Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 27

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuopa Yehova?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuopa Yehova?

“Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa.”​—SAL. 25:14.

NYIMBO NA. 8 Yehova Ndiye Pothawirapo Pathu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1-2. Mogwirizana ndi Salimo 25:14, kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikufuna kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova?

 KODI mukuganiza kuti ndi makhalidwe ati ofunika kuti mukhale pa ubwenzi ndi munthu wina? Mosakayikira, mungafotokoze kuti mabwenzi enieni amafunika kuti azikondana komanso azithandizana. N’kutheka kuti simunaganizirepo kuti mantha ndi khalidwe lofunika kuti anthu akhale mabwenzi abwino. Komabe, monga mmene lemba lotsogolera nkhaniyi likusonyezera, anthu amene amafuna kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ayenera ‘kumamuopa.’​—Werengani Salimo 25:14.

2 Kaya takhala tikutumikira Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tiyenera kupitiriza kumuopa kwambiri. Koma kodi kuopa Mulungu kumatanthauza chiyani? Kodi tingaphunzire bwanji kuopa Yehova? Nanga tingaphunzire chiyani kwa Obadiya, Mkulu wa Ansembe Yehoyada komanso Mfumu Yehoasi pa nkhani yoopa Mulungu?

KODI KUOPA MULUNGU KUMATANTHAUZA CHIYANI?

3. Fotokozani zinthu zina zomwe zingatichititse mantha komanso mmene zingatikhudzire.

3 Nthawi zina timachita mantha ngati tikuona kuti tikumana ndi mavuto enaake. Mantha amenewa ndi oyenera ndipo angatithandize kuti tichite zinthu mwanzeru. Kuopa kugwa kumatichititsa kuti tisamayende m’mphepete mwa chiphedi. Kuopa kuvulala kumatichititsa kuti tithawe pamalo omwe ndi oopsa. Ndipo kuopa kuwononga ubwenzi wathu ndi munthu amene timamukonda kumatichititsa kuti tisalankhule kapena kuchita zinthu zomwe zingamukhumudwitse.

4. Kodi Satana amafuna kuti tizikhala ndi mantha otani ponena za Yehova?

4 Satana amafuna kuti anthu aziopa Yehova mosayenera. Iye amalimbikitsa maganizo omwe Elifazi anali nawo, oti Yehova ndi Mulungu yemwe amangopezera ena zifukwa, waukali komanso n’zosatheka kumusangalatsa. (Yobu 4:18, 19) Satana amafuna kuti tiziopa kwambiri Yehova mpaka kufika posiya kumutumikira. Kuti tipewe msampha umenewu, tiyenera kumalemekeza Mulungu komanso kumamuopa moyenera.

5. Kodi kuopa Mulungu kumatanthauza chiyani?

5 Munthu amene amaopa Mulungu moyenera amamukonda ndipo safuna kuchita chilichonse chomwe chingasokoneze ubwenzi wake ndi iye. Yesu ‘ankaopa Mulungu’ mwa njira imeneyi. (Aheb. 5:7) Iye sankaona Yehova ngati winawake woopsa. (Yes. 11:2, 3) M’malomwake, ankamukonda kwambiri ndipo ankafuna kumumvera. (Yoh. 14:21, 31) Mofanana ndi Yesu, ifenso timalemekeza kwambiri Yehova chifukwa ndi wachikondi, wanzeru, wachilungamo komanso wamphamvu. Timadziwanso kuti Yehova amatikonda kwambiri ndipo amakhudzidwa ndi zimene timachita akatipatsa malangizo. Tikhoza kumuchititsa kuti amve kupweteka mumtima kapenanso kusangalatsa mtima wake.​—Sal. 78:41; Miy. 27:11.

