Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 21

Kodi Timayamikira Zinthu Zimene Mulungu Anatipatsa?

Kodi Timayamikira Zinthu Zimene Mulungu Anatipatsa?

“Inu Yehova Mulungu wanga, mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa, ndipo mumatiganizira.”​SAL. 40:5.

NYIMBO NA. 5 Ntchito Zodabwitsa za Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Malinga ndi Salimo 40:5, kodi Yehova anatipatsa mphatso ziti, ndipo kuganizira kwambiri za mphatsozi kungatithandize bwanji?

YEHOVA ndi Mulungu wopatsa. Taganizirani zinthu zina zomwe anatipatsa, monga dziko lathu lokongolali, ubongo wathu wodabwitsa komanso Baibulo lomwe ndi Mawu ake amtengo wapatali. Iye anatipatsa dzikoli kuti tizikhalamo, anatipatsa ubongo kuti tizitha kuganiza ndi kulankhula komanso anatipatsa Baibulo mmene muli mayankho a mafunso ofunika kwambiri omwe timakhala nawo.​—Werengani Salimo 40:5.

2 Mu nkhaniyi, tikambirana mphatso zitatuzi zomwe Mulungu anatipatsa mosaumira. Tikamaganizira kwambiri za mphatsozi m’pamenenso timakhala ndi mtima woyamikira komanso timakhala ofunitsitsa kusangalatsa Yehova yemwe ndi Mlengi wathu. (Chiv. 4:11) Zingatithandizenso kudziwa mmene tingathandizire anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.

DZIKO LAPANSI

3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti dziko lathuli ndi pulaneti lapadera?

3 Timazindikira kuti Mulungu ndi wanzeru kwambiri tikaona mmene analengera dziko lapansili. (Aroma 1:20; Aheb. 3:4) Dziko lapansi ndi limodzi mwa mapulaneti ambiri omwe amazungulira dzuwa. Koma dziko lathuli ndi pulaneti lapadera kwambiri chifukwa lili ndi zonse zofunikira kuti tikhale ndi moyo.

4. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova anapanga dziko lapansi mwanzeru? Perekani chitsanzo.

4 Tingayerekezere dziko lapansili ndi sitima yodzaza ndi anthu yomwe ikuyenda pakatikati panyanja. Koma tingati pali kusiyana kwakukulu pakati pa sitima imeneyi ndi dziko lathu lapansili. Mwachitsanzo, kodi anthu amene ali musitimayi angakhale ndi moyo kwa nthawi yaitali bwanji ngati atamafunika kukonza okha mpweya, chakudya, madzi komanso ngati akungotaya zinyalala m’sitima momwemo? Sangakhale ndi moyo kwa nthawi yaitali. Komatu padzikoli anthu komanso zinyama mabiliyoni zikutha kukhala ndi moyo. Dzikoli limatulutsa mpweya, chakudya komanso madzi okwanira ndipo zinthuzi zimakhalapo nthawi zonse. Ngakhale kuti zinyalala zimatayidwa padziko lomweli, dzikoli limakhalabe lokongola komanso labwino kukhalapo. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Yehova anakonza dziko lapansili m’njira yoti zinthu zomwe zatha ntchito, zithe kukonzedwa ndi kugwiritsidwanso ntchito. Tsopano tikambirana mwachidule mmene mpweya wa okosijeni womwe timapuma umapangidwira komanso tikambirana zokhudza madzi.

5. Kodi mpweya wa okosijeni umapangidwa bwanji, nanga zimenezi zikutsimikizira mfundo iti?

5 Anthufe komanso zinyama timafunikira mpweya wa okosijeni kuti tikhale ndi moyo. Akatswiri ena amati pa chaka chimodzi chokha, timapuma mpweya wa okosijeni wokwana matani handiredi biliyoni. Ndiye tikamapuma, timatulutsa mpweya wotchedwa kaboni daiokisaidi. Komabe okosijeni samatha zamoyozi zikamapuma, komanso kaboni daiokisaidi safika pochuluka kwambiri moti n’kudzaza m’mlengalenga monse. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Zimatheka chifukwa choti Yehova analenganso zomera monga mitengo ndi zina. Zomerazi zimapuma kaboni daiokisaidi ndi kutulutsa okosijeni. Mpweya womwe timapumawu umapangidwa mwa njira imeneyi. Zimenezi zikutsimikizira mawu opezeka pa Machitidwe 17:24, 25, omwe amati: ‘Mulungu amapatsa anthu onse moyo komanso mpweya.’

6. Fotokozani mmene madzi amayendera. Kodi nanga zimenezi zimasonyeza chiyani? (Onaninso bokosi lakuti “ Yehova Anatipatsa Madzi.”)

