Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 12

Chikondi Chimatithandiza Kupirira Ena Akamadana Nafe

Chikondi Chimatithandiza Kupirira Ena Akamadana Nafe

“Ndikukulamulani zinthu izi, kuti muzikondana. Ngati dziko likudana nanu, mukudziwa kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu.”​—YOH. 15:17, 18.

NYIMBO NA. 129 Tipitirizabe Kupirira

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Mogwirizana ndi Mateyu 24:9, n’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa anthu ena akamadana nafe?

YEHOVA anatilenga kuti tizikonda anthu ena komanso kuti anthu enawo azitikonda. Choncho munthu wina akamadana nafe, timakhumudwa ndipo mwinanso timachita mantha. Mwachitsanzo, mlongo wina yemwe amakhala ku Europe, dzina lake Georgina, * ananena kuti: “Ndili ndi zaka 14, mayi anga ankadana nane chifukwa chotumikira Yehova. Ndinakhumudwa n’kumangodziona ngati ndili ndekha ndipo ndinkaganiza kuti mwina si ine munthu wabwino.” M’bale wina dzina lake Danylo, analemba kuti: “Asilikali atandimenya, kundinyoza komanso kundiopseza chifukwa choti ndine wa Mboni za Yehova, ndinachita mantha ndiponso ndinachita manyazi kwambiri.” Anthu ena akamadana nafe, zimatiwawa komabe zimenezi siziyenera kutidabwitsa chifukwa Yesu ananeneratu kuti ena adzadana nafe.​—Werengani Mateyu 24:9.

2-3. Kodi n’chifukwa chiyani anthu amadana ndi otsatira a Yesu?

2 Dzikoli limadana ndi otsatira a Yesu. N’chifukwa chiyani? Chifukwa mofanana ndi Yesu, ‘sitili mbali ya dzikoli.’ (Yoh. 15:17-19) Choncho ngakhale kuti timalemekeza maboma a anthu, sitimawalambira kapena kulemekeza zizindikiro zoimira mabomawo. Ife timalambira Yehova yekha basi. Timaona kuti Mulungu ndi amene ali woyenera kulamulira anthu koma Satana ndi “mbewu” yake amatsutsa kwambiri zimenezi. (Gen. 3:1-5, 15) Timalalikira kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetse mavuto onse a anthu komanso kuti Ufumuwu posachedwapa, uwononga onse otsutsa. (Dan. 2:44; Chiv. 19:19-21) Umenewutu ndi uthenga wabwino kwa anthu ofatsa koma kwa oipa, ndi wosasangalatsa.​—Sal. 37:10, 11.

3 Anthunso amadana nafe chifukwa timamvera mfundo zolungama za Mulungu. Mfundo zimenezi ndi zosiyana kwambiri ndi zomwe anthu a m’dzikoli amatsatira pa nkhani ya zabwino ndi zoipa. Mwachitsanzo, anthu ambiri masiku ano amavomereza makhalidwe oipa kwambiri ofanana ndi amene anachititsa kuti Mulungu awononge mizinda ya Sodomu ndi Gomora. (Yuda 7) Choncho, popeza timatsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhani yokhudza makhalidwe amenewo, anthu ambiri amatinyoza komanso amatinena kuti ndife amakani.​—1 Pet. 4:3, 4.

4. Kodi ndi makhalidwe ati omwe angatithandize ena akamadana nafe?

4 Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira anthu ena akamadana nafe komanso akamatinyoza? Tiyenera kumakhulupirira kwambiri kuti Yehova atithandiza. Mofanana ndi chishango, chikhulupiriro chathu chingathe ‘kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ (Aef. 6:16) Komabe chikhulupiriro pachokha sichokwanira. Timafunikanso kukhala ndi chikondi. N’chifukwa chiyani? Chifukwa pajatu chikondi “sichikwiya.” Icho chimakwirira komanso kupirira zinthu zonse zokhumudwitsa. (1 Akor. 13:4-7, 13) Tsopano tiyeni tione mmene chikondi chathu kwa Yehova, Akhristu anzathu, ngakhalenso adani athu, chingatithandizire kupirira ena akamadana nafe.

