Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova “Amakuderani Nkhawa”

Yehova “Amakuderani Nkhawa”

KODI tingatsimikize bwanji kuti mawu amenewa ndi oona? Chifukwa chakuti Baibulo pa 1 Petulo 5:7 limati: “Chitani zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.” Tiyeni tione umboni wosonyeza kuti Yehova Mulungu amatideradi nkhawa.

AMATIPATSA ZOFUNIKA KUTI TIKHALE NDI MOYO

Yehova ndi wokoma mtima komanso woolowa manja

Yehova ali ndi makhalidwe amene bwenzi labwino limakhala nawo. Anthu akamachitirana mokoma mtima komanso kupatsana zinthu moolowa manja, amakhala mabwenzi apamtima. Zimene Yehova amatichitira zimasonyeza kuti ndi wokoma mtima komanso woolowa manja. Mwachitsanzo, “amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mat. 5:45) Kodi dzuwa ndi mvula zimatithandiza bwanji? Zimatithandiza kuti tikolole zakudya zambiri n’kumasangalala. (Mac. 14:17) Yehova amaonetsetsa kuti dzikoli likutulutsa chakudya chambiri. Ndipotu tonsefe timasangalala tikadya chakudya chokoma.

Nanga n’chifukwa chiyani anthu ambiri amavutika ndi njala? Ndi chifukwa chakuti nthawi zambiri olamulira saganizira za anthu awo. M’malomwake amangoganizira zandale ndi zimene angachite kuti alemere. Koma posachedwapa Yehova adzathetsa vuto limeneli ndipo adzachotsa maufumu onse kuti alowedwe m’malo ndi Ufumu wakumwamba womwe wolamulira wake ndi Yesu. Pa nthawiyo aliyense adzakhala ndi chakudya chokwanira. Koma panopa Yehova amaonetsetsa kuti atumiki ake okhulupirika ali ndi zofunika pa moyo. (Sal. 37:25) Kodi umenewu si umboni woti amatidera nkhawa?

AMALOLA KUTI TIZILANKHULA NAYE KWA NTHAWI YAITALI

Yehova amalola kuti tizilankhula naye kwa nthawi yaitali

Mnzanu wapamtima amayesetsa kupeza nthawi yocheza nanu. Mukhoza kutha nthawi yaitali mukukambirana zinthu zimene zimakusangalatsani. Iye amamvetsera mukamamuuza mavuto anu komanso zimene zikukudetsani nkhawa. Kodi Yehova amachitanso zimenezi? Inde. Amamva mapemphero athu ndipo n’chifukwa chake Baibulo limatiuza kuti ‘tizilimbikira kupemphera’ komanso ‘tizipemphera mosalekeza.’—Aroma 12:12; 1 Ates. 5:17.

Kodi Yehova angatilole kupemphera kwa iye kwa nthawi yaitali bwanji? Zimene Yesu anachita zingatithandize kudziwa yankho la funsoli. Asanasankhe atumwi ake, “anachezera kupemphera kwa Mulungu usiku wonse.” (Luka 6:12) N’kutheka kuti popempherapo, anatchula mayina a ophunzira ake ambiri komanso makhalidwe awo abwino ndi zimene ankalephera kuchita. Anapemphanso Atate ake kuti amuthandize kusankha atumwi oyenera. Mmene kunja kunkacha, n’kuti ali ndi chikhulupiriro chonse kuti wasankha anthu oyenera. Yehova ndi “wakumva pemphero” ndipo amasangalala kumva anthu akupemphera kuchokera mumtima. (Sal. 65:2) Ngakhale munthu atapemphera kwa maola ambiri kumufotokozera nkhani imene ikumudetsa nkhawa, Yehova sadandaula kuti akumuchedwetsa.

AMATIKHULULUKIRA

Yehova amatikhululukira

Nthawi zina ngakhale anthu amene amagwirizana, zimawavuta kuti akhululukirane akalakwirana chachikulu. Ena amathetsa ubwenzi wawo wakalekale chifukwa choona kuti sangakhululuke zimene mnzawo wawachitira. Koma umu si mmene Yehova alili. Baibulo limalimbikitsa anthu amene alapa kuti abwerere kwa iye chifukwa “amakhululuka ndi mtima wonse.” (Yes. 55:6, 7) Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu amakhululuka ndi mtima wonse chonchi?

Yehova alibe wofanana naye pa nkhani ya chikondi. Iye anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake pofuna kupulumutsa anthu ku uchimo ndiponso mavuto onse. (Yoh. 3:16) Dipo limatithandiza kwambiri. Mulungu amagwiritsa ntchito nsembe ya Khristu kuti akhululukire anthu amene amawakonda. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Tikavomereza machimo athu, adzatikhululukira ndi kutiyeretsa ku ntchito zonse zoipa.” (1 Yoh. 1:9) Chifukwa choti Yehova amatikhululukira, timakhalabe naye pa ubwenzi, ndipo zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri.

AMATITHANDIZA TIKAKUMANA NDI MAVUTO

Yehova amatithandiza tikakumana ndi mavuto

Anthu amene amakondana amathandizana pa mavuto. Kodi Yehova amachitanso zimenezi? Inde. Mawu ake amati: “Ngakhale [mtumiki wa Mulungu] atapunthwa, sadzagweratu, pakuti Yehova wamugwira dzanja.” (Sal. 37:24) Yehova amathandiza atumiki ake m’njira zosiyanasiyana. Taganizirani zimene zinachitikira mtsikana wina amene amakhala ku Caribbean pachilumba chotchedwa St. Croix.

Mtsikanayu ankanyozedwa kwambiri ndi anzake a m’kalasi chifukwa choti sankachitira saluti mbendera. Koma atapempha Yehova kuti amuthandize, anaganiza zowafotokozera anzakewo zomwe amakhulupirira pa nkhaniyi. Choncho analemba lipoti lomwe anawerengera kalasi yonse. Anagwiritsa ntchito Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, ndipo anafotokoza mmene nkhani ya Sadirake, Mesake ndi Abedinego inamuthandizira kusankha zochita pa nkhaniyi. Iye anati: “Yehova anateteza anyamata achiheberi atatuwa chifukwa choti anakana kulambira fano.” Ndiyeno anauza anzake a m’kalasi mwakewo kuti aliyense amene akufuna akhoza kum’patsa bukulo. Ana 11 analandira bukuli. Mtsikanayu anasangalala kwambiri chifukwa anadziwa kuti Yehova anamupatsa nzeru komanso anamuthandiza kukhala wolimba mtima kuti athe kulalikira.

Ngati nthawi zina mumakayikira zoti Yehova amakuderani nkhawa, mungachite bwino kuganizira malemba monga Salimo 34:17-19; 55:22 ndi 145:18145:18, 19. Mungafunsenso anthu amene atumikira Mulungu kwa nthawi yaitali kuti akufotokozereni mmene Yehova wawathandizira. Ndiponso mukakhala ndi vuto linalake muzipemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni. Mukamachita zimenezi, mudzaona kuti nanunso Yehova “amakuderani nkhawa.”