Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 30

NYIMBO NA. 36 Timateteza Mtima Wathu

Zimene Tikuphunzira kwa Mafumu a Chiisiraeli

Zimene Tikuphunzira kwa Mafumu a Chiisiraeli

“Mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sakumutumikira.”MAL. 3:18.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Kuona zomwe Yehova ankayang’ana mwa mafumu a Chiisiraeli kutithandiza kuona zimene iye amafuna kuti atumiki ake azichita masiku ano.

1-2. Kodi Baibulo limatiuza zinthu ziti zokhudza mafumu ena a Isiraeli?

 BAIBULO limatiuza za amuna 40 omwe anakhala mafumu a Isiraeli. a Limafotokoza mosapita m’mbali zimene ena mwa mafumuwa anachita. Mwachitsanzo ngakhale mafumu ena abwino anachitanso zinthu zina zoipa. Chitsanzo ndi Davide yemwe anali mfumu yabwino. Yehova ananena kuti: “Davide mtumiki wanga. . . anasunga malamulo anga, kunditsatira ndi mtima wake wonse ndiponso kuchita zinthu zoyenera zokhazokha pamaso panga.” (1 Maf. 14:8) Komatu munthu ameneyu anachita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake ndipo anakonza zoti mwamuna wa mkaziyo aphedwe kunkhondo.—2 Sam. 11:​4, 14, 15.

2 Baibulo limatiuzanso za mafumu ambiri osakhulupirika omwe anachitanso zinthu zina zabwino. Chitsanzo ndi Mfumu Rehobowamu. Kwa Yehova “iye anachita zoipa.” (2 Mbiri 12:14) Koma Rehobowamu anamvera lamulo la Mulungu loti alole kuti ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli ukhale woima paokha. Anachitanso zinthu zothandiza mtundu wake pomanga mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.—1 Maf. 12:​21-24; 2 Mbiri 11:​5-12.

3. Kodi ndi funso lofunika liti lomwe tiyenera kuliganizira, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Funso lofunika kwambiri ndi lakuti: Ngati mafumu a Chiisiraeli ankachita zabwino ndi zoipa, n’chiyani chinkachititsa Yehova kuona mafumu ena kukhala okhulupirika? Yankho la funso limeneli litithandiza kudziwa zimene Yehova amafuna kuti ifeyo tizichita. Tikambirana zinthu zitatu zimene iye ankayang’ana mwa mafumu a Chiisiraeli. Iye ankayang’ana mtima wawo, kulapa kwawo komanso zimene ankachita popitirizabe kumulambira m’njira yolondola.

ANKATUMIKIRA YEHOVA NDI MTIMA WONSE

4. Kodi panali kusiyana kotani pakati pa mafumu okhulupirika ndi mafumu osakhulupirika?

4 Mafumu omwe Yehova anasangalala nawo ankamutumikira ndi mtima wonse. b Mwachitsanzo, Yehosafati yemwe anali mfumu yabwino, “anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.” (2 Mbiri 22:9) Pofotokoza za Yosiya, Baibulo limati: “Iye asanakhale mfumu, panalibe mfumu ina imene inabwerera kwa Yehova ndi mtima wake wonse.” (2 Maf. 23:25) Nanga bwanji za Solomo yemwe pamapeto pake anachita zoipa? Baibulo limati: “Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu.” (1 Maf. 11:4) Ndipo ponena za Abiyamu, yemwenso anali mfumu yosakhulupirika, Baibulo limati: “Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wonse.”—1 Maf. 15:3.

5. Fotokozani zimene kutumikira Yehova ndi mtima wonse kumatanthauza.

5 Ndiye kodi kutumikira Yehova ndi mtima wonse kumatanthauza chiyani? Munthu amene amatumikira Mulungu ndi mtima wake wonse samangomulambira chifukwa chakuti ndi zimene akuyenera kuchita. M’malomwake, amamutumikira chifukwa cha chikondi komanso mtima wodzipereka. Kuwonjezera pamenepo, amapitiriza kumukonda komanso kudzipereka kwa iye kwa moyo wake wonse.

6. Kodi tingatani kuti tipitirize kutumikira Mulungu ndi mtima wonse? (Miyambo 4:23; Mateyu 5:​29, 30)

6 Kodi tingatsanzire bwanji mafumu okhulupirika n’kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse? Tingachite zimenezi popewa zinthu zimene zingachititse kuti tikhale osakhulupirika. Mwachitsanzo, zosangalatsa zosayenera, kugwirizana ndi anthu oipa komanso kukonda chuma zingachititse kuti tisamatumikire Mulungu ndi mtima wonse. Tikazindikira kuti pali zinazake zomwe zikuchititsa kuti chikondi chathu kwa Yehova chiyambe kuchepa, tizichitapo kanthu mwamsanga.—Werengani Miyambo 4:23; Mateyu 5:​29, 30.

