Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 24

Yehova Amakhululuka Kwambiri Kuposa Aliyense

Yehova Amakhululuka Kwambiri Kuposa Aliyense

“Inu Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka. Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.”​—SAL. 86:5.

NYIMBO NA. 42 Pemphero la Munthu wa Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Mogwirizana ndi Mlaliki 7:20, kodi ndi mfundo ya choonadi iti yomwe Mfumu Solomo inafotokoza?

 MFUMU Solomo inalemba kuti: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.” (Mlal. 7:20) Zimenezitu ndi zoona chifukwa tonsefe ndi ochimwa. (1 Yoh. 1:8) Choncho timafuna kuti Mulungu komanso anzathu azitikhululukira.

2. Kodi timamva bwanji mnzathu wapamtima akatikhululukira?

2 Mwina mukukumbukira nthawi ina pamene munalakwira mnzanu wapamtima. Munkafuna kukonza zomwe munalakwitsazo komanso kuti muyambirenso kugwirizana. Choncho munapepesa mochokera pansi pa mtima. Kodi munamva bwanji mnzanuyo atakukhululukirani ndi mtima wonse? Muyenera kuti munamva bwino ndipo munasangalala kwambiri.

3. Kodi munkhaniyi tikambirana chiyani?

3 Timafuna kuti Yehova akhale mnzathu wapamtima, komabe nthawi zina tingalankhule kapena kuchita zinthu zomwe zingamukhumudwitse. Ndiye kodi tingatsimikizire bwanji kuti iye ndi wofunitsitsa kutikhululukira? Kodi pali kusiyana kotani pakati pa Yehova ndi anthufe pa nkhani yokhululuka? Ndipo kodi ndi anthu ati omwe Yehova angawakhululukire?

YEHOVA NDI WOKONZEKA KUKHULULUKA

4. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova ndi wokonzeka kukhululuka?

4 Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti iye ndi wokonzeka kukhululuka. Pamene iye ankadzifotokoza kwa Mose kudzera mwa mngelo paphiri la Sinai, ananena kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi. Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukira zolakwa ndi machimo.” (Eks. 34:6, 7) Yehova ndi Mulungu wokoma mtima komanso wachifundo, yemwe nthawi zonse amakhala wokonzeka kukhululukira ochimwa omwe alapa.​—Neh. 9:17; Sal. 86:15.

Yehova amadziwa zonse zomwe zakhala zikutiumba (Onani ndime 5)

5. Mogwirizana ndi Salimo 103:13, 14, kodi Yehova amachita chiyani chifukwa chowadziwa bwino anthu?

5 Monga Mlengi wathu, Yehova amadziwa chilichonse chokhudza anthufe. Ndiye tangoganizani, amadziwa chilichonse chokhudza munthu aliyense padzikoli. (Sal. 139:15-17) Choncho angathe kuona uchimo wonse womwe tinatengera kwa makolo athu. Kuwonjezera pamenepa, iye amadziwa zinthu zomwe zakhala zikutichitikira, zimene zimaumba umunthu wathu. Ndiye popeza kuti Yehova amadziwa kwambiri anthu, kodi zimenezi zimamuchititsa kutani? Zimamuchititsa kuti azitichitira chifundo.​—Sal. 78:39; werengani Salimo 103:13, 14.

6. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi wofunitsitsa kutikhululukira?

6 Yehova anasonyeza kuti ndi wofunitsitsa kutikhululukira. Iye amamvetsa kuti chifukwa cha zochita za munthu woyambirira Adamu, tonsefe ndi ochimwa ndipo timafa. (Aroma 5:12) Palibe chomwe tikanachita kuti tidzipulumutse kapena kupulumutsa ena ku temberero limeneli. (Sal. 49:7-9) Komabe Mulungu wathu wachikondi anatisonyeza chifundo ndipo anakonza zoti tipulumutsidwe. Kodi iye anachita bwanji zimenezi? Monga mmene lemba la Yohane 3:16 limanenera, Yehova anatumiza Mwana wake wobadwa yekha kuti adzatifere. (Mat. 20:28; Aroma 5:19) Yesu anazunzika komanso kuphedwa n’cholinga choti aliyense wokhulupirira mwa iye apulumutsidwe. (Aheb. 2:9) Ziyenera kuti zinamuwawa kwambiri Yehova kuona Mwana wake akufa imfa yopweteka komanso yochititsa manyazi. Apa n’zoonekeratu kuti Yehova sakanalola kuti Mwana wake afe zikanakhala kuti sakufuna kutikhululukira.