KUKONDA YEHOVA KUMATITHANDIZA KUTI TIZIPIRIRA

5. Kodi kukonda kwambiri Atate wake, kunamuthandiza bwanji Yesu?

5 Atatsala pang’ono kuphedwa ndi adani ake, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Ndimakonda Atate, [choncho] ndikuchita izi kutsatira lamulo limene Atatewo anandipatsa.” (Yoh. 14:31) Kukonda kwambiri Yehova, kunamuthandiza Yesu kuti athe kupirira mayesero aakulu amene anakumana nawo. Ifenso kukonda Yehova kungatithandize kupirira mayesero aliwonse.

6. Mogwirizana ndi Aroma 5:3-5, kodi atumiki a Yehova amamva bwanji anthu a m’dzikoli akamadana nawo?

6 Kukonda Mulungu kwathandiza atumiki a Yehova kuti azipirira akamazunzidwa. Mwachitsanzo, atumwi atalamulidwa ndi khoti lalikulu la Ayuda kuti asiye kulalikira, kukonda Mulungu kunawathandiza kuti ‘amvere Mulungu monga wolamulira, osati anthu.’ (Mac. 5:29; 1 Yoh. 5:3) Chikondi ngati chimenechi ndi chomwe chikuthandizanso abale athu masiku ano kukhalabe okhulupirika akamazunzidwa ndi maboma amphamvu komanso ankhanza. Choncho, m’malo mofooka anthu a m’dzikoli akamadana nafe, timasangalala.​—Mac. 5:41; werengani Aroma 5:3-5.

7. Kodi tiyenera kuchita chiyani achibale athu akamatitsutsa?

7 Chimodzi mwa zinthu zovuta kwambiri kupirira ndi kutsutsidwa ndi achibale athu. Pamene tayamba kusonyeza chidwi chofuna kuphunzira za Yehova, achibale athu angaganize kuti tasocheretsedwa. Ndipo ena akhoza kumaona kuti sitikuganiza bwino. (Yerekezerani ndi Maliko 3:21.) Mwinanso angamatichitire nkhanza. Komatu zimenezi siziyenera kutidabwitsa. Yesu ananena kuti: “Adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.” (Mat. 10:36) Koma ngakhale achibale athu azidana nafe, sitimawaona ngati adani athu. M’malomwake, tikamakonda kwambiri Yehova m’pamene timakondanso kwambiri anthu ena. (Mat. 22:37-39) Komabe sitimasiya kumvera malamulo ndi mfundo za m’Baibulo n’cholinga choti tisangalatse anthu.

Tingavutike kwa kanthawi koma Yehova amakhala nafe kuti azititonthoza komanso kutilimbikitsa (Onani ndime 8-10)

8-9. Kodi n’chiyani chinathandiza mlongo wina kukhalabe wokhulupirika ngakhale kuti ankatsutsidwa kwambiri?

8 Georgina, yemwe tamutchula kale uja, anapitirizabe kukhala wokhulupirika ngakhale kuti mayi ake ankamutsutsa kwambiri. Iye anafotokoza kuti: “Ine ndi mayi anga tinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni. Koma patapita miyezi 6, pamene ndinkafuna kuti ndiyambe kusonkhana, mayi anga anasintha kwambiri ndipo anayamba kundizunza. Ndinazindikira kuti ankagwirizana ndi a mpatuko ndipo ankagwiritsa ntchito mfundo zawo zabodza akamalankhula nane. Iwo ankandinyoza, kundikoka tsitsi, kundigwira pakhosi komanso kunditayira mabuku anga. Komabe nditakwanitsa zaka 15, ndinabatizidwa. Mayi anga anayesetsa kundichititsa kuti ndisiye kutumikira Yehova pokandisiya kunyumba yosungirako achinyamata ozunguza. Ena mwa achinyamatawa anali oti ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso anali atapalamula milandu yosiyanasiyana. Zimakhala zovuta kwambiri kupirira makamaka ukamatsutsidwa ndi munthu amene amayenera kukukonda komanso kukusamalira.”

