NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) May 2020

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira July 6–August 2, 2020.

Kodi “Mfumu ya Kumpoto” M’nthawi ya Mapeto Ndi Ndani?

Nkhani Yophunzira 19: July 6-12, 2020. Panopa tikuona umboni woti ulosi wa Danieli wonena za “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kum’mwera,” ukupitiriza kukwaniritsidwa. N’chifukwa chiyani tikutsimikiza chonchi? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kumvetsa bwino ulosiwu?

Mafumu Awiri Olimbana M’nthawi ya Mapeto

Maulosi onena za “mfumu ya kumpoto” komanso “mfumu ya kum’mwera,” amafotokoza zinthu zina zomwe zinachitika pa nthawi yofanana. Kodi maulosiwa amatithandiza bwanji kutsimikizira kuti dziko la Satanali litha posachedwapa?

Kodi “Mfumu ya Kumpoto” Ndi Ndani Panopa?

Nkhani Yophunzira 20: July 13-19, 2020. Kodi “mfumu ya kumpoto” ndi ndani masiku ano, nanga idzafika bwanji kumapeto a moyo wake? Kudziwa yankho la funsoli kungalimbitse chikhulupiriro chathu komanso kungatithandize kukonzekera mayesero omwe tidzakumane nawo m’tsogolomu.

Kodi Timayamikira Zinthu Zimene Mulungu Anatipatsa?

Nkhani yophunzira 21: July 20-26, 2020. Nkhaniyi itithandiza kuti tiziyamikira Yehova komanso mphatso zomwe anatipatsa. Ingatithandizenso kudziwa zomwe tingachite tikafuna kukambirana ndi anthu omwe amakayikira zoti kuli Mulungu.

Tiziyamikira Chuma Chosaoneka Chomwe Tili Nacho

Nkhani yophunzira 22: July 27–August 2, 2020. Mu nkhani yapitayi, tinakambirana zinthu zingapo zomwe Mulungu anatipatsa zimene tingathe kuziona. Koma mu nkhaniyi, tikambirana zinthu zomwe sitingathe kuziona. Tikambirananso zimene tingachite poyamikira zinthu zimenezi komanso poyamikira Yehova Mulungu yemwe amatipatsa zinthuzi.