7. Kodi ndi zitsanzo zina ziti za anthu otchulidwa m’Baibulo omwe Yehova anawakhululukira ndi mtima wonse?

7 M’Baibulo muli zitsanzo za anthu ambiri omwe Yehova anawakhululukira ndi mtima wonse. (Aef. 4:32) Kodi inuyo mukukumbukirako ndani? Mwina mukuganizira za Mfumu Manase. Munthu ameneyu anachita machimo akuluakulu komanso oipa kwambiri. Ankatsogolera anthu pa kulambira konyenga. Anapha ana ake powapereka nsembe kwa milungu yonyenga. Anafika mpaka popanga fano n’kukaliimika m’kachisi woyera wa Yehova. Ponena za Manase, Baibulo limati: “Iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.” (2 Mbiri 33:2-7) Komabe iye atalapa mochokera pansi pa mtima, Yehova anamukhululukira. Ndipotu mpaka anafika pomubwezeretsanso pa ufumu. (2 Mbiri 33:12, 13) N’kutheka kuti mukuganiziranso za Mfumu Davide, yemwe anachita machimo akuluakulu kuphatikizapo chigololo komanso kupha munthu. Komabe iye atalapa mochokera pansi pa mtima n’kuvomereza machimo ake, Yehova anamukhululukiranso. (2 Sam. 12:9, 10, 13, 14) Choncho tingakhale otsimikiza kuti Yehova ndi wofunitsitsa kukhululukira anthu omwe alapa. Ndipo monga mmene tionere, Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi anthufe pa nkhani yokhululuka.

ZIMENE ZIMASIYANITSA YEHOVA NDI ENA PA NKHANI YOKHULULUKA

8. Kodi kukhala Woweruza wabwino kwambiri kumakhudza bwanji mmene Yehova amachitira pa nkhani yokhululuka?

8 Yehova ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi.” (Gen. 18:25) Woweruza wabwino amafunika kudziwa bwino malamulo. Umu ndi mmene Yehova alili, chifukwa kuwonjezera pa kukhala Woweruza wathu, iye ndi Wotipatsa malamulo. (Yes. 33:22) Ndi Yehova yekha amene amamvetsa bwino pa nkhani ya chabwino ndi choipa. Kodi woweruza wabwino amafunikiranso kukhala wotani? Amafunika azimvetsa bwino mfundo zonse za nkhani asanaweruze. Choncho Yehova ndi Woweruza wabwino chifukwa amadziwa chilichonse.

9. Kodi ndi zinthu ziti zomwe Yehova amakhala kuti akudziwa akamafuna kukhululukira munthu?

9 Mosiyana ndi anthu oweruza, nthawi zonse Yehova amadziwa bwino mfundo za nkhani yomwe akufunika kuweruza. (Gen. 18:20, 21; Sal. 90:8) Iye amadziwa zoposa zimene anthu angaone kapena kumva. Amamvetsa bwino mmene munthu wachitira zinthu chifukwa cha chibadwa chake, mmene analeredwera, kumene amakhala, mmene amamvera komanso mmene amaganizira. Yehova amadziwanso zimene zili mumtima. Iye amamvetsa bwino zolinga, zolakalaka komanso zimene zimachititsa munthu aliyense kuchita zinazake. Palibe chomwe Yehova sachiona. (Aheb. 4:13) Choncho Yehova akamakhululuka, amakhala kuti akudziwa chilichonse chokhudza nkhaniyo.

Yehova ndi wachilungamo ndipo sakondera. Iye sangapatsidwe ziphuphu (Onani ndime 10)

10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti nthawi zonse Yehova amaweruza mwachilungamo? (Deuteronomo 32:4)

10 Nthawi zonse Yehova amaweruza mwachilungamo ndipo sakondera ngakhale pang’ono. Kuti akhululukire munthu sizitengera mmene munthuyo akuonekera, chuma, kutchuka kapena luso lake. (1 Sam. 16:7; Yak. 2:1-4) Palibe yemwe angamukakamize kuti achite zinazake kapena kumupatsa chiphuphu. (2 Mbiri 19:7) Iye sasankha zinthu chifukwa cha mkwiyo kapena mmene akumvera. (Eks. 34:7) N’zosakayikitsa kuti kuzindikira komanso kumvetsa bwino zinthu kumachititsa Yehova kukhala Woweruza wabwino kwambiri.​—Werengani Deuteronomo 32:4.

