Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata, Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?

Achinyamata, Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?

“Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo?”—LUKA 14:28.

NYIMBO: 120, 64

Nkhaniyi ndiponso yotsatira alembera achinyamata amene akuganizira zobatizidwa

1, 2. (a) Kodi tonsefe timasangalala ndi chiyani? (b) Kodi makolo komanso akulu angathandize bwanji achinyamata kuti akonzekere kubatizidwa?

MKULU wina anauza mnyamata wazaka 12, dzina lake Christopher, kuti: “Ndinakudziwa kuyambira uli wakhanda ndipo ndasangalala kuti ukufuna kubatizidwa. Komabe n’takufunsa, ‘N’chifukwa chiyani ukufuna kubatizidwa?’” Zimene mkuluyu anafunsazi n’zomveka. Tonsefe timasangalala kwambiri kuona kuti chaka chilichonse achinyamata ambiri amabatizidwa padziko lonse. (Mlal. 12:1) Komabe akulu ndiponso makolo achikhristu ayenera kuonetsetsa kuti achinyamatawa amasankha kubatizidwa chifukwa choti adziperekadi kwa Mulungu ndipo akudziwa zimene akuchita.

2 Baibulo limasonyeza kuti munthu akadzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa, amadalitsidwa kwambiri ndi Yehova koma amatsutsidwa ndi Satana. (Miy. 10:22; 1 Pet. 5:8) Choncho makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kuti azidziwa bwino udindo umene Mkhristu amakhala nawo. Nawonso akulu ayenera kuthandiza achinyamata amene makolo awo si Mboni kuti adziwe udindowu n’cholinga choti akonzekere bwino. (Werengani Luka 14:27-30.) Munthu amene akufuna kumanga nyumba, amafunika kukonzekera kuti adzaimalize bwino. N’chimodzimodzinso ndi kutumikira Yehova. Tiyenera kukonzekera bwino kuti tithe kumutumikira “mpaka pa mapeto.” (Mat. 24:13) M’nkhaniyi tikambirana zimene achinyamata angachite pokonzekera kuti athe kutumikira Yehova kwa moyo wawo wonse.

3. (a) Kodi mawu a Yesu komanso a Petulo akutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kubatizidwa? (Mat. 28:19, 20; 1 Pet. 3:21) (b) Kodi tikambirana mafunso ati, ndipo n’chifukwa chiyani mafunsowa ndi ofunika?

3 Kodi ndinu wachinyamata ndipo mukuganizira zobatizidwa? Ngati ndi choncho, mukuchita bwino kwambiri chifukwa ndi mwayi waukulu kubatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Ndipotu kubatizidwa n’kofunika kwambiri kwa Mkhristu chifukwa kungamuthandize kuti adzapulumuke. (Mat. 28:19, 20; 1 Pet. 3:21) Koma munthu akabatizidwa amayenera kukwaniritsa zimene analonjeza kwa Yehova, choncho ndi bwino kukonzekera musanabatizidwe. Kuti muone ngati ndinu wokonzeka kubatizidwa, mungadzifunse mafunso atatu awa: (1) Kodi ndine wokonzekadi kudzipereka kwa Yehova? (2) Kodi ndikufunadi kubatizidwa? (3) Kodi ndikudziwa kuti kudzipereka kwa Yehova kumatanthauza chiyani? Tiyeni tikambirane mafunso amenewa.

MUYENERA KUSONYEZA KUTI NDINU WOLIMBA

4, 5. (a) Kodi munthu ayenera kukhala wotani kuti abatizidwe? (b) Kodi wachinyamata angasonyeze bwanji kuti ndi wolimba?

4 Baibulo silinena kuti akuluakulu okha kapena munthu amene wafika zaka zinazake ndi amene ayenera kubatizidwa. Lemba la Miyambo 20:11 limati: “Mnyamata amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.” Achinyamata ena aang’ono amatha kudziwa zoyenera kuchita komanso amamvetsa bwino zimene kudzipereka kwa Mulungu kumatanthauza. Choncho achinyamata oterewa amasonyeza kuti ndi wolimba mwauzimu ndipo akhoza kudzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa.—Miy. 20:7.