TINGAPHUNZIRE KUOPA MULUNGU

6. Kodi ndi njira imodzi iti yomwe ingatithandize kuti tiphunzire kuopa Mulungu? (Salimo 34:11)

6 Tonsefe sitimabadwa ndi mtima woopa Yehova, m’malomwake timafunika kuyesetsa kuti tikhale nawo. (Werengani Salimo 34:11.) Njira imodzi yomwe tingachitire zimenezi ndi kuganizira zomwe iye analenga. Tikamaona nzeru, mphamvu komanso chikondi cha Mulungu kwa anthufe, zomwe zimaonekera “m’zinthu zimene anapanga,” timayamba kumulemekeza komanso kumukonda kwambiri. (Aroma 1:20) Mlongo wina dzina lake Adrienne ananena kuti, “Nzeru za Yehova, zomwe zimaonekera m’zinthu zimene analenga, zimandigometsa ndipo zimandithandiza kuzindikira kuti iye amadziwa zinthu zomwe ndi zabwino kwambiri kwa ine.” Kuganizira zimenezi mozama kunamuchititsa kunena kuti, “Ndiye ndingachitirenji zinthu zomwe zingasokoneze ubwenzi wanga ndi Yehova, yemwe anandipatsa moyo?” Kodi inunso mungapeze nthawi mlungu uno yoti muganizire chinachake chimene Yehova analenga? Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muzilemekeza komanso kukonda kwambiri Yehova.​—Sal. 111:2, 3.

7. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kuti tiziopa Yehova moyenera?

7 Chinthu china chomwe chingatithandize kuti tiziopa Mulungu ndi kupemphera nthawi zonse. Tikamapemphera kwambiri, m’pamenenso Yehova amakhala weniweni kwa ife. Nthawi iliyonse imene tamupempha kuti atipatse mphamvu kuti tipirire mayesero enaake, timakumbukira kuti iye ali ndi mphamvu zodabwitsa. Tikamayamikira Yehova chifukwa cha mphatso ya Mwana wake, zimatikumbutsa kuti iye amatikonda kwambiri. Ndipo tikamapemphera mapemphero opembedzera kuti atithandize pa vuto linalake, timakumbukira kuti iye ndi wanzeru kwambiri. Mapemphero oterewa amatichititsa kuti tizimulemekeza kwambiri. Ndipo amatipangitsa kukhala otsimikiza kuti tisachite chilichonse chomwe chingawononge ubwenzi wathu ndi iye.

8. Kodi tingatani kuti tipitirize kuopa Mulungu?

8 Tikhoza kupitiriza kuopa Mulungu powerenga Baibulo n’cholinga choti tiphunzire pa zitsanzo zabwino komanso zoipa zomwe zili m’bukuli. Tiyeni tikambirane zitsanzo ziwiri za atumiki okhulupirika a Yehova, omwe ndi Mkulu wa Ansembe Yehoyada komanso Obadiya, yemwe anali woyang’anira nyumba ya mfumu. Kenako tiona zomwe tingaphunzire kwa Mfumu Yehoasi ya ku Yuda, yemwe anayamba bwino koma kenako anasiya kutumikira Yehova.

MUZIKHALA OLIMBA MTIMA NGATI OBADIYA, YEMWE ANKAOPA MULUNGU

9. Kodi kuopa Mulungu kunathandiza bwanji Obadiya? (1 Mafumu 18:3, 12)

9 Baibulo limayamba kufotokoza za Obadiya b ndi mawu akuti: “Obadiya anali atasonyeza kuti anali munthu woopa Yehova kwambiri.” (Werengani 1 Mafumu 18:3, 12.) Kodi mantha oyenerawa anathandiza bwanji Obadiya? Mwa zina; anamuthandiza kuti akhale woona mtima komanso wodalirika, zomwe zinachititsa kuti mfumu imuike kukhala woyang’anira nyumba yake. (Yerekezerani ndi Nehemiya 7:2.) Kuopa Mulungu kunathandizanso Obadiya kukhala wolimba mtima kwambiri, ndipo iye ankafunikadi kukhala ndi khalidweli. Iye anakhala ndi moyo pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Ahabu yemwe “anachita zoipa kwambiri pamaso pa Yehova kuposa [mafumu] onse amene anakhalapo iye asanakhale.” (1 Maf. 16:30) Komanso, Yezebeli mkazi wa Ahabu, yemwe ankalambira Baala, ankadana kwambiri ndi Yehova, moti anayesa kuthetseratu kulambira koona mu ufumu wa ku mpoto. Iye anaphanso aneneri ambiri a Mulungu. (1 Maf. 18:4) Mosakayikira, Obadiya ankalambira Yehova pa nthawi yovuta.

