Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 26

Tizithandiza Anthu Amene Ali ndi Nkhawa

Tizithandiza Anthu Amene Ali ndi Nkhawa

“Nonsenu mukhale amaganizo amodzi, omverana chisoni, okonda abale, achifundo chachikulu, ndiponso amaganizo odzichepetsa.”​—1 PET. 3:8.

NYIMBO NA. 107 Tizitsanzira Chikondi cha Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi tingatsanzire bwanji Atate wathu Yehova?

YEHOVA amatikonda kwambiri. (Yoh. 3:16) Ndipo tonsefe timafuna kutsanzira Atate wathu wachikondi. Choncho timayesetsa ‘kumvera chisoni anthu onse, kuwakonda ndiponso kuwachitira chifundo’ koma makamaka “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.” (1 Pet. 3:8; Agal. 6:10) N’chifukwa chake timayesetsa kuthandiza Akhristu anzathu akakumana ndi mavuto.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Munthu aliyense amene akufuna kukhala m’banja la Yehova adzakumana ndi mavuto. (Maliko 10:29, 30) Ndipo pamene mapeto akuyandikira, mavutowa aziwonjezereka. Ndiye kodi tingatani kuti tizithandizana? Tiyeni tikambirane zimene tingaphunzire pa nkhani za m’Baibulo zokhudza Loti, Yobu ndi Naomi. Tikambirananso mavuto ena amene abale ndi alongo athu akukumana nawo masiku ano komanso mmene tingawathandizire.

TIZIKHALA OLEZA MTIMA

3. Kodi lemba la 2 Petulo 2:7, 8 limasonyeza kuti Loti sanasankhe mwanzeru pa nkhani iti, nanga zotsatira zake zinali zotani?

3 Loti sanasankhe zinthu mwanzeru pamene anapita kukakhala ku Sodomu kumene kunali anthu a makhalidwe oipa kwambiri. (Werengani 2 Petulo 2:7, 8.) Kudera limeneli munthu akanatha kupeza chuma chambiri. Koma popeza anthu ake anali oipa, Loti anakumana ndi mavuto aakulu atasamukirako. (Gen. 13:8-13; 14:12) Zikuoneka kuti mkazi wake ankakonda kwambiri mzindawu kapena anthu ena akumeneko moti sanamvere Yehova. Choncho anaphedwa pamene Mulungu anagwetsa moto ndi sulufule m’derali. Nawonso amuna amene ankafuna kukwatira ana aakazi a Loti anaphedwa. Nyumba ya Loti komanso katundu wake zinawonongedwanso. Zonsezi ziyenera kuti zinamupweteka Loti koma makamaka kuphedwa kwa mkazi wakeyu. (Gen. 19:12-14, 17, 26) Kodi Yehova anasiya kumulezera mtima Loti pa nthawi yovutayi? Ayi.

Yehova anasonyeza chifundo potumiza angelo kuti akapulumutse Loti ndi banja lake (Onani ndime 4)

4. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anali woleza mtima kwa Loti? (Onani chithunzi patsamba loyamba la magaziniyi.)

4 Ngakhale kuti Loti anasankha yekha kuti akakhale ku Sodomu, Yehova anamuchitira chifundo n’kutumiza angelo kuti akamupulumutse limodzi ndi banja lake. Koma angelo atamuuza kuti achoke mwamsanga ku Sodomu, Loti ‘ankazengereza.’ Choncho angelowo anamugwira dzanja n’kumuthandiza kuti athawe limodzi ndi banja lake. (Gen. 19:15, 16) Angelowo anamuuza kuti athawire kumapiri. Koma m’malo mongomvera Yehova, Loti anapempha kuti apite kutauni ina yapafupi. (Gen. 19:17-20) Yehova anamulezera mtima ndipo anamulola kuti apite kutauni imeneyo. Koma kenako Loti anayamba kuopa kukhala m’tauniyi ndipo anasamukira kumapiri kumene Yehova anamuuza kuti apite kuja. (Gen. 19:30) Apatu Yehova anasonyeza kuleza mtima kwambiri. Kodi tingamutsanzire bwanji?

5-6. Kodi lemba la 1 Atesalonika 5:14 lingatithandize bwanji tikamatsanzira Mulungu?

