Dzina la M’Baibulo Linapezeka Pamtsuko Wakale
Mu 2012 anthu ofukula zinthu zakale anapeza mapale a mtsuko winawake womwe unaumbidwa zaka 3,000 zapitazo. Anthuwa anasangalala kwambiri ataona zimene zinalembedwa pamapalewo.
Atalumikiza mapalewo anapeza kuti pamtsukowo panalembedwa mawu achikanani. Mawu ake anali oti: “Esibaala Ben Beda” kutanthauza kuti “Esibaala mwana wa Beda.” Aka kanali koyamba kuti anthu apeze dzinali m’zinthu zakale.
Baibulo limatchulanso munthu wina dzina lake Esibaala. Munthuyu anali mwana wa Mfumu Sauli. (1 Mbiri 8:33; 9:39) Pulofesa wina amene anali m’gulu la ofukulawa anati: “N’zochititsa chidwi kuti dzina loti Esibaala, lomwe limapezeka m’Baibulo lapezekanso pamapalewa ndipo zikusonyeza kuti linkagwiritsidwa ntchito pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Davide.” Apanso zinthu zimene ofukula zakale apeza zatsimikizira kuti Baibulo ndi lolondola.
M’Baibulo, mwana wa Sauli dzina lake Esibaala amatchedwanso Isi-boseti. Izi zikusonyeza kuti mawu oti “baala” anawasintha n’kuika oti “boseti.” (2 Sam. 2:10) N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Ofufuza zinthu zakale amanena kuti wolemba buku la 2 Samueli sanafune kugwiritsa ntchito dzina loti Esibaala poopa kuti anthu aziganizira za mulungu wa mphepo wa Akanani dzina lake Baala. Koma dzina loti Esibaala limapezeka m’buku la 1 Mbiri.