Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ubwino​—Kodi Tingatani Kuti Tikhale ndi Khalidweli?

Ubwino​—Kodi Tingatani Kuti Tikhale ndi Khalidweli?

ALIYENSE amafuna kudziwika kuti ndi munthu wabwino. Koma masiku ano, kukhala munthu wabwino si kophweka. Zili choncho chifukwa anthu ambiri ndi “osakonda zabwino.” (2 Tim. 3:3) Iwo amangoyendera zimene akuona kuti n’zabwino basi moti afika pomanena kuti “chabwino n’choipa ndipo choipa n’chabwino.” (Yes. 5:20) Ndipo aliyense amakhala ndi mavuto ake chifukwa cha uchimo komanso mmene tinakulira. Mwina tingakhale ndi maganizo ofanana ndi a mlongo wina dzina lake Anne. * Ngakhale kuti wakhala akutumikira Yehova kwa nthawi yaitali, iye ananena kuti: “Zimandivuta kukhulupirira kuti ndikhoza kukhala munthu wabwino.”

Koma chosangalatsa n’chakuti tonsefe tikhoza kukhala anthu abwino. Tikutero chifukwa ubwino ndi khalidwe limene mzimu woyera wa Mulungu umatulutsa. Mzimuwu ndi wamphamvu kwambiri kuposa uchimo umene tinatengera komanso zinthu zina zimene zingatilepheretse kukhala abwino. Tiyeni tikambirane za ubwino komanso tione zimene tingachite kuti tizisonyeza kwambiri khalidweli.

KODI TINGASONYEZE BWANJI KHALIDWELI?

Munthu wabwino amayesetsa kuchita zinthu zabwino. Makhalidwe ake amakhala abwino ndipo amapewa kuchita zoipa. Khalidweli limaonekera tikamachita zinthu zothandiza ena.

Mwina munaonapo anthu ena amene amayesetsa kuchitira anthu a m’banja mwawo komanso anzawo zinthu zabwino. Koma zinthu ngati zimenezi pazokha sizipangitsa munthu kukhala wabwino. N’zoona kuti sitingakwanitse kusonyeza khalidweli popanda kulakwitsa chifukwa si ife angwiro. Ndipo Baibulo limanena kuti: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.” (Mlal. 7:20) Paulo ananena moona mtima kuti: “Ndikudziwa kuti mwa ine, ndikunenatu za m’thupi langa simukhala kanthu kabwino.” (Aroma 7:18) Choncho kuti tikhale anthu abwino tiyenera kuphunzira kwa Yehova chifukwa iye ndiye kuchimake kwa khalidweli.

YEHOVA NDI WABWINO

Yehova Mulungu ndi woyenera kutiuza kuti izi n’zabwino izi n’zoipa. Baibulo limanena za Yehova kuti: “Inu ndinu wabwino ndipo mukuchita zabwino. Ndiphunzitseni malamulo anu.” (Sal. 119:68) Tiyeni tsopano tikambirane mbali ziwiri za ubwino wa Yehova zotchulidwa muvesili.

Yehova ndi wabwino. Yehova ndi wabwino ndipo sasintha khalidweli. Taganizirani zimene anauza Mose zakuti: “Ineyo ndidzakuonetsa ubwino wanga wonse.” Pamene ulemerero wa Yehova, kuphatikizapo ubwino wake, zinkadutsa, Mose anamva mawu akuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi. Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukira zolakwa ndi machimo, koma wosalekerera konse wolakwa osam’langa.” (Eks. 33:19; 34:6, 7) Mawu amenewa akutitsimikizira kuti Yehova amasonyeza ubwino pa zonse zimene amachita. Yesu nayenso anali wabwino kuposa munthu aliyense koma ananena kuti: “Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.”​—Luka 18:19.

