Kodi Mumalola Kuti Yehova Azikuumbani?
“Taonani! Mofanana ndi dongo limene lili m’manja mwa woumba mbiya, ndi mmene inunso mulili kwa ine.”—YER. 18:6.
NYIMBO: 60, 22
1, 2. N’chifukwa chiyani Mulungu ankaona kuti Danieli anali “munthu wokondedwa kwambiri,” nanga kodi ifeyo tingatani kuti tikhale omvera ngati iyeyo?
AYUDA atatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo, anapeza kuti anthu amumzindawo ankakonda kulambira mafano komanso ankachita zamizimu. Komabe Ayuda okhulupirika, monga Danieli ndi anzake atatu sanalole kuumbidwa ndi anthu a ku Babulo. (Dan. 1:6, 8, 12; 3:16-18) Danieli ndi anzakewo ankafunitsitsa kuti aziumbidwa ndi Yehova yekha basi. Zimenezi zinathekadi chifukwa ngakhale kuti Danieli anakhala ku Babulo pafupifupi kwa moyo wake wonse, mngelo wa Mulungu ananena kuti iye anali “munthu wokondedwa kwambiri.”—Dan. 10:11, 19.
2 Kale, woumba ankatenga dongo n’kulikanikiza pachinthu chinachake kuti aumbe chimene akufuna. Masiku ano atumiki a Yehova amadziwa kuti Yehova ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse ndipo ali ndi mphamvu zoti angaumbe mitundu ya anthu. (Werengani Yeremiya 18:6.) Mulungu akhozanso kuumba munthu aliyense payekha. Komabe iye amalemekeza ufulu wosankha zochita umene anthufe tili nawo ndipo amafuna kuti tizimumvera mwakufuna kwathu. Tiyeni tione zimene tingachite kuti Yehova azitiumba ndipo tikambirana mbali zitatu izi: (1) Kodi tingapewe bwanji makhalidwe amene angatilepheretse kutsatira malangizo a Yehova? (2) Kodi tingatani kuti tipitirize kukhala ndi makhalidwe amene angathandize kuti Yehova azitiumba? (3) Kodi makolo angatsatire bwanji malangizo a Mulungu poumba ana awo?
MUZIPEWA MAKHALIDWE AMENE ANGAUMITSE MTIMA WANU
3. Kodi ndi makhalidwe ati amene angawononge mtima wathu? Perekani chitsanzo.
3 Lemba la Miyambo 4:23 limati: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.” Ndiyeno kodi ndi makhalidwe ati amene angawononge mtima wathu? Pali makhalidwe monga kunyada, chizolowezi chochita machimo ndiponso kusowa chikhulupiriro. Makhalidwe amenewa angachititse kuti tikhale ndi mtima woipa komanso wosamvera. (Dan. 5:1, 20; Aheb. 3:13, 18, 19) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mfumu ya Ayuda dzina lake Uziya. (Werengani 2 Mbiri 26:3-5, 16-21.) Poyamba, Uziya ankachita “zoyenera pamaso pa Yehova” ndipo “anali kufunafuna Mulungu.” Koma “atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza” n’kuiwala kuti Mulungu ndi amene anamupatsa mphamvuzo. Iye anafika popereka nsembe ngakhale kuti umenewu unali udindo wa ansembe a m’banja la Aroni. Ndiyeno ansembewo atamudzudzula, anakwiya koopsa. Zotsatira zake zinali zakuti Yehova anachititsa kuti akhale wakhate mpaka imfa yake.—Miy. 16:18.
4, 5. Kodi chingachitike n’chiyani tikalekerera mtima wonyada? Perekani chitsanzo
4 Mtima wonyada ukhozanso kutichititsa kuti ‘tizidziganizira kuposa mmene tiyenera kudziganizira,’ mwina mpaka kufika pokana malangizo ochokera m’Malemba. (Aroma 12:3; Miy. 29:1) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mbale wina dzina lake Jim. M’baleyu anali mkulu ndipo anasiyana maganizo ndi akulu anzake pa nkhani inayake. A Jim anati: “Ndinawauza abalewo kuti alibe chikondi ndipo ndinachoka pa zokambiranazo.” Patatha miyezi 6, anasamukira mumpingo wina wapafupi koma sanaloledwe kukhala mkulu kumeneko. A Jim anati: “Zinandiwawa koopsa. Mtima wodziona kuti ndine wolungama kwambiri unachititsa kuti ndisiye choonadi.” Iwo anasiya gulu la Yehova kwa zaka 10 ndipo anati: “Mtima wanga wonyada unafika poipa kwambiri ndipo ndinayamba kuimba mlandu Yehova. Abale ankabwera kuti andithandize koma ndinkachita makani.”
