Msampha Wina wa Satana
PA NTHAWI imene Aisiraeli ankafuna kuwoloka mtsinje wa Yorodano kuti alowe m’dziko limene Mulungu anawalonjeza, kunafika alendo. Alendowo anali akazi amtundu wina ndipo anaitanira amuna achiisiraeli kuphwando. Mwina amunawo anaona kuti unali mwayi wapadera woti apeze anzawo atsopano, avine komanso adye chakudya chabwino. Koma miyambo ndiponso makhalidwe a akaziwo sankagwirizana ndi Chilamulo cha Mulungu. N’kutheka kuti amuna achiisiraeli ankaganiza kuti: ‘Tikhala osamala. Sitingapange nawo zoipa zawozo.’
Kodi n’chiyani chinachitika? Baibulo limanena kuti: “Iwo anayamba kuchita chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu.” Akaziwo ankafuna kuti amunawo ayambe kulambira milungu yonyenga ndipo zinathekadi. Choncho “mkwiyo wa Yehova unawayakira.”—Aisiraeliwo anaphwanya malamulo awiri a m’Chilamulo cha Mulungu. Iwo anagwadira mafano komanso kuchita chiwerewere. Izi zinachititsa kuti anthu masauzande ambiri afe. (Eks. 20:4, 5, 14; Deut. 13:6-9) Zimene zinachitikazi zinali zomvetsa chisoni kwambiri chifukwa Aisiraeliwo anali atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa.—Num. 25:5, 9.
Pa nkhani imeneyi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Zinthu zimenezi zinali kuwagwera monga zitsanzo, ndipo zinalembedwa kuti zitichenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikira.” (1 Akor. 10:7-11) N’zosachita kufunsa kuti Satana anasangalala kwambiri kuti Aisiraeliwo analephera kulowa m’Dziko Lolonjezedwa chifukwa cha tchimo lawoli. Tingachite bwino kwambiri kutsatira chenjezo limene Paulo anaperekali chifukwa zimene Satana akufuna n’zoti nafenso tilephere kulowa m’dziko latsopano la Mulungu.
MSAMPHA WOOPSA KWAMBIRI
Satana amagwiritsa ntchito misampha imene amaidziwa bwino komanso yomwe yamuthandiza kukola anthu ambiri. Monga taonera, iye anagwiritsa ntchito msampha wa chiwerewere kuti apusitse Aisiraeli. Msampha umenewu akuugwiritsabe ntchito masiku ano ndipo ukumuthandiza. Nyambo ina imene amagwiritsa ntchito pa msamphawu ndi kuonera zolaula.
Masiku ano, munthu akhoza kuonera zolaula popanda anthu ena kudziwa. Kale, kuti munthu aonere zolaula ankafunika kupita kumalo oonetsa mafilimu kapena kupita kusitolo yapadera yogulitsa mabuku a zolaula. Ndiye anthu ambiri sankapita kumalo oterewa chifukwa choopa kuti ena angawaone. Koma masiku ano munthu akhoza kuonera zolaula ngati atalowa pa intaneti kumalo ena monga kuntchito. M’mayiko ambiri, munthu akhoza kuonera zolaula ngakhale ali m’nyumba mwake.
Komatu si zokhazi. Zipangizo zamakono monga mafoni zachititsa kuti anthu aziona zolaula mosavuta. Munthu amatha kuzionera pachipangizo chake akuyenda, ali m’basi kapena ali musitima.
Popeza anthu amatha kuonera zolaula mosavuta popanda ena kudziwa, vuto limeneli lafika poipa kwambiri kusiyana ndi m’mbuyomu. Anthu ambiri amene amaonera zolaula amasokoneza mabanja awo, amadzichotsera ulemu komanso amawononga chikumbumtima chawo. Koma choopsa kwambiri n’chakuti akhoza kuwononga ubwenzi wawo ndi Mulungu. Choncho tinganene kuti munthu akamaonera zolaula amadzibweretsera mavuto ochuluka. Nthawi zambiri, munthu woonera zolaula amasokoneza maganizo ake. Ngakhale kuti zimenezi zikhoza kusintha pakapita nthawi, kwa anthu ena sizitheratu.
Chosangalatsa n’chakuti Yehova amatithandiza kuti tipewe msampha umenewu. Koma kuti atithandize, tiyenera kuchita zinthu mosiyana ndi amuna achiisiraeli aja. Tiyenera kumvera Mawu a Mulungu ndi mtima wonse. (Eks. 19:5) Tiyeneranso kuzindikira kuti Mulungu amadana kwambiri ndi zolaula. N’chifukwa chiyani tikutero?
