Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 20

Kodi “Mfumu ya Kumpoto” Ndi Ndani Panopa?

Kodi “Mfumu ya Kumpoto” Ndi Ndani Panopa?

“Iyo idzafika kumapeto a moyo wake ndipo sipadzapezeka woithandiza.”​—DAN. 11:45.

NYIMBO NA. 95 Kuwala Kukuwonjezerekabe

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi tikambirana chiyani mu nkhaniyi?

PANOPA tili ndi umboni wochuluka wosonyeza kuti tili kumapeto kwenikweni kwa masiku otsiriza. Posachedwapa, Yehova ndi Yesu Khristu awononga maboma onse amene akulimbana ndi Ufumu wa Mulungu. Koma zimenezi zisanachitike, mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera apitiriza kulimbana okhaokha komanso kulimbana ndi anthu a Mulungu.

2 Mu nkhaniyi, tikambirana ulosi wa pa Danieli 11:40–12:1. Tidziwa amene ali mfumu ya kumpoto masiku ano. Tionanso kuti sitiyenera kuda nkhawa ndi zimene zili m’tsogolo koma tizidalira kuti Yehova adzatipulumutsa zivute zitani.

MFUMU YA KUMPOTO YATSOPANO

3-4. Kodi mfumu ya kumpoto ndi ndani masiku ano? Fotokozani.

3 Ulamuliro wa Soviet Union utatha mu 1991, anthu a Mulungu omwe ankakhala m’madera olamuliridwa ndi bomali anakhala pa ufulu kwa kanthawi. Danieli anatchula ufulu umenewu kuti “thandizo lochepa.” (Dan. 11:34) Zimenezi zinathandiza kuti azilalikira mwaufulu ndipo pasanapite nthawi chiwerengero cha ofalitsa m’mayiko amenewa chinawonjezereka kwambiri. Koma patadutsa zaka, dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo anakhala mfumu ya kumpoto. Monga tinaonera mu nkhani yapita ija, kuti ulamuliro ukhale mfumu ya kumpoto kapena mfumu ya kum’mwera uyenera kuchita zinthu zitatu izi: (1) kulamulira komanso kuzunza anthu a Mulungu, (2) kuchita zinthu zosonyeza kuti amadana ndi Yehova komanso anthu ake, ndiponso (3) kulimbirana ulamuliro ndi mfumu inayo.

4 Tinganene kuti masiku ano mfumu ya kumpoto ndi dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo pazifukwa izi: (1) Iwo akuukira anthu a Mulungu poletsa ntchito yolalikira komanso kuzunza abale ndi alongo ambiri omwe amakhala m’mayikowo. (2) Zimene akuchita zikusonyeza kuti amadana ndi Yehova komanso anthu ake. (3) Akulimbana ndi mfumu ya kum’mwera, yomwe ndi ulamuliro wa Britain ndi America. Tiyeni tione zimene dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo achita, zomwe zikutitsimikizira kuti ndi amene panopa ali mfumu ya kumpoto.

MFUMU YA KUMPOTO NDI MFUMU YA KUM’MWERA AKULIMBANABE

5. Kodi ulosi wa pa Danieli 11:40-43 umanena za nthawi iti, ndipo chikuchitika n’chiyani m’nthawi imeneyi?

5 Werengani Danieli 11:40-43. Mavesi amenewa amafotokoza zochitika za m’nthawi yamapeto. Amafotokozanso zimene mfumu ya kumpoto ndi ya kum’mwera akuchita polimbana. Danieli analosera kuti m’nthawi ya mapeto, mfumu ya kum’mwera “idzayamba kukankhana” ndi mfumu ya kumpoto.​—Dan. 11:40.

6. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti mafumu awiriwa akhala akukankhana?