5 Nkhaniyi ikusonyeza kuti mtima wonyada ungachititse kuti tizidziona kuti ndife olungama n’kukhala ngati dongo louma gwa. (Yer. 17:9) A Jim anati: “Ndinkangoona kuti abale enawo ndi amene ali ndi vuto.” Kodi inunso munakhumudwapo chifukwa cha zochita za Mkhristu wina kapena chifukwa choti mwasiyitsidwa udindo winawake? Ngati ndi choncho kodi munatani? Kodi kamtima kodzikuza kanayamba kuonekera? Kapena munkafunitsitsa kukhalanso pa mtendere ndi anzanuwo komanso kukhala okhulupirika kwa Yehova?—Werengani Salimo 119:165; Akolose 3:13.
6. Kodi chingachitike n’chiyani tikakhala ndi chizolowezi chochita machimo?
6 Chizolowezi chochita machimo mwamtseri, chingachititse kuti tizilephera kutsatira malangizo a Mulungu. Kenako tingamaone kuti palibe vuto lililonse tikachita tchimo. M’bale wina ananena kuti pa nthawi ina anazolowera kuchita zinthu zolakwika moti chikumbumtima chake sichinkamuvutanso. (Mlal. 8:11) M’bale winanso amene anali ndi chizolowezi choonera zolaula anati: “Ndinayamba mtima wotsutsa zimene akulu ankachita.” Chizolowezi chakechi chinkawononga kwambiri mtima wake. Kenako zinadziwika kuti ankaonera zolaula ndipo anathandizidwa. N’zoona kuti tonsefe si angwiro. Koma tikakhala ndi chizolowezi chomangotsutsa ena kapena chodzikhululukira tikachita tchimo, mtima wathu ukhoza kuipa kwambiri.
7, 8. (a) Kodi Aisiraeli anakumana ndi mavuto otani chifukwa chosowa chikhulupiriro? (b) Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani?
7 Kusowa chikhulupiriro kukhozanso kuwononga mtima wathu. Izi n’zimene zinachitikira Aisiraeli amene Yehova anawapulumutsa ku Iguputo. Iwo anaona Yehova akuchita zinthu zamphamvu pofuna kuwapulumutsa. Koma atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, chikhulupiriro chawo chinachepa. M’malo mokhulupirira Yehova anayamba kuchita mantha n’kuyamba kung’ung’udza motsutsana ndi Mose. Iwo anafika poganiza zobwerera ku ukapolo ku Iguputo. Nkhani imeneyi inamupweteka kwambiri Yehova ndipo anati: “Kodi anthu awa apitiriza kundinyoza kufikira liti?” (Num. 14:1-4, 11; Sal. 78:40, 41) Aisiraeli amene mitima yawo inali youma chifukwa chosowa chikhulupiriro, anathera m’chipululu.
8 Ifenso tangotsala pang’ono kulowa m’dziko latsopano ndipo chikhulupiriro chathu chikuyesedwa kwambiri. Choncho ndi bwino kudzifufuza ngati tidakali ndi chikhulupiriro cholimba. Mwachitsanzo tingadzifunse kuti, ‘Kodi timakhulupirira mawu a Yesu a pa Mateyu 6:33? Kodi zimene ndimasankha pa moyo wanga zimasonyeza kuti ndimakhulupiriradi mawuwa? Kodi ndimasankha kujomba kumisonkhano kapena mu utumiki n’cholinga choti ndikokere? Kodi ndingatani ngati mavuto azachuma atawonjezeka? Kodi ndidzalola kuti dzikoli lindikanikizire m’chikombole chake n’kusiya gulu la Yehova?’
9. N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kupitiriza kudziyesa’ ngati tili ndi chikhulupiriro, ndipo tingachite bwanji zimenezi?
