Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 29

NYIMBO NA. 121 Timafunika Kukhala Odziletsa

Tiyenera Kukhala Maso Kuti Tizipewa Mayesero

Tiyenera Kukhala Maso Kuti Tizipewa Mayesero

“Khalani maso ndipo mupitirize kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.”MAT. 26:41.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Nkhaniyi itithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tizipewa kuchita tchimo komanso zimene zingachititse kuti tichite tchimolo.

1-2. (a) Kodi Yesu anawachenjeza chiyani ophunzira ake? (b) N’chifukwa chiyani ophunzirawo anamuthawa Yesu? (Onaninso zithunzi.)

 YESU ananena kuti: “Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” a (Mat. 26:41b) Ponena zimenezi, iye anasonyeza kuti ankamvetsa kuti anthufe si angwiro. Koma mawu akewanso ndi chenjezo loti tizipewa kudzidalira. Usiku womwewo asananene mawu amenewa, ophunzira ake anali atasonyeza kudzidalira ponena kuti sadzasiya Mbuye wawo. (Mat. 26:35) Iwo anali ndi zolinga zabwino koma sankadziwa kuti sizikanakhala zophweka kuchita zimenezi ngati zinthu zikanavuta kwambiri. Choncho Yesu anawachenjeza kuti: “Khalani maso ndipo mupitirize kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.”—Mat. 26:41a.

2 N’zomvetsa chisoni kuti ophunzirawo analephera kukhala maso. Yesu atamangidwa, iwo anachita mantha ndipo anamuthawa. Chifukwa chakuti sanali maso ophunzirawo anachita ndendende zomwe ananena kuti sangachite, zomwe ndi kumusiya Yesu.—Mat. 26:56.

Yesu anauza ophunzira ake kuti akhale maso n’cholinga choti asayesedwe, koma iwo anamuthawa (Onani ndime 1-2)


3. (a) Kuti tipitirize kukhala okhulupirika kwa Yehova, n’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kudzidalira? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Sitiyenera kudzidalira kwambiri kuti nthawi zonse tidzachita zoyenera. N’zoona kuti timafunitsitsa kuti tisachite chilichonse chomwe chingakhumudwitse Yehova. Komabe si ife angwiro choncho tikhoza kuyesedwa kuti tichite zoipa. (Aroma 5:12; 7:​21-23) Mosayembekezera, tingapezeke kuti tayamba kuona zinthu zinazake zoipa ngati zabwino. Kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova ndi Yesu, tiyenera kutsatira malangizo a Yesu oti tikhalebe maso. Nkhaniyi itithandiza kuti tizichita zimenezi. Choyamba, tikambirana zinthu zimene tiyenera kusamala nazo. Kenako tiona zimene tingachite kuti tizipewa mayesero. Pomaliza tikambirana zomwe zingatithandize kuti tipitirize kukhala maso.

KODI TIYENERA KUKHALA MASO PA ZINTHU ZITI?

4-5. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhalanso maso ndi machimo ang’onoang’ono?

4 Ngakhale machimo amene amaoneka ang’onoang’ono angathe kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Angachititsenso kuti tichite machimo akuluakulu.

5 Tonsefe timayesedwa kuti tichite zoipa. Koma aliyense ali ndi zofooka zake, kaya zomwe zingachititse kuti achite tchimo lalikulu, ayambe kuchita makhalidwe oipa kapena kugwera mumsampha woyamba kuganiza ngati anthu a m’dzikoli. Wina angakhale ndi chilakolako champhamvu chofuna kuchita zoipa monga kuseweretsa maliseche kapena kuonera zolaula. Pamene wina angamalimbane ndi vuto la kuopa anthu, kufuna kumangoyendera maganizo ake okha, kukwiya msanga ndi zina. Monga mmene Yakobo ananenera, “munthu aliyense amayesedwa ndi chilakolako chake chimene chimamukopa ndi kumukola.”—Yak. 1:14.

6. Kodi tiyenera kukhala oona mtima pa nkhani iti?

6 Kodi mumadziwa zinthu zimene zingakuyeseni inuyo mosavuta? Simuyenera kumadzinamiza n’kumanyalanyaza zofooka zanu kapena kumaganiza kuti ndinu wolimba kwambiri moti simungachite zoipa. (1 Yoh. 1:8) Ndipotu Paulo ananena kuti ngakhale anthu “amene ndi oyenerera mwauzimu” akhoza kuyesedwa ngati sangakhale maso. (Agal. 6:1) Choncho tiyenera kukhala oona mtima n’kumazindikira zofooka zathu.—2 Akor. 13:5.

