Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kale Lathu

“Kwa Amene Apatsidwa Ntchitoyi”

“Kwa Amene Apatsidwa Ntchitoyi”

PASANAFIKE pa September 1, 1919, mumzinda wa Cedar Point ku Ohio m’dziko la United States, munali mvula komanso mphepo. Komabe pa tsikuli kunja kunacha bwino ndipo ngakhale kuti kunali dzuwa, sikunkatentha kwambiri. Masana a tsikuli anthu osakwana 1,000 anasonkhana muholo yokwana anthu 2,500 pamsonkhano wachigawo womwe unachitika mumzindawu. Pofika madzulo kunafikanso anthu ena okwana 2,000. Anthuwa anabwera pamaboti, magalimoto komanso pa sitima. Patsiku lotsatira, panali anthu ambiri oti sakanakwana muholo ija, choncho msonkhano unayamba kuchitikira panja pansi pa mitengo.

Anthu ankaoneka bwino kwambiri chifukwa kadzuwa komwe kanalipo kankachititsa kuti mithunzi ya masamba a mitengo izioneka pazovala za anthuwo. Nazonso zipewa za alongo zinali petupetu chifukwa cha kamphepo kayaziyazi kochokera m’nyanja ya Erie. M’bale wina anati: “Pamalowa pankakongola kwambiri moti zinkangokhala ngati tili m’paradaiso.”

Koma chomwe chinali chosangalatsa kwambiri ndi anthu omwe anali pamalowa. Nyuzipepala ina inati: “Anthu onse ankaoneka kuti ndi Akhristu odzipereka komanso anali ansangala.” Ophunzira Baibulowa anali osangalala kwambiri chifukwa choti zaka zingapo m’mbuyomu zinthu sizinali bwino. Kunali nkhondo, ankatsutsidwa, anthu mumpingo sankagwirizana ndiponso Beteli ya ku Brooklyn inatsekedwa. Komanso anthu ambiri anamangidwa chifukwa cholalikira za Ufumu ndipo ena anali abale 8 amene ankatsogolera. Ena a abalewa analamulidwa kuti akhale m’ndende zaka 20. *

Chifukwa cha mavutowa, Ophunzira Baibulo ena anasiya kulalikira. Komabe ambiri sanagonje ngakhale kuti ankatsutsidwa ndi akuluakulu a boma. Mwachitsanzo, wapolisi wina anafotokoza kuti Ophunzira Baibulo amene anawafunsa ananena motsimikiza kuti apitirizabe “kulalikira Mawu a Mulungu mpaka mapeto.”

Pa nthawi yovutayi Ophunzira Baibulo okhulupirika ankapempha Atate nthawi zonse kuti aziwatsogolera ndipo ankaona kuti akuwatsogoleradi. Ndiyeno ali pamsonkhanowu, mlongo wina anafotokoza maganizo amene anthu ambirinso anali nawo. Anati pa nthawi yovuta ija ankalakalaka “nthawi yoti adzayambirenso kulalikira bwinobwino ngati gulu.” Anthuwa ankafunitsitsa kuti ayambenso kugwira ntchito yolalikira.

MAGAZINI YATSOPANO

Kwa mlungu wathunthu umene anthuwa anali pamsonkhano, ankangodabwa ndi zilembo zakuti “GA” zomwe zinali papulogalamu ya msonkhano, pamakadi olandirira anthu komanso pamalo ena. Koma Lachisanu M’bale Joseph F. Rutherford anakamba nkhani imene inathandiza anthu okwana 6,000 omwe anali pamsonkhanowu kudziwa tanthauzo la zilembozo. Anati zilembozi zinkaimira dzina la magazini yatsopano yotchedwa The Golden Age. *

Ponena za odzozedwa anzake, M’bale Rutherford ananena kuti iwo anali ndi chikhulupiriro chakuti mavuto adzatha ndipo mu ulamuliro wa Mesiya zinthu zidzakhala bwino kwambiri mogwirizana ndi dzina la magaziniyi. Ananena kuti ankaonanso kuti ndi udindo wawo kuuza anthu za nthawi imeneyo ndipo Mulungu ndi amene anawapatsa ntchitoyi.