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa zinthu zimene zingachititse kuti tisiye kukonda Mulungu?

7 Tisamalole kuti mtima wathu ukhale wogawanika. Ngati sitingasamale tikhoza kumadzinamiza n’kumaona kuti ngati tikuchita zambiri potumikira Yehova, palibe chimene chingachititse kuti tichite zoipa. Tiyerekeze kuti kunja kuli chimphepo komanso fumbi. Ndiye inu mwakonza bwinobwino m’nyumba mwanu. Kodi mungasiye mawindo ndi zitseko zili zotsegula kuti fumbi lizilowa m’nyumbamo? Ayi. Mfundo yake ndi yakuti timafunika kuchita zambiri osati kungodya chakudya chauzimu chomwe chimatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Tiyeneranso kutseka chitseko, kunena kwake titero, kuti fumbi la m’dzikoli kapena zinthu zimene Mulungu amadana nazo zisalowe mumtima mwathu n’kuugawanitsa.—Aef. 2:2.

ANALAPA MACHIMO AWO

8-9. Kodi Mfumu Davide ndi Mfumu Hezekiya anachita bwanji atadzudzulidwa? (Onaninso chithunzi chapachikuto.)

8 Monga taonera kale, Mfumu Davide inachita tchimo lalikulu. Koma mneneri Natani atamudzudzula chifukwa cha tchimo lakelo, Davide anadzichepetsa n’kulapa. (2 Sam. 12:13) Mawu ake opezeka mu Salimo 51 akusonyeza kuti iye analapadi mochokera pansi pa mtima. Sikuti Davide anangoyerekezera kudzimvera chisoni pofuna kupusitsa Natani kapena kuzemba kulandira chilango.—Sal. 51:​3, 4, 17, timawu tapamwamba.

9 Mfumu Hezekiya nayonso inachimwira Yehova. Baibulo limati: “Mtima wake unayamba kudzikuza ndipo zimenezi zinachititsa kuti Mulungu amukwiyire iyeyo, Yuda ndiponso Yerusalemu.” (2 Mbiri 32:25) N’chifukwa chiyani Hezekiya anayamba kunyada? N’kutheka kuti iye ankadziona kuti ndi wapamwamba chifukwa cha chuma chake, kupambana kwake pankhondo yolimbana ndi Asuri, kapenanso kuchiritsidwa kwake modabwitsa. N’kutheka kuti kunali kunyada komwe kunamuchititsa kuti aonetse Ababulo chuma chake ndipo mneneri Yesaya anamudzudzula. (2 Maf. 20:​12-18) Koma mofanana ndi Davide, Hezekiya anadzichepetsa n’kulapa. (2 Mbiri 32:26) Zotsatira zake n’zakuti Yehova ankamuona monga mfumu yokhulupirika yomwe ‘inkachita zoyenera.’—2 Maf. 18:3.

Mfumu Davide komanso Mfumu Hezekiya anadzichepetsa n’kulapa atadzudzulidwa chifukwa cha machimo awo (Onani ndime 8-9)


10. Kodi Mfumu Amaziya anatani atadzudzulidwa?

10 Mosiyana ndi Davide ndi Hezekiya, Mfumu Amaziya ya ku Yuda anachita zoyenera “koma osati ndi mtima wonse.” (2 Mbiri 25:2) Kodi analakwitsa pati? Yehova atamuthandiza kugonjetsa Aedomu, Amaziya anayamba kulambira Milungu yawo. c Ndiye mneneri wa Yehova atabwera kudzamudzudzula, Amaziya anachita makani n’kumuthamangitsa.—2 Mbiri 25:​14-16.

11. Mogwirizana ndi 2 Akorinto 7:​9, 11, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atikhululukire? (Onaninso zithunzi.)

11 Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzozi? Tiyenera kulapa machimo athu n’kuyesetsa kuti tisawabwerezenso. Nanga kodi tizitani akulu akatipatsa malangizo pa zinthu zooneka ngati zazing’ono? Tisamaone ngati akuluwo komanso Yehova satikonda. Ngakhale mafumu abwino a ku Isiraeli ankafunikanso kupatsidwa malangizo komanso kudzudzulidwa. (Aheb. 12:6) Choncho tikamapatsidwa malangizo, tiyenera (1) kuwalandira modzichepetsa, (2) kusintha pamene pakufunika kutero, komanso (3) kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Tikalapa machimo athu Yehova adzatikhululukira.—Werengani 2 Akorinto 7:​9, 11.