MUZIDANA NAZO NGATI MMENE YEHOVA AMACHITIRA
Malamulo amene Yehova anapatsa Aisiraeli anali osiyana ndi malamulo amene mitundu ina inkayendera. Tingati malamulowo anali ngati mpanda chifukwa ankateteza Aisiraeli kuti asamachite zinthu zoipa zimene anthu ena ankachita. (Deut. 4:6-8) Malamulowo ankasonyeza momveka bwino kuti Yehova amadana ndi chiwerewere.
Yehova anauza Aisiraeli makhalidwe oipa amene mitundu ina inkachita. Kenako anawauza kuti: “Musakachite zimene amachita m’dziko la Kanani, kumene ndikukulowetsani. . . . Dzikolo Lev. 18:3, 25.
n’lodetsedwa, ndipo ndidzalilanga chifukwa cha kulakwa kwake.” Popeza Mulungu ndi woyera, iye ankaona kuti makhalidwe a anthu a ku Kanani anali oipa kwambiri moti zinapangitsa kuti ngakhale dziko lawo likhale lodetsedwa.—Ngakhale kuti Yehova analanga anthu a ku Kanani, anthu ambiri anapitirizabe kuchita zachiwerewere. Patapita zaka zoposa 1,500, Paulo anafotokoza za anthu am’mayiko amene Akhristu ankakhala. Iye ananena kuti ‘sankathanso kuzindikira makhalidwe abwino.’ Ananenanso kuti anthuwo “anadzipereka okha ku khalidwe lotayirira kuti achite chonyansa chamtundu uliwonse mwadyera.” (Aef. 4:17-19) Masiku anonso anthu ambiri amachita makhalidwe oipa mopanda manyazi. Koma Akhristufe tiyenera kuyesetsa kupewa kuonera zinthu zonyansa zimene anthu akuchita m’dzikoli.
Anthu oonera zolaula amasonyeza kuti salemekeza Mulungu ngakhale pang’ono. Iye analenga anthu m’chifaniziro chake komanso m’njira yoti azilemekezeka. Mulungu anasonyeza kuti ndi wanzeru popereka malamulo okhudza kugonana. Iye ankafuna kuti anthu okwatirana okha azisangalala ndi mphatso ya kugonana. (Gen. 1:26-28; Miy. 5:18, 19) Koma anthu amene amapanga zolaula kapena kulimbikitsa anthu kuti aziziona amakhala akunyalanyaza mfundo zamakhalidwe abwino za Mulungu. Zimene anthuwa amachita zimanyoza Yehova ndipo iye adzawaweruza.—Aroma 1:24-27.
Anthu ena amawerenga kapena kuona zolaula mwadala ndipo amaganiza kuti ndi zosangalatsa basi. Koma akamachita zimenezi amakhala akuthandiza anthu amene amanyalanyaza mfundo za Yehova. Mwina cholinga chawo sichikhala chimenechi akamayamba kuona zolaulazo. Komatu Baibulo limasonyeza momveka bwino kuti anthu amene amalambira Mulungu woona ayenera kudana kwambiri ndi zolaula. Paja limati: “Inu okonda Yehova danani nacho choipa.”—Sal. 97:10.
N’zoona kuti kutsatira malangizo amenewa kungakhale kovuta ngakhale kwa amene safuna kuona zolaula. Tikutero chifukwa tonse si angwiro ndipo tingafunike kulimbana ndi maganizo olakwika okhudza kugonana. Mtima wathu wonyengawu ungatipangitse kuganiza kuti kungoonera Yer. 17:9) Koma anthu ambiri amene ayamba kulambira Yehova akwanitsa kuthana ndi maganizo amenewa. Mfundo imeneyi ingakulimbikitseni ngati nanunso muli ndi vuto limeneli. Tiyeni tione mmene Mawu a Mulungu angakuthandizireni kupewa msampha wa Satanawu.
pang’ono zolaula sikungatisokoneze. (MUZIPEWA KUGANIZIRA ZINTHU ZACHIWEREWERE
Monga tanena kale, Aisiraeli ambiri anakopeka ndi zinthu zoipa zimene ankalakalaka ndipo zotsatira zake sizinali zabwino. Zimenezi zikhoza kuchitikanso masiku ano. Yakobo, yemwe anali m’bale wake wa Yesu, anapereka chenjezo lakuti: ‘Munthu aliyense amakopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake. Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo.’ (Yak. 1:14, 15) Chilakolako chikakula mumtima wa munthu zimakhala zosavuta kuti achimwe. Choncho zinthu zolakwika zikabwera m’maganizo mwathu, tiyenera kuzichotsa osati kupitiriza kuziganizira.