5 Mofanana ndi Loti, Mkhristu mnzathu akhoza kusankha zinthu mopanda nzeru n’kukumana ndi mavuto. Kodi mungatani zimenezi zitachitika? Mwina tingafune kungomuuza zoona kuti akukolola zimene anafesa. (Agal. 6:7) Koma tingachite bwino kutsanzira mmene Yehova anathandizira Loti. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

6 Yehova anatumiza angelo kuti akachenjeze Loti komanso kuti akamuthandize kutuluka mumzinda wa Sodomu. Ifenso tingafunike kuchenjeza m’bale wathu tikaona kuti akhoza kukumana ndi mavuto. Koma mwina tingamuthandizenso kupewa mavutowo. Ndipo tiyenera kumulezera mtima ngati sakutsatira mwamsanga malangizo ochokera m’Baibulo amene wapatsidwa. Tiyenera kutsanzira angelo awiri aja. M’malo motaya mtima n’kungomusiya m’bale wathuyo, tiyenera kuyesetsa kuona mmene tingamuthandizire. (1 Yoh. 3:18) Mwina tiyenera kuchita ngati tamugwira dzanja n’kumuthandiza kuti atsatire malangizo anzeru amene wapatsidwa.​—Werengani 1 Atesalonika 5:14.

7. Kodi tingatsanzire bwanji zimene Yehova anachitira Loti?

7 Yehova akanatha kumangoganizira zinthu zimene Loti ankalakwitsa. Koma m’malomwake, anauzira mtumwi Petulo kulemba kuti Loti anali munthu wolungama. N’zosangalatsa kwambiri kuti Yehova saganizira kwambiri zimene timalakwitsa. (Sal. 130:3) Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhaniyi? Tikamaganizira kwambiri makhalidwe abwino a abale ndi alongo athu, tikhoza kuwalezera mtima kwambiri. Ndipo iwo sangakane thandizo limene tingawapatse.

TIZIKHALA ACHIFUNDO

8. Kodi chifundo chingatilimbikitse kuchita chiyani mnzathu akakhala pa mavuto?

8 Mosiyana ndi Loti, mavuto a Yobu sanabwere chifukwa chosankha zinthu mopanda nzeru. Koma iye anakumana ndi mavuto akuluakulu monga kuwonongeredwa katundu, kunyozedwa komanso kudwala. Kuwonjezera pamenepo, ana ake onse anaphedwa. Anzake atatu anabweranso n’kuyamba kumuimba mlandu. N’chifukwa chiyani anzakewo sanamuchitire chifundo? Iwo ankangoona nkhaniyi pamwambamwamba. Izi zinachititsa kuti akhale ndi maganizo olakwika n’kuyamba kumuweruza Yobu kuti walakwitsa zinazake. Kodi ifeyo tingapewe bwanji zimene anthuwa anachita? Tizikumbukira kuti munthu akakumana ndi vuto, Yehova yekha ndi amene amadziwa nkhani yonse. Choncho ndi bwino kumvetsera mosamala pamene munthu akufotokoza mavuto ake. M’malo mongomva zimene akunena, tiziyesanso kumva ululu umene ali nawo mumtima mwake. Tikatero m’pamene tingamumvere chisoni kwambiri.

9. Kodi mtima wachifundo ungatithandize kupewa chiyani? Fotokozani.

9 Mtima wachifundo ungatithandizenso kuti tizipewa kufalitsa miseche yokhudza mavuto amene anzathu akukumana nawo. M’malo molimbikitsa anthu, munthu wamiseche amachititsa kuti anthu asamagwirizane mumpingo. (Miy. 20:19; Aroma 14:19) M’malo mokhala wokoma mtima, amalankhula mosaganiza ndipo zonena zake zimapweteka munthu amene akukumana kale ndi mavuto. (Miy. 12:18; Aef. 4:31, 32) Choncho ndi bwino kuganizira makhalidwe abwino amene munthu ali nawo komanso zimene tingachite kuti timuthandize pa mavuto ake.

Tizimvetsera moleza mtima pamene Mkhristu mnzathu akulankhula “zopanda pake” ndipo tizimulimbikitsa pa nthawi yoyenera (Onani ndime 10-11) *

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a pa Yobu 6:2, 3?

10 Werengani Yobu 6:2, 3Nthawi zina Yobu ankalankhula zinthu “zopanda pake.” Koma kenako anavomereza kuti zinthu zina zimene analankhula sizinali zabwino. (Yobu 42:6) Mofanana ndi Yobu, munthu amene akukumana ndi mavuto angalankhule zinthu zopanda pake zomwe akhoza kudandaula nazo pambuyo pake. Ngati zimenezi zitachitika, kodi tiyenera kutani? Tiyenera kumuchitira chifundo, osati kumuimba mlandu. Tizikumbukira kuti cholinga cha Yehova sichinali choti anthufe tizikumana ndi mavuto amene tikuzunzika nawo masiku ano. Choncho n’zosadabwitsa ngati mtumiki wokhulupirika wa Yehova atalankhula zolakwika chifukwa chopanikizika ndi mavuto. Ngakhale atanena zinthu zolakwika zokhudza Yehova kapena ifeyo, sitiyenera kufulumira kumukwiyira kapena kumuweruza.​—Miy. 19:11.