Tikapatsidwa malangizo, tiyenera (1) kuwalandira modzichepetsa, (2) kusintha, komanso (3) kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse (Onani ndime 11) f


ANKALAMBIRA YEHOVA M’NJIRA YOYENERA

12. Kodi mafumu okhulupirika ankasiyana bwanji ndi mafumu osakhulupirika?

12 Yehova ankaona kuti mafumu omwe ankamulambira m’njira yoyenera ndi okhulupirika. Mafumuwo ankalimbikitsanso anthu awo kuti azichita zomwezo. Monga taonera, n’zoona kuti iwo ankalakwitsa zinthu zina. Koma iwo ankalambira Yehova yekha ndipo ankayesetsa kuwononga mafano m’dzikolo. d

13. N’chifukwa chiyani Yehova anaweruza kuti Ahabu anali wosakhulupirika?

13 N’chifukwa chiyani Yehova anaweruza mafumu ena kuti anali osakhulupirika? Sikuti zonse zimene mafumuwa ankachita zinali zoipa. Ngakhale Ahabu yemwe anali mfumu yoipa anadzichepetsa komanso kukhudzidwa chifukwa chochititsa kuti Naboti aphedwe. (1 Maf. 21:​27-29) Iye anamanganso mizinda ndipo anapambana nkhondo zambiri ku Isiraeli. (1 Maf. 20:​21, 29; 22:39) Koma Ahabu anachita zoipa kwambiri pomwe anamvera mkazi wake n’kumalimbikitsa Aisiraeli kuti azilambira mafano. Atachita zimenezi iye sanalape.—1 Maf. 21:​25, 26.

14. (a) N’chifukwa chiyani Yehova ankaona kuti Rehobowamu anali mfumu yosakhulupirika? (b) Kodi n’chiyani chomwe chinkachitika mu ulamuliro wa mafumu oipa?

14 Chitsanzo chinanso cha mfumu yosakhulupirika ndi Rehobowamu. Monga taonera kale, mu ulamuliro wake iye anachita zinthu zina zabwino. Koma ufumu wake utakhala wamphamvu iye anasiya kutsatira Chilamulo cha Yehova n’kuyamba kulambira mafano. (2 Mbiri 12:1) Choncho ankalambira Yehova kwinaku n’kumalambira milungu yabodza. (1 Maf. 14:​21-24) Rehobowamu ndi Ahabu si mafumu okhawo amene anasiya kulambira Yehova m’njira yoyenera. Ndipotu mafumu ambiri osakhulupirika ankalambira mafano komanso kulimbikitsa ena kuti azichita zomwezo. Choncho n’zoonekeratu kuti kulambira Yehova m’njira yoyenera ndi chifukwa chachikulu chomwe chinkachititsa Yehova kuti aziona mfumu kukhala yabwino kapena yoipa.

15. N’chifukwa chiyani kulambira m’njira yoyenera kuli kofunika kwa Yehova?

15 N’chifukwa chiyani Yehova ankaona kuti nkhani yokhudza kulambira ndi yofunika kwambiri? Chifukwa chimodzi n’chakuti mafumuwa anali ndi udindo waukulu wotsogolera anthu a Mulungu kuti azimulambira m’njira yoyenera. Komanso kulambira mafano kumachititsa kuti ena azichita machimo akuluakulu komanso zopanda chilungamo. (Hos. 4:​1, 2) Kuwonjezera pamenepo, mafumuwo komanso anthuwo anali mtundu wodzipereka kwa Yehova. N’chifukwa chake Baibulo limayerekezera kulambira kwawo mafano ndi chigololo. (Yer. 3:​8, 9) Munthu amene wachita chigololo amakhala kuti walakwira kwambiri mwamuna kapena mkazi wake. Mofanana ndi zimenezi mtumiki wodzipereka wa Yehova yemwe amalambira mafano amakhala kuti wamulakwira kwambiri Yehova. eDeut. 4:​23, 24.

16. Kodi n’chiyani chimachititsa Yehova kuona kuti munthu ndi wolungama kapena woipa?

16 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiyenera kuyesetsa kuti tizipewa kulambira milungu yabodza. Koma tiyeneranso kupitiriza kulambira Yehova m’njira yoyenera n’kumachita zambiri pomutumikira. Mneneri Malaki anafotokoza momveka bwino zimene zimachititsa Yehova kuona kuti munthu ndi wabwino kapena woipa. Iye analemba kuti: “Mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sakumutumikira.” (Mal. 3:18) Choncho sitiyenera kulola chilichonse, kaya zofooka zathu kapena zimene timalakwitsa, kuti zitikhumudwitse mpaka kufika posiya kutumikira Mulungu. Kusiya kutumikira Yehova pakokha ndi tchimo lalikulu.

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala posankha wokwatirana naye?