9 Taganiziraninso chitsanzo china. Pali abale ndi alongo ena amene zimawavuta kutsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhani zokhudza ochotsedwa, zosangalatsa kapena anthu ocheza nawo. Mungadzifunse kuti: ‘Kodi ine ndimachita bwanji pa nkhani zimenezi?’ Ngati taona kuti tili ndi vuto, tiyenera kuyesetsa kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu. Paja Baibulo limati: “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.” (2 Akor. 13:5) Nthawi zonse tiyenera kumadzifufuza pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu.
PITIRIZANI KULOLA KUTI MULUNGU AZIKUUMBANI
10. N’chiyani chingatithandize kuti tikhale ngati dongo losavuta kuumbidwa?
10 Mulungu watipatsa zinthu monga Mawu ake, mpingo komanso ntchito yolalikira kuti zitithandize kukhala ngati dongo losavuta kuumbidwa. Madzi amathandiza kuti dongo lifewe bwino. Nafenso tikamawerenga Baibulo tsiku lililonse komanso kuganizira kwambiri zimene tawerengazo, zimakhala zosavuta kuti Yehova atiumbe. Yehova anauza mafumu achiisiraeli kuti azikopera Chilamulo n’kumachiwerenga tsiku lililonse. (Deut. 17:18, 19) Nawonso atumwi ankadziwa kuti kuwerenga Malemba komanso kusinkhasinkha kunali kofunika kwambiri. Polemba Baibulo anagwira mawu Malemba Achiheberi kambirimbiri ndipo akamalalikira ankalimbikitsanso anthu kuchita chimodzimodzi. (Mac. 17:11) Nafenso timadziwa kuti kuwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse komanso kuganizira zimene tawerengazo n’kofunika kwambiri. (1 Tim. 4:15) Kuchita zimenezi kumatithandiza kuti tikhalebe odzichepetsa kuti Yehova apitirize kutiumba.
11, 12. Kodi Yehova angagwiritse ntchito bwanji mpingo kuti atiumbe? Perekani chitsanzo.
11 Yehova amagwiritsanso ntchito mpingo kuti atiumbe mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu. M’bale Jim, amene tamutchula poyamba uja anasintha mkulu wina Yehova Sayenera Kuimbidwa Mlandu’ ndi yakuti, ‘Tumikirani Yehova Mokhulupirika’ mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1992.”
atamusonyeza chikondi komanso kumuganizira. Iye anati: “Mkuluyu sankandinyoza kapena kundiimba mlandu. M’malomwake ankalankhula zolimbikitsa komanso ankaoneka kuti akufunadi kundithandiza.” Patatha miyezi itatu mkuluyo anaitanira a Jim kumisonkhano. A Jim anati: “Anthu kumpingo anandilandira ndi manja awiri ndipo anandisonyeza chikondi. Izi zinapangitsa kuti ndiganize zobwerera. Ndinaona kuti si bwino kumangoganizira za ineyo. Abale komanso mkazi wanga, yemwe anakhalabe wokhulupirika, anandithandiza kwambiri moti patapita nthawi ndinabwerera. Ndinalimbikitsidwanso kwambiri nditawerenga nkhani yakuti, ‘12 Patapita nthawi a Jim anayambanso kutumikira monga mkulu ndipo akhala akuthandiza abale ena kuti ayambirenso kutumikira Yehova. M’bale Jim anati: “Poyamba ndinkaganiza kuti ndili ndi chikhulupiriro cholimba, koma sizinali choncho. Panopa ndimanong’oneza bondo kuti ndinalola kunyada kundilepheretsa kuzindikira zinthu zofunika kwambiri komanso ndinkangoganizira zolakwa za abale.”—1 Akor. 10:12.
13. Kodi ntchito yolalikira ingatithandize kukhala ndi makhalidwe ati, ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?
13 Kodi ntchito yolalikira imatithandiza bwanji kuti tiumbidwe n’kukhala anthu abwino? Kugwira nawo ntchitoyi kungapangitse kuti tikhale odzichepetsa komanso kuti tikhale ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Kodi inuyo ntchito yolalikira yakuthandizani kukhala ndi makhalidwe ati? Chofunikanso n’chakuti tikakhala ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa, anthu amakopeka ndi uthenga wathu. Chitsanzo ndi zimene zinachitika ku Australia. Pamene a Mboni awiri ankalalikira, anakumana ndi mayi wina amene anawalankhula mwachipongwe. Koma a Mboniwo anamvetsera mwaulemu zonse zimene mayiyo ananena. Patapita nthawi mayiyo anazindikira kuti sanachite bwino, ndipo analemba kalata yopepesa ku ofesi ya nthambi. M’kalatayo anati: “Mundipepesere kwa anthuwa chifukwa ngakhale kuti ndinalankhula zachipongwe, iwo anali oleza mtima komanso odzichepetsa. Ndikuona kuti ndinachita zopusa ponyoza anthu amene ankalalikira Mawu a Mulungu.” Kodi mayiyu akanalemba zimenezi zikanakhala kuti a Mboniwo anapsa mtima n’kumubwezera chipongwe? Izitu zikusonyeza kuti ntchito yolalikira imathandiza ifeyo komanso anthu amene timawalalikira.