9 Kodi n’chiyani chinathandiza Georgina kuti apirire? Iye anati: “Tsiku limene mayi anga anayamba kudana nane, ndinali nditangomaliza kuwerenga Baibulo lonse. Tsopano ndinatsimikiza kuti ndapeza choonadi ndipo ndinkaona kuti ndili pa ubwenzi ndi Yehova. Ndinkapemphera pafupipafupi kwa iye ndipo ankamvetsera mapemphero anga. Ndikukhala kumalo kumene anakandisiya kuja, mlongo wina ankandiitanira kunyumba kwake ndipo tinkaphunzirira Baibulo limodzi. Pa nthawi yonseyi, ndinkalimbikitsidwa ndi abale ndi alongo ku Nyumba ya Ufumu. Iwo ankandiona ngati m’bale wawo weniweni. Ndinaoneratu kuti Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa adani athu, kaya adaniwo akhale ndani.”

10. Kodi tiyenera kukhulupirira kuti Yehova Mulungu wathu adzachita chiyani?

10 Mtumwi Paulo analemba kuti palibe chimene chingathe “kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:38, 39) Ngakhale kuti tingakumane ndi mavuto kwa kanthawi, Yehova adzapitirizabe kukhala kumbali yathu kuti atilimbikitse komanso kutipatsa mphamvu. Ndipo monga mmene taonera pa zimene zinachitikira Georgina, Yehova amatithandizanso pogwiritsa ntchito abale ndi alongo athu mumpingo.

KUKONDA AKHRISTU ANZATHU KUMATITHANDIZA KUTI TIZIPIRIRA

11. Kodi chikondi chimene Yesu anafotokoza pa Yohane 15:12, 13, chikanathandiza bwanji ophunzira ake? Perekani chitsanzo.

11 Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anakumbutsa otsatira ake kuti azikondana. (Werengani Yohane 15:12, 13.) Iye ankadziwa kuti kukhala ndi chikondi chololera kuvutikira ena n’kumene kukanawathandiza kukhala ogwirizana komanso kupirira anthu ena akamadana nawo. Taganizirani chitsanzo cha mpingo wa ku Tesalonika. Kungochokera pamene mpingowu unakhazikitsidwa, Akhristu a mumpingowo ankangokhalira kuzunzidwa. Koma iwo anakhalabe zitsanzo zabwino pa nkhani yopirira komanso kusonyeza chikondi. (1 Ates. 1:3, 6, 7) Paulo anawalimbikitsa kuti apitirize kusonyeza chikondi “mowonjezereka.” (1 Ates. 4:9, 10) Chikondi chikanawathandiza kuti azilimbikitsa a mtima wachisoni komanso kuthandiza ofooka. (1 Ates. 5:14) Akhristuwo anatsatira malangizo a Paulowa chifukwa m’kalata yake yachiwiri, imene anawalembera patatha pafupifupi chaka, iye anawauza kuti: “Chikondi cha aliyense wa inu kwa mnzake chikuwirikiza.” (2 Ates. 1:3-5) Choncho, chikondi chinawathandiza kupirira mavuto komanso kuzunzidwa.

Chikondi chingatithandize kuti tizipirira anthu ena akamadana nafe (Onani ndime 12) *

12. Kodi abale ndi alongo m’dziko lina anasonyeza bwanji kuti amakondana pa nthawi imene kunali nkhondo?

12 Taganizirani zimene zinachitikira Danylo, yemwe tamutchula kale uja ndi mkazi wake. Nkhondo imene inkachitika m’dziko lawo itafika m’dera lomwe ankakhala, iwo anapitirizabe kupezeka pamisonkhano, kulalikira mmene angathere komanso kugawana chakudya chomwe anali nacho ndi abale ndi alongo awo. Ndiyeno tsiku lina, kunyumba kwa Danylo kunabwera asilikali atanyamula mfuti. Iye anati: “Asilikaliwo anandikakamiza kuti ndinene kuti ndasiya kukhala wa Mboni. Nditakana, anandimenya n’kundilozetsa mfuti m’mutu ngati akufuna kundiombera koma n’kuombera pambali. Asanapite, anandiuza kuti akabweranso kudzagwiririra mkazi wanga. Koma mwansanga abale anatilipirira sitima kuti tithawire m’tawuni ina. Sindidzaiwala chikondi chimene abalewa anatisonyeza. Titafika m’tawuni inayo, abale kumeneko anatipatsa chakudya ndiponso anandithandiza kuti ndipeze ntchito komanso nyumba. Zimenezi zinathandiza kuti ifenso tithe kulandira a Mboni ena omwe ankathawa nkhondo m’madera awo n’kumakhala nawo.” Zochitika ngati zimenezi zikusonyeza kuti Akhristufe tikamakondana, zimatithandiza kuti tizipirira anthu ena akamadana nafe.

