Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiziyamikira Kuti Yehova Amatiumba

Tiziyamikira Kuti Yehova Amatiumba

“Yehova, . . . inu ndinu Wotiumba. Tonsefe ndife ntchito ya manja anu.”—YES. 64:8.

NYIMBO: 89, 26

1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti pa nkhani youmba, palibe amene angafanane ndi Yehova?

MU NOVEMBER 2010, mphika wa maluwa wakalekale womwe unaumbidwa ku China ankautsatsa pa mtengo wa madola 70 miliyoni ku London. Izi zikusonyeza kuti oumba mbiya akhoza kupanga chinthu chodula kwambiri pogwiritsa ntchito zinthu wamba monga dongo. Koma pa nkhani youmbayi, palibe amene angafanane ndi Yehova. Pa tsiku la 6 lolenga zinthu, Mulungu “anaumba munthu kuchokera kufumbi [dongo] lapansi.” (Gen. 2:7) Adamu anali wangwiro ndipo ankatha kusonyeza makhalidwe a Mulungu. Mpake kuti munthuyu anali “mwana wa Mulungu.”—Luka 3:38.

2, 3. Kodi tingatsanzire bwanji Aisiraeli a nthawi ya Yesaya, omwe analapa?

2 Koma Adamu anachimwa ndipo mwayi wokhala mwana wa Mulungu unathera pomwepo. Komabe ana ena a Adamu akhala akumvera ulamuliro wa Mulungu ndipo ali ngati “mtambo wa mboni waukulu.” (Aheb. 12:1) Anthu amenewa asonyeza kuti amafuna kuti Yehova akhale Atate awo komanso kuti aziwaumba. Iwo akana kuumbidwa ndi Satana komanso kukhala ana ake. (Yoh. 8:44) Zimenezi zikutikumbutsa mawu amene Yesaya ananena okhudza Aisiraeli omwe analapa. Iye analemba kuti: “Inu Yehova, inu ndinu Atate wathu. Ife ndife dongo ndipo inu ndinu Wotiumba. Tonsefe ndife ntchito ya manja anu.”—Yes. 64:8.

3 Masiku anonso, anthu amene amalambira Yehova motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi amayesetsa kukhala ndi maganizo amenewa. Amaona kuti ndi mwayi waukulu kuumbidwa ndi Yehova komanso kukhala ana ake. Kodi inuyo muli ngati dongo lofewa lokonzeka kuumbidwa n’kukhala chinthu chamtengo wapatali pamaso pa Yehova? Nanga mumaona kuti Akhristu anzanu ali ngati chinthu choti chikuumbidwabe ndi Yehova? Tiyeni tsopano tione zimene Yehova amachita poumba anthu. Kodi iye amasankha bwanji anthu oti awaumbe? Kodi amawaumba bwanji? Nanga n’chifukwa chiyani amawaumba?

YEHOVA AMASANKHA ANTHU OTI AWAUMBE

4. Kodi Yehova amasankha bwanji anthu oti awaumbe? Perekani zitsanzo.

4 Yehova akafuna kusankha munthu woti amuumbe sayang’ana nkhope koma mtima. (Werengani 1 Samueli 16:7b.) Mfundo imeneyi imaonekera bwino kwambiri tikaona zimene anachita pamene ankakhazikitsa mpingo wachikhristu. Ena amene anawasankha ankaoneka ngati osayenera. (Yoh. 6:44) Chitsanzo ndi Mfarisi wina, dzina lake Saulo, yemwe anali “wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe.” (1 Tim. 1:13) Popeza Yehova “amayesa mitima” sanaone kuti Saulo sangatheke kuumbidwa. (Miy. 17:3) M’malomwake ankaona kuti akhoza kumuumba n’kukhala chiwiya cha mtengo wapatali “chochita kusankhidwa” kuti akachitire umboni “kwa anthu a mitundu ina, komanso kwa mafumu ndi ana a Isiraeli.” (Mac. 9:15) Anthu ena omwe Mulungu ankawaona kuti ndi ‘ziwiya zolemekezeka’ poyamba anali oledzera, achiwerewere komanso akuba. (Aroma 9:21; 1 Akor. 6:9-11) Koma anthuwa ataphunzira za Mulungu n’kuyamba kumukhulupirira, analola kuti iye awaumbe.

5, 6. Kodi mfundo yoti Yehova amaumba anthu ingakhudze bwanji mmene timaonera (a) anthu a m’gawo lathu? (b) abale ndi alongo athu?