M’bale J. M. Norris ananena kuti magaziniyi inali “Yonena Zoona, Yopereka Chiyembekezo Ndiponso Yolimbitsa Chikhulupiriro.” Magazini imeneyi inali yoti aziigwiritsa ntchito polalikira kunyumba ndi nyumba n’kumauza anthu kuti alembetse kuti azilandira magaziniyi. Ndiyeno atafunsa amene akufuna kugwira nawo ntchitoyi, anthu onse pamsonkhanowo anaimirira. Kenako anaimba ndi mtima wonse nyimbo yopempha Ambuye kuti atumize kuwala ndi choonadi. M’bale J. M. Norris ananenanso kuti: “Sindidzaiwala zimene zinachitika pa tsikuli. Anthu anaimba mokweza kwambiri moti zinkangokhala ngati mitengo ija ikugwedera.”

Pa nthawi yopuma anthu anathamangira pamzere kuti akhale oyambirira kulembetsa kuti azilandira magaziniyi. Anthu ambiri anali ndi maganizo amene Mlongo Mabel Philbrick anali nawo. Iye anati: “Zinali zosangalatsa kuona kuti tiyambiranso ntchito yolalikira.”

“KWA AMENE APATSIDWA NTCHITOYI”

Ophunzira Baibulo okwana 7,000 anakonzeka kuti agwire nawo ntchitoyi. Panali kabuku kakuti Kwa Amene Apatsidwa Ntchitoyi komanso kapepala kena kamene kanafotokoza mmene ntchitoyi iziyendera. Anati kulikulu kukhazikitsidwa Dipatimenti ya Utumiki kuti iziyang’anira ntchitoyi. Mipingo inayenera kukhalanso ndi Komiti ya Utumiki komanso m’bale woti azipereka malangizo. Anafunika kupanga magawo a nyumba kuyambira 150 kufika 200. Anatinso Lachinayi lililonse, pazikhala msonkhano wa utumiki kuti abale azikambirana zimene akumana nazo komanso kupereka malipoti.

M’bale Herman Philbrick anati: “Titangobwerera kunyumba, tonse tinayamba kugwira ntchito youza anthu kuti alembetse zoti azilandira magazini.” Ndipo ankapeza anthu ambiri omvetsera moti M’bale Beulah Covey anati: “Zikuoneka kuti pambuyo pa nkhondo ija aliyense ankafuna kumva uthenga wabwino.” M’bale Arthur Claus anati: “Tinadabwa kwambiri ndi kuchuluka kwa anthu amene analembetsa.” Mmene pankatha miyezi iwiri n’kuti atagawira magazini okwana 500,000 ndipo anthu okwana 50,000 anali atalembetsa kuti azilandira magaziniyi.

Mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1920 munali nkhani yakuti, “Uthenga Wabwino Wonena za Ufumu.” Patapita nthawi M’bale A. H. Macmillan ananena kuti, aka kanali koyamba kuti gulu lilimbikitse abale ndi alongo padziko lonse kuti azilalikira za Ufumu wa Mulungu. Nkhaniyi inalimbikitsa Akhristu odzozedwa onse kuti “azilalikira padziko lonse kuti Ufumu wakumwamba wayandikira.” Masiku ano Abale a Yesu, “amene apatsidwa ntchitoyi” limodzi ndi anthu mamiliyoni akulalikira modzipereka pamene akuyembekezera madalitso a Ufumu wa Mesiya.

^ ndime 5 Onani buku lachingelezi lakuti, Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, mutu 6.

^ ndime 9 Mu 1937 magaziniyi inayamba kudziwika kuti Consolation ndipo mu 1946 inayamba kudziwika kuti Awake! kutanthauza Galamukani!