5 Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti ndinu wolimba moti mukhoza kubatizidwa? Izi sizidalira msinkhu kapena zaka zanu zobadwa. Baibulo limasonyeza kuti anthu olimba, kapena kuti “okhwima mwauzimu,” ndi ‘amene aphunzitsa mphamvu zawo za kuzindikira kuti azitha kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ (Aheb. 5:14) Choncho munthu wolimba amazindikira zimene Yehova amafuna ndipo amatsimikiza mtima kuti azichita zimenezo. Satengeka ndi zinthu zoipa ndipo sachita kuuzidwa kuti azichita zoyenera. Ndiyetu wachinyamata amene akufuna kubatizidwa ayenera kukhala kuti amatsatira mfundo za m’Baibulo, ngakhale pamene makolo ake kapena anthu ena aakulu palibe.—Yerekezerani ndi Afilipi 2:12.

6, 7. (a) Fotokozani zimene Danieli anakumana nazo ku Babulo. (b) Kodi Danieli anasonyeza bwanji kuti anali wolimba?

6 Koma kodi n’zothekadi kuti achinyamata akhale olimba? Inde. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Danieli. N’kutheka kuti anali ndi zaka 13 kapena 14 zokha pamene anatengedwa n’kupita naye ku Babulo kopanda makolo ake. Kumeneko ankakhala ndi anthu amene sankalambira Mulungu. Koma panalinso vuto lina. Akuluakulu a ku Babulo ankaona kuti Danieli ndi munthu wofunika kwambiri. Ndipotu Danieli anali mmodzi wa achinyamata amene anasankhidwa kuti akaonekere kwa mfumu. (Dan. 1:3-5, 13) Choncho Danieli anapatsidwa mwayi umene mwina sakanaupeza kudziko lakwawo.

7 Koma kodi Danieli anatani? Kodi anatengeka ndi zinthu zimenezi? Nanga kodi iye analola kuti moyo umene ankakhala ku Babulo umulepheretse kutumikira Yehova mokhulupirika? Ayi. Baibulo limati, “Danieli anatsimikiza mumtima mwake kuti sadzidetsa” ndi chilichonse chokhudza kulambira milungu yonyenga. (Dan. 1:8) Apatu Danieli anasonyeza kuti anali wolimba.

Wachinyamata wolimba sachita zinthu ngati Mkhristu akakhala ku Nyumba ya Ufumu koma n’kumachita zinthu ngati anthu a m’dzikoli akakhala kusukulu (Onani ndime 8)

8. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Danieli?

8 Chinthu chimodzi chimene tikuphunzira pa chitsanzo cha Danieli n’chakuti, wachinyamata wolimba mwauzimu nthawi zonse amayesetsa kutsatira zimene amakhulupirira. Sakhala ngati bilimankhwe amene amasintha mtundu kuti agwirizane ndi malo amene ali. Mwachitsanzo, wachinyamata wolimba sachita zinthu ngati Mkhristu akakhala ku Nyumba ya Ufumu koma n’kumachita zinthu ngati anthu a m’dzikoli akakhala kusukulu. Satengekanso ndi makhalidwe oipa koma amakhalabe wokhulupirika ngakhale atakumana ndi mayesero.—Werengani Aefeso 4:14, 15.

9, 10. (a) Kodi n’chifukwa chiyani wachinyamata ayenera kuganizira zimene amachita akakumana ndi mayesero? (b) Kodi munthu akabatizidwa amasonyeza chiyani?

9 Kaya ndife achikulire kapena achinyamata, tonsefe timalakwitsa nthawi zina. (Mlal. 7:20) Komabe ngati mukufuna kubatizidwa, muyenera kuganizira zimene mumachita kuti muone ngati mukuyesetsa kutsatira mfundo za Yehova. Mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndakhala ndikutsatira bwinobwino zimene Mulungu amafuna? Kodi ndimatani ndikakumana ndi mayesero? Nanga kodi ndimasonyeza kuti ndimatha kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera? Kodi ndingatani ngati anthu a m’dzikoli atandiuza kuti ndili ndi luso ndipo ndikhoza kuchita zinazake zaphindu? Kodi nthawi zonse ‘ndimazindikira chifuniro cha Yehova,’ ngakhale pamene ndakumana ndi mayesero?’—Aef. 5:17.