10. Kodi Obadiya anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima kwambiri?

10 Kodi Obadiya anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima kwambiri? Yezebeli atayamba kufunafuna aneneri a Mulungu kuti awaphe, Obadiya anabisa aneneri 100 ‘m’magulu awiri a aneneri 50 gulu lililonse, ndipo anali kuwapatsa mkate ndi madzi.’ (1 Maf. 18:13, 14) Ngati izi zikanadziwika, n’zosakayikitsa kuti munthu wolimba mtimayu akanaphedwa. N’zoona kuti Obadiya anali munthu ngati ife tomwe ndipo sankafuna kufa. Koma iye ankakonda kwambiri Yehova komanso atumiki ake kuposa mmene ankakondera moyo wake.

Ngakhale kuti ntchito yathu ndi yoletsedwa m’dziko lake, molimba mtima, m’bale akupereka chakudya chauzimu kwa a Mboni anzake (Onani ndime 11) c

11. Kodi atumiki a Yehova a masiku ano akufanana bwanji ndi Obadiya? (Onaninso chithunzi.)

11 Masiku ano atumiki ambiri a Yehova akukhala mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Iwo amapereka ulemu woyenerera kwa akuluakulu a boma, koma mofanana ndi Obadiya, amapereka ulemu waukulu kwambiri kwa Yehova ndipo sasiya kumulambira. (Mat. 22:21) Iwo amasonyeza kuti amaopa Mulungu pomumvera m’malo moopa anthu. (Mac. 5:29) Amachita zimenezi popitirizabe kulalikira uthenga wabwino komanso kuchita misonkhano mobisa. (Mat. 10:16, 28) Iwo amaonetsetsa kuti abale ndi alongo awo akupeza chakudya chauzimu chomwe akufunikira. Taganizirani chitsanzo cha Henri, yemwe amakhala ku Africa m’dziko lina lomwe ntchito yathu inali yoletsedwa kwa kanthawi. Panthawiyo, iye anadzipereka kuti azikapereka chakudya chauzimu kwa a Mboni anzake. Henri analemba kuti: “Mwachibadwa ndine wamanyazi. Ndimakhulupirira kuti ulemu waukulu womwe ndimapereka kwa Yehova ndi umene unandithandiza kuti ndikhale wolimba mtima.” Inunso mungakhale wolimba mtima ngati Henri. Zimenezi zingatheke ngati mumaopa Mulungu moyenera.

MUZIKHALA OKHULUPIRIKA NGATI MKULU WA ANSEMBE YEHOYADA, YEMWE ANKAOPA MULUNGU

12. Kodi Yehoyada ndi mkazi wake anasonyeza bwanji kuti anali okhulupirika kwambiri kwa Yehova?

12 Mkulu wa Ansembe Yehoyada ankaopa Yehova, ndipo zimenezi zinamuchititsa kuti akhale wokhulupirika komanso azilimbikitsa kulambira koona. Umboni wa zimenezi unaonekera pamene Ataliya, mwana wa Yezebeli, analanda ufumu ku Yuda. Panali zifukwa zomveka zoti anthu aziopera Ataliya. Iye anali wankhanza ndipo chifukwa chofunitsitsa kukhala wolamulira, anafika mpaka poyesa kupha ana onse a mfumu, omwe anali zidzukulu zake. (2 Mbiri 22:10, 11) Yehoasi, yemwe anali mmodzi wa anawo, sanaphedwe chifukwa choti Yehosabati mkazi wa Yehoyada anamupulumutsa. Iye ndi mwamuna wake anamubisa n’kumamusamalira. Zimene Yehoyada ndi Yehosabati anachita zinathandiza kuteteza mzere wa mafumu wa Davide. Yehoyada anali wokhulupirika kwa Yehova ndipo sanachite mantha ndi Ataliya.​—Miy. 29:25.