7. Kodi tiyenera kudziwa bwino chiyani? Perekani chitsanzo.

7 Kodi tiyenera kuchita chiyani tikazindikira zinthu zimene zingachititse kuti tiyesedwe mosavuta? Tizichita khama kuti tizipewa zinthu zimenezo. Mwachitsanzo, mizinda yakale yomwe inkakhala ndi mipanda inkatetezedwa kwambiri pageti chifukwa ndi pamene adani akanadzera mosavuta kuti aukire. Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kudziwa bwino zofooka zathu n’cholinga choti tizitha kupewa mayesero.—1 Akor. 9:27.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZIPEWA MAYESERO

8-9. Kodi wachinyamata wotchulidwa pa Miyambo chaputala 7 akanatani kuti apewe kuchita tchimo? (Miyambo 7:​8, 9, 13, 14, 21)

8 Kodi tingatani kuti tizipewa mayesero? Tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa wachinyamata wotchulidwa pa Miyambo chaputala 7. Iye anagona ndi mkazi wachiwerewere. Vesi 22 limatiuza kuti “mwadzidzidzi,” wachinyamatayo anayamba kulondola mkaziyo. Koma mavesi a m’mbuyo amasonyeza kuti iye anachitanso zinthu zina zomwe mwapang’onopang’ono zinamufikitsa poti achite tchimo.

9 Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinachititsa kuti achite tchimo? Choyamba, iye “ankadutsa mumsewu pafupi ndi mphambano” yolowera kunyumba ya mkazi wachiwerewereyo. Kenako anayamba kulowera kunyumba ya mkaziyo. (Werengani Miyambo 7:​8, 9.) Iye atamuona mayiyo sanatembenuke n’kubwerera. M’malomwake analola kuti mkaziyo amukise komanso anamumvetsera pomwe ankafotokoza kuti anakapereka nsembe zamgwirizano. Mwina ankamuuza zimenezi pofuna kumuchititsa mnyamatayo kuti azimuona kuti iye si munthu woipa. (Werengani Miyambo 7:​13, 14, 21.) Wachinyamatayo akanapewa zinthu zimenezi akanatetezeka ndipo sakanachita tchimo.

10. Kodi masiku ano munthu angachite bwanji zinthu ngati wachinyamata wotchulidwa m’buku la Miyambo?

10 Nkhani imene Solomo analembayi ikusonyeza zimene zingachitikire mtumiki wa Yehova aliyense. Iye angathe kuchita tchimo lalikulu n’kumaona kuti zachitika “mwadzidzidzi.” Kapenanso angathe kunena kuti “zangochitika.” Koma ataganizira bwinobwino zimene zinachitika, akhoza kupeza kuti pali zina zomwe anachita mosaganiza bwino zomwe zachititsa kuti achite tchimolo. Zinthu zimenezi zingaphatikizepo zosangalatsa zosayenera, kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa kapena kupezeka m’malo okayikitsa, kaya malo enieni kapena pa intaneti. N’kuthekanso kuti mwina anasiya kupemphera, kuwerenga Baibulo, kupezeka pamisonkhano kapenanso kugwira ntchito yolalikira. Choncho mofanana ndi wachinyamata wa m’buku la Miyambo, tchimo lake silingakhale kuti langochitika “mwadzidzidzi.”

11. Kodi tiyenera kupewa zinthu ziti kuti tisachite tchimo?

11 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Sitiyenera kungopewa tchimo, koma tiyeneranso kupewa zinthu zimene zingachititse kuti tichite tchimolo. Solomo anamveketsa bwino mfundo imeneyi pomwe anafotokoza nkhani ya wachinyamata ndi mkazi wachiwerewere. Pochenjeza za mkaziyo Solomo anati: “Musasochere nʼkuyamba kuyenda mʼnjira zake.” (Miy. 7:25) Ananenanso kuti: “Ukhale kutali kwambiri ndi iye. Usayandikire pakhomo la nyumba yake.” (Miy. 5:​3, 8) Choncho timapewa machimo poyesetsa kupewa zinthu zimene zingachititse kuti tichite machimowo. b Izi zikuphatikizapo kupewa zinthu zimene si zolakwika kwenikweni kwa Akhristu koma zikhoza kuchititsa kuti tiyesedwe.—Mat. 5:​29, 30.

