NKHANI YOPHUNZIRA 26
Pitirizani Kukonzekera Tsiku la Yehova
“Tsiku la Yehova lidzabwera ndendende ngati mbala usiku.”—1 ATES. 5:2.
NYIMBO NA. 143 Pitirizani Kugwira Ntchito, Kukhala Maso ndi Kudikira
ZIMENE TIPHUNZIRE a
1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzapulumuke pa tsiku la Yehova?
BAIBULO likamanena za “tsiku la Yehova,” limatanthauza nthawi imene iye adzawononge adani ake ndi kupulumutsa anthu ake. M’mbuyomu, nthawi zina Yehova ankawononga adani ake. (Yes. 13:1, 6; Ezek. 13:5; Zef. 1:8) M’masiku athu ano, “tsiku la Yehova” lidzayamba ndi kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu ndipo lidzafika pachimake pa nkhondo ya Aramagedo. Kuti tidzapulumuke pa “tsiku” limeneli, tiyenera kukonzekera panopa. Yesu anaphunzitsa kuti, sikuti tiyenera kungokonzekera “chisautso chachikulu” koma tiyeneranso kupitirizabe ‘kukhala okonzeka.’—Mat. 24:21; Luka 12:40.
2. Kodi buku la 1 Atesalonika lingatithandize bwanji?
2 M’kalata yake youziridwa yoyamba yomwe analembera Akhristu a ku Tesalonika, mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito mafanizo angapo pofuna kuwathandiza kuti apitirize kukonzekera tsiku lalikulu la Yehova. Iye ankadziwa kuti tsikuli silinali pafupi pa nthawiyo. (2 Ates. 2:1-3) Komabe, analimbikitsa abale akewo kuti azikonzekera tsikuli ngati kuti libwera mawa ndipo ifenso tiyenera kugwiritsa ntchito malangizo akewa. Tiyeni tikambirane mmene iye anafotokozera zinthu zotsatirazi: (1) mmene tsiku la Yehova lidzafikire, (2) amene sadzapulumuka pa tsikuli komanso (3) mmene tingakonzekerere kuti tidzapulumuke.
KODI TSIKU LA YEHOVA LIDZAFIKA BWANJI?
3. Kodi tsiku la Yehova lidzafika ngati mbala usiku m’njira yotani? (Onaninso chithunzi.)
3 “Ngati mbala usiku.” (1 Ates. 5:2) Awa ndi mawu oyamba mwa mawu atatu ofotokoza mwafanizo za kubwera kwa tsiku la Yehova. Nthawi zambiri mbala zimachita zinthu mofulumira komanso usiku pa nthawi imene anthu sakuyembekezera. Mofanana ndi zimenezi, tsiku la Yehova lidzafika mosayembekezereka ndipo izi zidzadzidzimutsa anthu ambiri. Ngakhalenso Akhristu oona angadzadabwe chifukwa cha mmene zinthu zidzachitikire mofulumira. Koma mosiyana ndi anthu oipa, ifeyo sitidzawonongedwa nawo.
4. Kodi tsiku la Yehova likufanana bwanji ndi zowawa za pobereka?
4 “Monga zowawa za pobereka za mkazi wapakati.” (1 Ates. 5:3) Mayi woyembekezera sangadziwiretu nthawi yeniyeni yomwe abereke mwana. Komabe iye samakayikira kuti nthawi yoberekayo ifika. Nthawiyo imafika modzidzimutsa, amamva ululu waukulu komanso palibe chomwe angachite kuti zimenezi zisachitike. Mofanana ndi zimenezi, ifenso sitimadziwa nthawi yeniyeni yomwe tsiku la Yehova lidzayambe. Komabe, sitimakayikira kuti lidzafika komanso kuti chiweruzo cha Mulungu kwa anthu oipa chidzakhala chodzidzimutsa ndiponso chosapeweka.
5. Kodi chisautso chachikulu chikufanana bwanji ndi m’bandakucha?
5 Ngati m’bandakucha. Fanizo lachitatu la Paulo likunenanso za mbala zikuba usiku. Koma pa nthawiyi, iye akusintha mmene akufotokozera fanizoli ndipo akuyerekezera tsiku la Yehova ndi m’bandakucha. (1 Ates. 5:4) Anthu akuba, usiku akhoza kuyamba kutanganidwa kwambiri ndi zomwe akuchita moti kunja kungawachere modzidzimutsa, zomwe zingachititse kuti anthu awaone. Mofanana ndi zimenezi, pa chisautso chachikulu, anthu omwe ali ngati mbala ndipo ali mumdima popitirizabe kuchita zinthu zimene Mulungu sasangalala nazo, adzaonekera. Mosiyana ndi anthu amenewa, ifeyo tingakhale okonzeka popewa makhalidwe omwe Yehova sasangalala nawo n’kumachita “chilichonse chabwino ndi chilichonse cholungama ndi choona.” (Aef. 5:8-12) Kenako, Paulo anatchulanso mafanizo awiri ofanana pofotokoza za anthu omwe sadzapulumuka.