6 Mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera, akulimbirana kukhala ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse lapansi. Chitsanzo ndi zimene zinachitika nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itatha, boma la Soviet Union ndi mayiko ogwirizana nalo anayamba kulamulira madera ambiri a ku Europe. Zimenezi zinachititsa mfumu ya kum’mwera kupanga bungwe lotchedwa NATO, momwe muli mayiko ena a ku Europe omwe anagwirizana kuti azithandizana pankhondo. Komanso mafumuwa amawononga ndalama zambiri popanga zida zankhondo zamphamvu kwambiri. Mfumu iliyonse imathandiza adani a mfumu inzake pankhondo m’mayiko a ku Africa, Asia ndi Latin America. M’zaka zaposachedwapa, mphamvu za dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo, zakhala zikukulirakulira. Mfumuyi imapanganso uchigawenga wa pa intaneti polimbana ndi mfumu ya kum’mwera. Mfumu iliyonse imaloza chala inzake kuti imapanga mapulogalamu a pakompyuta ndi cholinga chofuna kusokoneza chuma ndi ulamuliro wa inzake. Komanso mogwirizana ndi ulosi wa Danieli, mfumu ya kumpoto ikupitiriza kuukira anthu a Mulungu.​—Dan. 11:41.

MFUMU YA KUMPOTO YALOWA “M’DZIKO LOKONGOLA”

7. Kodi “dziko lokongola” ndi chiyani?

7 Lemba la Danieli 11:41 limati mfumu ya kumpoto idzalowa “m’Dziko Lokongola.” Kodi dziko limeneli ndi chiyani? M’nthawi yakale, dziko la Isiraeli ndi lomwe linkaonedwa kuti linali “dziko lokongola kwambiri kuposa mayiko onse.” (Ezek. 20:6) Chimene chinkapangitsa dzikoli kukhala lapadera n’chakuti ndi komwe anthu ankalambirako Yehova. Koma kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E., “dziko” lokongolali si dziko linalake lapadera. Tikutero chifukwa masiku ano anthu a Mulungu akupezeka kulikonse padziko lapansi. Choncho masiku ano, “dziko lokongola” likuimira zimene anthu a Yehova amachita monga kusonkhana komanso kulalikira.

8. Kodi mfumu ya kumpoto yakhala ikulowa bwanji mu “dziko lokongola”?

8 M’masiku otsiriza, mfumu ya kumpoto yakhala ikulowa mobwerezabwereza mu “dziko lokongola.” Mwachitsanzo, pamene dziko la Germany linali mfumu ya kumpoto, makamaka pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, mfumuyi inalowa mu “dziko lokongola” pozunza ndi kupha anthu a Mulungu. Komanso nkhondoyi itatha, mfumu ya kumpoto imene pa nthawiyo inali boma la Soviet Union, inalowanso mu “dziko lokongola” pozunza anthu a Mulungu komanso kuwathamangitsira m’mayiko ena.

9. M’zaka zaposachedwapa, kodi dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo alowa bwanji mu “dziko lokongola”?

9 M’zaka zaposachedwa, dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo analowanso mu “dziko lokongola.” Kodi anachita bwanji zimenezi? Mu 2017, mfumu ya kumpoto yatsopanoyi, inaletsa ntchito ya anthu a Yehova ndi kumanga abale ndi alongo athu ena. Inaletsanso mabuku athu kuphatikizapo Baibulo la Dziko Latsopano. Komanso inalanda ofesi yathu ya nthambi ya ku Russia, Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano. Zimenezi zitachitika, mu 2018 Bungwe Lolamulira linanena kuti dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo ndi mfumu ya kumpoto. Komabe anthu a Yehova salimbana ndi boma lililonse kapena kuyesa kuti alisinthe ngakhale pamene akuzunzidwa kwambiri. M’malomwake iwo amatsatira malangizo a m’Baibulo akuti azipempherera “anthu onse apamwamba,” makamaka pamene anthuwo akusankha zochita pa nkhani zomwe zingakhudze ufulu wakulambira.​—1 Tim. 2:1, 2.

KODI MFUMU YA KUMPOTO IDZAGONJETSA MFUMU YA KUM’MWERA?

10. Kodi mfumu ya kumpoto idzagonjetsa mfumu ya kum’mwera? Fotokozani.

10 Ulosi wa pa Danieli 11:40-45, kwenikweni umanena za zimene mfumu ya kumpoto idzachite. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti idzagonjetsa mfumu ya kum’mwera? Ayi. Tikutero chifukwa mfumu ya kum’mwera idzakhala ‘idakali moyo’ kapena kuti ilipobe pamene Yehova ndi Yesu azidzawononga maboma a anthu pankhondo ya Aramagedo. (Chiv. 19:20) Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Tiyeni tione zimene maulosi opezeka m’buku la Danieli komanso Chivumbulutso amanena.