10 N’chifukwa chiyani muyenera kudzifunsa mafunso amenewa? Chifukwa choti angakuthandizeni kudziwa ngati ndinu wokonzeka kubatizidwa. Paja ubatizo umasonyeza kuti munthu analonjeza Mulungu kuti azimukonda ndiponso kumutumikira ndi mtima wonse mpaka kalekale. (Maliko 12:30) Munthu akabatizidwa ayenera kuyesetsa kuti akwaniritse lonjezo limeneli.—Werengani Mlaliki 5:4, 5.

KODI MUKUFUNADI KUBATIZIDWA?

11, 12. (a) Kodi munthu amene akufuna kubatizidwa ayenera kutsimikizira za chiyani? (b) N’chiyani chingakuthandizeni kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya kubatizidwa?

11 Baibulo limati anthu a Mulungu, ngakhale achinyamata, “adzadzipereka mofunitsitsa” kuti amutumikire. (Sal. 110:3) Choncho munthu amene akuganiza zobatizidwa ayenera kutsimikizira kuti akufunadi ndi mtima wonse kubatizidwa. Munthuyo ayenera kudzifufuza bwinobwino kuti adziwe zimenezi. Kudzifufuza n’kofunika makamaka kwa achinyamata amene anakulira m’banja la Mboni.

12 N’kutheka kuti mwaona anzanu kapena achibale anu akubatizidwa. Komabe muyenera kusamala kuti musaganize kuti muyenera kubatizidwa chifukwa choti mwakwanitsa zaka zinazake kapena chifukwa choti anzanu onse akubatizidwa. Ndiye kodi mungatani kuti mukhale ndi maganizo oyenera pa nkhani imeneyi? Muyenera kuganizira kwambiri chifukwa chake munthu ayenera kubatizidwa. Nkhaniyi komanso yotsatira ikuthandizani kuchita zimenezi.

13. Kodi mungadziwe bwanji ngati mukufunadi kubatizidwa?

13 Pali zinthu zingapo zimene zingakuthandizeni kudziwa ngati mukufunadi kubatizidwa. Mwachitsanzo, mapemphero anu angasonyeze ngati mukufunadi kutumikira Yehova. Munthu amene ali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova amapemphera pafupipafupi ndipo amamuuza zakukhosi kwake. (Sal. 25:4) Nthawi zambiri Yehova amayankha mapemphero athu pogwiritsa ntchito Mawu ake. Choncho mukamaphunzira Baibulo mwakhama mumasonyezanso kuti mukufuna kutumikira Yehova ndi mtima wonse komanso kukhala naye pa ubwenzi wolimba. (Yos. 1:8) Ndiyeno mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimauza Yehova zakukhosi kwanga? Kodi ndimaphunzira Baibulo nthawi zonse?’ Komanso ngati banja lanu limachita Kulambira kwa Pabanja, mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimasangalala kuchita nawo zimenezi?’ Zimene mungayankhe pa mafunsowa zingakuthandizeni kudziwa ngati mukufunadi kubatizidwa.

KODI KUDZIPEREKA KUMATANTHAUZA CHIYANI?

14. Kodi kudzipereka kumasiyana bwanji ndi kubatizidwa?

14 Anthu ena satha kusiyanitsa pakati pa kudzipereka ndi kubatizidwa. Mwachitsanzo, achinyamata ena amati anadzipereka kwa Yehova koma sanakonzeke kuti abatizidwe. Kodi zimenezi n’zomveka? Ayi, chifukwa munthu akadzipereka kwa Yehova ndiye kuti wamulonjeza kuti akufuna kumutumikira moyo wake wonse. Ndiyeno pamene akubatizidwa amakhala akuuza anthu onse kuti anapemphera kwa Yehova ndipo anamulonjeza kuti wadzipereka kwa iye. Choncho ubatizo umathandiza anthu kudziwa kuti munthuyo anadzipereka. Koma munthu aliyense asanabatizidwe amafunika kumvetsa kuti kudzipereka kumatanthauza chiyani.