KODI NDI NDANI AMENE SADZAPULUMUKA PA TSIKU LA YEHOVA?
6. Kodi anthu ambiri akugona m’njira yotani? (1 Atesalonika 5:6, 7)
6 “Ogona.” (Werengani 1 Atesalonika 5:6, 7.) Paulo anayerekezera amene sadzapulumuka pa tsiku la Yehova ndi anthu amene akugona. Iwo sakudziwa zimene zikuchitika kapenanso kuti nthawi ikudutsa. Choncho, sangazindikire zinthu zofunika zomwe zikuchitika kapenanso kuchitapo kanthu. Masiku ano, anthu ambiri akugona mwauzimu. (Aroma 11:8) Iwo sakhulupirira umboni woti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ komanso kuti chisautso chachikulu chiyamba posachedwapa. Zochitika zikuluzikulu za m’dzikoli zingachititse kuti ena adzuke mwauzimu n’kuyamba kuchita chidwi ndi uthenga wa Ufumu. Komabe, ambiri amayambiranso kugona m’malo mokhalabe maso. Ngakhalenso ena omwe amakhulupirira kuti kuli tsiku lachiweruzo, amaona kuti lili kutali kwambiri. (2 Pet. 3:3, 4) Koma ifeyo tsiku lililonse timazindikira kuti malangizo akuti tikhalebe maso ndi ofunika kwambiri.
7. Kodi anthu amene akuyembekezera mkwiyo wa Mulungu akufanana bwanji ndi oledzera?
7 “Amene amaledzera.” Mtumwiyu anayerekezera anthu amene akuyembekezera mkwiyo wa Mulungu ndi oledzera. Munthu amene waledzera amachedwa kuzindikira zinthu ndipo sasankha zochita mwanzeru. Mofanana ndi zimenezi, anthu oipa samvera machenjezo a Mulungu. Iwo amasankha kumachita zinthu zowawonongetsa. Koma Akhristu amauzidwa kuti ayenera kukhalabe maso kuti akhale oganiza bwino. (1 Ates. 5:6) Katswiri wina wa Baibulo anafotokoza kuti kuganiza bwino kumeneku ndi “kukhala ndi maganizo odekha ndiponso osatekeseka komanso kuyerekezera bwino zinthu, zomwe zimathandiza kuti munthu asankhe bwino zochita.” N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi maganizo odekha komanso osatekeseka? Kukhala ndi maganizo otere, kungatithandize kuti tisamalowerere ndale kapena zochitika za m’dzikoli. Pamene tsiku la Yehova likuyandikira, tizikakamizidwa kwambiri kuti tizichita nawo zinthu zimenezi. Komabe, sitiyenera kuda nkhawa kuti tidzatani tikadzakumana ndi zoterezi. Mzimu wa Mulungu udzatithandiza kukhala ndi maganizo odekha komanso osatekeseka ndipo tidzasankha zochita mwanzeru.—Luka 12:11, 12.
KODI TINGAKONZEKERE BWANJI TSIKU LA YEHOVA?
8. Kodi lemba la 1 Atesalonika 5:8, likusonyeza bwanji makhalidwe omwe angatithandize kukhalabe maso komanso kuganiza bwino? (Onaninso chithunzi.)
8 “Tivale chodzitetezera pachifuwa . . . ndi . . . chisoti.” Paulo amatiyerekezera ndi asilikali omwe ali tcheru ndipo avala zovala za kunkhondo. (Werengani 1 Atesalonika 5:8.) Msilikali yemwe ali pantchito yake, nthawi zonse amayembekezeredwa kukhala wokonzeka kumenya nkhondo. N’chimodzimodzinso ndi ifeyo. Timapitiriza kukonzekera tsiku la Yehova povala chodzitetezera pachifuwa chachikhulupiriro ndi chikondi komanso chisoti chachipulumutso. Makhalidwe amenewa angatithandize kwambiri.
