Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 14

“Mwakutero, Onse Adzadziwa Kuti Ndinu Ophunzira Anga”

“Mwakutero, Onse Adzadziwa Kuti Ndinu Ophunzira Anga”

“Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”​—YOH. 13:35.

NYIMBO NA. 106 Khalani Achikondi

ZIMENE TIPHUNZIRE a

Kodi anthu omwe si a Mboni amakhudzidwa bwanji akaona chikondi chimene anthu a Yehova amasonyezana? (Onani ndime 1)

1. N’chiyani chimachititsa chidwi anthu ambiri omwe abwera pamisonkhano yathu? (Onaninso chithunzi.)

 YEREKEZERANI kuti banja lina lapita ku Nyumba ya Ufumu kukasonkhana ndi a Mboni za Yehova kwa nthawi yoyamba. Iwo asangalala kwambiri chifukwa choona mmene awalandirira komanso chikondi chomwe abale ndi alongo akusonyezana. Pamene akubwerera kwawo, mkazi akuuza mwamuna wake kuti, ‘Ndaona kuti a Mboni za Yehova ndi osiyana kwambiri ndi anthu ena ndipo ndinasangalala kusonkhana nawo.’

2. Kodi ena anakhumudwa chifukwa chiyani?

2 Chikondi chimene chili pakati pa Akhristu oona n’chochititsa chidwi kwambiri. Komabe a Mboni za Yehova si anthu angwiro. (1 Yoh. 1:8) Choncho pamene tikuyamba kuwadziwa bwino abale ndi alongo, m’pamenenso timadziwa kwambiri zofooka zawo. (Aroma 3:23) N’zomvetsa chisoni kuti ena anakhumudwa chifukwa cha zolakwa za anzawo.

3. Kodi chizindikiro cha otsatira oona a Yesu n’chiyani? (Yohane 13:34, 35)

3 Taganiziraninso lemba lomwe likutsogolera nkhaniyi. (Werengani Yohane 13:34, 35.) Kodi chizindikiro cha otsatira oona a Khristu n’chiyani? Ndi chikondi, osati ungwiro. Onaninso kuti Yesu sananene kuti: ‘Mwakutero, inuyo mudzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.’ M’malomwake anati: “Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.” Choncho Yesu anasonyeza kuti ngakhale anthu omwe sali mumpingo wa Chikhristu adzazindikira otsatira ake chifukwa amasonyezana chikondi chopanda dyera.

4. Kodi anthu ena angafune kudziwa chiyani zokhudza Akhristu oona?

4 Anthu ena omwe si a Mboni za Yehova angafunse kuti: ‘Kodi chikondi chimadziwikitsa bwanji otsatira oona a Yesu? Kodi Yesu anawasonyeza bwanji chikondi atumwi ake? Nanga kodi zingatheke bwanji kuti tizitsanzira Yesu masiku ano?’ A Mbonife tingachitenso bwino kuganizira mayankho a mafunso amenewa. Kuchita zimenezi kungathandize kuti tizikondana kwambiri makamaka pamene talakwirana.​—Aef. 5:2.

N’CHIFUKWA CHIYANI CHIKONDI CHILI CHIZINDIKIRO CHA AKHRISTU OONA OKHA?

5. Kodi mawu a Yesu a pa Yohane 15:12, 13 amatanthauza chiyani?

5 Yesu anafotokoza momveka bwino kuti otsatira ake azidzadziwika ndi chikondi chapadera. (Werengani Yohane 15:12, 13.) Onani kuti Yesu analamula kuti: “Mukondane monga mmene inenso ndakukonderani.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Monga mmene Yesu anafotokozera, ichi ndi chikondi chololera kuvutikira ena, chomwe chimachititsa Mkhristu kukhala wokonzeka ngakhale kufera Mkhristu mnzake ngati pakufunika kutero. b

6. Kodi Mawu a Mulungu amasonyeza bwanji kuti chikondi n’chofunika?

6 Mawu a Mulungu amasonyeza kuti chikondi ndi chofunika kwambiri. Pa mavesi amene anthu ambiri amawakonda, pamakhalanso mavesi monga akuti: “Mulungu ndiye chikondi.”(1 Yoh. 4:8) “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mat. 22:39) “Chikondi chimakwirira machimo ochuluka.” (1 Pet. 4:8) “Chikondi sichitha.” (1 Akor. 13:8) Mavesi amenewa ndi ena ayenera kuthandiza aliyense kuona kufunika kokhala ndi khalidwe lochititsa chidwili ndiponso kulisonyeza.

7. N’chifukwa chiyani Satana sangachititse kuti anthu akhale ogwirizana komanso azisonyezana chikondi chenicheni?

7 Anthu ambiri amafunsa kuti: ‘Kodi zingatheke bwanji kudziwa chipembedzo choona? Zipembedzo zonse zimanena kuti zimaphunzitsa choonadi, komatu zimaphunzitsa zosiyana pa nkhani yokhudza Mulungu.’ Satana wakwanitsa kusokoneza anthu pokhazikitsa zipembedzo zambirimbiri zabodza. Koma iye sangakwanitse kukhazikitsa gulu lapadziko lonse la Akhristu okondana. Yehova yekha ndi amene angachite zimenezi. Ndipo izi n’zomveka chifukwa chikondi chenicheni chimachokera kwa iye. Okhawo amene Yehova wawadalitsa komanso kuwapatsa mzimu wake ndi amene angakhale ndi chikondi chenicheni pakati pawo. (1 Yoh. 4:7) Ndiye kodi n’zodabwitsa kuti Yesu ananena kuti otsatira ake oona azidzadziwika ndi chikondi chopanda dyera?

8-9. Kodi anthu ena anakhudzidwa bwanji poona chikondi chimene a Mboni za Yehova amasonyezana?

8 Monga mmene Yesu ananenera, anthu ambiri akwanitsa kuzindikira otsatira ake enieni poona chikondi chenicheni chimene amasonyezana. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Ian amakumbukirabe msonkhano woyambirira womwe anakapezekako, umene unachitikira m’bwalo lamasewera pafupi ndi kwawo. Iye anali atapitako kukaonerera masewera m’bwalolo m’mbuyomu ndipo anati: “Zimene zinachitika pamsonkhanowo ndi pa nthawi ya masewerawo zinali zosiyana kwambiri. A Mboniwo anali aulemu ndipo anavala bwino komanso ana awo anali akhalidwe labwino.” Iye anawonjezera kuti: “Koposa zonse, anthuwa ankaoneka okhutira komanso kuti ali pamtendere, zomwe inenso ndinkafuna. Sindikukumbukira nkhani iliyonse yomwe inakambidwa pamsonkhanowu, koma ndimakumbukirabe mmene a Mboniwa ankachitira zinthu.” c Timasonyeza makhalidwe amenewa chifukwa chakuti timakondana mochokera pansi pa mtima. Popeza kuti timakonda abale ndi alongo athu, timawakomera mtima komanso timawalemekeza.

9 M’bale wina dzina lake John anachitanso chidwi kwambiri atapita kumisonkhano yampingo kwa nthawi yoyamba. Iye anati: “Ndinagoma kuona mmene anthu ake ankachitira zinthu mwaubwenzi ndipo ankangokhala ngati ndi anthu angwiro. Ndinatsimikiza kuti ndapeza chipembedzo choona chifukwa cha chikondi chimene ankasonyezana pakati pawo.” d Mobwerezabwereza zochitika ngati zimenezi zakhala zikusonyeza kuti anthu a Yehova ndi Akhristu enieni.

10. Kodi ndi pa nthawi iti pomwe timakhala ndi mwayi wosonyeza kuti timakonda abale athu? (Onaninso mawu a m’munsi.)

10 Monga tafotokozera kumayambiriro kuja, palibe Mkhristu yemwe ndi wangwiro. Nthawi zina abale athu anganene kapena kuchita zinthu zotikhumudwitsa. e (Yak. 3:2) Pa nthawi ngati imeneyi timakhala ndi mwayi wowasonyeza kuti timawakonda. Pa nkhaniyi, kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yesu?​—Yoh. 13:15.

KODI YESU ANASONYEZA BWANJI KUTI ANKAKONDA ATUMWI AKE?

Yesu anachita zinthu mwachikondi ndi atumwi ake pamene iwo anasonyeza makhalidwe oipa (Onani ndime 11-13)

11. Kodi ndi makhalidwe oipa ati omwe Yakobo ndi Yohane anasonyeza? (Onaninso chithunzi.)

11 Yesu sankayembekezera kuti otsatira ake azichita zinthu popanda kulakwitsa kalikonse. M’malomwake, mwachikondi iye anawathandiza kusiya makhalidwe oipa n’cholinga choti Yehova azisangalala nawo. Pa nthawi ina atumwi ake awiri, Yakobo ndi Yohane, anauza mayi awo kuti akapemphe Yesu kuti adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu. (Mat. 20:20, 21) Apatu Yakobo ndi Yohane anasonyeza kunyada ndi kudzikuza.​—Miy. 16:18.

