NKHANI YOPHUNZIRA 28
Kuopa Mulungu Kungatithandize Kuti Tipitirize Kulandira Madalitso
“Munthu woyenda mowongoka mtima amaopa Yehova.”—MIY. 14:2.
NYIMBO NA. 122 Khalani Olimba Komanso Osasunthika
ZIMENE TIPHUNZIRE a
1-2. Mofanana ndi Loti, kodi Akhristu masiku ano amakumana ndi vuto liti?
MAKHALIDWE oipa omwe dzikoli limalimbikitsa angatichititse kumva ngati mmene anamvera Loti, yemwe anali wolungama. Iye “anavutika mtima kwambiri ndi kulowerera kwa anthu ophwanya malamulo mu khalidwe lawo lotayirira” podziwa kuti Atate wathu wakumwamba amadana ndi makhalidwe oipawa. (2 Pet. 2:7, 8) Kuopa komanso kukonda Mulungu kunachititsa Loti kuti azipewa makhalidwe oipa omwe anthu omuzungulira ankachita. Ifenso tazunguliridwa ndi anthu amene salemekeza mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Ngakhale zili choncho, tingakhalebe ndi makhalidwe abwino ngati titapitiriza kukonda Mulungu komanso kumulemekeza kwambiri.—Miy. 14:2.
2 Pofuna kutithandiza kuchita zimenezi, Yehova amatilimbikitsa mwachikondi pogwiritsa ntchito buku la Miyambo. Akhristu onse, amuna, akazi, ana komanso achikulire angapindule kwambiri potsatira malangizo anzeru opezeka m’bukuli.
KUOPA MULUNGU KUMATITETEZA
3. Mogwirizana ndi Miyambo 17:3, kodi ndi chifukwa chimodzi chiti chomwe chingatichititse kuteteza mtima wathu? (Onaninso chithunzi.)
3 Chifukwa chachikulu chotichititsa kuti tiziteteza mtima wathu ndi chakuti Yehova amafufuza mtima. Zimenezi zikutanthauza kuti iye samangoona mmene timaonekera kwa anthu ena, koma amaonanso zimene zili mumtima mwathu. (Werengani Miyambo 17:3.) Iye adzapitiriza kutikonda ngati timaganizira nzeru zake, zomwe zingatithandize kuti tikhale ndi moyo mpaka kalekale. (Yoh. 4:14) Tikatero, sitidzasokonezedwa ngakhale pang’ono ndi makhalidwe omwe Satana ndi dziko loipali amalimbikitsa. (1 Yoh. 5:18, 19) Pamene tikuyesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, tidzayamba kumukonda komanso kumulemekeza kwambiri. Chifukwa choti sitifuna kukhumudwitsa Atate wathu, tidzadana ngakhale ndi maganizo oti tichite zoipa. Tikamayesedwa kuti tichite zoipa tidzadzifunsa kuti: ‘Ndingakhumudwitse bwanji mwadala Yehova, yemwe amandikonda kwambiri?’—1 Yoh. 4:9, 10.
4. Kodi kuopa Yehova kunathandiza bwanji mlongo wina kuti asagonje pa mayesero?
4 Mlongo wina wa ku Croatia dzina lake Marta, yemwe anayesedwa kuti achite makhalidwe oipa, analemba kuti: “Ndinaona kuti zinkandivuta kukhala ndi maganizo oyenera komanso kulimbana ndi mtima wolakalaka kuchita zoipa, zomwe ndikanangosangalala nazo kwa nthawi yochepa. Koma kuopa Yehova kunanditeteza.” b Kodi kuopa Mulungu kunathandiza bwanji Marta? Iye anaganizira zomwe zikanachitika ngati akanasankha zinthu molakwika. Ifenso tingachite chimodzimodzi. Choopsa kwambiri n’chakuti ngati tingakhumudwitse Yehova, tingataye mwayi wodzamulambira mpaka kalekale.—Gen. 6:5, 6.
5. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Leo?
5 Tikamaopa Yehova, timakhala osamala kuti tisamagwirizane ndi anthu amene amachita makhalidwe oipa. Zimenezi ndi zomwe Leo yemwe amakhala ku Congo anaphunzira. Patapita zaka 4 kuchokera pamene anabatizidwa anayamba kugwirizana ndi anthu oipa. Iye ankaganiza kuti ngati sakuchita nawo zoipa zomwe anzakewo ankachita ndiye kuti sakuchimwira Yehova. Posakhalitsa, anthu oipa omwe ankagwirizana nawowo anamuchititsa kuti ayambe kuledzera komanso kuchita zachiwerewere. Koma kenako anayamba kuganizira zimene makolo ake anamuphunzitsa komanso kuti pa nthawiyi sankasangalala. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Nzeru zinayamba kumubwerera. Atathandizidwa ndi akulu, anabwerera kwa Yehova. Panopa iye ndi mkulu komanso mpainiya wapadera ndipo akusangalala.
