NKHANI YOPHUNZIRA 11
Tizimvetsera Mawu a Yehova
“Uyu ndiye Mwana wanga . . . muzimumvera.”—MAT. 17:5.
NYIMBO NA. 89 Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1-2. (a) Kodi Yehova wakhala akulankhula ndi anthu m’njira ziti? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
YEHOVA amakonda kulankhula ndi anthufe. M’mbuyomu ankagwiritsa ntchito aneneri, angelo komanso Mwana wake, Khristu Yesu, pofuna kuti anthu adziwe maganizo ake. (Amosi 3:7; Agal. 3:19; Chiv. 1:1) Koma masiku ano amagwiritsa ntchito Baibulo lomwe ndi Mawu ake. Iye anatipatsa Baibulo n’cholinga choti tizidziwa maganizo ake komanso njira zake.
2 Yesu ali padzikoli, Yehova analankhula katatu kuchokera kumwamba. Tiyeni tsopano tikambirane zimene Yehova ananena. Tionanso ubwino wotsatira zimene ananenazo.
“IWE NDIWE MWANA WANGA WOKONDEDWA”
3. Malinga ndi Maliko 1:9-11, kodi Yehova ananena kuti chiyani Yesu atangobatizidwa, nanga m’mawu amenewo anatsimikizira mfundo zitatu ziti?
3 Lemba la Maliko 1:9-11 limafotokoza zimene zinachitika pa nthawi yoyamba imene Yehova analankhula. (Werengani.) Iye anati: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.” Yesu ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kumva Atate ake akulankhula mawu olimbikitsa komanso osonyeza kuti amamukonda. Mawu amene Yehova ananenawa anatsimikizira mfundo zitatu zofunika kwambiri zokhudza Yesu. Yoyamba ndi yakuti Yesu ndi Mwana wake. Yachiwiri ndi yakuti Yehova amakonda Mwana wakeyo. Ndipo yachitatu ndi yakuti Yehova amakondwera ndi Mwana wake. Tiyeni tikambirane bwinobwino mfundo zitatuzi.
4. Kodi chinachitika n’chiyani pamene Yesu anabatizidwa, nanga zinkatanthauza chiyani?
4 “Iwe ndiwe Mwana wanga.” Mawu amenewa anasonyeza Luka 1:31-33; Aheb. 1:8, 9; 2:17) Choncho m’pomveka kuti pa nthawi ya ubatizoyi, Yehova anauza Yesu kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga.”—Luka 3:22.
kuti ubwenzi wapadera unali utayambika pakati pa Yehova ndi Yesu. Yesu ali kumwamba anali mwana wauzimu wa Mulungu. Koma pa nthawi ya ubatizo wake, iye anadzozedwa ndi mzimu woyera. Pa nthawiyi Mulungu anasonyeza kuti Yesu, yemwe anadzozedwa, tsopano ankayembekezera kubwerera kumwamba n’kukakhala Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe wosankhidwa ndi Mulungu. (5. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yosonyeza chikondi komanso kuyamikira ena?
5 “Ndiwe . . . wokondedwa.” Zimene Yehova anachita polimbikitsa Mwana wake komanso kusonyeza kuti amamukonda, zikutikumbutsa mfundo yoti nafenso tiziyesetsa kulimbikitsa anzathu. (Yoh. 5:20) Anthufe timamva bwino kwambiri anthu amene timawakonda akatisonyeza chikondi komanso kuyamikira zabwino zimene tachita. Abale ndi alongo komanso anthu a m’banja lathu amafunanso kuti tiziwakonda komanso kuwalimbikitsa. Tikamayamikira anzathu timawathandiza kuti chikhulupiriro chawo chilimbe komanso azitumikira Yehova mokhulupirika. Makolo makamaka amafunika kulimbikitsa ana awo. Ana amakula bwino akamayamikiridwa ndi makolo awo komanso kusonyezedwa chikondi.
