Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 25

Zimene Akulu Angaphunzire pa Chitsanzo cha Gidiyoni

Zimene Akulu Angaphunzire pa Chitsanzo cha Gidiyoni

Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni.”​—AHEB. 11:32.

NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Mogwirizana ndi 1 Petulo 5:2, kodi akulu anapatsidwa udindo wotani?

 AKULU anapatsidwa udindo wosamalira nkhosa zamtengo wapatali za Yehova. Amuna odziperekawa amayamikira mwayi wotumikira abale ndi alongo awo ndipo amachita khama kuti akhale ‘abusa omwe . . . amaweta’ nkhosa za Mulungu. (Yer. 23:4; werengani 1 Petulo 5:2.) Timayamikira kwambiri kukhala ndi amuna ngati amenewa m’mipingo yathu.

2. Kodi ndi mavuto ati omwe akulu ena angakumane nawo?

2 Akulu amakumana ndi mavuto ambiri akamagwira ntchito yawo. Mwa zina, iwo amafunika kugwira ntchito mwakhama kuti azisamalira mpingo. Tony, yemwe ndi mkulu ku United States, anafunika kuzindikira zimene angakwanitse pa nkhani yovomera ntchito zimene wapatsidwa. Iye anafotokoza kuti: “Mliri wa COVID-19 utangoyamba kumene, ndinkatanganidwa kwambiri kuthandiza abale ndi alongo kuti azichita misonkhano komanso kulalikira. Ngakhale kuti ndinkachita zambiri, pankakhalabe zinthu zinanso zambiri zoti ndichite. Pang’ono ndi pang’ono, ndinayamba kumasowa nthawi yowerenga Baibulo, kuphunzira pandekha komanso kupemphera.” Mkulu wina wa ku Kosovo dzina lake Ilir, anakumananso ndi vuto lina. Pamene m’dera lakwawo munali nkhondo, iye anaona kuti sizinali zophweka kumvera malangizo a gulu. Iye anati: “Kulimba mtima kwanga kunayesedwa pamene ofesi ya nthambi inandipempha kuti ndikathandize abale ndi alongo m’dera lina lomwe linali loopsa. Ndinkachita mantha ndipo malangizo omwe ndinapatsidwawo ankaoneka ngati osathandiza.” Tim, yemwe ndi mmishonale ku Asia, ankaona kuti zinkamuvuta kuchita zinthu zonse zomwe ankafunika kuchita tsiku lililonse. Iye anati: “Nthawi zina ndinkatopa kwambiri moti ndinkaona kuti sindingathe kuthandiza abale ndi alongo.” Kodi n’chiyani chomwe chingathandize akulu omwe akukumana ndi mavuto ngati amenewa?

3. Kodi tonsefe tingapindule bwanji poganizira chitsanzo cha Gidiyoni?

3 Akulu angaphunzirepo kanthu pa chitsanzo cha Gidiyoni, yemwe anali woweruza. (Aheb. 6:12; 11:32) Iye ankateteza komanso kutsogolera anthu a Mulungu. (Ower. 2:16; 1 Mbiri 17:6) Mofanana ndi Gidiyoni, akulu apatsidwa udindo wosamalira anthu a Mulungu pa nthawi yovuta kwambiri. (Mac. 20:28; 2 Tim. 3:1) Tingaphunzire zambiri kwa Gidiyoni pa nkhani ya kudzichepetsa komanso kumvera. Kupirira kwake kunayesedwa pamene ankagwira ntchito yake. Choncho kaya ndife mkulu kapena ayi, tonsefe tingamayamikire kwambiri akulu. Tingathandize abale akhamawa, omwe amagwira ntchito yotisamalira mumpingo.​—Aheb. 13:17.

PAMENE KUSONYEZA KUDZICHEPETSA KUNGAKHALE KOVUTA

4. Kodi Gidiyoni anasonyeza bwanji kuti ankadziwa malire ake komanso anali wodzichepetsa?

4 Gidiyoni ankazindikira malire ake ochitira zinthu komanso anali wodzichepetsa. b Pamene mngelo wa Yehova anauza Gidiyoni kuti iye ndi amene wasankhidwa kuti akalanditse Aisiraeli m’manja mwa Amidiyani, omwe anali amphamvu, munthu wodzichepetsayu anayankha kuti: “Banja lathu ndilo laling’ono zedi m’fuko lonse la Manase, ndipo m’nyumba ya bambo anga, wamng’ono kwambiri ndine.” (Ower. 6:15) Iye ankaona kuti sangakwanitse ntchito yomwe anapatsidwayi, koma Yehova ankaona kuti angakwanitse. Mothandizidwa ndi Yehova, Gidiyoni anakwanitsa utumiki womwe anapatsidwa.

