Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumakhalabe Bwenzi Labwino Zinthu Zikavuta?

Kodi Mumakhalabe Bwenzi Labwino Zinthu Zikavuta?

M’bale Gianni ndi M’bale Maurizio ankagwirizana kwambiri kwa zaka pafupifupi 50. Koma kenako panachitika zinthu zina zimene zikanasokoneza ubwenzi wawo. A Maurizio anati: “Nthawi ina zinthu zitandisokonekera, ndinalakwitsa zinazake ndipo zinachititsa kuti tisiye kugwirizana.” A Gianni anati: “A Maurizio ndi amene anandiphunzitsa Baibulo. Ankandipatsa chitsanzo chabwino ndipo ankandithandiza kwambiri. Choncho atachita zinthu zina zolakwika, sindinamvetse. Ndinkangoona ngati dziko latha chifukwa ndinkadziwa kuti zisokoneza ubwenzi wathu. Ndinkaona kuti mnzangayu wanditaya.”

KUKHALA ndi mnzako wapamtima ndi chinthu chamtengo wapatali, ndipo pamafunika khama kuti ubwenzi woterewu upitirire. Kodi tiyenera kutani ngati pachitika zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu? Kuti tiyankhe funsoli tiyeni tikambirane zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene ankagwirizana kwambiri koma kenako panachitika zinthu zomwe zikanasokoneza ubwenzi wawo.

MNZATHU AKALAKWITSA ZINAZAKE

Paja Davide anali m’busa komanso mfumu choncho ayenera kuti anali ndi anzake apamtima ambiri. Mwina mukukumbukira za Yonatani. (1 Sam. 18:1) Koma Davide ankagwirizananso kwambiri ndi mneneri Natani. Baibulo silinena kuti ubwenzi wawo unayamba liti. Koma pa nthawi ina, Davide anauza Natani zakukhosi kwake ngati mmene mabwenzi amachitira. Iye ankafuna kumanga nyumba ya Yehova. Mfumu Davide anamvera maganizo a Natani chifukwa anali mnzake komanso mzimu wa Yehova unali naye.—2 Sam. 7:2, 3.

Kenako panachitika zinazake zomwe zikanasokoneza ubwenzi wawo. Mfumu Davide inachita chigololo ndi Bati-seba ndipo inakonza zoti Uriya, mwamuna wa Bati-sebayo aphedwe. (2 Sam. 11:2-21) Davide anali atakhala wokhulupirika kwa Yehova kwa zaka zambiri ndipo ankachita zinthu mwachilungamo. Koma apa anachita machimo aakulu. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Davide achite izi? Kodi sankadziwa kuopsa kwake, kapena ankaganiza kuti angabisire Mulungu tchimo lake?

Ndiye kodi Natani akanatani? Kodi akanasiya kuti munthu wina ndiye akalankhule ndi mfumuyi? Kapena akanachita mantha poganiza kuti ngati Davide anapha Uriya wosalakwa akhoza kumuphanso iyeyo akafunsa za nkhaniyi? Mwinanso Natani akanaganiza kuti, ‘Anthu enanso akudziwa kuti Davide anakonza zoti Uriya aphedwe. Ndiye palibe chifukwa choti ineyo ndilowerere nkhaniyi n’kusokoneza ubwenzi wanga ndi Davide.’

Koma Natani anali mneneri wa Mulungu. Iye ankadziwa kuti akangokhala chete, chikumbumtima chake chizimuvutitsa komanso ubwenzi wake ndi Davideyo usokonekera. Zimene Davide anachita sizinasangalatse Yehova. Choncho ankafunika kuthandizidwa kuti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. Apa Davide ankafunika mnzake weniweni ndipo Natani anasonyeza kuti anali mnzake wabwino. Iye anakumbukira kuti poyamba Davide anali m’busa choncho anapeza fanizo labwino loti likamufike pa mtima. Natani anauza Davide uthenga wochokera kwa Mulungu m’njira yoti azindikire kukula kwa machimo ake, n’kusintha.2 Sam. 12:1-14.