9. Kodi chikhulupiriro chathu chimatiteteza bwanji?
9 Chodzitetezera pachifuwa chinkateteza mtima wa msilikali. Chikhulupiriro komanso chikondi, zimateteza mtima wathu wophiphiritsa. Makhalidwewa amatithandiza kuti tipitirizebe kutumikira Mulungu komanso kutsatira Yesu. Chikhulupiriro chimatithandiza kukhala otsimikiza kuti Yehova adzatipatsa mphoto chifukwa chomufunafuna ndi mtima wonse. (Aheb. 11:6) Chimatithandizanso kukhalabe okhulupirika kwa Mtsogoleri wathu, Yesu, ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto. Tingalimbitse chikhulupiriro chathu kuti tizipirira mavuto, poganizira zitsanzo za masiku ano za anthu omwe anakhalabe okhulupirika ngakhale kuti ankazunzidwa kapenanso ankakumana ndi mavuto a zachuma. Tingapewe msampha wokonda chuma potsanzira anthu amene anasankha kukhala ndi moyo wosalira zambiri n’cholinga choti aziika zinthu za Ufumu pamalo oyamba. b
10. Kodi kukonda Mulungu komanso anthu, kumatithandiza bwanji kuti tizipirira?
10 Chikondi n’chofunikanso kuti tikhalebe maso komanso tiziganiza bwino. (Mat. 22:37-39) Kukonda Mulungu kumatithandiza kuti tizipirira tikamagwira ntchito yolalikira ngakhale pamene kuchita zimenezi kungatibweretsere mavuto. (2 Tim. 1:7, 8) Chifukwa chokonda anthu omwe satumikira Yehova, timapitirizabe kulalikira m’gawo lathu ngakhalenso kulalikira kudzera pafoni komanso polemba makalata. Sitifooka chifukwa timayembekezera kuti tsiku lina, anthu amenewa adzasintha n’kuyamba kuchita zinthu zabwino.—Ezek. 18:27, 28.
11. Kodi kukonda Akhristu anzathu kumatithandiza bwanji? (1 Atesalonika 5:11)
11 Kukonda anthu kumaphatikizapo kukonda Akhristu anzathu. Timasonyeza chikondichi ‘potonthozana ndi kulimbikitsana.’ (Werengani 1 Atesalonika 5:11.) Mofanana ndi asilikali, omwe amathandizana pa nthawi ya nkhondo, ifenso timalimbikitsana. N’zoona kuti msilikali angavulaze msilikali mnzake pa nthawi ya nkhondo, koma sikuti angachite zimenezi mwadala. Mofanana ndi zimenezi, ifenso sitingakhumudwitse mwadala abale ndi alongo athu kapenanso kuwabwezera zoipa. (1 Ates. 5:13, 15) Timasonyezanso chikondi polemekeza abale omwe amatsogolera mumpingo. (1 Ates. 5:12) Pamene Paulo ankalemba kalatayi, panali pasanathe chaka kuchokera pamene mpingo wa ku Tesalonika unakhazikitsidwa. Abale amene ankatsogolera, ayenera kuti anali asakudziwa zambiri komanso mwina ankalakwitsa zinthu zina. Komabe, iwo ankafunika kulemekezedwa. Kuposa kale lonse, pamene chisautso chachikulu chizidzayamba, tidzafunika kudalira kwambiri malangizo omwe akulu m’mipingo yathu angadzatipatse. Mwina pa nthawiyo sitingadzathe kulandira malangizo kuchokera kulikulu kapena ku ofesi ya nthambi, choncho n’zofunika kuphunzira kukonda komanso kulemekeza akulu panopa. Kaya zinthu zidzakhala bwanji, tiyeni tipitirize kukhala oganiza bwino, osamaganizira zimene iwo amalakwitsa koma tiziganizira mfundo yakuti Yehova kudzera mwa Khristu, akutsogolera amuna okhulupirikawa.
12. Kodi chiyembekezo chimateteza bwanji maganizo athu?
12 Monga mmene chisoti chimatetezera mutu wa msilikali, chiyembekezo chathu chachipulumutso chimateteza maganizo athu. Chifukwa chokhala ndi chiyembekezo cholimba, timadziwa kuti zimene dzikoli limapereka, n’zachabechabe. (Afil. 3:8) Chiyembekezo chathu chimatithandiza kukhala odekha komanso osatekeseka. Umu ndi mmenenso zinalili ndi Wallace ndi Laurinda, omwe akutumikira ku Africa. M’milungu itatu yokha, aliyense analandira uthenga woti kholo lake lamwalira. Koma chifukwa cha mliri wa COVID-19, iwo sanathe kupita kwawo kuti akakhale limodzi ndi achibale awo pa nthawi ya maliro. Wallace analemba kuti: “Chiyembekezo choti akufa adzauka, chimandithandiza kuti ndiziganizira osati mmene zinthu zinalili m’masiku omaliza a moyo wawo, koma mmene zidzakhalire m’masiku oyambirira a moyo wawo m’dziko latsopano. Chiyembekezochi chimandithandiza kuti mtima wanga uzikhala m’malo ndikamavutika ndi chisoni.”
13. Kodi tingatani kuti tizilandira mzimu woyera?
13 “Musazimitse moto wa mzimu.” (1 Ates. 5:19) Paulo anayerekezera mzimu woyera ndi moto umene ungakhale ngati uli mkati mwathu. Tikakhala ndi mzimu wa Mulungu, timakhala a khama komanso ofunitsitsa kuchita zoyenera ndipo timakhalanso ndi mphamvu zotumikira Yehova. (Aroma 12:11) Kodi tingatani kuti tizilandira mzimu woyera? Tiziupempha, kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kukhalabe m’gulu lotsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu. Kuchita zimenezi, kungatithandize kukhala ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.”—Agal. 5:22, 23.
14. Kodi tiyenera kupewa chiyani ngati tikufuna kupitiriza kulandira mzimu wa Mulungu? (Onaninso chithunzi.)
14 Mulungu akatipatsa mzimu wake woyera, tiyenera kusamala kuti ‘tisazimitse moto wa mzimu.’ Mulungu amapereka mzimu wake kwa anthu okhawo amene amapitirizabe kuganiza zoyenera komanso kukhala ndi makhalidwe abwino. Iye angasiye kutipatsa mzimu wake ngati timapitiriza kuganizira zinthu zoipa komanso kumazichita. (1 Ates. 4:7, 8) Kutinso tipitirize kulandira mzimu woyera, ‘tisamanyoze mawu aulosi.’ (1 Ates. 5:20) Pavesili, “mawu aulosi” akuimira mauthenga operekedwa ndi mzimu wa Mulungu kuphatikizapo okhudza tsiku la Yehova komanso kuti tsikulo lili pafupi. Nthawi zonse timakumbukira za tsikuli ndipo sitimaganiza kuti Aramagedo siidzafika mu nthawi yathu. M’malomwake, tsiku lililonse timasonyeza kuti timaliganizira komanso kuyembekezera kuti lifika posachedwapa, popitiriza kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kutanganidwa ndi ‘ntchito zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu.’—2 Pet. 3:11, 12.
“TSIMIKIZIRANI ZINTHU ZONSE”
15. Kodi tingapewe bwanji kupusitsidwa ndi mfundo zachinyengo komanso mabodza a ziwanda? (1 Atesalonika 5:21)
15 Posachedwapa anthu omwe amatsutsa Mulungu, mwanjira inayake adzalengeza kuti: “Bata ndi mtendere!” (1 Ates. 5:3) Mabodza a ziwanda adzakhala paliponse padzikoli ndipo adzasocheretsa anthu ambiri. (Chiv. 16:13, 14) Nanga bwanji ifeyo? Sitidzapusitsidwa ngati ‘timatsimikizira [kapena kuti kuyesa] zinthu zonse.’ (Werengani 1 Atesalonika 5:21.) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti ‘kutsimikizira,’ ankagwiritsidwa ntchito pofotokoza njira yomwe anthu ankagwiritsa ntchito poyesa zitsulo zamtengo wapatali. Choncho, tiyenera kuyesa zimene timamva kapena kuwerenga kuti titsimikizire ngati zili zoona. Kuchita zimenezi kunali kofunika kwa Akhristu a ku Tesalonika ndipo kudzakhalanso kofunika kwambiri kwa ife pamene chisautso chachikulu chikuyandikira. M’malo momangokhulupirira zilizonse, timagwiritsa ntchito luso lathu loganiza kuti tiziyerekezera zimene tawerenga kapena kumva ndi zomwe Baibulo komanso gulu la Yehova limanena. Tikamachita zimenezi, sitidzapusitsidwa ndi mabodza a ziwanda.—Miy. 14:15; 1 Tim. 4:1.
16. Kodi tili ndi chiyembekezo chotsimikizirika chiti, nanga ndife otsimikiza kuchita chiyani?
16 Monga gulu, atumiki a Mulungu adzapulumuka pa chisautso chachikulu. Komabe, aliyense payekha sadziwa zamawa. (Yak. 4:14) Ndiponso kaya tidzakhala tili ndi moyo pa nthawiyo kapena tidzakhala titamwalira, tidzapatsidwa mphoto ya moyo wosatha ngati titakhalabe okhulupirika. Odzozedwa adzakakhala ndi Khristu kumwamba. A nkhosa zina adzakhala m’Paradaiso padziko lapansili. Tiyeni tonsefe tiziganizira kwambiri za chiyembekezo chathu chosangalatsachi ndiponso kupitiriza kukonzekera tsiku la Yehova.
NYIMBO NA. 150 Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke
a Muchaputala 5 cha 1 Atesalonika, timapezamo mafanizo omwe amatiphunzitsa za tsiku la Yehova lomwe likubwera. Kodi “tsiku” limeneli ndi la chiyani, nanga lidzafika bwanji? Ndi ndani omwe adzapulumuke? Komanso ndi ndani omwe sadzapulumuka? Nanga tingakonzekere bwanji tsikuli? Tikambirana zimene mtumwi Paulo ananena ndipo tipeza mayankho a mafunso amenewa.
b Onani nkhani zakuti “Anadzipereka ndi Mtima Wonse.”