11. Kodi Yehova ndi wosiyana bwanji ndi anthu pa nkhani yokhululuka?

11 Anthu omwe ankalemba Malemba a Chiheberi ankazindikira kuti Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi ena pa nkhani yokhululuka. Nthawi zina iwo ankagwiritsa ntchito mawu a Chiheberi omwe buku lina linafotokoza kuti “amanena makamaka zimene Mulungu amachita pokhululukira wochimwa, ndipo sanena za mlingo wakukhululuka umene munthu amachitira munthu mnzake, womwe ndi wochepa.” Yehova yekha ndi amene angathe kukhululukira kotheratu munthu yemwe walapa. Ndiye kodi chimachitika n’chiyani Yehova akatikhululukira?

12-13. (a) Kodi munthu amasangalala ndi zinthu ziti Yehova akamukhululukira? (b) Kodi munthu amasangalala kwa nthawi yaitali bwanji ndi madalitso obwera chifukwa choti Yehova wamukhululukira?

12 Tikavomereza kuti Yehova watikhululukira timasangalala ndi “nyengo zotsitsimutsa,” zomwe zikuphatikizapo kukhala ndi mtendere wa m’maganizo komanso chikumbumtima choyera. Yehova yekha ndi amene angatikhululukire choncho osati anthu. (Mac. 3:19) Iye akatikhululukira, timakhala nayenso pa ubwenzi wabwino ngati kuti sitinachimwe n’komwe.

13 Yehova akatikhululukira satiimbanso mlandu kapena kutilanga chifukwa cha tchimo lomwe tinachitalo. (Yes. 43:25; Yer. 31:34) Iye amaika machimo athu kutali, “monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo.” * (Sal. 103:12) Tikaganizira zimene Yehova amachita potikhululukira timasowa chonena ndipo timamuyamikira kwambiri. (Sal. 130:4) Koma kodi Yehova amakhululukira anthu otani?

KODI YEHOVA AMAKHULULUKIRA ANTHU OTANI?

14. Kodi taphunzira chiyani pa nkhani ya zimene Yehova amachita akafuna kusankha kukhululuka?

14 Monga mmene taonera, sikuti Yehova amasankha kutikhululukira potengera kukula kwa tchimo lomwe tachita. Taphunziranso kuti akafuna kusankha kuti akhululuke, Yehova amagwiritsa ntchito zomwe amadziwa monga Mlengi wathu, Wotipatsa malamulo komanso Woweruza wathu. Ndiye kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova amaganizira?

15. Mogwirizana ndi Luka 12:47, 48, kodi ndi chinthu china chiti chomwe Yehova amaganizira akafuna kukhululuka?

15 Yehova amaganizira ngati munthu yemwe wachita tchimoyo amadziwa kuti zomwe akuchitazo ndi zolakwika. Yesu anafotokoza momveka bwino mfundo imeneyi pa Luka 12:47, 48. (Werengani.) Munthu yemwe amachita kukonzekera kuti achite zinthu zoipa koma akudziwa bwino kuti zomwe akufuna kuchitazo Yehova amadana nazo, amakhala kuti akuchita tchimo lalikulu. Munthu wotereyu amakhala pa chiopsezo choti sangakhululukidwe. (Maliko 3:29; Yoh. 9:41) Komabe tivomereze kuti nthawi zina timakhala kuti tikudziwa kuti zomwe tinachita ndi zolakwika. Ndiye zikatere, kodi pakhoza kukhala chiyembekezo choti tingakhululukidwe? Inde. Zimenezi zikutifikitsa pa chinthu chinanso chomwe Yehova amaganizira.

Tisamakayikire kuti Yehova angatikhululukire ngati talapa mochokera pansi pa mtima (Onani ndime 16-17)

16. Kodi kulapa n’kutani, nanga n’kofunika bwanji kuti Yehova atikhululukire?

16 Chinthu china chomwe Yehova amaganizira ndi kuona ngati munthu wochimwayo walapa mochokera pansi pa mtima. Kodi kulapa n’kutani? Kumatanthauza “kusintha maganizo, mmene timaonera zinthu komanso zolinga zathu.” Kumaphatikizapo kudzimvera chisoni kwambiri chifukwa cha zinthu zoipa zomwe tachita kapena chifukwa chosachita zinthu zoyenera. Sikuti munthu wolapa amangomva chisoni chifukwa cha zoipa zomwe wachita koma chifukwa cholepheranso kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova zomwe zachititsa kuti achite tchimolo. Kumbukirani kuti Mfumu Manase ndi Mfumu Davide anachitanso machimo akuluakulu, komabe Yehova anawakhululukira chifukwa chakuti analapa mochokera pansi pa mtima. (1 Maf. 14:8) Choncho kuti Yehova atikhululukire, ayenera kuona umboni wosonyeza kuti talapa. Koma sizokwanira kungodzimvera chisoni pa machimo athu, tiyenera kukhala okonzeka kuchitapo kanthu. * Izi zikutifikitsanso pa chinthu china chimene Yehova amaganizira.