17 Ngati mukuganizira zolowa m’banja, mawu omwe Malaki ananena okhudza kutumikira Mulungu angakuthandizeni kusankha bwino wokwatirana naye. Munthu akhoza kukhala ndi makhalidwe ena abwino. Koma ngati sakutumikira Mulungu woona, kodi Yehova akhoza kumuona ngati munthu wolungama? (2 Akor. 6:14) Ngati mutakhala naye m’banja, kodi angakulimbikitseni pa nkhani yotumikira Mulungu? Taganizirani izi: N’kutheka kuti akazi achikunja a Solomo anali ndi makhalidwe ena abwino. Koma popeza kuti sankatumikira Yehova, pang’ono ndi pang’ono anapatutsa mtima wake moti anayamba kulambira milungu yabodza.—1 Maf. 11:​1, 4.

18. Kodi makolo ayenera kuphunzitsa chiyani ana awo?

18 Makolo, mungathe kugwiritsa ntchito nkhani zokhudza mafumu otchulidwa m’Baibulo pothandiza ana anu kuti azitumikira Yehova ndi mtima wawo wonse. Muziwathandiza kudziwa kuti Yehova ankaona mfumu kukhala yabwino kapena yoipa malinga ndi zimene inkachita polimbikitsa kulambira koona. Zolankhula komanso zochita zanu zizisonyeza kuti zinthu zokhudza kulambira monga kuphunzira Baibulo, kupezeka pamisonkhano komanso kugwira ntchito yolalikira ndi zofunika kwambiri kuposa chilichonse. (Mat. 6:33) Kupanda kutero, anawo akhoza kumangoona ngati ndi a Mboni za Yehova chifukwa chakuti akungotsatira makolo awo. Zotsatira zake n’zakuti sangamaike pamalo oyamba kulambira koona mwinanso kungosiyiratu kulambira Yehova.

19. Kodi pali mwayi wotani kwa amene anasiya kutumikira Yehova? (Onaninso bokosi lakuti “ Mukhoza Kubwerera kwa Yehova.”)

19 Kodi munthu amene wasiya kutumikira Yehova sangadzakhalenso naye pa ubwenzi? Ayi, chifukwa akhoza kulapa n’kuyambiranso kumulambira m’njira yoyenera. Kuti zimenezi zitheke, ayenera kudzichepetsa n’kulola kuti athandizidwe ndi akulu. (Yak. 5:14) N’zoona kuti angafunike kuchita khama, koma khamalo limapindula chifukwa amayambiranso kukhala pa ubwenzi ndi Yehova.

20. Kodi Yehova adzationa bwanji tikamatsanzira mafumu okhulupirika?

20 Ndiye kodi taphunzira chiyani kuchokera kwa mafumu a Chiisiraeli? Tikhoza kukhala ngati mafumu okhulupirika ngati titapitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Tiziphunzira pa zimene talakwitsa, kulapa komanso kusintha. Tizikumbukiranso kufunika kolambira Mulungu woona yekha. Mukapitiriza kukhala okhulupirika kwa Yehova iye adzakuonani inuyo monga munthu amene amachita zoyenera.

NYIMBO NA. 45 Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga

a Munkhaniyi, mawu akuti “mafumu a Isiraeli” akunena za mafumu onse omwe analamulira anthu a Yehova, kaya mu ufumu wa Yuda wa mafuko awiri kapena wa Isiraeli wa mafuko 10, kapenanso omwe analamulira mafuko onse 12.

b TANTHAUZO LA MAWU ENA: Nthawi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “mtima” pofotokoza mmene munthu alili, zomwe zikuphatikizapo zimene amalakalaka, zimene amaganiza, khalidwe lake, luso, komanso zolinga zake.

c Zikuoneka kuti nthawi zambiri, mafumu achikunja ankalambira milungu ya mitundu imene aigonjetsa.

d Mfumu Asa anachita machimo aakulu. (2 Mbiri 16:​7, 10) Koma Baibulo limasonyeza kuti Yehova ankamuona kuti anachita zabwino. Ngakhale kuti poyamba anakana atadzudzulidwa, n’kutheka kuti pambuyo pake analapa. Koma zabwino zimene anachita ndi zambiri tikayerekezera ndi zimene analakwitsa. Chofunika kwambiri ndi chakuti Asa ankalambira Yehova yekha ndipo anayesetsa kuchotsa mafano mu ufumu wake.—1 Maf. 15:​11-13; 2 Mbiri 14:​2-5.

e Tikudziwa kuti nkhani ya kulambira ndi yofunika kwambiri kwa Yehova chifukwa chakuti malamulo awiri oyamba mu Chilamulo cha Mose ankaletsa kulambira munthu kapena chinthu chilichonse koma Yehova yekha.—Eks. 20:​1-6.

f MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mkulu wachinyamata akupereka malangizo kwa m’bale wina pa nkhani yokhudza mowa. M’baleyo wavomera malangizowo modzichepetsa, wasintha ndipo akupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika.