Mafunso Ochokera kwa Owerenga
N’chifukwa chiyani munthu wina amene Baibulo limangomutchula kuti “Uje” ananena kuti kukwatira Rute ‘kungawononge’ cholowa chake? (Rute 4:1, 6)
Kale mwamuna akamwalira wopanda mwana pankakhala mafunso ena. Mwachitsanzo: Kodi malo omwe anali nawo akhala a ndani? Kodi dzina la banja lake lithera pomwepo? M’Chilamulo cha Mose munkapezeka mayankho a mafunso ngati amenewa.
N’chiyani chomwe chinkachitikira malo a munthu yemwe wamwalira kapena amene wasauka n’kugulitsa malo akewo? M’bale wake kapena wachibale wina wapafupi ankatha kuwawombola, kapena kuti kuwagulanso. Zimenezi zinkathandiza kuti malowo akhalebe a banja lawo.—Lev. 25:23-28; Num. 27:8-11.
Kodi dzina la banja la munthu amene wamwalira linkatetezedwa bwanji? Zimenezi zinkatheka pochita ukwati wachokolo kapena kuti wapachilamu ngati mmene zinalili ndi Rute. Mwamuna ankakwatira mkazi wa m’bale wakeyo n’cholinga choti abereke mwana yemwe adzatenge dzina la womwalirayo komanso cholowa chake. Makonzedwe achikondiwa ankathandizanso kuti mayi wamasiyeyo azisamalidwa mwachikondi.—Deut. 25:5-7; Mat. 22:23-28.
Taganizirani mmene zinalili ndi Naomi. Iye anakwatiwa ndi munthu wina dzina lake Elimeleki. Mwamunayo ndi ana ake awiri atamwalira Naomi anatsala wopanda womusamalira. (Rute 1:1-5) Atabwerera ku Yuda, Naomi anauza Rute mpongozi wake kuti auze Boazi kuti awombole malo awo. Iye anali wachibale wapafupi wa Elimeleki. (Rute 2:1, 19, 20; 3:1-4) Koma Boazi ankadziwa kuti munthu wina yemwe Baibulo limangomutchula kuti “Uje” ndi amene anali wachibale wapafupi kwambiri. Choncho iye ndi amene anali woyenera kukhala woyamba kupatsidwa mwayi woti awawombole.—Rute 3:9, 12, 13.
Poyamba “Uje” ankafuna kuthandizapo. (Rute 4:1-4) Ngakhale kuti iye akanatha kuwononga ndalama kuti agule malowo, ankadziwa kuti Naomi sakanatha kubereka mwana yemwe akanadzatenga cholowa cha Elimeleki. Apa mwachionekere malowo akanakhala ake ndipo ankaona kuti akanapeza phindu.
Koma munthuyu anasintha maganizo atazindikira kuti ankafunikanso kukwatira Rute. Iye anati: “Sinditha kuuwombola, kuopera kuti ndingawononge cholowa changa.” (Rute 4:5, 6) Ndiye kodi n’chifukwa chiyani anasintha maganizo?
Ngati uje kapena munthu wina akanakwatira Rute n’kubereka mwana wamwamuna, mwanayo ndi amene akanadzatenga cholowa cha Elimeleki. Koma kodi zimenezi ‘zikanawononga’ bwanji “cholowa” cha uje? Baibulo silifotokoza koma n’kutheka kuti pali zifukwa zingapo.
Choyamba, iye akanawononga ndalama zake kugula malo a Elimeleki koma pamapeto pake malowo sakanakhala ake. Akanadzakhala a mwana wa Rute.
Chachiwiri iye akanakhalanso ndi udindo wosamalira Rute ndi Naomi.
Chachitatu, ngati Rute akanabereka ana ena, anawo limodzi ndi ana amene munthuyo anali nawo kale akanadzagawana chuma chake.
Cha 4, ngati uje analibe ana, mwana amene Rute akanadzabereka akanakhala ndi ufulu wolandira cholowa cha ujeyu komanso cha Elimeleki. Choncho ngati akanamwalira, malo amene anali nawo akanapita kwa mwana amene ali ndi dzina la Elimeleki osati lake. Uje sankafuna kuwononga cholowa chake pothandiza Naomi. Choncho iye anasankha kupereka mwayi wowawombola kwa munthu wina yemwe ndi Boazi. Boazi anachita zimenezi chifukwa ankafuna kuti “dzina la mwamuna wake [wa Rute] amene anamwalira libwerere pacholowa chake.”—Rute 4:10.
Zikuoneka kuti uje ankafunitsitsa kuti asawononge dzina lake komanso cholowa chake. Iye anali ndi maganizo odzikonda. Ngakhale kuti ankafuna kuteteza dzina lake, dzinalo linaiwalika ndipo silipezekanso mu mbiri yakale. Iye anatayanso mwayi womwe Boazi analandira wokhala mumzera wa makolo umene Mesiya, Yesu Khristu, anabadwiramo. Izitu n’zotsatirapo zomvetsa chisoni zimene zinachitikira uje chifukwa cholephera kuthandiza munthu amene ankafunika kuthandizidwa.—Mat. 1:5; Luka 3:23, 32.