5. Kodi ndi pa nthawi iti pomwe zingakhale zovuta kuti mkulu azindikire malire ake komanso adzichepetse?

5 Akulu amayesetsa kuti azizindikira malire awo komanso kukhala odzichepetsa pa zinthu zonse. (Mika 6:8; Mac. 20:18, 19) Iwo samadzitamandira chifukwa cha zimene akwanitsa kuchita, komanso samadziona kuti ndi achabechabe chifukwa cha zimene amalakwitsa. Komabe, nthawi zina mkulu zingamuvute kukhala wodzichepetsa kapena kuzindikira malire ake. Mwachitsanzo, iye angavomere ntchito zosiyanasiyana zomwe wapatsidwa koma n’kumalephera kuzikwaniritsa. Kapena angamaimbidwe mlandu chifukwa cha mmene wachitira zinthu zina kapenanso angamatamandidwe chifukwa cha mmene wagwirira ntchito inayake. Kodi akulu angaphunzire chiyani kwa Gidiyoni, chomwe chingawathandize pa zochitika ngati zimenezi?

Potsanzira Gidiyoni, mkulu yemwe ndi wodzichepetsa akupempha malangizo a mmene angachitire ulaliki wapashelefu (Onani ndime 6)

6. Kodi akulu angaphunzire chiyani kwa Gidiyoni pa nkhani yozindikira malire awo? (Onaninso chithunzi.)

6 Muzipempha ena kuti akuthandizeni. Munthu amene amazindikira malire ake amadziwa zimene sangakwanitse. Gidiyoni ankadziwa zomwe sangakwanitse popempha ena kuti amuthandize. (Ower. 6:27, 35; 7:24) Akulu anzeru amachitanso chimodzimodzi. Tony, yemwe tamutchula koyambirira kuja, anafotokoza kuti: “Chifukwa cha mmene ndinaleredwera, ndinkakonda kuvomera ntchito zambiri kuposa zimene ndingakwanitse kugwira. Choncho ndinaganiza kuti pakulambira kwathu kwa pabanja tikambirane nkhani yokhudza kuzindikira malire athu komanso ndinafunsa mkazi wanga kuti andifotokozere mmene ndimachitira pa nkhaniyi. Ndinaoneranso pa jw.org vidiyo yakuti Muziphunzitsa, Kukhulupirira Komanso Kuthandiza Ena Ngati Mmene Yesu Amachitira.” Tony anayamba kupempha ena kuti azimuthandiza ntchito zomwe anali nazo. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Tony anati: “Panopa ntchito zonse mumpingo zimayenda bwino ndipo inenso ndimapeza nthawi yambiri yolimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova.”

7. Kodi akulu angatsanzire bwanji Gidiyoni, ena akamawaimba mlandu? (Yakobo 3:13)

7 Musamakwiye ena akamakuimbani mlandu. Nthawi zina, akulu angayesedwe pamene akuimbidwa mlandu chifukwa cha zimene achita. Apanso chitsanzo cha Gidiyoni chingawathandize. Iye ankadziwa kuti nayenso ankalakwitsa zinthu, ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti ayankhe modekha pamene amuna a ku Efuraimu ankamuimba mlandu. (Ower. 8:1-3) Gidiyoni sanayankhe mokwiya. Iye anasonyeza kuti anali wodzichepetsa powamvetsera komanso kulankhula nawo mokoma mtima, zomwe zinachititsa kuti mitima ya anthuwo ikhale m’malo. Akulu anzeru amatsanzira Gidiyoni pomvetsera mosamala komanso kuyankha modekha akamaimbidwa mlandu. (Werengani Yakobo 3:13.) Akamachita zimenezi amathandiza kuti mumpingo mukhale mtendere.

