Kodi Gayo Ankathandiza Bwanji Akhristu Anzake?
GAYO ndiponso Akhristu ena a m’nthawi ya atumwi anakumana ndi mavuto. Anthu ena amene ankaphunzitsa zinthu zachinyengo ankayesetsa kusokoneza mgwirizano mumpingo. (1 Yoh. 2:18, 19; 2 Yoh. 7) Munthu wina dzina lake Diotirefe ankanenera Yohane ndiponso abale ena “zamwano,” ankakana kulandira oyang’anira oyendayenda komanso ankaletsa ena kuti awalandire. (3 Yoh. 9, 10) Izi n’zimene zinkachitika pamene Yohane ankalembera kalata Gayo. Yohane analemba kalatayi cha m’ma 98 C.E. ndipo imadziwika kuti “Kalata Yachitatu ya Yohane.”
Ngakhale kuti Gayo ankakumana ndi mavutowa, anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika. Kodi anasonyeza bwanji kuti anali wokhulupirika? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kumutsanzira masiku ano? Kodi kalata ya Yohane ingatithandize bwanji pa nkhaniyi?
KALATA YOPITA KWA MNZAKE WAPAMTIMA
M’kalata yakeyi, Yohane anangodzitchula kuti “mkulu.” Gayo atangoona mawu amenewa anazindikira kuti kalatayo yachokera kwa mtumwi Yohane. Yohane anayamba kalatayi ndi mawu akuti: “Ndikulembera wokondedwa Gayo, amene ndimamukonda kwambiri.” Kenako ananena kuti akupemphera kuti Gayo akhale ndi “thanzi labwino” mofanana ndi mmene moyo wake wauzimu unalili. Mawu amenewa anali olimbikitsa kwambiri.—3 Yoh. 1, 2, 4.
N’kutheka kuti pa nthawiyo Gayo anali mkulu ngakhale kuti kalatayi sisonyeza zimenezi. Yohane anayamikira Gayo chifukwa choti ankalandira abale achilendo kunyumba kwake. Yohane ankaona kuti umenewu unali umboni wakuti Gayo anali wokhulupirika. Anatero chifukwa choti kuyambira kale atumiki okhulupirika a Mulungu akhala akulandira bwino alendo.—Gen. 18:1-8; 1 Tim. 3:2; 3 Yoh. 5.
Zimene Yohane ananena poyamikira Gayo zikusonyeza kuti abale ankayenda kuchokera kumene Yohane ankakhala kupita m’mipingo yosiyanasiyana. Ndipo abalewo ayenera kuti ankafotokozera Yohane zimene anakumana nazo. Mwina njira imeneyi ndi imene inkathandiza Yohane kudziwa zimene zinkachitika m’mipingo.
Abale amene ankayendayendawo ankasangalala kufikira m’nyumba za Akhristu anzawo. Zinali choncho chifukwa chakuti
m’nyumba zambiri zofikira alendo munkakhala moipa, alendo sankasamaliridwa bwino ndipo munkachitika zachiwerewere. Choncho m’pomveka kuti abalewo ankakonda kufikira kwa Akhristu anzawo.“ANAPITA KUKALALIKIRA ZA DZINA LA MULUNGU”
Yohane analimbikitsanso Gayo kuti azisamalira bwino alendo pomuuza kuti “akamachoka, utsanzikane nawo m’njira imene Mulungu angasangalale nayo.” Apa ankatanthauza kuti potsanzikana nawo awapatse zonse zofunika pa ulendo wawo zomwe zingawathandize mpaka akafike kumene akupita. Zikuoneka kuti Gayo ankachita kale zimenezi ndipo alendo amene ankawalandirawo anauza Yohane kuti Gayo anali wachikondi komanso wokhulupirika.—3 Yoh. 3, 6.
N’kutheka kuti alendowo anali amishonale, anthu amene Yohane anatumiza kapena oyang’anira oyendayenda. Mulimonse mmene zinalili mfundo ndi yakuti anthuwo anali pa ulendo wokhudza uthenga wabwino. Yohane anati: “Iwo anapita kukalalikira za dzina la Mulungu.” (3 Yoh. 7) Choncho abalewo ankafunikira kulandiridwa bwino ndi Akhristu anzawo. N’chifukwa chake Yohane analemba kuti: “Ife tili ndi udindo wolandira bwino anthu amenewa ndi kuwachereza, kuti akhale antchito anzathu m’choonadi.”—3 Yoh. 8.
ANAMUTHANDIZA PA NTHAWI YOVUTA KWAMBIRI
Cholinga cha kalata ya Yohane sichinali kungoyamikira Gayo. Iye ankafunanso kumuthandiza pa vuto lina lalikulu. Munthu wina wamumpingo wawo dzina lake Diotirefe sankafuna kulandira Akhristu oyendayenda ndipo ankaletsa anthu ena kuti awalandire.—3 Yohane 9, 10.