Zinthu zimene Yehova analenga zimasonyeza kuti iye ndi wabwino

Zochita za Yehova zimakhala zabwino. Ubwino wa Yehova umaonekera mu zinthu zonse zimene amachita. Paja Baibulo limanena kuti: “Yehova amakomera mtima aliyense, ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.” (Sal. 145:9) Yehova amasonyeza ubwino mopanda tsankho. Iye anapereka moyo kwa anthu komanso zinthu zonse zothandiza kuti moyowo upitirire. (Mac. 14:17) Yehova amasonyezanso kuti ndi wabwino potikhululukira. Paja wolemba Masalimo ananena kuti: “Pakuti inu Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.” (Sal. 86:5) Tisamakayikire kuti “Yehova samana anthu oyenda mosalakwa chinthu chilichonse chabwino.”​—Sal. 84:11.

“PHUNZIRANI KUCHITA ZABWINO”

Anthufe tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu choncho tikhoza kuchita zinthu zabwino ndiponso kukhala anthu abwino. (Gen. 1:27) Komabe Mawu a Mulungu amalimbikitsa atumiki a Mulungu kuti ‘aphunzire kuchita zabwino.’ (Yes. 1:17) Koma kodi tingakulitse bwanji khalidwe limeneli mumtima mwathu? Pali zinthu zitatu zimene tingachite.

Choyamba, tiyenera kupempha mzimu woyera umene ungatithandize kukhala abwino kwambiri. (Agal. 5:22) Mzimu wa Mulungu ungatithandize kuti tizikonda zabwino n’kumadana ndi zoipa. (Aroma 12:9) Baibulo limasonyeza kuti Yehova angatithandize kuti tikhale olimba “muntchito yabwino iliyonse ndiponso m’mawu.”​—2 Ates. 2:16, 17.

Chachiwiri, tiyenera kuwerenga Mawu ouziridwa ndi Mulungu. Tikamachita zimenezi Yehova amatithandiza kudziwa “njira yonse ya zinthu zabwino.” (Miy. 2:9) Amatithandizanso kuti ‘tikhale okonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.’ (2 Tim. 3:17) Tikamawerenga Mawu a Mulungu komanso kuwaganizira kwambiri, zimathandiza kuti mumtima mwathu mudzaze zinthu zabwino zokhudza Mulungu ndi cholinga chake. Zikatero timawonjezera chuma mumtima mwathu chimene tingachigwiritse ntchito m’tsogolo.​—Luka 6:45; Aef. 5:9.

Chachitatu, tiyenera kuyesetsa kwambiri ‘kutsanzira zabwino.’ (3 Yoh. 11) M’Baibulo muli zitsanzo zabwino zimene tingatengere. Koma amene amapereka chitsanzo chabwino kwambiri ndi Yehova ndi Yesu. Palinso anthu ena amene amadziwika m’Baibulo kuti anali anthu abwino. Ena mwa iwo ndi Tabita ndi Baranaba. (Mac. 9:36; 11:22-24) Kuganizira nkhani zawo komanso zimene ankachitira anthu ena kungatithandize kuti tikhale anthu abwino. Kenako tiyenera kuganizira zimene tingachite kuti tithandize anthu a m’banja lathu komanso mumpingo. Tiziganiziranso madalitso amene Tabita ndi Baranaba anapeza chifukwa chokhala anthu abwino. Nanunso mukhoza kudalitsidwa kwambiri.

Masiku anonso pali anthu ambiri amene amachita zabwino. Mwachitsanzo, mumpingo timakhala ndi akulu amene amagwira ntchito mwakhama komanso, ‘amakonda zabwino.’ Palinso alongo okhulupirika amene mawu ndi zochita zawo zimasonyeza kuti ndi “aphunzitsi a zinthu zabwino.” (Tito 1:8; 2:3) Mlongo wina dzina lake Roslyn anati: “Ndili ndi mnzanga amene amachita chilichonse chimene angathe kuti athandize anthu mumpingo. Iye amaganizira mavuto amene anthu akukumana nawo ndipo nthawi zambiri amawapatsa mphatso kapena kuwathandiza m’njira zina. Ndimaona kuti mlongoyu ndi munthu wabwino kwambiri.”

