Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Lamulo la Kukoma Mtima Kosatha” Lizikutsogolerani

“Lamulo la Kukoma Mtima Kosatha” Lizikutsogolerani

LISA * anati: “Ndinakhudzidwa mtima kwambiri ndi kukoma mtima kwa abale ndi alongo.” Iye ankafotokoza za chinthu choyamba chomwe chinamuchititsa kuti ayambe choonadi. N’chimodzimodzinso ndi Anne yemwe ananena kuti: “Ndinakopeka ndi kukoma mtima komwe a Mboni ankandisonyeza osati zimene ankandiphunzitsa.” Alongo awiriwa amasangalala kuwerenga Baibulo komanso kuganizira mozama mfundo zake, koma anakhudzidwa kwambiri ndi khalidwe la kukoma mtima.

Kodi tingatani kuti tizisonyeza khalidwe la kukoma mtima lomwe limakhudza kwambiri anthu omwe timachita nawo zinthu? Tikambirana njira ziwiri izi: mmene timalankhulira komanso zochita zathu. Kenako tikambirana anthu omwe tiyenera kuwasonyeza kukoma mtima.

“LAMULO LA KUKOMA MTIMA KOSATHA” LIZIKHALA PA LILIME LANU

Zimene mkazi wabwino wotchulidwa pa Miyambo 31 amalankhula zimasonyeza kuti amatsatira “lamulo la kukoma mtima kosatha.” (Miy. 31:26) ‘Lamuloli’ limamuthandiza kudziwa zoyenera kulankhula komanso mmene angazilankhulire. Nawonso abambo zolankhula zawo ziyenera kusonyeza kuti amatsatira “lamulo” limeneli. Makolo ambiri amadziwa kuti mawu opweteka omwe angalankhule angakhudze kwambiri ana awo. Ngati makolo amalankhula mwaukali, zingachititse kuti ana awo asamawamvere. Koma ngati angamalankhule nawo mokoma mtima, zingakhale zosavuta kuti anawo aziwamvera.

Kaya ndinu makolo kapena ayi, kodi mungatani kuti muzilankhula mokoma mtima? Mfundo yothandiza tingaipeze m’mbali yoyamba ya pa Miyambo 31:26, pomwe pamati: “Amatsegula pakamwa pake mwanzeru.” Zimenezi zikuphatikizapo kusankha bwino mawu komanso kuwalankhula m’njira yoyenera. Tingachite bwino kumadzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndilankhule zichititsa kuti ena akwiye, kapena zichititsa kuti pakhale mtendere?’ (Miy. 15:1) Choncho ndi nzeru kumaganizira kaye tisanalankhule.

Mwambi wina umati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga.” (Miy. 12:18) Tikamaganizira kuti mawu athu komanso mmene tingawalankhulire zingakhudze ena, tidzayesetsa kulamulira lilime lathu. Choncho kutsatira “lamulo la kukoma mtima kosatha,” kungatithandize kuti tisamalankhule mawu opweteka ndiponso mwaukali. (Aef. 4:31, 32) M’malo moganizira zoipa komanso kulankhula molakwika, tidzayamba kulankhula mawu abwino komanso m’njira yoyenera. Yehova anatipatsa chitsanzo chabwino pankhaniyi pamene ankalimbikitsa mtumiki wake Eliya, yemwe anali ndi mantha. Mngelo yemwe ankaimira Yehova, ankamulankhula ndi “mawu achifatse apansipansi.” (1 Maf. 19:12) Komabe, kukhala wokoma mtima kumaphatikizapo zambiri osati kungolankhula. Timayeneranso kuchita zinthu mokoma mtima. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

KUCHITA ZINTHU MOKOMA MTIMA KUMALIMBIKITSA ENA

Tikamatsanzira Yehova, timalankhula komanso kuchita zinthu mokoma mtima. (Aef. 4:32; 5:1, 2) Lisa, yemwe tamutchula kale uja, anafotokoza mmene a Mboni anathandizira banja lake mokoma mtima. Iye anati: “Banja lathu litauzidwa mwadzidzidzi kuti lisamuke, mabanja ena awiri a mumpingo womwe tinkasonkhana, sanapite kuntchito kwawo n’cholinga choti adzatithandize kulongedza katundu. Komatu panthawiyo ndinali ndisanayambe n’komwe kuphunzira Baibulo.” Kukoma mtima komwe Lisa anasonyezedwa, kunamuchititsa kuti ayambe kufuna kudziwa zambiri zokhudza choonadi.

Anne, yemwe tamutchula kumayambiriro uja, anayamikiranso kukoma mtima komwe a Mboni anamusonyeza. Iye anati: “Chifukwa cha mmene anthu amachitira zinthu ndi ena m’dzikoli, sindinkakhulupirira aliyense.” Anawonjezera kuti: “Nditakumana ndi a Mboni za Yehova, ndinkawakayikira. Ndinkadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani amachita nane chidwi?’ Koma chifukwa choti amene ankandiphunzitsa Baibulo ankandisonyeza chikondi chenicheni, ndinayamba kumukhulupirira.” Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Iye anati: “Ndinayamba kuchita chidwi kwambiri ndi zimene ankandiphunzitsa.”