6. Kodi tsopano tikambirana za akazi awiri ati ophiphiritsa?
6 Tiyeni tikambirane Miyambo chaputala 9, pomwe timawerenga za nzeru ndi kupusa, makhalidwe omwe mophiphiritsa awayerekezera ndi akazi awiri. (Yerekezerani ndi Aroma 5:14; Agalatiya 4:24.) Pamene tikuchita zimenezo, muzikumbukira kuti dziko lolamuliridwa ndi Satanali ndi lodzadza ndi zachiwerewere komanso zolaula. (Aef. 4:19) Choncho n’zofunika kuti tipitirizebe kuopa Mulungu komanso kumapewa zoipa. (Miy. 16:6) Tonsefe, kaya amuna kapena akazi, tingapindule ndi zimene timawerenga m’chaputalachi. Mkazi aliyense akufotokozedwa ngati kuti akuitana munthu “wosadziwa zinthu,” kapena kuti wopanda nzeru. Zili ngati aliyense akuitana kuti, ‘Bwera kunyumba kwanga udzadye chakudya.’ (Miy. 9:1, 5, 6, 13, 16, 17) Koma pali kusiyana kwakukulu pa zimene zikuchitikira aliyense woitanidwa ndi akaziwa.
MUSAMATSATIRE MKAZI WOPUSA
7. Mogwirizana ndi Miyambo 9:13-18, kodi n’chiyani chomwe chimachitikira munthu wovomera kuitana kwa mkazi wopusa? (Onaninso chithunzi.)
7 Taganizirani zimene timawerenga zokhudza “mkazi wopusa.” (Werengani Miyambo 9:13-18.) Mopanda manyazi, iye amaitanira wopanda nzeru kuti akadye kunyumba yake ponena kuti, ‘patukira kuno’. Kodi zotsatira zake zimakhala zotani? Baibulo limati “kumeneko kuli akufa.” Mwina mwakumbukira mawu ena ophiphiritsa ofanana ndi amenewa omwe ali m’machaputala oyambirira a buku la Miyambo. Timachenjezedwa za “mkazi wachilendo” ndiponso “wochokera kwina,” kapena kuti wachiwerewere. Ponena za iye, timauzidwa kuti: “Nyumba yake imatsikira kumanda.” (Miy. 2:11-19) Pa Miyambo 5:3-10, timachenjezedwa za “mkazi wachilendo” winanso yemwe “mapazi ake amatsikira ku imfa.”
8. Kodi timafunika kusankha pa nkhani iti?
8 Amene amamva kuitana kwa “mkazi wopusa” amafunika kusankha, kaya kuvomera kupita kapena kukana. Ifenso nthawi zina tingafunike kusankha pa nkhani yofanana ndi imeneyi. Ngati tayesedwa kuti tichite chiwerewere kapena tionere zolaula, kaya pa TV kapena pa intaneti, kodi tidzasankha kuchita chiyani?
9-10. Kodi ndi zifukwa zina ziti zotichititsa kupewa khalidwe lachiwerewere?
9 Pali zifukwa zomveka zotichititsa kupewa zachiwerewere. “Mkazi wopusa” akufotokozedwa ngati akunena kuti: “Madzi akuba amatsekemera.” Kodi “madzi akuba” akutchulidwawa ndi chiyani? Baibulo limayerekezera kugonana pakati pa anthu okwatirana ndi madzi otsitsimula. (Miy. 5:15-18) Mwamuna ndi mkazi okwatirana mwalamulo ndi amene amaloledwa kuti azigonana. Ndiye kodi zimenezi zikusiyana bwanji ndi “madzi akuba.” Madziwa ndi zachiwerewere zomwe n’zosaloleka. Nthawi zambiri zoterezi zimachitika mwachinsinsi, ngati mmene zimakhalira ndi wakuba. “Madzi akuba” angamaoneke ngati otsekemera makamaka ngati anthu ochita zachiwerewerewo akuona kuti sakukumana ndi vuto lililonse chifukwa cha zoipa zomwe akuchitazo. Kumenekutu n’kudzinamiza chifukwa Yehova amaona zonse. Palibe chinthu chowawa kwambiri kuposa kusiya kukondedwa ndi Yehova, ndipo palibe chilichonse “chotsekemera” kapena kuti chosangalatsa ndi kutaya mwayi wamtengo wapataliwu. (1 Akor. 6:9, 10) Koma palinso mavuto ena.
