yehova anagwiritsa ntchito Mose kenako Yoswa popereka malangizo kwa Aisiraeli. (Yos. 1:​16, 17) Aisiraeli ankadalitsidwa akamaona anthu amenewa ngati oimira Yehova Mulungu. Patapita zaka zambiri, mpingo wa Chikhristu unakhazikitsidwa ndipo atumwi 12 ndi amene ankapereka malangizo. (Mac. 8:​14, 15) Kenako m’gulu la anthu opereka malangizowa munalinso akulu a ku Yerusalemu. Chifukwa chotsatira malangizo a amuna okhulupirikawa, “anthu m’mipingo anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndipo chiwerengero chinkawonjezeka tsiku ndi tsiku.” (Mac. 16:​4, 5) Masiku anonso timadalitsidwa tikamatsatira malangizo ochokera kugulu la Yehova. Koma kodi Yehova angamve bwanji ngati sitimvera anthu amene iye wawasankha kuti azititsogolera? Tingapeze yankho la funsoli poganizira zimene zinachitika pamene Aisiraeli ankapita kukalowa m’Dziko Lolonjezedwa.

11. Kodi n’chiyani chinachitikira Aisiraeli omwe sankalemekeza Mose amene Mulungu anamusankha kuti aziwatsogolera? (Onaninso chithunzi.)

11 Pa nthawi ina Aisiraeli ali pa ulendo wokalowa m’Dziko Lolonjezedwa, amuna ena otchuka ankatsutsa Mose komanso udindo umene Yehova anamupatsa. Iwo ananena kuti: “Gulu lonseli [osati Mose yekha] ndi loyera, ndipo Yehova ali pakati pawo.” (Num. 16:​1-3) N’zoona kuti Mulungu ankaona kuti ‘gulu lonselo’ linali loyera, koma Yehova anali atasankha Mose kuti azitsogolera anthu ake. (Num. 16:28) Potsutsana ndi Mose, anthu oukirawa ankatsutsana ndi Yehova. M’malo moganizira zimene Yehova ankafuna, iwo ankaganizira kwambiri zimene iwowo ankafuna. Ankafuna kuti akhale ndi mphamvu zambiri komanso kutchuka. Mulungu anapha anthu amene ankatsogolera pa kuukirako komanso anthu masauzande ambiri amene anali kumbali yawo. (Num. 16:​30-35, 41, 49) Masiku anonso, timadziwa kuti Yehova sasangalala ndi anthu amene salemekeza malangizo ochokera ku gulu lake.

Kodi mukanakhala kumbali ya ndani? (Onani ndime 11)


12. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira gulu la Yehova?

12 Tiyenera kupitiriza kukhulupirira gulu la Yehova. Ngati pakufunika kusintha zimene timakhulupirira pa mfundo zina zake za m’Baibulo kapenanso njira imene timagwirira ntchito za Ufumu, anthu amene amatitsogolera sazengereza kusintha. (Miy. 4:18) Iwo amachita zimenezi chifukwa amafunitsitsa kusangalatsa Yehova. Iwo amayesetsanso kusankha zochita pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu chifukwa m’Baibulo ndi momwe muli mfundo zimene Akhristu onse amatsatira.

13. Kodi mawu akuti “chitsanzo cha mawu olondola” amatanthauza chiyani, nanga tiyenera kuchita chiyani ndi mfundozi?

13 “Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola.” (2 Tim. 1:13) Mawu akuti “chitsanzo cha mawu olondola,” amatanthauza mfundo za m’Baibulo zimene Akhristu amakhulupirira. (Yoh. 17:17) Chilichonse chimene timakhulupirira chimachokera pa mfundo zimenezi. Gulu la Yehova latiphunzitsa kuti tizigwiritsitsa mfundozi. Tikamachita zimenezi tidzadalitsidwa.