KUKONDA ADANI ATHU KUMATITHANDIZA KUTI TIZIPIRIRA

13. Kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji kupirira tikamatumikira Yehova ngakhale anthu ena azidana nafe?

13 Yesu anauza otsatira ake kuti azikonda adani awo. (Mat. 5:44, 45) Kodi zimenezi ndi zophweka? Ayi ndithu. Koma mzimu woyera wa Mulungu ungatithandize kuti tikwanitse kuchita zimenezi. Makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa akuphatikizapo chikondi, kuleza mtima, kukoma mtima, kufatsa komanso kudziletsa. (Agal. 5:22, 23) Makhalidwe amenewa amatithandiza kupirira anthu ena akamadana nafe. Anthu ambiri omwe poyamba anali otsutsa, anasintha chifukwa amuna awo, akazi awo, ana awo kapena oyandikana nawo nyumba ankasonyeza makhalidwe amenewa. Ndipo ena mwa anthu amene ankatsutsawo, panopa ndi abale ndi alongo athu. Choncho ngati zimakuvutani kuti muzikonda anthu amene amadana nanu chifukwa chotumikira Yehova, muzipemphera kwa iye kuti akupatseni mzimu woyera. (Luka 11:13) Ndipo muzikhulupirira kuti kumvera Mulungu nthawi zonse n’kofunika kwambiri.​—Miy. 3:5-7.

14-15. Kodi malangizo a pa Aroma 12:17-21, anathandiza bwanji Yasmeen kukonda mwamuna wake ngakhale kuti ankamutsutsa kwambiri?

14 Taganizirani chitsanzo cha Yasmeen, yemwe amakhala ku Middle East. Atangokhala wa Mboni za Yehova, mwamuna wake ankaganiza kuti wasocheretsedwa ndipo ankafuna kumusiyitsa kutumikira Mulungu. Iye ankamunyoza ndiponso analimbikitsa achibale ake, m’busa wachipembedzo chake ndi munthu wina wa zamatsenga kuti amuopseze komanso kumuimba mlandu woti akuthetsa banja lake. Mwamunayo anafika pokalalatira abale pa nthawi ya misonkhano. Mavuto amenewa anachititsa kuti nthawi zambiri Yasmeen azingokhalira kulira.

15 Ku Nyumba ya Ufumu abale ndi alongo ake a Yasmeen ankamutonthoza komanso kumulimbikitsa. Akulu anamulimbikitsa kuti azitsatira malangizo a pa Aroma 12:17-21. (Werengani.) Yasmeen anati: “Zinali zovuta kwambiri, koma ndinapempha Yehova kuti andithandize. Ndipo ndinayesetsa kuti ndizichita zimene Baibulo limanena. Choncho mwamuna wanga akatayira zinthu mwadala m’khitchini ndinkakonzamo, akandinyoza ndinkayankha mwaulemu ndipo akadwala ndinkamusamalira.”

Tikamakonda anthu amene amatizunza, akhoza kusintha (Onani ndime 16-17) *

16-17. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yasmeen?

16 Yasmeen anadalitsidwa chifukwa chokonda mwamuna wake. Iye anati: “Mwamuna wanga anayamba kundikhulupirira kwambiri chifukwa ankadziwa kuti nthawi zonse ndimalankhula zoona. Anayamba kumvetsera mwaulemu tikamakambirana nkhani zachipembedzo ndipo anavomera kuti tizikhala mwamtendere. Panopa amandilimbikitsa kuti ndizipita kumisonkhano. Zinthu zinasintha kwambiri m’banja lathu moti tsopano timakhala mwamtendere. Ndikuyembekezera kuti mwamuna wanga adzatsegula mtima wake kuti aphunzire choonadi n’kuyamba kutumikira limodzi Yehova.”