6. N’chifukwa chiyani sitikayikira Yesu ngakhale pang’ono?
6 “Ndimakondwera nawe.” Ponena mawu amenewa, Yehova anasonyeza kuti sankakayikira zoti Yesu adzachita bwinobwino zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Atate ake. Ngati Yehova amakhulupirira Mwana wake chonchi, nafenso sitiyenera kukayikira zoti Yesu adzakwaniritsa zinthu zonse zimene Yehova walonjeza. (2 Akor. 1:20) Kuganizira chitsanzo cha Yesu kungatithandize kuti tizichita zonse zimene tingathe pophunzira za iye komanso kutengera chitsanzo chake. Yehova sakayikiranso kuti anthu ake, monga gulu, adzapitiriza kuphunzira zinthu kwa Mwana wakeyu.—1 Pet. 2:21.
“MUZIMUMVERA”
7. Malinga ndi lemba la Mateyu 17:1-5, kodi Yehova analankhulanso kuchokera kumwamba pa nthawi iti, nanga ananena kuti chiyani?
7 Werengani Mateyu 17:1-5. Ulendo wachiwiri pamene Yehova analankhula kuchokera kumwamba ndi pa nthawi imene Yesu “anasandulika.” Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane n’kupita nawo kuphiri lalitali. Ali kuphiriko, ophunzirawo anaona zinthu zodabwitsa kwambiri. Nkhope ya Yesu inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinawalanso kwambiri. Kenako panaoneka Mose ndi Eliya akulankhula naye zokhudza imfa yake. Ngakhale kuti ophunzira akewa anali “atatopa ndi tulo,” iwo anaona bwinobwino masomphenya odabwitsawa. (Luka 9:29-32) Kenako mtambo waukulu unawaphimba ndipo panamveka mawu a Mulungu kuchokera mumtambowo. Pa nthawi ya ubatizo ija, Yehova anasonyeza kuti amakonda Mwana wake komanso amakondwera naye ponena kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.” Koma pa nthawiyi anawonjezerapo mawu akuti: “Muzimumvera.”
8. Kodi masomphenyawa anathandiza bwanji Yesu ndi ophunzira ake?
8 Masomphenya amenewa ankasonyeza zimene zidzachitike Yesu akadzalandira mphamvu ndi ulemerero monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. N’zosachita kufunsa kuti Yesu analimbikitsidwa kwambiri moti anali wokonzeka kupirira mavuto ndi imfa zimene anali atatsala pang’ono kukumana nazo. Zimene ophunzirawa anaona zinalimbitsanso chikhulupiriro chawo n’kuwapatsa mphamvu kuti adzapirire komanso kugwira ntchito mwakhama m’tsogolo. Patapita zaka 30, mtumwi Petulo anafotokoza za masomphenya amenewa ndipo izi zikusonyeza kuti ankawakumbukirabe.—2 Pet. 1:16-18.
9. Kodi Yesu anapereka malangizo othandiza ati kwa ophunzira ake?
9 “Muzimumvera.” Yehova anasonyeza kuti amafuna kuti tizimvera mawu a Mwana wake. Ndiye kodi ndi zinthu ziti zimene Yesu ananena ali padzikoli? Iye ananena zinthu zambiri zofunika kuzitsatira. Mwachitsanzo, iye anaphunzitsa bwino ophunzira ake ntchito yolalikira uthenga wabwino ndipo anawauza mobwerezabwereza kuti ayenera kukhala maso. (Mat. 24:42; 28:19, 20) Iye anawauzanso kuti azichita zinthu mwamphamvu komanso kuti asafooke. (Luka 13:24) Yesu anauzanso ophunzira ake kuti ayenera kukondana, kukhala ogwirizana komanso kutsatira malamulo ake. (Yoh. 15:10, 12, 13) Apatu tingati Yesu anapereka malangizo abwino kwa ophunzira ake. Malangizo amenewa ndi othandizanso masiku ano.
10-11. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timamvera Yesu?
10 Yesu ananena kuti: “Aliyense amene ali kumbali ya choonadi amamvera mawu anga.” (Yoh. 18:37) Ndiye timasonyeza kuti tikumvera mawu ake tikamapitiriza “kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.” (Akol. 3:13; Luka 17:3, 4) Timasonyezanso kumvera mawu ake tikamalalikira uthenga wabwino mwakhama “m’nthawi yabwino ndi m’nthawi yovuta.”—2 Tim. 4:2.