8. Kodi akulu ayenera kutani ena akamawatamanda? Perekani chitsanzo.

8 Muzilola kuti ulemerero wonse uzipita kwa Yehova. Pamene anthu anayamba kutamanda Gidiyoni chifukwa chopambana pankhondo yolimbana ndi Amidiyani, iye anathandiza anthuwo kuti apereke ulemerero kwa Yehova. (Ower. 8:22, 23) Kodi abale audindo angatsanzire bwanji Gidiyoni? Iwo ayenera kupereka ulemerero kwa Yehova chifukwa cha zimene akwanitsa kuchita. (1 Akor. 4:6, 7) Mwachitsanzo, ngati mkulu akutamandidwa chifukwa cha luso lophunzitsa lomwe ali nalo, iye angathandize anthuwo kuti aziganizira kumene kukuchokera mfundo zomwe amaphunzitsazo, komwe ndi m’Mawu a Mulungu, kapena maphunziro omwe gulu la Yehova limapereka. Nthawi ndi nthawi, akulu ayenera kumadzifufuza kuti aone ngati akuchititsa anthu kuti azitamanda iwowo m’malo mwa Yehova. Taganizirani zomwe zinachitikira mkulu wina dzina lake Timothy. Atangoikidwa kumene kukhala mkulu, ankasangalala kukamba nkhani za onse. Iye anati: “Ndinkayamba nkhani zanga ndi mawu ambirimbiri ndiponso ndinkagwiritsa ntchito zitsanzo zovuta kumvetsa. Zimenezi zinkachititsa kuti ena azinditamanda. Choncho anthu ankaganizira kwambiri za ineyo m’malo moganizira za Baibulo kapena Yehova.” M’kupita kwa nthawi, Timothy anaona kuti ankafunika kusintha mmene ankaphunzitsira kuti asamachititse ena kuti azingoganizira za iyeyo. (Miy. 27:21) Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Iye anafotokoza kuti: “Panopa abale ndi alongo ambiri amandiuza mmene nkhani yanga yawathandizira kulimbana ndi mavuto awo, kupirira mayesero kapena kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ndimasangalala ndi zimene amalankhulazo kuposa mmene ndinkasangalalira pa nthawi imene ankanditamanda zaka zambiri zapitazo.”

PAMENE KUMVERA KAPENA KULIMBA MTIMA KUNGAKHALE KOVUTA

Gidiyoni anamvera Yehova ndipo anachepetsa chiwerengero cha asilikali ake posankha amuna 300 omwe anasonyeza kuti ndi atcheru (Onani ndime 9)

9. Kodi kumvera komanso kulimba mtima kwa Gidiyoni kunayesedwa bwanji? (Onani chithunzi chapachikuto.)

9 Gidiyoni ataikidwa kukhala woweruza ankafunika kukhala womvera komanso wolimba mtima. Iye anapatsidwa ntchito yovuta yoti akagwetse guwa lansembe la bambo ake, lomwe ankalambirirapo Baala. (Ower. 6:25, 26) Kenako atasonkhanitsa asilikali, kawiri konse iye anauzidwa kuti achepetse chiwerengero chawo. (Ower. 7:2-7) Pamapeto pake, anauzidwa kuti akaukire adani awo pakati pa usiku.​—Ower. 7:9-11.

10. Kodi mkulu angayesedwe bwanji pa nkhani ya kumvera?

10 Akulu ayenera kukhala ‘okonzeka kumvera.’ (Yak. 3:17) Mkulu womvera amakhala wofunitsitsa kugonjera zimene Malemba amanena komanso kutsatira malangizo ochokera ku gulu la Mulungu. Akatero amapereka chitsanzo chabwino kwa ena. Koma ngakhale zili choncho, nthawi zina zingamuvute kuti amvere. Mwachitsanzo, mwina zingamuvute kutsatira malangizo amene aperekedwa. Pa zochitika zina, iye angamakayikire ngati malangizo enaake alidi anzeru kapena othandiza. Kapena mwina angapemphedwe kuti agwire ntchito inayake yomwe ingachititse kuti amangidwe. Kodi akulu angatsanzire bwanji Gidiyoni pa zochitika ngati zimenezi?

11. Kodi n’chiyani chingathandize akulu kukhala omvera?

11 Muzimvetsera malangizo mosamala komanso kuwagwiritsa ntchito. Mulungu anauza Gidiyoni mmene angagwetsere guwa lansembe la bambo ake, kumene angamange guwa lansembe la Yehova komanso nyama yomwe ankafunika kupereka nsembe. Gidiyoni sanakayikire n’komwe malangizo omwe anapatsidwawa, anangowatsatira. Masiku ano akulu amalandira malangizo kuchokera ku gulu la Yehova kudzera m’makalata, zilengezo komanso malangizo ena otithandiza kukhala otetezeka ndiponso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Timakonda kwambiri akulu chifukwa chotsatira mokhulupirika malangizo omwe gulu la Yehova limapereka ndipo mpingo wonse umapindula.​—Sal. 119:112.