12. Kodi Yobu anatsimikiza mtima kuchita chiyani, nanga zimenezi zinamuthandiza bwanji kuti asayesedwe? (Yobu 31:1)

12 Tiyenera kukhala otsimikiza mumtima mwathu kuti tipewe zinthu zomwe zingatichimwitse. Izi ndi zimene Yobu anachita. Iye ‘anachita pangano ndi maso ake’ kuti asayang’ane akazi ena mowasirira. (Werengani Yobu 31:1.) Kuchita zinthu mogwirizana ndi panganolo kunamuthandiza kuti asachite chigololo. Ifenso tiyenera kupewa chilichonse chomwe chingachititse kuti tiyesedwe.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kuteteza maganizo athu? (Onaninso zithunzi.)

13 Tiyeneranso kuteteza maganizo athu. (Eks. 20:17) Ena amaganiza kuti si kulakwa kuganizira zinthu zoipa bola ngati sakuchita zinthuzo. Koma maganizo amenewa ndi olakwika. Munthu amene amaganizira kwambiri zinthu zolakwika amayamba kuzilakalaka kwambiri. Akamachita zimenezi zimakhala zovuta kuti apewe mayesero. N’zoona kuti nthawi zina tikhoza kuyamba kuganizira zinthu zolakwika. Koma chofunika ndi kusiya kuganizira zimenezo n’kuyamba kuganizira zinthu zabwino. Tikatero maganizo oipawo sakula n’kufika pokhala chilakolako champhamvu chomwe chingachititse kuti tichite tchimo lalikulu.—Afil. 4:8; Akol. 3:2; Yak. 1:​13-15.

Tiyenera kupewa chilichonse chomwe chingachititse kuti tiyesedwe (Onani ndime 13)


14. Kodi n’chiyaninso chingatithandize kuti tipewe mayesero?

14 Kodi n’chiyaninso chingatithandize kuti tipewe mayesero? Tiyenera kutsimikizira kuti nthawi zonse kumvera malamulo a Yehova n’kothandiza. N’zoona kuti nthawi zina tikhoza kuvutika kuti maganizo athu komanso zimene timalakalaka zigwirizane ndi zomwe Yehova amafuna. Koma tikayesetsa kutero timakhala ndi mtendere mumtima.

15. Kodi kulakalaka zinthu zoyenera kungatithandize bwanji kupewa mayesero?

15 Tiyenera kuyesetsa kuti tizilakalaka zinthu zoyenera. Tikaphunzira ‘kudana ndi choipa n’kumakonda chabwino’ tidzatsimikiza mtima kuti tizichita zoyenera n’kumapewa zinthu zimene zingachititse kuti tichimwe. (Amosi 5:15) Kulakalaka zinthu zoyenera kudzatithandiza kuti tisatengeke tikakumana ndi mayesero amene sitimayembekezera kapenanso ovuta kuwapewa.

16. Kodi kutanganidwa ndi zinthu zokhudza kulambira kungatiteteze bwanji? (Onaninso zithunzi.)

16 Kodi tingatani kuti tizilakalaka zinthu zoyenera? Tiyenera kumatanganidwa ndi zinthu zokhudza kulambira. Tikakhala pamisonkhano kapena mu utumiki zimakhala zovuta kuti tiyesedwe. M’malomwake timalimbikitsidwa kukhala ndi mtima wofuna kusangalatsa Yehova. (Mat. 28:​19, 20; Aheb. 10:​24, 25) Tikamawerenga, kuphunzira komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu timayamba kukonda zabwino ndipo timadana ndi zoipa. (Yos. 1:8; Sal. 1:​2, 3; 119:​97, 101) Kumbukirani kuti Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mupitirize kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.” (Mat. 26:41) Tikamapemphera kwa Atate wathu wakumwamba, iye amatithandiza ndipo ifeyo timafunitsitsa kumusangalatsa.—Yak. 4:8.

Kuchita zinthu zimene zingatichititse kukhala pa ubwenzi ndi Yehova nthawi zonse kungatithandize kuti tipewe mayesero (Onani ndime 16) c


PITIRIZANI KUKHALA MASO

17. Kodi Petulo ankalimbana ndi vuto liti mobwerezabwereza?

17 Anthufe tikhoza kusiyiratu makhalidwe ena oipa. Koma tikhoza kumavutikabe ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtumwi Petulo. Chifukwa choopa anthu iye anakana Yesu katatu. (Mat. 26:​69-75) Koma pamene analankhula molimba mtima pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, zinkaoneka ngati anasiya kuchita mantha. (Mac. 5:​27-29) Koma pa nthawi ina patapita zaka zingapo, iye anasiya kudya ndi Akhristu a mitundu ina “chifukwa ankaopa anthu odulidwawo.” (Agal. 2:​11, 12) Apa tingati anayambiranso kuopa anthu. N’kutheka kuti vuto lake la manthali linali lisanatheretu.

