Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pochita zinthu ndi ogwira ntchito m’boma, sitiyenera kuchita zimene zikutsutsana ndi chikumbumtima chathu

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Mkhristu angadziwe bwanji ngati n’zoyenera kupereka ndalama kwa ogwira ntchito m’boma?

Pali mfundo zingapo zofunika kuziganizira pa nkhaniyi. Akhristu ayenera kupewa chinyengo. Iwo amafunika kumvera malamulo a boma amene sasemphana ndi malamulo a Yehova. (Mat. 22:21; Aroma 13:1, 2; Aheb. 13:18) Komanso amayesetsa kulemekeza zimene anthu a m’dera lawo amachita ndiponso ‘kukonda anzawo mmene amadzikondera.’ (Mat. 22:39; Aroma 12:17, 18; 1 Ates. 4:11, 12) Izi zingachititse kuti Akhristu a m’mayiko osiyanasiyana asankhe zosiyananso pa nkhaniyi.

M’mayiko ambiri, anthu samafunika kupereka kenakake kwa ogwira ntchito m’boma kuti awachitire zinazake. Ogwira ntchito m’bomawo amangodalira malipiro awo ndipo sayembekezera kuti anthu awapatse kenakake akawachitira zinazake. M’mayiko ambiri ndi mlandu kupempha kapena kulandira kanthu pogwira ntchito za boma. Anthu amaona kuti zimenezi ndi ziphuphu ngakhale zitakhala kuti sizisintha mmene agwirire ntchitoyo. M’mayiko ngati amenewa, zimene tikukambiranazi si nkhani chifukwa n’zodziwikiratu kuti kupereka kangachepe n’kulakwa.

Koma m’mayiko ena mulibe malamulo ngati amenewa ndipo ngati alipo satsatiridwa. Ndiyeno ogwira ntchito za boma amaona kuti si kulakwa kulandira kenakake. Ena amapezerapo mwayi pa udindo wawo ndipo safuna kugwira ntchito popanda kulandira kangachepe kwa anthu. Amene amakonda kwambiri zimenezi ndi anthu omangitsa maukwati, okhometsa misonkho, ogawa malo ndi ena. Ngati sanalandire kenakake amazengereza kapena kukana ntchito zimene amayenera kugwira. Akuti m’dziko lina anthu ozimitsa moto sayamba kugwira ntchito yawo ngati sanalandire kangachepe.

Nthawi zina si kulakwa kupereka kenakake pothokoza zimene ena atichitira

M’mayiko amene mumachitika zimenezi, anthu amaona kuti kupereka zinthu kwa ogwira ntchito m’boma n’kosapeweka. Iwo amangoona kuti ndalama zimenezi zimangokhala zowonjezera pa mtengo umene atchajidwa. Koma m’mayiko amene muli chinyengo kwambiri, Akhristu ayenera kusamala kwambiri kuti azitha kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika pamaso pa Mulungu. Kupereka mphatso kuti munthu athandizidwe, n’kosiyana ndi kupereka mphatso kuti munthu achitiridwe zimene samayenera kuchitiridwa. Ena amapereka ndalama kuti alandire zinthu zimene samayenera kulandira ndipo ena amapereka ndalama kwa anthu ngati apolisi n’cholinga choti asalipire chindapusa. Koma kupereka kapena kulandira ziphuphu n’kulakwa chifukwa kumasokoneza chilungamo.—Eks. 23:8; Deut. 16:19; Miy. 17:23.

Akhristu ambiri ozindikira salola kupereka ndalama kapena zinthu zina ngati wogwira ntchito m’boma wawapempha. Amaona kuti zimenezi zingalimbikitse chinyengo.

Monga tanena kale, kupereka kangachepe kuti upeze zinthu zimene sumayenera kulandira n’kulakwa. Koma m’madera ena Akhristu amapereka kamphatso poyamikira zimene ena awachitira kapena pofuna kuti asachedwetsedwe kwambiri pochita zinthu zina. Ena amapereka mphatso poyamikira dokotala kapena nesi amene wawathandiza kuchipatala. Iwo amachita zimenezi pambuyo polandira thandizolo n’cholinga choti zisaoneke ngati akupereka chiphuphu kapena kunyengerera kuti achitiridwe zinazake.