10 Khalidwe lachiwerewere lingachititse kuti munthu azichita manyazi, azidziona kuti ndi wachabechabe, atenge mimba yosayembekezera komanso lingasokoneze mabanja. Kunena zoona, ndi nzeru kukana kupita ndi kukadya ‘kunyumba’ ya mkazi wopusa. Kuwonjezera pa kuwononga ubwenzi wawo ndi Yehova, ambiri amene amachita khalidwe lachiwerewere amatenga matenda, zomwe zimachititsa kuti afe msanga. (Miy. 7:23, 26) Vesi 18 ya chaputala 9, imamaliza ndi mawu akuti: “Amene amaitanidwa ndi mkaziyu ali kumalo otsika a ku Manda.” Ndiye n’chifukwa chiyani anthu ambiri amavomera akaitanidwa ndi mkaziyu ngakhale kuti amakumana ndi mavuto?—Miy. 9:13-18.
11. N’chifukwa chiyani kuonera zolaula n’koopsa kwambiri?
11 Msampha wofala kwambiri ndi kuonera zolaula. Ena amaona kuti kuonera zolaula kulibe vuto lililonse. Koma zoona n’zakuti kuonera zolaula n’koopsa, kumamuchotsera munthu ulemu komanso zimamuvuta kuti asiye. Zithunzi zolaula zimakhazikika m’maganizo ndipo zimakhala zovuta kuziiwala. Kuonera zolaula sikuthandiza munthu kuti athetse chilakolako cha kugonana, koma kumangochiwonjezera. (Akol. 3:5; Yak. 1:14, 15) Anthu ambiri amene amaonera zolaula amafika mpaka pochita zachiwerewere.
12. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timasamala ndi zithunzi zomwe zingachititse kuti tikhale ndi chilakolako cha kugonana?
12 Monga Akhristu, kodi tiyenera kuchita chiyani ngati pachipangizo chathu chamakono pabwera chithunzi cholaula? Mwamsanga tiyenera kupewa kuchiyang’ana. Zingakhale zosavuta kuchita zimenezi ngati timaona kuti chinthu chofunika kwambiri ndi ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndipotu zithunzi zimene anthu saziona kuti ndi zolaula kwenikweni zingachititse kuti munthu akhale ndi chilakolako cha kugonana. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa zithunzi zotere? Chifukwa sitifuna ngakhale pang’ono kuti tiziganizira zachiwerewere mumtima mwathu. (Mat. 5:28, 29) Mkulu wina wa ku Thailand dzina lake David ananena kuti: “Ndimadzifunsa kuti, ‘Ngakhale kuti zithunzizi si zolaula, kodi Yehova angasangalale ngati nditapitiriza kuziyang’ana?’ Kuganiza mwa njira imeneyi kumandithandiza kuti ndisankhe zochita mwanzeru.”
13. Kodi n’chiyani chimene chimatithandiza kuti tizichita zinthu mwanzeru?
13 Kuopa kukhumudwitsa Yehova kumatithandiza kuti tizisankha zochita mwanzeru. Kuopa Mulungu ndi “chiyambi cha nzeru.” (Miy. 9:10) Zimenezi zikufotokozedwa bwino kumayambiriro kwa Miyambo chaputala 9, komwe timawerenga za mkazi winanso wophiphiritsa, yemwe akutchulidwa kuti “nzeru yeniyeni.”
MUZIVOMERA “NZERU YENIYENI” IKAKUITANANI
14. Kodi ndi kuitana kwina kuti komwe kwafotokozedwa pa Miyambo 9:1-6?
14 Werengani Miyambo 9:1-6. Palembali, Mwiniwake wa nzeru yeniyeni komanso Mlengi wathu akutiitana. (Miy. 2:6; Aroma 16:27) Mwa fanizo, timawerenga za nyumba yaikulu yomwe ili ndi zipilala 7. Izitu zikusonyeza kuti Yehova ndi wowolowa manja ndipo amalandira onse omwe amafuna kugwiritsa ntchito nzeru zake pa moyo wawo.
15. Kodi Mulungu amatipempha kuti tichite chiyani?
15 Yehova amapereka zinthu mowolowa manja. Timaona zimenezi tikaganizira za “nzeru yeniyeni” yomwe pa Miyambo chaputala 9, ikufotokozedwa ngati mkazi. Nkhaniyi imasonyeza kuti mkazi wophiphiritsayu wapha nyama yake, wasakaniza vinyo komanso wayala patebulo pake. (Miy. 9:2) Kuwonjezera pamenepo, mogwirizana ndi vesi 4 ndi 5, “nzeru [mkazi wophiphiritsayu] ikumuuza kuti, ‘Bwerani mudzadye chakudya changa.’” N’chifukwa chiyani tiyenera kupita kunyumba ya nzeru yeniyeni komanso kukadya chakudya chake? Yehova amafuna kuti ana ake akhale anzeru ndiponso otetezeka. Iye safuna kuti tiziphunzira m’njira yowawa kapena kuchita zinthu zimene pambuyo pake tingadzanong’oneze nazo bondo. N’chifukwa chake “anthu owongoka mtima, iye amawasungira nzeru zopindulitsa.” (Miy. 2:7) Ngati timalemekeza kwambiri Yehova, tidzafuna kuti tizichita zimene zimamusangalatsa. Timamvetsera malangizo ake anzeru ndipo timasangalala kuwatsatira.—Yak. 1:25.