18. Kodi n’chiyani chomwe chingachitike ndi makhalidwe ena oipa omwe tingakhale nawo?

18 Mofanana ndi Petulo, mwina ifenso tingamalimbane ndi vuto linalake mobwerezabwereza, lomwe tinkaganiza kuti tinathana nalo. Mwachitsanzo, m’bale wina ananena kuti: “Ndinasiya kuonera zolaula kwa zaka 10, ndipo ndinkaganiza kuti basi vutoli ndathana nalo. Koma vutoli linangobisala n’kumayembekezera nthawi yoti lionekerenso.” N’zosangalatsa kuti m’baleyu sanagonje. Iye anaona kuti anafunika kuchita khama tsiku lililonse kuti azilimbana ndi vutoli, mwinanso kwa moyo wake wonse m’dziko loipali. Mothandizidwa ndi mkazi wake komanso akulu, iye anachita zonse zomwe akanatha kuti azipewa kuonera zolaula.

19. Kodi tingatani ngati tili ndi vuto limene sitinaligonjetsebe?

19 Kodi tingatani kuti vuto lomwe sitinathane nalo lisatichimwitse? Chomwe chingatithandize ndi kutsatira malangizo a Yesu pa nkhani ya mayesero. Iye anati: “Khalani maso.” Ngakhale pa nthawi imene mukuona kuti ndinu olimba mwauzimu, muzipitiriza kupewa zinthu zimene zingachititse kuti mulowe m’mayesero. (1 Akor. 10:12) Muzipitiriza kuchita zinthu zimene zinakuthandizani kuti mugonjetse vutolo. Lemba la Miyambo 28:14 limati: “Wosangalala ndi munthu amene nthawi zonse amasamala zochita zake.”—2 Pet. 3:14.

MADALITSO AMENE TINGAPEZE CHIFUKWA CHOKHALABE MASO

20-21. (a) Kodi ndi madalitso ati omwe tingapeze tikamakhala maso kuti tipewe mayesero? (b) Ngati ife titachita mbali yathu, kodi Yehova adzatithandiza bwanji? (2 Akorinto 4:7)

20 Tisamakayikire kuti kukhalabe maso n’kothandiza nthawi zonse. Machimo amangochititsa kuti munthu ‘asangalale kwa nthawi yochepa’ koma kutsatira mfundo za Yehova kumachititsa kuti munthu akhale wosangalala kwambiri. (Aheb. 11:25; Sal. 19:8) Zili choncho chifukwa chakuti anthufe tinalengedwa m’njira yoti tizitsatira mfundo za Mulungu. (Gen. 1:27) Tikamachita zimenezi, timakhala ndi chikumbumtima choyera komanso timayembekezera moyo wosatha.—1 Tim. 6:12; 2 Tim. 1:3; Yuda 20, 21.

21 N’zoona kuti “thupi ndi lofooka.” Koma sizikutanthauza kuti tilibiretu mtengo wogwira. Yehova ndi wokonzeka kutipatsa mphamvu. (Werengani 2 Akorinto 4:7.) Onani kuti Mulungu amapereka mphamvu yoposa yachibadwa. Koma choyamba, tiyenera kugwiritsa ntchito mphamvu yathu yachibadwa polimbana ndi mayesero tsiku lililonse. Tikachita mbali yathu tisamakayikire kuti Yehova adzayankha mapemphero athu potipatsa mphamvu zowonjezereka zomwe tingafunikire. (1 Akor. 10:13) Choncho mothandizidwa ndi Yehova tikhoza kukhala maso n’kumapewa mayesero.

NYIMBO NA. 47 Muzipemphera kwa Yehova Tsiku Lililonse

a MATANTHAUZO A MAWU ENA: “Mzimu” wotchulidwa pa Mateyu 26:​41, ndi mphamvu yomwe imakhala mkati mwathu, imene imachititsa kuti tizimva kapena kuchita zinthu m’njira inayake. Mawu akuti “thupi” akutanthauza kuti si ife angwiro. Choncho tingakhale ndi zolinga zoyenera zoti tizichita zabwino, koma ngati sitingasamale tingathe kugonja tikayesedwa kuti tichite zimene Baibulo limanena kuti ndi zoipa.

b Munthu amene wachita tchimo lalikulu angapeze mfundo zothandiza m’buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, phunziro 57 mfundo 1-3 komanso mu nkhani yakuti “Maso Ako Aziyang’ana pa Zinthu Zakutsogolo” mu Nsanja ya Olonda ya November 2020, tsamba 27-29, ndime 12-17.

c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akuwerenga lemba la tsiku m’mawa, akuwerenga Baibulo pa nthawi yopuma masana, ndipo madzulo wapezeka pamisonkhano.