Kodi inuyo mungatani mnzanu atalakwitsa zinazake kapena atachita tchimo lalikulu? Kodi mungalephere kumufunsa poopa kuti ubwenzi wanu usokonekera? Kapena kodi mungaganize kuti kuulula zimene wachitazo kwa akulu kusonyeza kuti ndinu wosakhulupirika kwa mnzanuyo?

A Gianni amene tawatchula poyamba paja anati: “Ndinazindikira kuti a Maurizio sankamasuka nanenso ngati poyamba. Ndinaganiza zokalankhula nawo ngakhale kuti zinali zovuta kwambiri. Ndinkadzifunsa kuti: ‘Kodi ndingakawauze chiyani chomwe sakuchidziwa? Mwinatu angandikwiyire kwambiri.’ Koma nditakumbukira zimene tinkakambirana pophunzira Baibulo, ndinalimba mtima n’kukalankhula nawo. Ndinakumbukiranso kuti nawonso ankandithandiza zikandivuta. Sikuti ndinkafuna kuti ubwenzi wathu usokonekere koma ndinkafuna kuwathandiza popeza ndinkawakonda kwambiri.”

A Maurizio anati: “A Gianni analankhula moona mtima ndipo ankanenadi zoona. Ndinkadziwa kuti si iwo kapena Mulungu amene anachititsa kuti ndikumane ndi zotsatira za zimene ndinachita. Choncho ndinalandira chilango chimene ndinapatsidwa ndipo patapita nthawi ubwenzi wanga ndi Yehova unayambanso kuyenda bwino.”

MNZATHU AKAKHALA PA MAVUTO

Davide ankagwirizananso ndi anthu ena amene anakhalabe okhulupirika kwa iye pa nthawi ya mavuto. Mmodzi mwa anthuwa anali Husai ndipo Baibulo limati iye anali “mnzake wa Davide.” (2 Sam. 16:16; 1 Mbiri 27:33) Husai ayenera kuti ankagwira ntchito kunyumba ya mfumuyi ndipo nthawi zina ankatumidwa kuchita zinthu zachinsinsi.

Pamene mwana wa Davide dzina lake Abisalomu ankafuna kulanda ufumu, Aisiraeli ambiri anakhala kumbali yake. Koma Husai anakhala kumbali ya Davide. Pamene Davide anathawa, Husai anapita naye limodzi. Davide anakhumudwa kwambiri poona kuti anthu amene ankawakhulupirira komanso mwana wake weniweni amuukira. Koma Husai anakhalabe wokhulupirika kwa Davide ndipo anaika moyo wake pachiswe n’kuchita zimene Davide anamuuza kuti chiwembu cha Abisalomu chilephereke. Sikuti Husai anangochita izi chifukwa choti ankagwira ntchito kwa mfumu. Koma n’chifukwa choti anali wokhulupirika kwa mnzakeyu.2 Sam. 15:13-17, 32-37; 16:15-23;17:16.

Masiku anonso n’zosangalatsa kuona kuti abale ndi alongo amagwirizana kwambiri. Iwo amachitirana zabwino osati chifukwa choti ali ndi udindo wochita zimenezi basi, koma chifukwa chokondana. Akamachita zimenezi amasonyeza kuti samangokonda mnzawoyo mwamwambo, koma amamuona kuti ndi wofunika kwambiri.

Izi n’zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake Federico. Mnzake wina dzina lake Antonio anamuthandiza kwambiri pamene zinthu zinamusokonekera. Federico anati: “Antonio atasamukira mumpingo wathu, tinayamba kucheza. Tonse tinali atumiki othandiza ndipo tinkachitira zinthu limodzi. Pasanapite nthawi, Antonio anakhala mkulu. Iye anali mnzanga wapamtima komanso ndinkayesetsa kutengera chitsanzo chake.” Koma kenako Federico anachita tchimo. Iye anafotokozera akulu za tchimo lakelo ndipo anamuthandiza. Komabe sanayenererenso kukhala mpainiya kapena mtumiki wothandiza. Ndiye kodi Antonio anatani?