12. Kodi akulu angatsatire bwanji malangizo a pa Aheberi 13:17, ngati malangizo a gulu asintha?

12 Muzikhala okonzeka kusintha. Kumbukirani kuti Yehova analamula Gidiyoni kuti achepetse kwambiri chiwerengero cha asilikali ake. (Ower. 7:8) Iye akanatha kuganiza kuti, ‘Koma kodi ndikufunikadi kuchita zimenezi? Kodi n’zothandiza?’ Ngakhale zinali choncho, Gidiyoni anamvera. Masiku anonso, akulu amatsanzira Gidiyoni potsatira malangizo a gulu la Yehova amene asintha. (Werengani Aheberi 13:17.) Mwachitsanzo, mu 2014, Bungwe Lolamulira linasintha njira yolipirira ndalama zomangira Nyumba za Ufumu komanso Malo a Misonkhano. (2 Akor. 8:12-14) Mipingo siinkafunikanso kubweza ngongole. M’malomwake, zopereka za mipingo padziko lonse zinayamba kumagwiritsidwa ntchito pomangira malowa kulikonse kumene akufunikira, posatengera kuti mipingo ina siingakwanitse kulipira ndalama zonse. José atamva za kusinthaku anakayikira ngati izi zingakhaledi zothandiza, ndipo ankaganiza kuti: ‘Umu si mmene zinthu zimachitikira kwathu kuno. Sizidzatheka kumanga ngakhale nyumba imodzi.’ Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza José kutsatira malangizowa? Iye anati: “Mawu a pa Miyambo 3:5, 6 anandikumbutsa kuti ndiyenera kumakhulupirira Yehova. Zotsatirapo zake n’zakuti zinthu zakhala zikuyenda bwino kwambiri. Sikuti tikungomanga Nyumba za Ufumu zambiri, koma taphunziranso mmene tingathandizire m’njira zosiyanasiyana ndi zopereka zathu kuti pakhale kufanana.”

Ngakhale pamene boma laletsa ntchito yathu, tikhoza kumalalikirabe molimba mtima (Onani ndime 13)

13. (a) Kodi Gidiyoni sankakayikira za chiyani? (b) Kodi akulu angamutsanzire bwanji? (Onaninso chithunzi.)

13 Molimba mtima, muzichita zimene Yehova amafuna. Gidiyoni anamvera ngakhale kuti ankachita mantha komanso zimene ankafunika kuchitazo zinali zoopsa. (Ower. 9:17) Yehova atamutsimikizira, Gidiyoni sankakayikira kuti Mulungu adzamuthandiza akamadzamenya nkhondo yoteteza anthu a Yehova. Akulu amene amakhala m’madera omwe ntchito yathu ndi yoletsedwa amatsanzira Gidiyoni. Molimba mtima, iwo amatsogolera pamisonkhano komanso pa ntchito yolalikira ngakhale kuti akhoza kumangidwa, kufunsidwa mafunso, kuchitiridwa zachiwawa kapenanso kuchotsedwa ntchito. c Pa nthawi ya chisautso chachikulu, akulu adzafunika kulimba mtima kuti adzatsatire malangizo omwe adzapatsidwe posatengera kuti akumana ndi zoopsa zotani. Malangizowa angadzakhale okhudza mmene angadzalengezere uthenga wokhala ngati matalala komanso mmene abale ndi alongo angadzapulumukire akamadzaukiridwa ndi Gogi wa ku Magogi.​—Ezek. 38:18; Chiv. 16:21.

PAMENE KUPIRIRA KUNGAKHALE KOVUTA

14. Kodi Gidiyoni anayesedwa bwanji pa nkhani ya kupirira?

14 Gidiyoni ankafunika kuchita zinthu mwakhama pa ntchito yake monga woweruza. Amidiyani atathawa usiku pankhondo, iye anawathamangitsa kuchokera kuchigwa cha Yezereeli mpaka kukafika kumtsinje wa Yorodano, komwe n’kutheka kuti kunali kowirira. (Ower. 7:22) Ndiye kodi Gidiyoni anasiya kuwathamangitsa atafika kumtsinjeko? Ayi. Ngakhale kuti anali atatopa, iye ndi amuna 300 omwe anali nawo anawoloka mtsinjewo n’kupitiriza kuwathamangitsa. Pamapeto pake anawapeza ndipo anawagonjetsa.​—Ower. 8:4-12.

15. Kodi ndi pa nthawi iti pomwe kupirira kungakhale kovuta kwa akulu?

15 Nthawi zina mkulu angamamve kuti watopa kwambiri chifukwa cha ntchito zimene wagwira mumpingo kapenanso posamalira banja lake. Pa zochitika ngati zimenezi, kodi akulu angatsanzire bwanji Gidiyoni?