6 Dzikoli linatalikirana ndi dzuwa pamtunda wabwino moti madzi satentha kwambiri n’kukhala nthunzi kapena kuzizira kwambiri mpaka kuundana. Koma ngati likanayandikira pang’ono, madzi onse akanauma ndipo padzikoli pakanakhala potentha kwambiri komanso popanda zamoyo. Ndipo ngati likanatalikiranso pang’ono, madzi onse akanaundana ndipo dziko lonseli likanakhala ayezi yekhayekha. Choncho Yehova anaika dziko ndi dzuwa pamtunda wabwino zimene zimachititsa kuti padzikoli pakhale madzi omwe amathandiza zamoyo. Dzuwa likawala, madzi apadzikoli amakwera m’mwamba ngati nthunzi ndipo imakakhala mitambo. Chaka chilichonse, madzi amene amakwera m’mwambawa akhoza kudzaza madamu 500,000. Damu lililonse kukula kwake kilomita imodzi m’litali, m’lifupi komanso kuya kwake. Madziwa amakhala m’mlengalenga kwa masiku pafupifupi 10 asanagwe ngati mvula kapena sinowo. Zikatero madziwo amabwereranso m’nyanja kapena m’mitsinje ndipo zimenezi zimachitika mobwerezabwereza. Izi zimasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wanzeru komanso wamphamvu.​—Yobu 36:27, 28; Mlal. 1:7.

7. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira mphatso yomwe yatchulidwa pa Salimo 115:16?

7 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziyamikira dziko lathu lokongolali ndi zinthu zonse zomwe zilimo? (Werengani Salimo 115:16.) Njira imodzi ndi kuganizira mozama zinthu zimene Yehova analenga. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tizimuthokoza tsiku lililonse pa zinthu zabwino zimene amatipatsa. Komanso timasonyeza kuyamikira tikamayesetsa kusamalira malo amene timakhala kuti azikhala aukhondo.

UBONGO WATHU

8. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ubongo wathu unapangidwa modabwitsa?

8 Ubongo wathu unapangidwa modabwitsa kwambiri. Mwana akamakula m’mimba mwa mayi ake, ubongo wake umapangika motsatira dongosolo lapadera ndipo pa miniti iliyonse pamapangika maselo masauzande ambiri. Akatswiri ena amati ubongo wa munthu wamkulu umakhala ndi maselo okwana 100 biliyoni otchedwa manyuroni. Ubongo wamunthu umalemera pafupifupi kilogalamu imodzi ndi hafu, ndipo umapangidwa ndi maselo amenewa. Tiyeni tikambirane zinthu zochepa zomwe zikusonyeza kuti ubongo wathu ndi wogometsa.

9. Kodi n’chiyani chimakutsimikizirani kuti kulankhula ndi mphatso yochokera kwa Mulungu?

9 Kulankhula kumachitika m’njira yodabwitsa kwambiri. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamalankhula? Kuti mutulutse mawu enaake, ubongo wanu umawongolera kayendedwe ka minofu pafupifupi 100 yalilime, yapakhosi, yansagwada, yapachifuwa komanso yamilomo. Kuti mawuwo akhale omveka bwino, minofuyi imafunika kuyenda mwadongosolo. Zotsatira za kafukufuku wina zimene zinatuluka mu 2019 zinasonyeza kuti ana ongobadwa kumene amatha kuzindikira mawu ena ndi ena. Izi zikugwirizana ndi zimene ochita kafukufuku ambiri amakhulupirira kuti anthufe timabadwa ndi luso lozindikira komanso kuphunzira zilankhulo. Kunena zoona, kulankhula ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.​—Eks. 4:11.

10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mphatso ya kulankhula yomwe Mulungu anatipatsa?

10 Kukambirana ndi anthu amene amadabwa kuti n’chifukwa chiyani sitikhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha, ndi njira imodzi imene tingasonyezere kuti timayamikira mphatso ya kulankhula. (Sal. 9:1; 1 Pet. 3:15) Anthuwa amanena kuti dzikoli komanso zamoyo zinangokhalako zokha. Ngati tingagwiritse ntchito Baibulo komanso mfundo zomwe zafotokozedwa mu nkhaniyi, tikhoza kuthandiza anthu kudziwa za Atate wathu wakumwamba. Tingathandizenso anthu a maganizo abwino kuti adziwe chifukwa chake timakhulupirira kuti Yehova ndi amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi.​—Sal. 102:25; Yes. 40:25, 26.

11. N’chiyani chikusonyeza kuti ubongo wathu ndi wodabwitsa?

11 Timakumbukira zinthu modabwitsa kwambiri. M’mbuyomo, katswiri wina wolemba mabuku ananena kuti ubongo wa munthu ukhoza kukumbukira zinthu zomwe zikhoza kulembedwa m’mabuku okwana pafupifupi 20 miliyoni. Koma posachedwapa, akatswiri anapeza kuti ubongo wathu ukhoza kukumbukira zinthu zambiri kuposa pamenepa. Ndiye chifukwa chakuti ubongo wathu umakumbukira zinthu moteremu, kodi timatha kuchita chiyani?