17 Chitsanzo cha Yasmeen chikutithandiza kuona kuti chikondi “chimakwirira zinthu zonse, . . . chimayembekezera zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse.” (1 Akor. 13:4, 7)” Chidani chingakhale chopweteka ndiponso champhamvu koma chikondi ndi champhamvu kwambiri kuposa chidani. Tikamakonda ena, akhoza kusintha n’kusiya kutitsutsa ndipo izi zingachititse kuti Yehova azisangalala. Ngakhale otsutsa atapitiriza kudana nafe, tikhoza kumakhalabe osangalala. Kodi zimenezi zingatheke bwanji?

TIZISANGALALA ENA AKAMADANA NAFE

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kumasangalala anthu ena akamadana nafe?

18 Yesu ananena kuti: “Ndinu odala anthu akamadana nanu.” (Luka 6:22) Sitimachita kusankha kuti anthu azidana nafe komanso kutizunza chifukwa cha zimene timakhulupirira. Ndiye n’chifukwa chiyani timasangalala ena akamadana nafe? Pali zifukwa zitatu. Choyamba, tikapirira timakhala ovomerezeka pamaso pa Mulungu. (1 Pet. 4:13, 14) Chachiwiri, chikhulupiriro chathu chimayengedwa ndipo zikatero chimalimba kwambiri. (1 Pet. 1:7) Ndipo chachitatu, tidzapeza mphoto yamtengo wapatali, yomwe ndi moyo wosatha.​—Aroma 2:6, 7.

19. N’chifukwa chiyani atumwi anasangalala atakwapulidwa?

19 Pasanapite nthawi kuchokera pamene Yesu anaukitsidwa, atumwi anayamba kuona chimwemwe chimene Yesu anawafotokozera. Atawakwapula n’kuwalamula kuti asiye kulalikira, iwo anasangalala. Chifukwa chiyani? “Chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.” (Mac. 5:40-42) Iwo ankakonda kwambiri Mbuye wawo kuposa mmene ankaopera anthu amene ankadana nawo. Ndipo anasonyeza chikondi chawo popitiriza kulalikira uthenga wabwino “mwakhama.” Abale athu ambiri masiku ano, akupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika ngakhale kuti akukumana ndi mavuto. Iwo amadziwa kuti Yehova sadzaiwala ntchito yawo komanso chikondi chomwe amasonyeza pa dzina lake.​—Aheb. 6:10.

20. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

20 Anthu adzapitiriza kudana nafe mpaka pamene dziko loipali lidzawonongedwe. (Yoh. 15:19) Koma sitiyenera kuchita mantha. Monga mmene tidzaonere munkhani yotsatira, Yehova apitiriza ‘kulimbitsa ndi kuteteza’ atumiki ake okhulupirika. (2 Ates. 3:3) Choncho tiyeni tipitirize kukonda Yehova, abale ndi alongo athu komanso ngakhale adani athu. Tikamatsatira malangizo amenewa, tidzakhalabe ogwirizana ndipo chikhulupiriro chathu chidzalimba. Tidzathandiza kuti Yehova alemekezedwe komanso tidzasonyeza kuti chikondi ndi champhamvu kwambiri kuposa chidani.

NYIMBO NA. 106 Khalani Achikondi

^ ndime 5 Munkhaniyi, tiona mmene kukonda Yehova, Akhristu anzathu ngakhalenso adani athu, kungatithandizire kupirira anthu ena m’dzikoli akamadana nafe. Tionanso chifukwa chake Yesu ananena kuti tikhoza kukhala osangalala ngakhale anthu ena azidana nafe.

^ ndime 1 Mayina asinthidwa.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Danylo ataopsezedwa ndi asilikali, abale anamuthandiza limodzi ndi mkazi wake kuti asamuke ndipo kumene anapitako, abale anawalandira ndi manja awiri.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mwamuna wa Yasmeen ankamutsutsa koma akulu anamupatsa malangizo abwino. Iye anasonyeza kuti ndi mkazi wabwino posamalira mwamuna wake pamene ankadwala.