Federico atakumana ndi mavuto, Antonio ankamumvetsera komanso kumulimbikitsa

Federico anati: “Ndinkaona kuti Antonio akundimvera chisoni ndipo anayesetsa kundithandiza. Ankandilimbikitsa kuti ndikonze ubwenzi wanga ndi Yehova ndipo sanandisiye pa nthawi yovutayi. Ankandiuza kuti ndisataye mtima.” Antonio anati: “Ndinkayesetsa kupeza nthawi yambiri yocheza ndi Federico. Ndinkafuna kuti azimasuka kundiuza chilichonse komanso mmene akumvera.” Patapita nthawi, Federico anakhalanso mpainiya komanso mtumiki wothandiza. Antonio anati: “Ngakhale kuti panopa ine ndi Federico tili m’mipingo yosiyana, timagwirizanabe kwambiri.”

KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

Kodi mungamve bwanji ngati mnzanu atakusiyani pa nthawi imene mwakumana ndi mavuto? Izitu zingakhale zowawa kwambiri. Kodi mnzanu wotereyu mungamukhululukire? Nanga kodi ubwenzi wanu ungakhalebe wolimba ngati poyamba?

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira Yesu. Iye ankagwirizana ndi atumwi ake okhulupirika ndipo anakhala nawo nthawi yaitali. Yesu anafika powatchula kuti anzake. (Yoh. 15:15) Koma Yesu atamangidwa, atumwi akewo anamuthawa. Petulo ananena pagulu kuti sangasiye Yesu, koma usiku womwewo anakana zoti amamudziwa.Mat. 26:31-33, 56, 69-75.

N’zoona kuti Yesu ankadziwa kuti akumana ndi mayesero omaliza ali yekhayekha. Komabe akanatha kukhumudwa mwinanso kukwiya chifukwa cha zimene atumwi akewa anachita. Koma Yesu sanachite zimenezi. Iye ataukitsidwa sanasonyeze kuti wakhumudwa, wakwiya kapena wataya mtima. Komanso sanayambe kuwakumba atumwiwo ponena kuti anamuthawa komanso kuti ankalakwitsa zinthu zina.

M’malomwake analimbikitsa Petulo ndi atumwi enawo. Iye anasonyeza kuti amawadalira ndipo anawapatsa malangizo owathandiza kugwira ntchito yofunika kwambiri padziko lonse yophunzitsa anthu. Yesu ankaona kuti atumwiwo ndi anzakebe. Chikondi chimene anawasonyeza chinawakhudza kwambiri moti anayesetsa kuti asakhumudwitsenso Mbuye wawoyo. Atumwiwo anagwira bwino ntchito imene Yesu anawasiyira.Mac. 1:8; Akol. 1:23.

Mlongo wina dzina lake Elvira amakumbukirabe zimene zinachitika atasiyana maganizo ndi mnzake wina dzina lake Giuliana. Iye anati: “Ndinadabwa kwambiri mnzangayo atandiuza kuti wakhumudwa ndi zimene ndinachita. Mlongoyu akanandikwiyira zikanakhala zomveka. Koma ndinadabwa kuona kuti ankaganizira kwambiri za ineyo komanso mavuto amene ndingakumane nawo ndikapitiriza khalidwe langalo. Ndimayamikira kwambiri kuti sankaganizira kwambiri zimene ndinamulakwira koma mavuto amene ndingakumane nawo. Ndimathokoza Yehova kuti ndinapeza mnzanga amene amaganizira zofuna zanga osati zake.”

Malinga ndi zimene takambiranazi, kodi munthu angatani kuti akhalebe bwenzi labwino zinthu zikavuta? Ayenera kukambirana ndi mnzakeyo momasuka koma mokoma mtima. Akatero adzakhala ngati Natani ndi Husai amene anakhalabe okhulupirika pa nthawi yovuta komanso ngati Yesu amene anakhululukira atumwi ake. Ndiye kodi inuyo mungachite zimenezi?