12. Kodi amene anasonyeza makhalidwe oipa anali Yakobo ndi Yohane basi? Fotokozani.

12 Yakobo ndi Yohane si atumwi okhawo omwe anasonyeza makhalidwe oipa pa nthawiyi. Taonani zimene atumwi enawonso anachita: “Ophunzira 10 ena aja atamva zimenezi, anakwiya ndi amuna awiri apachibalewo.” (Mat. 20:24) N’kutheka kuti atumwi enawo anakangana ndi Yakobo ndi Yohane. Mwina ena a iwo ankanena kuti: ‘Kodi inuyo mukudziona ngati ndani kuti mufike popempha malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu? Ifensotu timagwira ntchito mwakhama ndi Yesu komanso ndife oyenerera mwayi wapaderawu.’ Kaya zinthu zinali bwanji, mfundo yoona ndi yoti atumwiwa analola kuti zimenezi zichititse kuti asiye kukondana pa nthawiyi.

13. Kodi Yesu anatani pa zomwe atumwi ake ankalakwitsa? (Mateyu 20:25-28)

13 Ndiye kodi Yesu anatani pa nkhaniyi? Iye sanawakwiyire. Sananene kuti apeza atumwi ena abwino, odzichepetsa kwambiri ndiponso omwe akanamasonyezana chikondi nthawi zonse. M’malomwake, iye ankawathandiza moleza mtima chifukwa choti iwo ankafunitsitsa kuchita zoyenera. (Werengani Mateyu 20:25-28.) Iye anapitiriza kuchita nawo zinthu mwachikondi ngakhale kuti imeneyi sinali nthawi yoyamba kapena yomaliza kuti iwo akangane pa nkhani yoti wamkulu anali ndani pakati pawo.​—Maliko 9:34; Luka 22:24.

14. Kodi zinthu zinali bwanji pa nthawi imene atumwi a Yesu ankakula?

14 N’zosakayikitsa kuti Yesu ankaganizira chikhalidwe chomwe atumwiwo anakuliramo. (Yoh. 2:24, 25) Pamene iwo ankakula, atsogoleri achipembedzo ankachititsa anthu kuona kuti chofunika kwambiri ndi kutchuka komanso kukhala ndi udindo. (Mat. 23:6; yerekezerani ndi nkhani yakuti “Sunagoge Anali Malo Amene Yesu ndi Ophunzira Ake Ankakonda Kulalikira,” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2010, tsamba 16-18.) Atsogoleri achipembedzo a Chiyuda ankadziona kuti ndi olungama kwambiri. f (Luka 18:9-12) Yesu ankadziwa kuti zimenezi zikanakhudza mmene atumwiwo ankadzionera komanso mmene ankaonera ena. (Miy. 19:11) Iye sankayembekezera kuti iwo azichita zinthu popanda kulakwitsa chilichonse ndipo ankawalezera mtima akalakwitsa chinachake. Yesu ankadziwa kuti iwo anali ndi mitima yabwino, choncho ankawathandiza moleza mtima kuti asiye kunyada komanso kudzikuza, koma akhale achikondi.

KODI TINGATSANZIRE BWANJI YESU?

15. Kodi tingaphunzire chiyani pa nkhani yokhudza Yakobo ndi Yohane?

15 Tingaphunzire zambiri pa nkhani yokhudza Yakobo ndi Yohane. Iwo analakwitsa popempha malo apamwamba mu Ufumu. Atumwi enawonso analakwitsa polola kuti zimenezi zisokoneze mgwirizano wawo. Komabe Yesu anachita zinthu mokoma mtima ndiponso mwachikondi ndi atumwi 12 onsewo. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Sikuti nkhani imangogona pa zimene ena amachita, koma imaphatikizaponso zimene ifeyo timachita ena akalakwitsa zinthu. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize? Tikakhumudwa chifukwa cha zimene Mkhristu wina wachita tingadzifunse kuti: ‘N’chifukwa chiyani ndikudandaula ndi zomwe wachita? Kodi izi zikusonyeza kuti ndili ndi khalidwe linalake lomwe ndikufunika kusintha? Kodi n’kutheka kuti munthu yemwe wandikhumudwitsayu akulimbana ndi vuto linalake? Ngakhale kuti pali zifukwa zomveka zokhumudwira, kodi ndingasonyeze chikondi chenicheni pongonyalanyaza nkhaniyo?’ Tikamayesetsa kuchita zinthu mwachikondi ndi anthu ena, m’pamenenso timasonyeza kwambiri kuti ndife otsatira oona a Yesu.