13. Pamene Yehoasi anali ndi zaka 7, kodi Yehoyada anasonyezanso bwanji kuti anali wokhulupirika?

13 Pamene Yehoasi anali ndi zaka 7, Yehoyada anasonyezanso kuti anali wokhulupirika kwa Yehova. Iye anakonza zoti Yehoasi akhale mfumu. Ngati izi zikanatheka ndiye kuti munthu woyenerera akanakhala pampando wachifumu wa Davide. N’zoonekeratunso kuti ngati zikanalephereka, Yehoyada akanaphedwa. Mothandizidwa ndi Yehova, zimene anakonzazi zinatheka. Yehoyada anathandizidwa ndi atsogoleri a magulu a asilikali komanso Alevi, poika Yehoasi kukhala mfumu ndipo Ataliya anaphedwa. (2 Mbiri 23:1-5, 11, 12, 15; 24:1) Kenako Yehoyada “anachita pangano pakati pa Yehova, mfumu, ndi anthu, kuti anthuwo azisonyeza kuti ndi anthu a Yehova.” (2 Maf. 11:17) Komanso iye “anaika alonda a pazipata pafupi ndi zipata za nyumba ya Yehova kuti aliyense wodetsedwa mwa njira ina iliyonse asalowe.”​—2 Mbiri 23:19.

14. Kodi Yehoyada analemekezedwa bwanji chifukwa cholemekeza Yehova?

14 Nthawi ya Yehoyada isanafike, Yehova anali atanena kuti: “Amene akundilemekeza ndiwalemekeza.” Ndipotu iye anadalitsadi Yehoyada. (1 Sam. 2:30) Mwachitsanzo, iye analola kuti zabwino zimene mkulu wa ansembeyu anachita zilembedwe m’Mawu ake kuti zizitilangiza. (Aroma 15:4) Komanso Yehoyada atamwalira, anapatsidwa ulemu wapadera poikidwa m’manda “mu Mzinda wa Davide, chifukwa anachita zabwino mu Isiraeli ndiponso kwa Mulungu woona ndi nyumba Yake.”​—2 Mbiri 24:15, 16.

Mofanana ndi Mkulu wa Ansembe Yehoyada, kuopa Mulungu kungatichititse kuti tizithandiza mokhulupirika abale athu (Onani ndime 15) d

15. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Yehoyada? (Onaninso chithunzi.)

15 Nkhani ya Yehoyada ingatithandize tonsefe kuti tiziopa Mulungu. Akulu angatsanzire Yehoyada pokhala tcheru n’kumateteza nkhosa za Mulungu mokhulupirika. (Mac. 20:28) Achikulire angaphunzireponso kanthu kwa Yehoyada kuti ngati atamaopa Yehova n’kukhalabe okhulupirika, iye angawagwiritse ntchito pokwaniritsa cholinga chake. Iye samawaona kuti ndi osafunika. Achinyamata angaphunzirepo kanthu poona mmene Yehova anachitira zinthu ndi Yehoyada n’kumamutsanzira polemekeza achikulire, makamaka amene atumikira Mulungu mokhulupirika kwa nthawi yaitali. (Miy. 16:31) Pomaliza, tonsefe tingaphunzirepo kanthu kwa atsogoleri a magulu a asilikali komanso Alevi omwe anathandiza Yehoyada. Tiyeni tizithandiza mokhulupirika ‘amene akutsogolera pakati pathu’ pomawamvera.​—Aheb. 13:17.

MUSAMAKHALE NGATI MFUMU YEHOASI

16. Kodi Mfumu Yehoasi anasonyeza bwanji kuti anali wofooka?

16 Zochita za Yehoyada zinathandiza Yehoasi kuti akhale mfumu yabwino. (2 Maf. 12:2) Zotsatira zake n’zakuti mfumu yachinyamatayi inkafuna kusangalatsa Yehova. Koma Yehoyada atamwalira, Yehoasi anamvera akalonga ampatuko. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Iye ndi anthu ake ‘anayamba kutumikira mizati yopatulika ndiponso mafano.’ (2 Mbiri 24:4, 17, 18) Ngakhale kuti Yehova anakhumudwa ndi zimenezi, “anapitiriza kutumiza aneneri pakati pawo kuti awabwezere kwa iye . . . , koma sanamvere.” Iwo sanamvere ngakhale Zekariya mwana wa Yehoyada, yemwe sikuti anangokhala mneneri ndi wansembe wa Yehova, koma analinso wachibale wa Yehoasi. Ndipotu Mfumu Yehoasi sanasonyeze kuyamikira zimene banja la Zekariya linachita populumutsa moyo wake, moti mpaka anafika pochititsa kuti Zekariya aphedwe.​—2 Mbiri 22:11; 24:19-22.