15. Kodi kudzipereka kumatanthauza chiyani?

15 Mwachidule tingati, munthu akadzipereka kwa Yehova amakhala kuti wasankha zoti azichita zofuna za Yehovayo osati zake. Amalonjeza kuti aziyesetsa kuti zinthu zina zisamamulepheretse kuchita zimene Yehova amafuna. (Werengani Mateyu 16:24.) Munthu akalonjeza zinazake amafunika kukwaniritsa. Choncho n’kofunika kwambiri kuti tizikwaniritsa zimene tinalonjeza kwa Yehova. (Mat. 5:33) Koma kodi mungasonyeze bwanji kuti munadziperekadi kwa Yehova ndipo mukufuna kuchita zofuna zake osati zanu?—Aroma 14:8.

16, 17. (a) Kodi munthu angasonyeze bwanji kuti anadziperekadi kwa Yehova? Perekani chitsanzo. (b) Kodi munthu akadzipereka kwa Yehova amakhala kuti wamuuza chiyani?

16 Tiyerekeze kuti munthu wina wakugulirani galimoto ngati mphatso. Ndiyeno akukupatsani mapepala osonyeza kuti galimotoyo ndi yanu koma kenako akukuuzani kuti: “Koma makiyi ndizisunga ndine ndipo ndiziyendetsanso galimotoyi ndi ineyo.” Kodi mungamve bwanji? Kodi mungaganize kuti munthuyo wakupatsanidi galimotoyo ndi mtima wonse?

17 Kodi mukuganiza kuti Mulungu amayembekezera chiyani kwa munthu amene anadzipereka kwa iye? Nanga angamve bwanji ngati munthuyo atayamba moyo wachiphamaso, mwina kuchita chibwenzi ndi munthu woti si Mboni? Komanso angamve bwanji ngati munthuyo atayamba ntchito yomwe ikumulepheretsa kupeza nthawi yokwanira yolalikira kapena yosonkhana? Kodi zimenezi sizingafanane ndi kugulira munthu galimoto koma n’kukana kumupatsa makiyi? Paja munthu akadzipereka amakhala kuti wauza Yehova kuti: “Ndikupereka moyo wanga kwa inu, ndipo tsopano ndine wanu. Ndimaona kuti zofuna zanu ndi zofunika kwambiri kuposa zanga ndipo ndiziyesetsa kuchita zofuna zanuzo nthawi zonse.” Maganizo amenewa ndi ofanana ndi amene Yesu anali nawo. Paja iye anati: “Ndinatsika kuchokera kumwamba kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa.”—Yoh. 6:38.

18, 19. (a) Kodi zimene ananena Rose komanso Christopher zikusonyeza bwanji kuti munthu akabatizidwa amapeza madalitso ambiri? (b) Kodi inuyo muli ndi maganizo otani pa nkhani ya kubatizidwa?

18 Apa n’zoonekeratu kuti sitiyenera kuganiza kuti kubatizidwa ndi nkhani yaing’ono. Komabe tizidziwanso kuti ndi mwayi waukulu kudzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa. Achinyamata amene amakonda Yehova ndiponso amamvetsa zimene kudzipereka kumatanthauza, sazengereza kubatizidwa. Komanso sanong’oneza bondo pambuyo poti abatizidwa. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Rose anati: “Ndimakonda Yehova ndipo ndimaona kuti palibe chosangalatsa kwambiri kuposa kumutumikira. Sindinong’oneza bondo ngakhale pang’ono kuti ndinasankha kubatizidwa.”

19 Christopher amene tamutchula koyambirira uja anabatizidwa ali ndi zaka 12 ndipo zikuoneka kuti analidi atakonzekera chifukwa akusangalalabe ndi zimene anasankhazi. Pamene anali ndi zaka 17, anayamba upainiya wokhazikika, atafika zaka 18 anakhala mtumiki wothandiza ndipo panopa akutumikira pa Beteli. Christopher anati: “Ndinachita bwino kubatizidwa. Panopa ndikusangalala kwambiri ndi ntchito imene ndikugwira potumikira Yehova komanso anthu ake.” Ngati inunso mukuganiza zodzabatizidwa, kodi mungakonzekere bwanji? Nkhani yotsatira idzayankha funso limeneli.