16. Kodi tingaphunzirenso chiyani pa chitsanzo cha Yesu?

16 Chitsanzo cha Yesu chikutiphunzitsanso kuti tiziyesetsa kuwamvetsa Akhristu anzathu. (Miy. 20:5) N’zoona kuti Yesu ankatha kudziwa zimene zili mumtima mwa munthu. Ifeyo sitingathe kutero. Komabe tingathe kuleza mtima abale ndi alongo athu akatikhumudwitsa. (Aef. 4:1, 2; 1 Pet. 3:8) Kuchita zimenezi sikungakhale kovuta ngati titawadziwa bwino. Tiyeni tione chitsanzo.

17. Kodi woyang’anira dera wina anapindula bwanji chifukwa choyesetsa kuti adziwe bwino Mkhristu mnzake?

17 Woyang’anira dera wina yemwe anatumikirapo ku East Africa amakumbukirabe m’bale wina yemwe iye ankamuona kuti sanali wokoma mtima. Ndiye kodi woyang’anira derayo anatani? Iye anati: “M’malo momamupewa, ndinaganiza zoti ndimudziwe bwino.” Zimenezi zinathandiza woyang’anira derayo kudziwa mmene m’baleyo analeredwera komanso mmene zimenezo zinamukhudzira. Woyang’anira derayo anawonjezera kuti: “Nditamvetsa mmene m’baleyo anayesetsera kuti asinthe zinthu pa moyo wake komanso zomwe anali atakwanitsa kuchita kuti azigwirizana ndi abale ndi alongo ndinachita naye chidwi, moti anakhala mnzanga wapamtima.” Choncho tikamayesetsa kuwamvetsa abale ndi alongo athu, zimakhala zosavuta kuti tiziwakonda.

18. Kodi tingadzifunse mafunso ati ngati Mkhristu mnzathu watilakwira? (Miyambo 26:20)

18 Nthawi zina tingaone kuti n’zofunika kuti tikambirane ndi Mkhristu mnzathu yemwe watilakwira. Koma choyamba tingachite bwino kudzifunsa mafunso monga: ‘Kodi ndikudziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyi?’ (Miy. 18:13) ‘Kodi n’kutheka kuti iye sanandilakwire mwadala?’ (Mlal. 7:20) ‘Kodi inenso ndinayamba ndalakwitsapo mwanjira imeneyi?’ (Mlal. 7:21, 22) ‘Ngati nditakambirana naye, kodi ndichititsa kuti nkhaniyi ikule kwambiri m’malo moti ithe?’ (Werengani Miyambo 26:20.) Pambuyo poganizira mafunso amenewa, tingaone kuti chifukwa chokonda m’bale wathuyo tingonyalanyaza nkhaniyo.

19. Kodi mwatsimikiza kuchita chiyani?

19 Monga gulu, a Mboni za Yehova amasonyeza kuti ndi ophunzira enieni a Yesu. Komanso patokha timasonyeza kuti ndife wotsatira weniweni wa Yesu ngati timakonda abale ndi alongo athu ngakhale kuti amalakwitsa zinthu zina. Tikamachita zimenezi timathandiza kuti anthu ena azindikire chipembedzo choona komanso kuti nawonso ayambe kulambira Yehova, yemwe ndi Mulungu wachikondi. Choncho tiyeni tikhale otsimikiza kuti tipitiriza kusonyeza chikondi chomwe chimadziwikitsa Akhristu oona.

NYIMBO NA. 17 “Ndikufuna”

a Anthu ambiri amafunitsitsa kuphunzira choonadi chifukwa choona chikondi chenicheni pakati pathu. Komabe si ife angwiro, choncho nthawi zina zingamativute kuti tichite zinthu mwachikondi ndi Akhristu anzathu. Tiyeni tikambirane chifukwa chake chikondi chili chofunika komanso mmene tingatsanzirire Yesu pa nkhani yochita zinthu ndi anthu omwe alakwitsa zinazake.

c Onani nkhani yakuti “Tsopano Ndinapeza Cholinga cha Moyo Wanga,” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2012, tsamba 13-14.

d Onani nkhani yakuti “Zinthu Zinkaoneka Ngati Zikundiyendera Bwino,” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2012, tsamba 18-19.

e Nkhaniyi sikunena za machimo akuluakulu omwe tiyenera kudziwitsa akulu, ngati omwe atchulidwa pa 1 Akorinto 6:9, 10.

f Lipoti lina linanena kuti patapita zaka zingapo, rabi wina ananena kuti: “M’dzikoli muli anthu osapitirira 30 olungama ngati mmene analili Abulahamu. Ngatidi alipo 30, ine ndi mwana wanga tili m’gulu limenelo, ngati alipo 10, ine ndi mwana wanga tili m’gulu limenelo, ngati alipo 5, ine ndi mwana wanga tili m’gulu limenelo, ngati alipo awiri, ndiye kuti ndi ine ndi mwana wanga, koma ngati alipo mmodzi, ndi ineyo.”