Pankhondo ya Aramagedo, Ufumu wa Mulungu umene wayerekezeredwa ndi mwala, udzathetsa maulamuliro a anthu, omwe akuimiridwa ndi chifaniziro chachikulu (Onani ndime 11)

11. Kodi ulosi wa pa Danieli 2:43-45 umatanthauza chiyani? (Onani chithunzi chapachikuto.)

11 Werengani Danieli 2:43-45. Mneneri Danieli anafotokoza za chifaniziro chachikulu chimene thupi lake linapangidwa ndi zitsulo zosiyanasiyana. Mbali iliyonse ya chifanizirochi imaimira maboma osiyanasiyana omwe analamulira madera amene anthu a Mulungu ankakhala. Mabomawa analamulira pa nthawi zosiyanasiyana. Mapazi a chifanizirochi omwe anali achitsulo chosakanizika ndi dongo akuimira ulamuliro womaliza wa Britain ndi America. Ulosiwu ukutanthauza kuti boma la Britain ndi America lidzakhala likulamulirabe pamene Ufumu wa Mulungu uzidzawononga maboma onse a anthu.

12. Kodi mutu wa 7 ukuimira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani kudziwa zimenezi n’kofunika?

12 Mtumwi Yohane nayenso anafotokoza za maulamuliro amphamvu padziko lonse omwe analamulira anthu a Yehova. Iye anayerekezera maulamulirowa ndi chilombo cha mitu 7. Mutu wa 7 wa chilombochi umaimira ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. Mfundo imeneyi ndi yofunika chifukwa ikutithandiza kudziwa kuti sipakubweranso mutu wina. Mutu umenewu ndi womwe udzakhale ukulamulira mpaka pamene Khristu ndi asilikali ake adzauwononge limodzi ndi chilombochi. *​—Chiv. 13:1, 2; 17:13, 14.

KODI MFUMU YA KUMPOTO ICHITA CHIYANI POSACHEDWAPA?

13-14. Kodi “Gogi wa kudziko la Magogi” ndi ndani, nanga n’chiyani chingadzamuchititse kuti aukire anthu a Mulungu?

13 Ulosi wa m’buku la Ezekieli umatithandiza kudziwa zimene zidzachitike mafumu awiriwa, mfumu ya kumpoto komanso mfumu ya kum’mwera, asanawonongedwe. Zikuoneka kuti maulosi opezeka pa Ezekieli 38:10-23; Danieli 2:43-45; 11:44–12:1 ndi Chivumbulutso 16:13-16, 21, amafotokoza zinthu zofanana. Ngati zili choncho, ndiye tikuona kuti pachitika zinthu zotsatirazi.

14 Chisautso chachikulu chikadzangoyamba, “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” adzapanga mgwirizano wa mayiko. (Chiv. 16:13, 14; 19:19) Mgwirizano umenewu ndi womwe Malemba amautchula kuti “Gogi wa kudziko la Magogi.” (Ezek. 38:2) Mayikowa adzaukira anthu a Mulungu pofuna kuwawononga kuti asadzapezekenso. Kodi n’chiyani chidzachititse kuti awaukire? Pofotokoza za nthawi imeneyi, mtumwi Yohane analosera kuti matalala aakulu adzagwera adani a Mulungu. N’kutheka kuti matalala aakuluwa akuimira uthenga wachiweruzo umene anthu a Yehova azidzalengeza. Mwina uthengawu ndi womwe udzachititse kuti Gogi wa ku Magogi aukire anthu a Mulungu n’cholinga choti awawonongeretu.​—Chiv. 16:21.

15-16. (a) Kodi ulosi wa pa Danieli 11:44, 45 ukhoza kukhala ukunena za chiyani? (b) Kodi n’chiyani chidzachitikire mfumu ya kumpoto limodzi ndi Gogi wa ku Magogi?

15 Uthenga wamphamvuwu komanso kuukira kwa adani a Mulungu zikhoza kukhala zinthu zomwe zatchulidwanso pa Danieli 11:44, 45. (Werengani.) Palembali Danieli anafotokoza kuti “kotulukira dzuwa ndi kumpoto kudzachokera mauthenga” amene adzasokoneze mfumu ya kumpoto ndipo idzapita ndi “ukali waukulu.” Mfumu ya kumpoto idzapita kuti “ikafafanize ndi kuwononga ambiri.” Zikuoneka kuti “ambiri” omwe akutchulidwa palembali ndi anthu a Yehova. * Pamenepa Danieli ayenera kuti ankanena za kuukiridwa kwa anthu a Mulungu n’cholinga choti awawonongeretu.