MUZITSATIRA MALANGIZO A MULUNGU POUMBA ANA ANU
14. Kodi makolo angatani ngati akufuna kuumba bwino ana awo?
14 Ana ambiri amakhala odzichepetsa ndipo amafuna kuphunzira zinthu. (Mat. 18:1-4) Choncho makolo anzeru amayesetsa kuphunzitsa ana awo kuti adziwe Mulungu komanso kuti azimukonda. (2 Tim. 3:14, 15) Koma kuti zimenezi zitheke, ayenera kuyamba iwowo kuphunzira Mawu Mulungu, kuwasunga mumtima mwawo ndiponso kuwatsatira pa moyo wawo. Paja ana amaphunzira mosavuta akamaona zimene makolo awo amachita. Komanso anawo amaona kuti makolo awo akamawalangiza ndi umboni woti iwowo ndiponso Yehova amawakonda.
15, 16. Kodi makolo angasonyeze bwanji kuti amakhulupirira Yehova, mwana wawo akachotsedwa?
15 Komabe ana ena, ngakhale amene anaphunzitsidwa bwino, akakula amasiya kutumikira Yehova ndipo amachotsedwa. Izi zimakhumudwitsa kwambiri makolo komanso achibale. Mlongo wina wa ku South Africa anati: “Mchimwene wanga atachotsedwa, zinatikhumudwitsa kwambiri moti tinkangomva ngati wamwalira.” Komabe mlongoyu ndi makolo ake anatsatira malangizo a Mulungu okhudza ochotsedwa. (Werengani 1 Akorinto 5:11, 13.) Makolowo anati: “Tinayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo podziwa kuti kuchita zimenezi n’kothandiza. Tinkaona kuti kuchotsedwako ndi chilango chochokera kwa Yehova. Tinkadziwanso kuti Yehova amapereka chilango choyenera ndipo amachita zimenezi chifukwa cha chikondi. Choncho tinkapewa kulankhula naye, pokhapokha ngati zili nkhani zapachibale zofunika kwambiri.”
16 Kodi mnyamatayo ankamva bwanji? Iye anati: “Ndinkadziwa kuti abale anga sakudana nane koma akungomvera Yehova ndi gulu lake. Popeza sindinkatha kulankhula ndi anthu a mumpingo komanso abale anga, ndinazindikira kuti Yehova yekha ndi amene angandithandize. Choncho ndinamupempha kuti andikhululukire komanso kuti andithandize kuti ndibwerere.” Taganizirani mmene banja lonse linasangalalira mnyamatayu atabwezeretsedwa. Izi zikusonyeza kuti tikamalemekeza Mulungu m’njira zathu zonse, zotsatira zake zimakhala zabwino kwambiri.—Miy. 3:5, 6; 28:26.
17. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera Yehova nthawi zonse, nanga tidzapeza madalitso otani tikamachita zimenezi?
17 Mneneri Yesaya analemba zimene Ayuda olapa ananena atatsala pang’ono kuchoka ku ukapolo. Iye analemba kuti: “Inu Yehova, inu ndinu Atate wathu. Ife ndife dongo ndipo inu ndinu Wotiumba. Tonsefe ndife ntchito ya manja anu.” Ndipo anachonderera Yehova kuti: “Musakumbukire zolakwa zathu kwamuyaya. Chonde, kumbukirani kuti tonsefe ndife anthu anu.” (Yes. 64:8, 9) Ifenso tiyenera kumvera Yehova modzichepetsa. Tikatero iye azitiona kuti ndife okondedwa kwambiri ngati mmene ankaonera Danieli. Komanso adzapitiriza kutiumba pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake komanso gulu lake. Ndipo m’dziko latsopano tidzakhala “ana” ake angwiro.—Aroma 8:21.