17. Kodi zinthu zinamuyendera bwanji Yehoasi?

17 Yehoasi sanapitirize kuopa Yehova ndipo zinthu sizinamuyendere bwino. Yehova anali atanena kuti: “Amene akundinyoza ndi opanda pake kwa ine.” (1 Sam. 2:30) Pasanapite nthawi, gulu laling’ono la nkhondo la ku Siriya linagonjetsa “gulu lankhondo lalikulu kwambiri” la Yehoasi ndipo linamusiya “akuvutika kwambiri” ndi mabala. Asiriyawo atachoka, Yehoasi anaphedwa ndi atumiki ake chifukwa chopha Zekariya. Anthu anaona kuti mfumuyi inali yoipa kwambiri moti sanaiike “m’manda a mafumu.”​—2 Mbiri 24:23-25.

18. Mogwirizana ndi Yeremiya 17:7, 8, kodi tingatani kuti tisakhale ngati Yehoasi?

18 Kodi tikuphunzira chiyani pachitsanzo cha Yehoasi? Iye anali ngati mtengo wa mizu yosazama womwe umadalira mtengo wina kuti uime bwino. Choncho Yehoyada yemwe anali ngati mtengo womwe ankadalira atamwalira, Yehoasi anayamba kumvetsera anthu ampatuko ndipo anakhala wosakhulupirika kwa Yehova. Zimenezi zikusonyeza kuti sitiyenera kungodalira chitsanzo chabwino cha Akhristu anzathu ngakhalenso achibale athu kuti tiziopa Mulungu. Kuti tipitirize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, ifenso patokha tiyenera kumamukonda komanso kumulemekeza kwambiri pophunzira Mawu ake nthawi zonse, kuwaganizira mozama komanso kupemphera.​—Werengani Yeremiya 17:7, 8; Akol. 2:6, 7.

19. Kodi Yehova amafuna kuti tizichita chiyani?

19 Yehova safuna zinthu zambiri kwa ife. Zimene amafuna zafotokozedwa palemba la Mlaliki 12:13, lomwe limati: “Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.” Tikamaopa Mulungu, tidzatha kupirira mavuto amene tingakumane nawo n’kukhalabe olimba ngati Obadiya ndi Yehoyada. Palibe chomwe chidzathe kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova.

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

a Monga mmene agwiritsidwira ntchito m’Malemba, mawu akuti ‘kuopa’ ali ndi matanthauzo ambiri. Mogwirizana ndi nkhani imene ikufotokozedwa, mawuwa angatanthauze mantha kapenanso ulemu. Nkhaniyi itithandiza kukhala ndi mantha omwe angatilimbikitse kukhala olimba mtima komanso okhulupirika potumikira Atate wathu wakumwamba.

b Obadiya ameneyu si mneneri Obadiya yemwe anadzakhala ndi moyo patapita zaka zambiri, amene analemba buku la m’Baibulo lodziwika ndi dzina lake.

c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pachithunzipa, m’bale akugawa chakudya chauzimu kwa Akhristu anzake pa nthawi yomwe ntchito yathu ndi yoletsedwa m’dziko lawo.

d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo wachitsikana akuphunzira kwa mlongo wachikulire mmene angachitire ulaliki wa patelefoni, m’bale wachikulire akupereka chitsanzo pa nkhani ya kulimba mtima pochita ulaliki wa m’malo opezeka anthu ambiri, m’bale wodziwa zambiri akuphunzitsa ena mmene angakonzere zinthu pa Nyumba ya Ufumu.