Kukoma mtima kumene abale ndi alongo osiyanasiyana anasonyeza, kunakhudza kwambiri Lisa ndi Anne, zomwe zinachititsa kuti ayambe kuphunzira choonadi. Kukoma mtima kumeneku kunawachititsa kuti ayambe kukhulupirira Yehova komanso anthu ake.

MUZITSANZIRA MULUNGU POSONYEZA ENA KUKOMA MTIMA

Anthu ena savutika kulankhula mokoma mtima komanso kumwetulira chifukwa cha chikhalidwe chawo. Ndi zabwino kuti ena amasonyeza zimenezi chifukwa cha chibadwa kapena chikhalidwe chawo. Koma ngati timangochita zinthu mokoma mtima chifukwa cha zimenezi, sizitanthauza kuti tikutsanzira Mulungu.​—Yerekezerani ndi Machitidwe 28:2.

Kukoma mtima komwe timakusonyeza potsanzira Mulungu ndi khalidwe lomwe mzimu woyera wa Mulungu umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Choncho kuti tikhale ndi khalidwe la kukoma mtima, tiyenera kulola kuti mzimu wa Mulungu uzititsogolera pa nkhani ya mmene timaganizira komanso mmene timachitira zinthu. Tikamachita zimenezi, tidzatha kutsanzira Yehova ndi Yesu. Ndipotu monga Akhristu, timasonyeza ena chidwi chenicheni. Choncho kukonda Yehova Mulungu komanso anthu anzathu kumatilimbikitsa kuchita zimenezi. Tikatero timayamba kusonyeza kwambiri khalidweli komanso mochokera pansi pa mtima zomwe zimasangalatsa Mulungu.

KODI NDI NDANI AMENE TIYENERA KUWAKOMERA MTIMA?

N’zosavuta kusonyeza kukoma mtima kwa anthu omwenso anatisonyeza kukoma mtima kapenanso amene timawadziwa. (2 Sam. 2:6) Njira imodzi yomwe tingachitire zimenezi ndi kuwathokoza. (Akol. 3:15) Koma bwanji ngati tikuona kuti munthu wina siwoyenera kumukomera mtima.

Taganizirani izi: Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza kukoma mtima kwakukulu, ndipo Mawu ake amatiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri pa nkhani yosonyeza khalidweli. Mawu akuti “kukoma mtima kwakukulu” amapezeka m’malo angapo m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu. Ndiye kodi Mulungu amatisonyeza bwanji kukoma mtima?

Taganizirani za anthu mamiliyoni omwe Yehova wakhala akuwasonyeza kukoma mtima powapatsa zinthu zomwe amafunikira kuti akhale ndi moyo. (Mat. 5:45) Ndipotu Yehova anayamba kuwasonyeza anthu chifundo asanamudziwe n’komwe. (Aef. 2:4, 5, 8) Mwachitsanzo, anapereka mphatso yabwino kwambiri kwa anthu onse, yomwe ndi Mwana wake wobadwa yekha. Mtumwi Paulo analemba kuti Yehova anapereka dipo “malinga ndi chuma cha kukoma mtima kwake kwakukulu.” (Aef. 1:7) Kuwonjezera pamenepo, ngakhale kuti timamuchimwira komanso kumukhumudwitsa, amapitiriza kutitsogolera komanso kutiphunzitsa. Ndipo malangizo komanso mawu ake ali ngati “mvula yowaza” yomwe imatsitsimula. (Deut. 32:2) Kunena zoona, sitingathe kumubwezera pa zabwino zonse zomwe amatichitira chifukwa cha kukoma mtima kwake. Ndipotu sitikanakhala ndi chiyembekezo cha m’tsogolo zikanakhala kuti Yehova sanatisonyeze kukoma mtima.​—Yerekezerani ndi 1 Petulo 1:13.

N’zosakayikitsa kuti timakopeka komanso kulimbikitsidwa ndi kukoma mtima kwa Yehova. Choncho m’malo mosonyeza kukoma mtima kwa anthu owerengeka okha, tiyenera kuyesetsa kutsanzira Yehova posonyeza khalidweli kwa anthu onse tsiku lililonse. (1 Ates. 5:15) Tikamayesetsa kusonyeza kukoma mtima mosalekeza, timakhala ngati moto womwe ukutenthera patsiku lomwe kukuzizira. Tikamachita zimenezi, timalimbikitsa anthu a m’banja lathu, Akhristu anzathu, anzathu a kuntchito, kusukulu komanso oyandikana nawo nyumba.

Taganizirani anthu a m’banja lanu kapena a mumpingo omwe angasangalale mutawalankhula kapena kuwachitira zinthu mokoma mtima. Mwina pangakhale munthu wina mumpingo mwanu yemwe angafunike kumuthandiza kusamalira nyumba, munda kapena kumakamugulira zinthu kumsika. Kuwonjezera pamenepo, kodi n’zotheka kuthandiza munthu winawake yemwe mwakumana naye mu utumiki, amene akufunika kuthandizidwa mwanjira inayake?

Potsanzira Yehova, tiyeni nthawi zonse tiziyesetsa kuti tizitsogoleredwa ndi “lamulo la kukoma mtima kosatha.”

^ Mayina asinthidwa.