11. Kodi akulu angatsanzire bwanji Elihu popereka malangizo?

11 Nthawi zina munthu amene akukumana ndi mavuto amafunika kulangizidwa. (Agal. 6:1) Ndiye kodi akulu angachite bwanji zimenezi? Iwo ayenera kutsanzira Elihu. Paja iye anamvetsera mwachifundo pamene Yobu ankalankhula. (Yobu 33:6, 7) Elihu anapereka malangizo pambuyo pomvetsa bwino maganizo a Yobu. Akulu amene amatsatira chitsanzo cha Elihu amamvetsera mosamala kuti amvetse mavuto amene munthu akukumana nawo. Akatero amatha kupereka malangizo ofika munthuyo pamtima.

TIZIWALIMBIKITSA

12. Kodi Naomi anatani mwamuna wake komanso ana ake awiri atamwalira?

12 Naomi ankakonda Yehova komanso kumutumikira mokhulupirika. Koma mwamuna wake ndi ana ake awiri atamwalira ankafuna kusintha dzina lake kuti likhale “Mara,” kutanthauza kuti “Kuwawa.” (Rute 1:3, 5, 20, mawu am’munsi, 21) Pa nthawi imeneyi, mpongozi wake dzina lake Rute sanamusiye koma ankamuthandiza ndiponso kumulimbikitsa. Iye ankalankhula mawu osavuta kumva komanso ochokera mumtima osonyeza kuti ankakonda Naomi.​—Rute 1:16, 17.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza anthu amene mwamuna kapena mkazi wawo anamwalira?

13 Mwamuna kapena mkazi wa Mkhristu mnzathu akamwalira, Mkhristuyo amafunika kuthandizidwa. Anthu okwatirana amafanana ndi mitengo imene yakulira limodzi. Pakapita zaka, mizu yake imalukanalukana. Ndiyeno mtengo umodzi ukazulidwa n’kufa, mtengo winawo umavutika. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene waferedwa mwamuna kapena mkazi wake. Iye akhoza kumva chisoni kwa nthawi yaitali. Mlongo wina dzina lake Paula, * yemwe mwamuna wake anamwalira mwadzidzidzi, anati: “Moyo wanga unasinthiratu ndipo ndinasowa mtengo wogwira. Ndinataya mnzanga wapamtima kwambiri. Ndinkauza mwamuna wanga chilichonse. Iye ankasangalala nane limodzi ndikakumana ndi zosangalatsa ndipo ankandithandiza ndikavutika. Ankandimvetsera ndikamamuuza mavuto anga. Choncho panopa ndimamva ngati ndinadulidwa pakati.”

Kodi tingalimbikitse bwanji anthu amene aferedwa? (Onani ndime 14-15) *

14-15. Kodi tingalimbikitse bwanji munthu amene mwamuna kapena mkazi wake wamwalira?

14 Kodi tingalimbikitse bwanji munthu amene mwamuna kapena mkazi wake wamwalira? Choyamba, tiyenera kulankhula ndi munthuyo ngakhale kuti zingativute kupeza mawu abwino omuuza. Paula, yemwe tamutchula kale uja, ananena kuti: “Ndikudziwa kuti anthu amavutika kulankhula ndi munthu yemwe waferedwa. Iwo amaopa kuti zimene anganene zingamukhumudwitse. Koma bola kumva mawu alionse amene anganenedwe kusiyana ndi kuti anthu azingokuyang’ana.” Munthu woferedwa sangayembekezere kuti tinene mawu anzeru kwambiri. Paula anati: “Ndinkayamikira anzanga akangonena kuti, ‘Pepani kwambiri chifukwa cha mavutowa.’”

15 M’bale wina dzina lake William, yemwe mkazi wake anamwalira zaka zingapo zapitazo, ananena kuti: “Ndimayamikira kwambiri anthu akafotokoza zinthu zabwino zokhudza mkazi wanga. Zimanditsimikizira kuti anthu ankamukonda komanso kumulemekeza ndipo zimandilimbikitsa kwambiri. Zili choncho chifukwa mkazi wanga anali wamtengo wapatali kwa ine ndipo ndinkamukonda kwambiri.” Mlongo wina wamasiye dzina lake Bianca anati: “Ndimalimbikitsidwa anthu ena akapemphera nane limodzi komanso kundiwerengera malemba. Zimandithandiza anthuwo akanena zinthu zabwino zokhudza mwamuna wanga kapena akamamvetsera ndikamawauza za iyeyo.”