16. Kodi kuopa Yehova kunathandiza bwanji Alain kusankha zochita mwanzeru, nanga zotsatira zake n’zotani?
16 Taganizirani mmene kuopa Mulungu kunathandizira Alain kusankha zochita mwanzeru. M’baleyu, yemwe anali mkulu komanso ankaphunzitsa pasukulu ina, ananena kuti: “Ambiri mwa aphunzitsi anzanga amaona mafilimu olaula ngati njira yophunzitsira zokhudza kugonana.” Koma Alain sanapusitsidwe ndi zimenezi. Iye anati: “Chifukwa chakuti ndimakonda komanso kulemekeza Yehova, ndinakanitsitsa kuonera mafilimuwo. Ndinafotokozeranso anzangawo chifukwa chake.” Alain ankatsatira malangizo a “nzeru yeniyeni” oti ‘ayende mowongoka m’njira yomvetsa zinthu.’ (Miy. 9:6) Pochita chidwi ndi kulimba mtima kwa Alain, panopa ena mwa aphunzitsi anzakewo akuphunzira Baibulo ndipo amapezeka pamisonkhano.
17-18. Kodi ndi madalitso otani omwe anthu ovomera kuitana kwa “nzeru yeniyeni” amapeza, nanga akuyembekezera chiyani m’tsogolo? (Onaninso chithunzi.)
17 Pogwiritsa ntchito fanizo la akazi awiri ophiphiritsa, Yehova watithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tikhale ndi tsogolo labwino. Anthu amene amavomera kuitanidwa ndi “mkazi wopusa” amangoganizira za “kutsekemera,” kapena kuti chisangalalo chimene angapeze chifukwa chochita zachiwerewere. Kunena zoona, iwo amangoganizira zosangalala panopa n’kumanyalanyaza zomwe zidzawachitikire m’tsogolo. Zotsatira zake n’zakuti adzakathera “kumalo otsika a ku Manda.”—Miy. 9:13, 17, 18.
18 Izitu n’zosiyana kwambiri ndi zimene zimachitikira amene amavomera kuitana kwa “nzeru yeniyeni.” Panopa alendo a mkazi ameneyu amasangalala ndi phwando la chakudya chauzimu chokonzedwa bwino. (Yes. 65:13) Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova amatiuza kuti: “Tcherani khutu kwa ine kuti mudye zabwino, ndiponso kuti moyo wanu usangalale kwambiri ndi zakudya zamafuta.” (Yes. 55:1, 2) Panopa tikuphunzira kukonda zimene Yehova amakonda komanso kudana ndi zimene amadana nazo. (Sal. 97:10) Timasangalalanso kuuza ena kuti adzasangalale ndi “nzeru yeniyeni.” Zimakhala ngati ‘tapita pamwamba pa zitunda za m’mudzi kukaitana anthu, kuti: “Aliyense wosadziwa zinthu apatukire kuno.”’ Sikuti ifeyo komanso anthu amene avomera kuitanidwa timangopeza madalitso panopa, koma tidzapezanso madalitso m’tsogolo ndipo ‘tidzakhala ndi moyo’ mpaka kalekale, pamene ‘tizidzayenda mowongoka m’njira yomvetsa zinthu.’—Miy. 9:3, 4, 6.
19. Mogwirizana ndi Mlaliki 12:13, 14, kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani? (Onaninso bokosi lakuti “Kuopa Mulungu Kumatithandiza.”)
19 Werengani Mlaliki 12:13, 14. Tiyeni tilole kuti kuopa Mulungu kupitirize kuteteza mtima wathu, komanso kutithandize kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova m’masiku otsiriza oipawa. Mantha oyenerawa adzatilimbikitsa kuti tipitirize kuitana anthu ambiri mmene tingathere kuti afunefune “nzeru yeniyeni” n’cholinga choti iwathandize.
NYIMBO NA. 127 Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala
a Akhristu amafuna kuti aziopa Mulungu moyenera. Mantha amenewa angateteze mtima wathu kuti tisamachite zachiwerewere kapena kuonera zolaula. Munkhaniyi, tikambirana chaputala 9 cha buku la Miyambo, chomwe chimafotokoza bwino kusiyana pakati pa nzeru ndi kupusa pogwiritsa ntchito akazi awiri ophiphiritsa. Malangizo a m’chaputalachi angatithandize panopa komanso mpaka kalekale.
b Mayina ena asinthidwa.