Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Aroma ankalola kuti munthu amene waphedwa popachikidwa pamtengo, ngati mmene zinalili ndi Yesu, aikidwe m’manda ngati anthu ena onse?

ANTHU ambiri amadziwa nkhani yonena kuti Yesu anapachikidwa pamtengo limodzi ndi zigawenga ziwiri. (Mat. 27:35-38) Komabe anthu ena amakayikira zimene Baibulo limanena zoti pambuyo pake thupi la Yesu linakonzedwa n’kuikidwa m’manda.​—Maliko 15:42-46.

Anthu ena omwe amatsutsa mabuku a Uthenga Wabwino, amakayikira ngati munthu yemwe anaphedwa popachikidwa pamtengo akanaikidwa m’manda molemekezeka, monga kuikidwa m’phanga. M’malomwake, otsutsawo amanena kuti anthu otere sankaikidwa m’manda molemekezeka. Mtolankhani wa magazini ina yotchedwa Smithsonian dzina lake Ariel Sabar, anafotokoza chifukwa chake anthu otsutsawa amaganiza choncho. Iye anati: “Kupachikidwa pamtengo chinali chilango chomwe chinkaperekedwa kwa anthu omwe ankaonedwa kuti ndi oipa kwambiri, choncho akatswiri ena amaona kuti Aroma sakanavomereza kuti munthu amene wafa imfa yotere aikidwe m’manda molemekezeka.” Aroma ankafuna kuti zigawenga zomwe zagamulidwa kuti ziphedwe zichititsidwe manyazi kwambiri, choncho nthawi zambiri mitembo yawo sinkachotsedwa pamtengo n’cholinga choti idyedwe ndi zinyama. N’kutheka kuti kenako mafupa otsalawo ankangowakwirira m’dzenje limodzi ndi mafupa a anthu ena.

Komabe, ofukula za m’mabwinja apeza zinthu zina, makamaka zokhudza mitembo ya Ayuda ena omwe anachita kuphedwa. Mu 1968, panapezeka mafupa a munthu amene anaphedwa popachikidwa pamtengo cha m’nthawi ya Yesu. Mafupawa anapezeka mu phanga lomwe linali manda a banja lina la Chiyuda pafupi ndi Yerusalemu, ali m’bokosi losungiramo mafupa. Pa mafupawo panalinso fupa la chidendene lomwe analikhomerera kuthabwa ndi msomali wautali masentimita 11.5. Sabar ananena kuti: “Fupalo, lomwe linali la munthu wina dzina lake Yehochanan, linathandiza kuthetsa kusamvana pa nkhani yokhudza kuikidwa m’manda kwa Yesu kofotokozedwa m’mabuku a Uthenga Wabwino.” N’zoonekeratu kuti “Yehochanan ndi chitsanzo chosonyeza kuti mu nthawi ya Yesu, Aroma ankalola kuti munthu amene wapachikidwa aikidwe m’manda mogwirizana ndi mwambo wa Chiyuda.”

N’kutheka kuti pangakhale kusiyana maganizo pa nkhani ya mmene Yesu anapachikidwira potengera zimene apeza pa fupa la Yehochanan. Koma mfundo yosatsutsika ndi yakuti zigawenga zina zomwe zinaphedwa popachikidwa pamtengo, zinaikidwa m’manda molemekezeka osati chabe kungoikidwa m’dzenje limodzi ndi mitembo ya anthu ena. Apa n’zoonekeratu kuti zimene Baibulo limanena zoti thupi la Yesu linaikidwa m’manda molemekezeka, n’zolondola. Umboni umene wapezeka ukutsimikizira zimenezi.

Chofunika kwambiri n’chakuti Yehova anali ataneneratu kuti Yesu adzaikidwa m’manda a munthu wolemera, ndipo palibe amene angachititse kuti mawu a Mulungu asakwaniritsidwe.​—Yes. 53:9; 55:11.