5 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene takambiranazi? Tisamaweruze anthu a m’gawo lathu komanso Akhristu anzathu podziwa kuti Yehova amaona mtima. Tizidziwanso kuti iye ndi amene amasankha anthu oti awaumbe. Taganizirani chitsanzo cha bambo ena dzina lawo a Michael. Iwo anati: “A Mboni za Yehova akabwera kwathu, sindinkafuna kulankhula nawo ndipo ndinkangokhala ngati sindikuwaona. Ndinali munthu wamwano kwambiri. Koma patapita nthawi, ndinakumana ndi banja lina limene linandichititsa chidwi chifukwa cha khalidwe lawo. Kenako ndinadabwa kwambiri nditamva kuti iwo ndi a Mboni. Izi zinachititsa kuti ndiyambe kufufuza zokhudza a Mboni za Yehova. Ndiyeno ndinapeza kuti ndinkadana nawo chifukwa chosadziwa zoona komanso chifukwa cha zabodza zimene anthu amanena zokhudza a Mboni.” Kuti adziwe zoona, a Michael anayamba kuphunzira Baibulo. Patapita nthawi anabatizidwa ndipo anayamba utumiki wa nthawi zonse.

6 Mfundo yoti Yehova amaona mitima komanso ndi amene amaumba anthu, imatithandiza kuti tiziona Akhristu anzathu moyenera. Kodi mumaona abale ndi alongo anu ngati mmene Yehova amawaonera, kuti ndi anthu oti akuumbidwabe? Popeza Yehova amaona mtima, amadziwa kuti munthu akhoza kusintha ndipo saganizira kwambiri zimene munthu amalakwitsa. (Sal. 130:3) Tingatsanzire Mulungu ngati ifenso timaona kuti Akhristu anzathu akhoza kusintha. Ndipotu tingathe kuthandiza Mulungu pa ntchito yake youmba anthu tikamathandiza abale ndi alongo kuti akhale olimba mwauzimu. (1 Ates. 5:14, 15) Akulu, omwe ndi “mphatso za amuna,” ayenera kukhala patsogolo pochita zimenezi.—Aef. 4:8, 11-13.

N’CHIFUKWA CHIYANI YEHOVA AMATIUMBA?

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira Yehova akamatilangiza?

7 Mwina munamvapo anthu ena akunena kuti: ‘Makolo anga akamandipatsa chilango ndinkangoona ngati akundilakwira. Koma nditakhala ndi ana, ndinayamba kuona kuti makolowo ankachita bwino.’ Tikakula ndi pamene timayamba kuona chilango mmene Yehova amachionera. Timaona kuti n’chothandiza komanso ndi umboni woti makolo athu amatikonda. (Werengani Aheberi 12:5, 6, 11.) Yehova ndi Atate wathu ndipo amatiumba chifukwa choti amatikonda. Amafuna kuti tikhale anzeru, tizisangalala komanso tizimukonda. (Miy. 23:15) Iye sasangalala tikamavutika komanso safuna kuti tidzafe monga “ana oyenera kulandira mkwiyo wa Mulungu,” chifukwa cha uchimo wochokera kwa Adamu.—Aef. 2:2, 3.

8, 9. Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji masiku ano, nanga adzapitiriza bwanji m’paradaiso?

8 Monga “ana oyenera kulandira mkwiyo wa Mulungu,” mwina poyamba tinali ndi makhalidwe osamusangalatsa. Ena anali ndi makhalidwe ngati a nyama zakutchire. Koma timayamikira kwambiri kuti Yehova akutiumba ndipo tsopano tili ngati ana a nkhosa. (Yes. 11:6-8; Akol. 3:9, 10) Yehova akutiumbira mu paradaiso wauzimu ndipo timaona kuti ndife otetezeka kudziko loipali. Kwa anthu amene anakulira m’banja lopanda chikondi komanso losagwirizana, amaona kuti tsopano ali ndi abale ndi alongo amene amawakonda kwambiri. (Yoh. 13:35) Yehova wawaphunzitsanso kuti azikonda anzawo. Tonsefe tadziwa Mulungu ndipo timaona kuti amatikonda monga Atate athu.—Yak. 4:8.