Mukangoyamba kuganizira zolakwika, muyenera kusintha maganizowo mwamsanga. Paja Yesu ananena kuti: “Ngati dzanja lako kapena phazi lako limakupunthwitsa, ulidule ndi kulitaya kutali. . . . Komanso ngati diso lako limakupunthwitsa ulikolowole n’kulitaya.” (Mat. 18:8, 9) Apa Yesu sankatanthauza kudula ziwalo zenizeni. Iye ankatanthauza kuti tiyenera kuchotsa mwamsanga chilichonse chimene chingatisokoneze. Ndiye kodi tingatsatire bwanji mfundo imeneyi pa nkhani ya zolaula?
Mukangoona zolaula musaganize kuti, ‘Aaa sizingandisokoneze.’ Koma muyenera kuyang’ana kumbali nthawi yomweyo. Muyeneranso kuthimitsa TV, kompyuta kapena foni yanu pompopompo. Mukatero muyambe kuganizira zinthu zina zabwino. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mupewe kuganizira zolakwika m’malo molola kuti zikusokonezeni.
KODI MUNGATANI NGATI MUKUVUTIKA KUIWALA ZOLAULA ZIMENE MUNAONA?
Kodi mungatani ngati mwakwanitsa kuthana ndi vuto loonera zolaula koma zimene munaonazo zimabwerabe m’maganizo mwanu? Zolaula sizichoka msanga m’maganizo ndipo munthu
akhoza kuzikumbukira nthawi iliyonse. Zimenezi zikachitika, zingakhale zosavuta munthu kuganiza zochita zinthu zodetsa monga kudziseweretsa maliseche. Choncho muyenera kudziwa kuti zolaula zikhoza kubwera m’maganizo mwanu ndipo muyenera kukhala wokonzeka kulimbana nazo.Muyenera kuyesetsa kuti zimene mumaganiza komanso kuchita zizigwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Muzitengera chitsanzo cha mtumwi Paulo yemwe ‘ankamenya thupi lake n’kulitsogolera ngati kapolo.’ (1 Akor. 9:27) Musalole kuti maganizo oipa azikulamulirani. Koma “sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Muzikumbukira kuti mudzakhala wosangalala kwambiri mukamaganiza komanso kuchita zimene Mulungu amafuna osati zinthu zoipa zimene mumalakalaka.
Mudzakhala wosangalala kwambiri mukamaganiza komanso kuchita zimene Mulungu amafuna osati zinthu zoipa zimene mumalakalaka
Mungachite bwino kuloweza mavesi ena a m’Baibulo n’cholinga choti maganizo olakwika akabwera muzisintha n’kuyamba kuganizira malembawo. Malemba monga Salimo 119:37; Yesaya 52:11; Mateyu 5:28; Aefeso 5:3; Akolose 3:5 ndi 1 Atesalonika 4:4-8 akhoza kukuthandizani kuti muzikhala ndi maganizo a Yehova pa nkhani ya zolaula komanso zimene amafuna kuti muzichita.
Koma kodi mungatani ngati mtima wofuna kuonera kapena kuganizira zolakwika ukukuvutani kwambiri? Muyenera kuchita zinthu ngati mmene Yesu anachitira. (1 Pet. 2:21) Iye atabatizidwa, Satana ankamuyesa. Kodi Yesuyo anatani? Iye anapitiriza kukana mayeserowo ndipo nthawi zonse ankagwiritsa ntchito malemba. Atanena kuti: “Choka Satana!” Satanayo anamusiya. Yesu sanasiye kulimbana ndi Mdyerekezi choncho nanunso simuyenera kusiya. (Mat. 4:1-11) Satana ndi dziko lakeli adzayesetsabe kukuchititsani kuti muzingoganizira zachiwerewere, koma musasiye kulimbana ndi maganizo olakwikawa. Yehova akhoza kukuthandizani kuti mupambane pa nkhondo yolimbana ndi vuto loonera zolaula n’kugonjetsa Satana.
MUZIPEMPHERA KOMANSO KUMVERA YEHOVA
Nthawi zonse muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Paulo ananena kuti: “Zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Mulungu adzakupatsani mtendere wamumtima womwe ungakuthandizeni pamene mukulimbana ndi maganizo olakwika. Kumbukirani kuti mukamayandikira Mulungu, “iyenso adzakuyandikirani.”—Yak. 4:8.
Chinthu chachikulu chimene chingakuthandizeni kuti mukhale otetezeka ku misampha ya Satana ndi kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse. Yesu ananena kuti: “Wolamulira wa dziko [Satana] akubwera. Iye alibe mphamvu pa ine.” (Yoh. 14:30) N’chifukwa chiyani Yesu ananena zimenezi? Iye anafotokoza kuti: “Amene ananditumayo ali ndi ine. Iye sandisiya ndekha, chifukwa ndimachita zinthu zomukondweretsa nthawi zonse.” (Yoh. 8:29) Inunso Yehova sadzakusiyani mukamachita zinthu zomusangalatsa. Mukamapewa msampha woonera zolaula, Satana sadzakhala ndi mphamvu pa inu.