Akulu achikondi akhala akulimbikitsa abale ndi alongo ambiri omwe akufunika thandizo (Onani ndime 16-17)

16-17. Kodi n’chiyani chinathandiza Gidiyoni kupirira, nanga akulu angakhale otsimikiza za chiyani? (Yesaya 40:28-31) (Onaninso chithunzi.)

16 Muzikhulupirira kuti Yehova adzakupatsani mphamvu. Gidiyoni ankakhulupirira kuti Yehova amupatsa mphamvu, ndipo sanagwiritsidwe fuwa la moto. (Ower. 6:14, 34) Gidiyoni ndi asilikali ake ankathamangitsa wapansi mafumu awiri a ku Midiyani, omwe mwina anali atakwera ngamila. (Ower. 8:12, 21) Komabe mothandizidwa ndi Mulungu, Aisiraeli akhamawa anapambana pankhondoyo. Mofananamo, akulu angamadalire Yehova yemwe “satopa kapena kufooka.” Iye adzawapatsa mphamvu pamene afooka.​—Werengani Yesaya 40:28-31.

17 Taganizirani zomwe zinachitikira Matthew, yemwe ali m’Komiti Yolankhulana ndi Achipatala. Kodi n’chiyani chimamuthandiza kupirira? Iye anati: “Ndaona kuti mfundo ya pa Afilipi 4:13 ndi yoona. Nthawi zambiri ndikatopa komanso ndikamaona kuti sindingathenso kuchita zina ndimapemphera kuchokera pansi pa mtima. Ndimapempha Yehova kuti andipatse mphamvu zomwe ndikufunikira kuti ndithandize abale ndi alongo anga. Pa zochitika ngati zimenezi ndaona kuti mzimu wa Yehova umandipatsa mphamvu zomwe zimandithandiza kuti ndipirire.” Mofanana ndi Gidiyoni, akulu odzipereka angakumane ndi mavuto pomwe akuweta nkhosa za Yehova. N’zoona kuti iwo amafunika kuzindikira zomwe sangakwanitse, n’kumachita zomwe angathe. Komabe iwo angamakhulupirire kuti Yehova adzamva mapemphero awo opempha kuti awathandize ndi kuwapatsa mphamvu zoti apirire.​—Sal. 116:1; Afil. 2:13.

18. Mogwirizana ndi zimene taphunzira, kodi akulu angatsanzire bwanji Gidiyoni?

18 Pali zambiri zimene akulu angaphunzire kwa Gidiyoni. Akulu ayenera kudziwa zimene sangakwanitse komanso kukhala odzichepetsa pa nkhani ya ntchito zimene amagwira ndiponso ena akamawaimba mlandu kapena kuwatamanda. Iwo ayenera kusonyeza kuti ndi omvera komanso olimba mtima makamaka pamene mapeto a dziko loipali akuyandikira kwambiri. Ayenera kumakhulupirira kuti kaya akumana ndi mavuto otani, Mulungu adzawapatsa mphamvu. Timayamikira kwambiri abusa akhamawa ndipo ‘abale okhala ngati amenewa tiziwalemekeza kwambiri.’​—Afil. 2:29.

NYIMBO NA. 120 Tikhale Ofatsa Ngati Khristu

a Gidiyoni anasankhidwa ndi Yehova kuti azitsogolera komanso kuteteza anthu a Mulungu pa nthawi yovuta kwambiri mumbiri ya Aisiraeli. Iye anachita utumikiwu mokhulupirika kwa zaka pafupifupi 40. Komabe iye anakumana ndi mavuto ambiri. Tikambirana mmene chitsanzo chake chingathandizire akulu masiku ano akamakumana ndi mavuto.

b Kudziwa malire athu n’kogwirizana ndi kudzichepetsa. Timasonyeza kuti tikuzindikira malire athu podziona moyenera n’kumadziwa kuti pali zina zomwe sitingakwanitse. Timasonyeza kuti ndife odzichepetsa tikamalemekeza ena komanso kuwaona kukhala otiposa. (Afil. 2:3) Kawirikawiri, munthu amene amazindikira zomwe sangakwanitse amakhalanso wodzichepetsa.

c Onani nkhani yakuti, “Tizilambirabe Yehova Ngakhale Boma Litatiletsa” mu Nsanja ya Olonda ya July 2019, tsamba 10-11, ndime 10-13.