Yehova amalimbikitsa anthu ake kuti ‘aziyesetsa kuchita zabwino.’ (Amosi 5:14) Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timakonda mfundo zake ndipo mtima wofuna kuchita zabwino umakula.

Tiziyesetsa kukhala anthu abwino komanso kuchita zabwino

Tisamaganize kuti pamafunika kuchita zinthu zikuluzikulu zokhazokha kuti tikhale anthu abwino. Mwachitsanzo, popenta chithunzi chokongola munthu samangolemba chimzere chimodzi chokha kapena mizere iwiri ikuluikulu. M’malomwake amalemba timizere tambirimbiri tosiyanasiyana. Nafenso timasonyeza kuti ndife anthu abwino tikamachitira anzathu zinthu zing’onozing’ono zabwino.

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizikhala okonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino. (2 Tim. 2:21; Tito 3:1) Ngati timaganizira mmene zinthu zilili pa moyo wa anthu ena, tingathe kuzindikira zoyenera kuchita kuti asangalale komanso alimbikitsidwe. (Aroma 15:2) Tingathandize ena powapatsa zinthu zimene tili nazo. (Miy. 3:27) Tingaitane anthu kuti adzadye nafe kapenanso kuti tidzacheze nawo. Ngati wina wadwala tingapite kukamuona, kumulembera meseji yolimbikitsa kapena kumuimbira foni. Tiyenera kuyesetsa kupeza mpata woti tilankhule mawu “alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikire, kuti asangalatse owamva.”​—Aef. 4:29.

Tiyenera kutsanzira Yehova pochitira anthu onse zinthu zabwino komanso kukhala opanda tsankho. Ntchito yolalikira imathandiza kwambiri kuti tichitire zabwino anthu onse. Paja Yesu anatilamula kuti tizichitira zabwino ngakhale anthu amene amatida. (Luka 6:27) Tiziyesetsa kukhala anthu okoma mtima komanso abwino ndipo “palibe lamulo loletsa zinthu zoterezi.” (Agal. 5:22, 23) Tikamakhala ndi khalidwe labwino ngakhale pamene tikuyesedwa kapena kutsutsidwa, anthu amakopeka ndi choonadi ndipo amalemekeza Mulungu.​—1 Pet. 3:16, 17.

ZOTSATIRA ZA KUKHALA WABWINO

Baibulo limanena kuti “munthu wabwino adzakhutira ndi zotsatira za zochita zake.” (Miy. 14:14) Kodi zotsatira za kukhala wabwino ndi ziti? Tikamachitira ena zabwino, nawonso amatichitira zabwino. (Miy. 14:22) Ngakhale anthu ena asatichitire zabwino, ifeyo tikapitiriza kuwachitira zabwino timafewetsa mtima wawo moti amatha kusintha maganizo.​—Aroma 12:20.

Anthu ambiri aonapo zotsatira za kuchita zabwino komanso kupewa zoipa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Nancy. Iye anati: “Ndinali munthu wovuta, wachiwerewere komanso wopanda ulemu. Koma nditayamba kuphunzira komanso kutsatira mfundo za Mulungu ndinayamba kukhala wosangalala. Panopa ndimamva bwino ndipo ndine munthu waulemu wake.”

Chifukwa chachikulu chokhalira munthu wabwino n’chakuti tikamachita zimenezi timasangalatsa Yehova. Ngakhale anthu ena asaone zabwino zimene timachita, Yehova amaona. Iye amadziwa zabwino zonse zimene timachita kapena kuganiza. (Aef. 6:7, 8) Ndiye kodi zotsatira zake zimakhala zotani? Baibulo limanena kuti: “Munthu wabwino Yehova amakondwera naye.” (Miy. 12:2) Choncho tiyeni tiziyesetsa kukhala anthu abwino. Yehova walonjeza kuti adzapereka “ulemerero, ulemu ndi mtendere” kwa munthu aliyense wochita zabwino.​—Aroma 2:10.

^ ndime 2 Mayina ena asinthidwa.