16. (a) Kodi tingathandize bwanji munthu amene waferedwa? (b) Malinga ndi Yakobo 1:27, kodi tili ndi udindo wotani?

16 Tiyenera kupitiriza kuthandiza anthu amene aferedwa ngati mmene Rute ankathandizira Naomi. Paula uja ananena kuti: “Mwamuna wanga atangomwalira, anthu ankandithandiza kwambiri. Kenako patapita nthawi, anayambanso kutanganidwa ndi zinthu zawo. Koma moyo wanga unali utasinthiratu. Zimakhala bwino kwambiri anthu akazindikira kuti munthu woferedwa amafuna kuthandizidwa kwa miyezi kapenanso zaka.” N’zoona kuti anthu amasiyana ndipo amamva chisoni mosiyananso. Ena amavomereza msanga zimene zawachitikira. Pomwe ena amavutika kwambiri nthawi iliyonse imene akuchita zinthu zimene kale ankachitira limodzi ndi mwamuna kapena mkazi wawo. Chofunika ndi kukumbukira kuti Yehova watipatsa mwayi komanso udindo wothandiza anthu amene aferedwa mwamuna kapena mkazi wawo.​—Werengani Yakobo 1:27.

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza anthu amene mwamuna kapena mkazi wawo anawasiya?

17 Anthu ena amavutika komanso kukhala ndi nkhawa chifukwa chakuti mwamuna kapena mkazi wawo wawasiya. Joyce, amene mwamuna wake anamusiya n’kutengana ndi mkazi wina, ananena kuti: “Ndikuganiza kuti zikundiwawa kwambiri kusiyana ndi mmene ndikanamvera akanakhala kuti wamwalira. Ndikutero chifukwa akanamwalira pa ngozi kapena chifukwa chodwala, zikanakhala kuti sanachite kufuna. Koma iye anasankha kundisiya. Zimenezi zinachititsa kuti ndizidziona ngati wachabechabe.”

18. Kodi tingathandize bwanji anthu amene asiyidwa kapena kuferedwa?

18 Tikamachita zinthu zing’onozing’ono zosonyeza kukoma mtima kwa anthu amene asiyidwa kapena kuferedwa timawatsimikizira kuti timawakonda. Zimenezi n’zofunika chifukwa pa nthawi yovutayi amafunikira anzawo abwino. (Miy. 17:17) Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu mnzawo wabwino? Mwina mukhoza kuwaitana kuti mudzadye nawo chakudya. Apo ayi, mungapite nawo kukacheza kwinakwake kapena kulowa nawo mu utumiki. Nthawi zina mukhoza kuwaitana kuti adzakhale nanu pa kulambira kwa pabanja. Mukamatero, Yehova adzasangalala kwambiri chifukwa iye amakhala “pafupi ndi anthu a mtima wosweka” ndipo amateteza akazi amasiye.​—Sal. 34:18; 68:5.

19. Malinga ndi 1 Petulo 3:8, kodi inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani?

19 Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira padzikoli, “masautso akale adzaiwalika.” Tikuyembekezera nthawi imene “zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.” (Yes. 65:16, 17) Pamene tikudikira nthawi imeneyi, tiyeni tipitirize kuthandizana ndipo zolankhula komanso zochita zathu zizisonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu.​—Werengani 1 Petulo 3:8.

NYIMBO NA. 111 Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

^ ndime 5 Loti, Yobu ndi Naomi ankatumikira Yehova mokhulupirika koma onsewa anakumana ndi mavuto amene ankawadetsa nkhawa. Munkhaniyi tikambirana zimene tingaphunzire kwa anthu amenewa. Tikambirananso chifukwa chake tiyenera kukhala oleza mtima, achifundo komanso olimbikitsa kwa abale ndi alongo amene akukumana ndi mavuto.

^ ndime 13 Mayina amunkhaniyi asinthidwa.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mkulu akumvetsera moleza mtima pamene m’bale akulankhula “zopanda pake” chifukwa chokwiya. Mtima wa m’baleyu utakhala m’malo, mkuluyo akumupatsa malangizo mokoma mtima.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Banja lachinyamata likucheza ndi m’bale amene waferedwa mkazi wake. Akukambirana zinthu zosangalatsa zokhudza mkazi wake amene wamwalirayo.