17. Kodi kutembenuka n’kutani, nanga kungatithandize bwanji kuti tisabwerezenso machimo? (Yesaya 55:7)

17 Chinthu china chofunika kwambiri chomwe Yehova amachiganizira kwambiri ndi “kutembenuka.” M’mawu ena, munthu ayenera kusiya zoipa zomwe amachita, n’kuyamba kuchita zimene Yehova amafuna. (Werengani Yesaya 55:7.) Munthuyo ayenera kusintha mmene amaganizira n’cholinga choti azitsogoleredwa ndi maganizo a Yehova. (Aroma 12:2; Aef. 4:23) Ayenera kukhala wotsimikiza mtima kuti asiye zinthu zoipa zomwe ankaziganizira komanso kuchita. (Akol. 3:7-10) Komanso tiyenera kukhulupirira nsembe ya Khristu kuti Yehova atikhululukire ndiponso kutiyeretsa ku machimo athu. Yehova angatikhululukire pogwiritsa ntchito nsembeyi ngati waona kuti tikuyesetsa kusintha moyo wathu.​—1 Yoh. 1:7.

MUSAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA ANGAKUKHULULUKIRENI

18. Kodi taphunzira chiyani zokhudza Yehova pa nkhani yokhululuka?

18 Tiyeni tikambirane mwachidule mfundo zina zikuluzikulu zimene taphunzira. Yehova ndi amene amakhululuka kwambiri m’chilengedwe chonse. N’chifukwa chiyani tikutero? Choyamba, nthawi zonse iye amakhala wokonzeka kukhululuka. Chachiwiri, amatidziwa bwino kwambiri. Amadziwa chilichonse chokhudza ife ndipo ndi amene angadziwe bwino ngati talapadi. Ndipo chachitatu, amatikhululukira kotheratu moti zimangokhala ngati kuti sitinachimwe n’komwe. Zimenezi zimatithandiza kuti tikhale ndi chikumbumtima choyera komanso kukhala naye pa ubwenzi wabwino.

19. Ngakhale kuti si ife angwiro ndipo tipitirizabe kulakwitsa zinthu, n’chifukwa chiyani tingakhale osangalala?

19 N’zoona kuti panopa tizipitirizabe kuchimwa popeza kuti si ife angwiro. Komabe tingalimbikitsidwe ndi mawu opezeka m’buku la Chingelezi la Insight, Voliyumu 2, tsamba 771, omwe amati: “Popeza mwachifundo Yehova amaganizira zofooka za atumiki ake, iwo sayenera kumangokhalira kudziimba mlandu chifukwa cha zimene amalakwitsa popeza si angwiro. (Sal. 103:8-14; 130:3) Ngati nthawi zonse amayesetsa kuchita zomwe Mulungu amafuna, angakhale osangalala. (Afil. 4:4-6; 1 Yoh. 3:19-22).” Zimenezitu n’zolimbikitsa.

20. Kodi tikambirana chiyani munkhani yotsatira?

20 Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa choti ndi wokonzeka kutikhululukira tikamadzimvera chisoni pa machimo omwe tachita. Ndiye kodi tingamutsanzire bwanji pa nkhani yokhululuka? Kodi timafanana ndi Yehova m’njira ziti pa nkhani yokhululuka, nanga timasiyana bwanji? Kodi kumvetsa kusiyana kumeneko n’kofunika bwanji? Nkhani yotsatira iyankha mafunso amenewa.

NYIMBO NA. 45 Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga

^ M’Mawu ake, Yehova amatitsimikizira kuti ndi wofunitsitsa kukhululukira anthu ochimwa omwe alapa. Koma nthawi zina tingamaone kuti si ife oyenera kuti atikhululukire. Munkhaniyi tiona chifukwa chake tingakhale otsimikiza kuti Mulungu wathu ndi wokonzeka kutikhululukira tikamadzimvera chisoni chifukwa cha machimo omwe tinachita.

^ TANTHAUZO LA MAWU ENA: “Kulapa” kumatanthauza kusintha maganizo komanso kudzimvera chisoni chifukwa cha zoipa zimene takhala tikuchita kapena chifukwa cholephera kuchita zoyenera. Kulapa kwenikweni kumakhala ndi zipatso zake, zomwe ndi kusintha mmene timachitira zinthu pa moyo wathu.