9 M’dziko latsopano tidzasangalala kwambiri chifukwa tidzakhala m’paradaiso weniweni ndipo Ufumu wa Mulungu ndi umene uzidzatilamulira. Pa nthawiyo Yehova adzapitiriza kutiumba ndiponso kutiphunzitsa zinthu zambiri. (Yes. 11:9) Adzatithandizanso kukhala ndi maganizo ndiponso matupi angwiro kuti tizidzatha kumvetsa bwino zimene azidzatiphunzitsa komanso tizidzamutumikira osalakwitsa chilichonse. Choncho tiyeni tipitirize kumvera Yehova ndipo tizidziwa kuti amatiumba chifukwa chotikonda.—Miy. 3:11, 12.

KODI YEHOVA AMATIUMBA BWANJI?

10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti Yehova ndi Woumba waluso komanso woleza mtima?

10 Popeza Yehova ndi Woumba waluso, akamafuna kuumba munthu amadziwa kuti munthuyo ndi wotani ndipo amamuumba mogwirizana ndi mmene alili. (Werengani Salimo 103:10-14.) Amaumba munthu aliyense payekha ndipo amaganizira zimene munthuyo sangakwanitse, zimene amalakwitsa komanso mmene amachitira pa zinthu zauzimu. Zimene Mwana wake ankachita ali padziko lapansi zimatithandiza kudziwa mmene Yehova amationera anthufe. Taganizirani zimene Yesu ankachita atumwi ake akamakangana kuti wamkulu ndani. Mukanakhala kuti munalipo pamene atumwiwo ankakangana, kodi mukanaganiza chiyani? Mwina mukanaona kuti ndi odzikuza ndipo sangaumbike. Komatu Yesu sanawaone choncho. Anadziwa kuti atumwi akewo angathe kuumbika. Ankangofunika kuwakomera mtima, kuwapatsa malangizo komanso kuwasonyeza chitsanzo cha kudzichepetsa. (Maliko 9:33-37; 10:37, 41-45; Luka 22:24-27) Yesu ataukitsidwa atumwiwo analandira mzimu woyera ndipo unawathandiza kuti asamaganizire kwambiri za udindo kapena kutchuka koma za ntchito imene anawapatsa.—Mac. 5:42.

11. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti ankalola Yehova kuti azimuumba, nanga tingamutsanzire bwanji?

11 Masiku ano Yehova amaumba atumiki ake pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu woyera komanso mpingo wachikhristu. Mawu a Mulungu amatiumba ngati timawawerenga, kusinkhasinkha mfundo zomwe tawerengazo komanso kupempha Yehova kuti atithandize kuzigwiritsa ntchito pa moyo wathu. Davide analemba kuti: “Ndikakumbukira inu ndili pabedi langa, pa nthawi za ulonda wa usiku ndimasinkhasinkha za inu.” (Sal. 63:6) Analembanso kuti: “Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo. Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolera.” (Sal. 16:7) Davide ankalola kuti malangizo a Mulungu akhazikike mumtima mwake komanso kuti aumbe maganizo ake. Iye ankachita zimenezi ngakhale kuti malangizo ena anali omudzudzula. (2 Sam. 12:1-13) Davide anapereka chitsanzo chabwino cha kudzichepetsa komanso kumvera Mulungu. Kodi inunso mumasinkhasinkha Mawu a Mulungu, n’kulola kuti zimene mwawerengazo zikhazikike mumtima mwanu? Tiyenera kumachita zimenezi nthawi zonse.—Sal. 1:2, 3.

12, 13. Kodi Yehova amatiumba bwanji pogwiritsa ntchito mzimu woyera komanso mpingo?

12 Mzimu woyera umatiumba m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, ungatithandize kutsanzira Khristu n’kukhala ndi makhalidwe amene mzimuwo umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Khalidwe lina limene mzimu woyera umatulutsa ndi chikondi. Timakonda Mulungu ndiponso timafuna kumumvera. Timasangalala akamatiumba chifukwa timadziwa kuti malamulo ake si olemetsa. Mzimu woyera umatipatsanso mphamvu kuti tisaumbidwe ndi dzikoli komanso mzimu wake woipa. (Aef. 2:2) Paulo ali mnyamata anatengera mtima wonyada wa atsogoleri achiyuda. Koma atakhala mtumwi analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afil. 4:13) Nafenso tiyeni tizipempha Mulungu kuti atipatse mzimu woyera ndipo iye adzayankha mapemphero athuwo.—Sal. 10:17.