16 Mfumu ya kumpoto limodzi ndi maboma onse a padziko lapansi akadzaukira anthu a Mulungu, Mulungu Wamphamvuyonse adzakwiya kwambiri ndipo nkhondo ya Aramagedo idzayamba. (Chiv. 16:14, 16) Pa nthawiyi, mfumu ya kumpoto ndi mayiko onse amene apanga Gogi wa ku Magogi, adzawonongedwa ndipo ‘sipadzapezeka wowathandiza’.​—Dan. 11:45.

Pankhondo ya Aramagedo, Yesu Khristu ndi gulu lake lankhondo la kumwamba adzawononga dziko loipa la Satanali ndi kupulumutsa anthu a Mulungu (Onani ndime 17)

17. Kodi Mikayeli “kalonga wamkulu” wotchulidwa pa Danieli 12:1 ndi ndani, nanga akuchita chiyani?

17 Vesi lotsatira mu ulosi wa Danieli limafotokoza za mmene mfumu ya kumpoto ndi mayiko ogwirizana nalo adzawonongedwere komanso mmene tidzapulumukire. (Werengani Danieli 12:1.) Kodi vesili likutanthauza chiyani? Mikayeli ndi dzina lina la Mfumu yathu Khristu Yesu. Iye wakhala ‘ataimirira’ kuti athandize anthu a Mulungu kuyambira mu 1914 pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba. Posachedwapa iye “adzaimirira” kapena kuti adzawononga adani ake pankhondo ya Aramagedo. Nkhondo imeneyi idzakhala chinthu chomaliza pa zomwe zidzachitike pa nthawi yomwe Danieli anaitchula kuti ndi “nthawi ya masautso” aakulu amene sanachitikepo. Ulosi wa Yohane wopezeka m’buku la Chivumbulutso umatchula nthawi imeneyi kuti “chisautso chachikulu.”​—Chiv. 6:2; 7:14.

KODI DZINA LANU “LIDZAKHALA LITALEMBEDWA M’BUKU”?

18. Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kudera nkhawa zam’tsogolo?

18 Tikamaganizira zam’tsogolo, sitiyenera kudera nkhawa chilichonse. Tikutero chifukwa Danieli komanso Yohane ananena kuti pa nthawi ya chisautso chachikulu, Yehova ndi Yesu adzapulumutsa anthu amene amawatumikira. Danieli ananena kuti anthu omwe adzapulumuke ndi amene mayina awo ‘analembedwa m’buku.’ (Dan. 12:1) Ndiye kodi tingatani kuti dzina lathu lilembedwe m’buku limeneli? Tiyenera kusonyeza kuti timakhulupirira Yesu yemwe ndi Mwanawankhosa wa Mulungu. (Yoh. 1:29) Tiyeneranso kudzipereka kwa Mulungu ndi kubatizidwa. (1 Pet. 3:21) Komanso tiyenera kusonyeza kuti tili kumbali ya Ufumu wa Mulungu pothandiza ena kudziwa Yehova.

19. Kodi tiyenera kuchita chiyani panopa, nanga n’chifukwa chiyani?

19 Panopa tiyenera kudalira kwambiri Yehova, ndiponso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye komanso atumiki ake okhulupirika. Inoyonso ndi nthawi imene tiyenera kusonyeza kuti tili kumbali ya Ufumu wa Mulungu. Tikamachita zimenezi, tidzapulumuka Ufumu wa Mulungu ukamadzawononga mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera.

NYIMBO NA.149 Tiimbire Yehova Chifukwa Wapambana

^ ndime 5 Kodi “mfumu ya kumpoto” ndi ndani masiku ano, nanga idzafika bwanji kumapeto a moyo wake? Kudziwa mayankho a mafunsowa kungalimbitse chikhulupiriro chathu komanso kungatithandize kukonzekera mayesero omwe tidzakumane nawo m’tsogolomu.

^ ndime 12 Kuti mumve zambiri zokhudza maulosi opezeka pa Danieli 2:36-45 komanso Chivumbulutso 13:1, 2, onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 2012, tsamba 7-19.