11 Yesu ananena kuti: “Nkhosa zanga zimamva mawu anga.” (Yoh. 10:27) Otsatira ake amasonyeza kuti amamva mawu ake osati pongomvetsera koma potsatira zimene watiuzazo. Iwo salola kusokonezeka ndi “nkhawa za moyo.” (Luka 21:34) Ngakhale zinthu zitavuta kwambiri, iwo amaona kuti chofunika kwambiri ndi kutsatira mawu a Yesu. Abale athu ambiri akukumana ndi mavuto akuluakulu monga kuzunzidwa, kusauka komanso ngozi zogwa mwadzidzidzi. Koma iwo amakhalabe okhulupirika kwa Yehova zivute zitani. Kwa anthu amene akukumana ndi mavutowa, Yesu akuwatsimikizira kuti: “Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda. Komanso wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso.”—Yoh. 14:21.
12. Fotokozani njira ina imene tingasonyezere kuti timamvera Yesu.
12 Kodi ndi njira ina iti imene tingasonyezere kuti timamvera Yesu? Njira yake ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi anthu amene asankhidwa kuti azititsogolera. (Aheb. 13:7, 17) Posachedwapa, gulu la Yehova lasintha zinthu zambiri. Mwachitsanzo, pali zinthu zatsopano zogwiritsa ntchito mu utumiki, njira zatsopano zolalikirira, njira yochitira misonkhano ya mkati mwa mlungu ndiponso njira zomangira Nyumba za Ufumu komanso kuzikonza. Kunena zoona malangizo amene timalandirawa amasonyeza kuti Yehova amatikonda. Sitikayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova adzatidalitsa tikamatsatira malangizo apanthawi yake amene gulu lake limatipatsa.
13. Kodi chimachitika n’chiyani tikamamvera mawu a Yesu?
13 Zinthu zimatiyendera bwino tikamamvera zonse zimene Yesu anatiphunzitsa. Yesu anauza ophunzira ake kuti mfundo zimene ankawaphunzitsa zidzawatsitsimula. Iye anati: “Mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Mawu a Mulungu, omwe akuphatikizapo mabuku 4 a Uthenga Wabwino, amatitsitsimula, kutipatsa mphamvu komanso kutithandiza kukhala anzeru. (Sal. 19:7; 23:3) Paja Yesu anati: “Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”—Luka 11:28.
‘DZINA LANGA NDIDZALILEMEKEZA’
14-15. (a) Malinga ndi Yohane 12:27, 28, kodi Yehova analankhulanso kuchokera kumwamba pa nthawi iti? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu a Yehovawa analimbikitsa Yesu?
14 Werengani Yohane 12:27, 28. Uthenga Wabwino wa Yohane umatchula nthawi yachitatu pamene Yehova analankhula kuchokera kumwamba. Kutatsala masiku ochepa kuti Yesu aphedwe, anapita ku Yerusalemu kuti akachite mwambo wa Pasika. Ndiye pa nthawiyi ananena kuti: “Moyo wanga ukusautsika.” Kenako anapemphera kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” Atatero Atate ake analankhula kuchokera kumwamba kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”
15 Yesu anasautsika mumtima poganizira udindo waukulu umene anali nawo woti akhalebe wokhulupirika kwa Yehova. Iye ankadziwa kuti adzazunzidwa komanso kuphedwa mwankhanza. (Mat. 26:38) Kwa Yesu, chinthu chofunika kwambiri chinali kulemekeza dzina la Atate ake. Koma anthu anamuimba mlandu wonyoza Mulungu ndipo Yesu anada nkhawa kwambiri poona kuti mwina imfa yake idzanyozetsa Mulungu. Ndiye mawu amene Yehova ananena pa nthawiyi ayenera kuti anamulimbikitsa kwambiri. Anamutsimikizira kuti dzina la Yehova lidzalemekezedwa. Zimene Atate akewa ananena ziyenera kuti zinamukhazika mtima m’malo komanso kumupatsa mphamvu kuti apirire mavuto amene anali m’tsogolo. Ngakhale kuti Yesu yekha ndi amene ayenera kuti anamva mawu amene Atate ake ananena pa nthawiyi, Yehova anaonetsetsa kuti mawuwo alembedwa n’cholinga choti nafenso tidziwe.—Yoh. 12:29, 30.
16. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingachititse kuganiza kuti dzina la Yehova linyozeka?
16 Nafenso tikhoza kumada nkhawa tikaganizira za kudetsedwa kwa dzina la Yehova. Mwina mofanana ndi Yesu, ifenso sitikuchitiridwa zinthu mwachilungamo. Apo ayi tingamade nkhawa ndi nkhani zabodza zimene adani athu angafalitse. Mwina tingafike poganiza kuti zinthu Afil. 4:6, 7) Yehova sangalephere kulemekeza dzina lake. Iye adzagwiritsa ntchito Ufumu wake kuti afufute zoipa zonse zimene Satana ndi dzikoli abweretsera atumiki ake okhulupirika.—Sal. 94:22, 23; Yes. 65:17.
zimenezi zinyozetsa Yehova ndi gulu lake. Pa nthawi ngati imeneyi, mawu a Yehovawa akhoza kutilimbikitsa. Si bwino kuda nkhawa kwambiri ndi zimenezi. Tisakayikire kuti “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima ndi maganizo [athu] mwa Khristu Yesu.” (MAWU A YEHOVA AMATILIMBIKITSA MASIKU ANO
17. Malinga ndi Yesaya 30:21, kodi Yehova amatilankhula bwanji masiku ano?
17 Yehova amalankhula nafenso masiku ano. (Werengani Yesaya 30:21.) N’zoona kuti sitichita kumva mawu akewo kuchokera kumwamba. Koma iye watipatsa Baibulo, lomwe ndi Mawu ake, kuti tizipezamo malangizo. Mzimu woyera umathandizanso “mtumiki woyang’anira nyumba wokhulupirika” kuti azipereka chakudya kwa Atumiki ake. (Luka 12:42) Panopa timalandira chakudya chauzimu chambiri kudzera m’mabuku, zinthu za pa intaneti, mavidiyo komanso zinthu zongomvetsera.
18. Kodi mawu a Yehova angatithandize bwanji kuti tilimbe mtima komanso tikhale ndi chikhulupiriro champhamvu?
18 Tiyeni tizikumbukira nthawi zonse mawu amene Yehova ananena pamene Yesu anali padzikoli. Tizichita zonse zimene tingathe kuti tilimbikitsidwe ndi mawu ake omwe ali m’Baibulo. Tizidziwa kuti Yehova akuona zonse zimene zikuchitika ndipo adzakonza mavuto onse amene anayamba chifukwa cha Satana ndi dziko loipali. Ndiye tiyeni tiziyesetsa kumvera mawu onse a Yehova. Tikatero tidzatha kupirira mavuto onse amene tingakumane nawo panopa kapena m’tsogolomu. Paja Baibulo limatiuza kuti: “Mukufunika kupirira, kuti mutachita chifuniro cha Mulungu, mudzalandire zimene Mulungu walonjeza.”—Aheb. 10:36.
NYIMBO NA. 4 “Yehova Ndi M’busa Wanga”
^ ndime 5 Yesu ali padzikoli, Yehova analankhula katatu kuchokera kumwamba. Pa ulendo wina Yehova anauza ophunzira a Khristu kuti azimvera Mwana wake. Masiku ano, Yehova amatilankhula kudzera m’Mawu ake, omwe amaphatikizapo zimene Yesu anaphunzitsa, komanso kudzera m’gulu lake. Munkhaniyi tikambirana ubwino womvera Yehova ndi Yesu.
^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mkulu akuona mtumiki wothandiza akugwira nawo ntchito yosamalira Nyumba ya Ufumu komanso kupereka mabuku kwa abale ndi alongo. Mkuluyo akumuyamikira kuchokera pansi pa mtima.
^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Banja la ku Sierra Leone likupereka kapepala koitanira anthu kumisonkhano kwa msodzi.
^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: A Mboni m’dziko limene ntchito yathu ndi yoletsedwa akusonkhana m’nyumba. Angovala m’njira yoti anthu asawakayikire.