Yehova amagwiritsa ntchito akulu potiumba, koma nafenso tiyenera kuchita mbali yathu (Onani ndime 12 ndi 13)

13 Yehova amagwiritsanso ntchito mpingo wachikhristu komanso akulu kuti atiumbe. Mwachitsanzo, akulu akazindikira kuti tili ndi mavuto ena ake, amayesetsa kutithandiza koma sadalira nzeru zawo. (Agal. 6:1) Iwo modzichepetsa amapempha Yehova kuti awathandize kukhala anzeru komanso ozindikira. Kenako amafufuza m’Mawu a Mulungu komanso m’mabuku athu. Zimenezi zimawathandiza kuti adziwe mmene angatithandizire. Choncho akamakuthandizani mokoma mtima komanso mwachikondi, mwina pa nkhani ya kavalidwe, kodi mumalandira malangizo awo podziwa kuti ndi umboni woti Yehova amakukondani? Mukamachita zimenezi, mumasonyeza kuti muli ngati dongo labwino m’manja mwa Yehova ndipo mukufuna kuti iye akuumbeni.

14. Ngakhale kuti Yehova angathe kuchita zimene akufuna potiumba, kodi amasonyeza bwanji kuti amalemekeza ufulu wathu wosankha zochita?

14 Kumvetsa mmene Mulungu amatiumbira kumatithandiza kuti tiziona moyenera Akhristu anzathu komanso anthu a m’gawo lathu, kuphatikizapo amene timaphunzira nawo Baibulo. Munthu woumba mbiya akakumba dothi, sikuti amangofikira kuyamba kuumba nthawi yomweyo. Amayamba kaye wachotsa zinthu zosafunika monga timiyala ndi zinyalala. Koma popeza Mulungu amalemekeza ufulu wathu wosankha zochita, akafuna kutiumba amatilola kuti tichotse kaye tokha timakhalidwe tosafunika. Kuti tithe kuchita zimenezi amatithandiza kuzindikira mfundo zake zolungama n’cholinga choti tidziwe zofunika kusintha.

15, 16. Kodi anthu ena amene akuphunzira Baibulo amasonyeza bwanji kuti akufuna kuti Yehova awaumbe? Perekani chitsanzo.

15 Taganizirani zimene zinachitikira mayi wina wa ku Australia, dzina lake Tessie. Mlongo amene ankaphunzira ndi mayiyu anati: “A Tessie ankakonda ndithu kuphunzira Baibulo. Koma ankaoneka ngati zimene akuphunzirazo sizikuwathandiza moti sankabwera kumisonkhano. Choncho nditaiganizira kwambiri nkhaniyi komanso kupemphera, ndinaganiza zoti ndisiye kuphunzira nawo. Koma nditapitako komaliza, ndinadabwa kwambiri ndi zimene anandiuza. Iwo anati ankakonda kwambiri kutchova juga choncho ankaona kuti chingakhale chinyengo kumasonkhana, kwinaku n’kumachitabe khalidwe loipali. Ndiyeno pa tsikuli anandiuza kuti aganiza zosiya kutchova juga.”

16 Pasanapite nthawi a Tessie anayamba kusonkhana ndipo anayamba kusonyeza makhalidwe abwino. Iwo sanagonje ngakhale kuti anzawo ankawanyoza. Mlongo uja anati: “A Tessie anabatizidwa ndipo kenako anayamba upainiya wokhazikika ngakhale kuti anali ndi ana aang’ono.” Izi zikusonyeza kuti ophunzira Baibulo akasintha moyo wawo n’cholinga choti akondweretse Mulungu, iye amakhala nawo pa ubwenzi ndipo amawaumba kuti akhale anthu abwino.

17. (a) Kodi mumamva bwanji mukaganiza mfundo yoti Yehova amatiumba? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

17 Mofanana ndi kale, anthu ambiri amaumba zinthu pamanja. Izi zimapangitsa kuti chinthu chimene chikuumbidwacho chizikhala pafupi ndi woumbayo. Nayenso Yehova akamatiumba amakhala nafe pafupi ndipo amatilezera mtima, kutipatsa malangizo n’kumaona ngati tikuwagwiritsa ntchito. (Werengani Salimo 32:8.) Kodi inuyo mumaona kuti Yehova amakukondani? Nanga mumaona kuti akukuumbani mwachikondi? Ngati ndi choncho, kodi mungatani kuti mukhalebe ngati dongo labwino m’manja mwake? Kodi ndi makhalidwe ati amene muyenera kupewa kuti musakhale ngati dongo lamiyala komanso lolimba? Nanga makolo angathandize bwanji kuti ana awo aumbidwe ndi Yehova? M’nkhani yotsatira tidzakambirana mafunso amenewa.