N’zosachita kufunsa kuti Akhristu okhulupirika sakanafuna kufikira kunyumba kwa Diotirefe ngakhale akanawaitana. Iye ankafuna kutchuka mumpingo, sankalandira mwaulemu chilichonse chochokera kwa Yohane ndipo ankanenera zamwano Yohane ndi anthu ena. Ngakhale kuti Yohane sananene kuti Diotirefe ankaphunzitsa zabodza, Diotirefeyo ankaderera udindo wa Yohane. Zimene iye ankachitazi zinkasonyeza kuti sanali wokhulupirika. Nkhani ya Diotirefeyi ikusonyeza kuti anthu odzikuza amene amafuna kutchuka akhoza kusokoneza mgwirizano mumpingo. Choncho Yohane anauza Gayo kuti: “Usamatsanzire zinthu zoipa.” (3 Yoh. 11) Malangizo amenewa ndi othandizanso kwa ifeyo.
CHIFUKWA CHOMVEKA CHOCHITIRA ZABWINO
Mosiyana ndi Diotirefe, panali Mkhristu wina dzina lake Demetiriyo yemwe Yohane ananena kuti ndi chitsanzo chabwino. Yohane anati: “Anthu onse amuchitira umboni Demetiriyo. . . . Ifenso tikuchitira umboni, ndipo iwenso ukudziwa kuti umboni umene timapereka ndi woona.” (3 Yoh. 12) Mwina Demetiriyo ankafunikira kuti Gayo amuthandize ndipo Yohane analemba kalata ya 3 Yohane n’cholinga choti auze Gayo za Demetiriyo komanso amulimbikitse kuti azimuthandiza. N’kutheka kuti Demetiriyo anapereka yekha kalatayi kwa Gayo. Demetiriyo ayenera kuti anatumizidwa ndi Yohane kapena anali woyang’anira woyendayenda ndipo n’kutheka kuti anathandiza Gayo kuona kuti mawu a Yohane ndi ofunika kwambiri.
Popeza Gayo ankalandira bwino alendo, n’chifukwa chiyani Yohane anamulimbikitsa kuti apitirize kuchita zimenezi? Mwina Yohane anaona kuti Gayo akufunikira kulimba mtima. Kapena ankadera nkhawa kuti Gayo angaope kulandira alendo chifukwa chakuti Diotirefe ankafuna kuchotsa mumpingo anthu amene ankalandira alendo. Kaya zinthu zinali bwanji, Yohane analimbikitsa Gayo kuti: “Munthu amene amachita zabwino ndi wochokera kwa Mulungu.” (3 Yoh. 11) Ichitu ndi chifukwa chomveka chochitira zabwino nthawi zonse.
Kodi kalata imene Yohane analembayi inalimbikitsa Gayo kuti apitirize kulandira bwino alendo? Popeza kuti kalata ya 3 Yohane ili m’Baibulo komanso ikulimbikitsabe anthu ena kuti ‘azitsanzira zabwino,’ ndiye kuti Gayo anatsatiradi malangizo a m’kalatayi.
ZIMENE TIKUPHUNZIRA PA 3 YOHANE
Sitikudziwa zambiri zokhudza m’bale wathu Gayo. Koma tikhoza kuphunzira zambiri pa mfundo zochepa zimene tikuzidziwa zokhudza m’baleyu.
Choyamba, tonsefe tinapeza mwayi wodziwa mfundo za m’Baibulo chifukwa choti anthu ena anadzipereka kuchoka kwawo kubwera kudzatilalikira. N’zoona kuti si tonse amene timayenda maulendo ataliatali opita kukalalikira. Koma mofanana ndi Gayo, tiyenera kuthandiza komanso kulimbikitsa anthu amene amayendayenda monga oyang’anira madera ndi akazi awo. Tikhozanso kuthandiza abale ndi alongo amene asamukira kumadera amene kukufunika anthu ambiri olalikira. Choncho tiyeni tonsefe ‘tikhale ochereza.’—Aroma 12:13; 1 Tim. 5:9, 10.
Chachiwiri, tisamadabwe ngati nthawi zina anthu ena angayambe kuderera oyang’anira mumpingo. Paja anthu ena ankaderera Yohane ndipo ena ankaderera Paulo. (2 Akor. 10:7-12; 12:11-13) Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani ngati zoterezi zitachitika mumpingo? Paulo anauza Timoteyo kuti: “Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse. Ayeneranso kukhala woyenerera kuphunzitsa, wougwira mtima pokumana ndi zoipa, ndi wolangiza mofatsa anthu otsutsa.” Tikamakhalabe odekha, ngakhale pamene ena atiputa, tikhoza kuthandiza anthu otsutsa kuti asinthe maganizo. Zikatero, mwina Yehova “angawalole kulapa, kuti adziwe choonadi molondola.”—2 Tim. 2:24, 25.
Chachitatu, anthu amene amatumikirabe Yehova mokhulupirika ngakhale akutsutsidwa ayenera kuyamikiridwa. Gayo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi Yohane ndipo izi zinamutsimikizira kuti akuchita bwino. Akulu ayenera kutsanzira Yohane n’kumalimbikitsanso abale ndi alongo kuti ‘asafooke.’—Yes. 40:31; 1 Ates. 5:11.
Pa mabuku onse a m’Baibulo, kalata imene Yohane analembera Gayo ndi imene ili yaifupi kwambiri. M’chigiriki, kalatayi inali ndi mawu 219 okha. Komabe ndi yothandiza kwambiri kwa Akhristu masiku ano.