14. Kodi Akhristu ena anatani kuti asiye kutsatira “chitsanzo cha mawu olondola”?

14 Kodi n’chiyani chingachitike ngati titasiya kutsatira “chitsanzo cha mawu olondola”? Taganizirani chitsanzo ichi. M’nthawi ya atumwi Akhristu ena ankafalitsa mphekesera yakuti tsiku la Yehova linali litafika. N’kutheka kuti panali kalata imene inanena zimenezi ndipo anthu ankaganiza kuti inalembedwa ndi Paulo. Akhristu ena a ku Tesalonika anayamba kukhulupirira komanso kufalitsa zimenezi asanafufuze. Iwo sakanapusitsidwa zikanakhala kuti anakumbukira zimene Paulo anawaphunzitsa pa nthawi imene anali nawo limodzi. (2 Ates. 2:​1-5) Iye analangiza abale akewo kuti asamangokhulupirira zilizonse zimene amva. Pofuna kuwathandiza kuti izi zisadzawachitikirenso m’tsogolo, Paulo anamaliza kalata yake yachiwiri yopita kwa Atesalonika ndi mawu akuti: “Landirani moni wanga, amene ineyo Paulo ndalemba ndi dzanja langa. Nthawi zonse ndimalemba chonchi mʼmakalata anga onse, kuti mudziwe kuti ndine amene ndalemba. Umu ndi mmene ndimalembera.”—2 Ates. 3:17.

15. Kodi tingadziteteze bwanji ku nkhani zabodza zomwe zingaoneke ngati zoona? Perekani chitsanzo. (Onaninso zithunzi.)

15 Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Paulo opita kwa Atesalonika? Tikamva zinazake zomwe sizikugwirizana ndi zomwe timaphunzira m’Baibulo kapenanso mphekesera, tiyenera kuchita zinthu mwanzeru. M’dziko lomwe poyamba linkatchedwa Soviet Union, adani athu anafalitsa kalata yooneka ngati ikuchokera kulikulu lathu. Kalatayo inalimbikitsa abale ena kuti apange kagulu kena kapadera koima pakokha. Kalatayo inkaoneka ngati yachokeradi kulikulu lathu. Koma abale okhulupirika sanapusitsidwe. Iwo anazindikira kuti uthenga wa m’kalatayo sunkagwirizana ndi zomwe akhala akuphunzitsidwa. Masiku anonso adani athu amagwiritsa ntchito njira zamakono pofuna kutisokoneza kapena kutichititsa kuti tisamagwirizane. M’malo molola kuti wina aliyense “asinthe maganizo [athu]” omwe ndi olondola, tingadziteteze poganizira mosamala ngati zimene tamva kapena kuwerenga zikugwirizana ndi mfundo za choonadi zomwe tikuzidziwa kale.—2 Ates. 2:2; 1 Yoh. 4:​1,

Musamapusitsidwe ndi nkhani zabodza zomwe zingaoneke ngati zoona (Onani ndime 15) a


16. Mogwirizana ndi Aroma 16:​17, 18, kodi tiyenera kuchita chiyani ngati ena akuchita zinthu zosemphana ndi choonadi?

16 Pitirizani kugwirizana ndi anthu omwe ndi okhulupirika kwa Yehova. Mulungu amafuna kuti tizimulambira mogwirizana ndi abale ndi alongo athu. Tingapitirizebe kukhala ogwirizana ngati tagwiritsitsa choonadi. Aliyense amene amachita zinthu zosemphana ndi choonadi, amayambitsa kuti anthu mumpingo asamagwirizane, n’chifukwa chake Mulungu amatilangiza kuti ‘tiziwapewa.’ Kupanda kutero tingapezeke kuti tapatutsidwa pa choonadi.—Werengani Aroma 16:​17, 18.

17. Kodi kuzindikira komanso kugwiritsitsa choonadi kumatithandiza bwanji?

17 Tikazindikira choonadi komanso kuchigwiritsitsa, timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso timakhala ndi chikhulupiriro cholimba. (Aef. 4:​15, 16) Sitimapusitsidwa ndi mabodza komanso ziwembu za Satana ndipo Yehova adzapitiriza kutiteteza pa chisautso chachikulu. Pitirizani kugwiritsitsa choonadi “ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.”—Afil. 4:​8, 9.

NYIMBO NA. 122 Khalani Olimba Komanso Osasunthika

a MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Chithunzi choyerekezera chosonyeza pamene abale athu a m’dziko lomwe linkatchedwa Soviet Union, analandira kalata yooneka ngati yochokera kulikulu lathu koma inali yochokera kwa adani. Masiku ano adani athu angagwiritse ntchito intaneti pofalitsa nkhani zabodza zokhudza gulu la Yehova.