N’zosatheka kuti m’nkhaniyi tifotokoze zonse zimene zimachitika m’mayiko osiyanasiyana. Kaya zinthu zili bwanji m’dziko lanu, Mkhristu aliyense ayenera kuchita zinthu zimene sizikutsutsana ndi chikumbumtima chake. (Aroma 14:1-6) Tiyeneranso kupewa kuphwanya malamulo. (Aroma 13:1-7) Komanso si bwino kuchita zinthu zimene zinganyozetse dzina la Yehova kapena kukhumudwitsa ena. (Mat. 6:9; 1 Akor. 10:32) Tiyeni tiziyesetsa kuti zochita zathu zonse zizisonyeza kuti timakonda anzathu.—Maliko 12:31.

Kodi tingasonyeze bwanji kusangalala tikamva chilengezo choti munthu wina wabwezeretsedwa?

M’chaputala 15 cha buku la Luka, muli fanizo la Yesu lonena za munthu wina amene anali ndi nkhosa 100. Nkhosa imodzi itasowa, munthuyo anasiya 99 zotsalazo n’kupita kukasaka yotaikayo mpaka ‘ataipeza.’ Yesu anati: “Akaipeza amainyamula paphewa pake ndipo amakondwera. Akafika kunyumba amasonkhanitsa mabwenzi ake ndi anthu oyandikana naye n’kuwauza kuti, ‘Kondwerani nane limodzi, chifukwa ndapeza nkhosa yanga imene inatayika ija.’” Ndiyeno pomaliza Yesu ananena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, kumwamba kudzakhalanso chisangalalo chochuluka chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa kuposa cha anthu 99 olungama osafunika kulapa.”—Luka 15:4-7.

Nkhaniyi imasonyeza kuti Yesu ananena izi podzudzula alembi ndi Afarisi, omwe ankamunena kuti amalakwa kucheza ndi okhometsa misonkho komanso anthu ochimwa. (Luka 15:1-3) M’fanizoli, Yesu anasonyeza kuti kumwamba kumakhala chimwemwe munthu wochimwa akalapa. Ndiye funso n’kumati, ‘Ngati kumwamba kumakhala chimwemwe munthu akalapa n’kuyambanso kutumikira Yehova, kodi si koyenera kuti padziko panonso tizisangalala?’—Aheb. 12:13.

Munthu akabwezeretsedwa mumpingo tiyenera kusangalala. N’zoona kuti munthuyo amafunika kupitirizabe kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. Koma ngati wafika pobwezeretsedwa ndiye kuti analapa, ndipo tiyenera kusangalala ndi zimenezi. Choncho tingathe kuwomba m’manja akulu akalengeza kuti winawake wabwezeretsedwa.

Kodi n’chiyani chinkachititsa kuti madzi apadziwe la Betesida ‘aziwinduka’?

M’nthawi ya Yesu, anthu a ku Yerusalemu ankakhulupirira kuti madzi apadziwe la Betesida akawinduka ankachiritsa. (Yoh. 5:​1-7) Izi zinkachititsa kuti anthu ambiri odwala azisonkhana padziweli.

Anthu ambiri amadziwa zoti Ayuda ankakhala ndi mwambo wokasamba padziwe limeneli. Pofuna kuti madzi asamathe, anakonza ngalande yoti madzi ochokera padziwe lina azifika padziwepo. Ochita kafukufuku anapeza kuti pakati pa mayiwe awiriwa panali damu lokhala ndi geti. Akatsegula getili, madzi adziwe linalo ankapita padziwe la Betesida mwamphamvu ndipo izi zinkachititsa kuti madzi ake awinduke.

Chochititsa chidwi n’chakuti mawu amene amapezeka m’Mabaibulo ena pa Yohane 5:4 osonyeza kuti mngelo ankavundula madzi, sapezeka m’mipukutu yakale yachigiriki yodalirika kwambiri (Codex Sinaiticus). Koma Yesu atafika pamalowa, anachiritsa munthu amene anadwala kwa zaka 38. Munthuyo anachira nthawi yomweyo popanda kulowa padziweli.