12. Kodi anthufe timasiyana bwanji ndi zamoyo zina pa nkhani yophunzira zinthu?

12 Pa zamoyo zonse zomwe zili padzikoli, ndi anthu okha omwe amatha kuphunzira zinthu pokumbukira zomwe zinawachitikira m’mbuyo. Zimenezi zimatithandiza kukhazikitsa mfundo zoti tiziyendera komanso kusintha mmene timaonera zinthu. (1 Akor. 6:9-11; Akol. 3:9, 10) Timatha kuphunzitsa chikumbumtima chathu kuti chizitha kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera. (Aheb. 5:14) Timathanso kuphunzira kukonda ndi kusonyeza chifundo anthu ena. Komanso timaphunzira kuchita zinthu mwachilungamo potsanzira Yehova.

13. Malinga ndi Salimo 77:11, 12, kodi tiyenera kugwiritsa ntchito bwanji mphatso yokumbukira zinthu yomwe tinapatsidwa?

13 Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timayamikira mphatso yokumbukira zinthu, ndi kuyesetsa kukumbukira maulendo onse omwe Yehova wakhala akutithandiza. Zimenezi zingatilimbitse mtima kuti ngakhale m’tsogolo, Yehova adzakhalabe nafe. (Werengani Salimo 77:11, 12; 78:4, 7) Njira inanso, ndi kukumbukira zinthu zabwino zomwe anthu ena anatichitira komanso kuwayamikira chifukwa cha zomwe amachita. Ochita kafukufuku anapeza kuti anthu amene amayamikira ena amakhala osangalala. Tingachitenso bwino kutsanzira Yehova posankha kuiwala zinthu zina. Timadziwa kuti iye amakumbukira bwino zinthu, komabe tikalapa zolakwa zathu, amatikhululukira ndipo amaiwala zomwe tamulakwirazo. (Sal. 25:7; 130:3, 4) Yehova amafunanso kuti tizichita zimenezi kwa anzathu akatipepesa pa zomwe anatilakwira.​—Mat. 6:14; Luka 17:3, 4.

Timasonyeza kuyamikira kuti Yehova anatipatsa ubongo tikamaugwiritsa ntchito pomulemekeza (Onani ndime 14) *

14. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira Mulungu kuti anatipatsa ubongo?

14 Tingasonyeze kuyamikira Mulungu kuti anatipatsa ubongo tikamaugwiritsa ntchito pomulemekeza. Anthu ena amagwiritsa ntchito ubongo wawo pochita zinthu zongodzisangalatsa. Amachita zimenezi posankha okha zomwe akuona kuti n’zoyenera ndi zosayenera. Koma ndi nzeru kuyembekezera kuti Yehova azitiuza zomwe zili zoyenera ndi zosayenera chifukwa iye ndi amene anatilenga. (Aroma 12:1, 2) Tikamatsatira mfundo zake, timakhala pamtendere. (Yes. 48:17, 18) Timamvetsanso kuti anatilenga n’cholinga choti tizimulemekeza monga Mlengi komanso Atate wathu ndiponso kuti tizichita zinthu zomusangalatsa.​—Miy. 27:11.

BAIBULO

15. Kodi Mulungu anasonyeza bwanji kuti amatikonda potipatsa Baibulo?

15 Baibulo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Atate wathu wakumwamba anauzira anthu ena kuti alembe bukuli chifukwa choti amatikonda kwambiri. Yehova amagwiritsa ntchito Baibulo potiyankha mafunso ofunika kwambiri omwe timakhala nawo. Mafunso monga akuti: Kodi anthufe tinachokera kuti? Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? Kodi tiziyembekezera zotani m’tsogolomu? Yehova amafuna kuti tonse tidziwe mayankho a mafunso amenewa, choncho kuyambira kalekale wakhala akuthandiza anthu kuti amasulire Baibulo m’zilankhulo zambiri. Masiku ano, Baibulo lonse kapena mbali yake, limapezeka m’zilankhulo zoposa 3,000. Palibe buku lomwe linamasuliridwapo komanso kufalitsidwa kwambiri kuposa Baibulo. Kulikonse anthu ali ndi mwayi wophunzira uthenga wa m’Baibulo m’zilankhulo zawo.​—Onani bokosi lakuti, “ Baibulo Likupezeka M’zilankhulo za ku Africa.”

16. Mogwirizana ndi Mateyu 28:19, 20, kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Baibulo?

16 Tingasonyeze kuyamikira Mulungu kuti anatipatsa Baibulo, tikamaliwerenga tsiku lililonse, kuganizira mozama zimene tikuphunzira komanso kuyesetsa kutsatira zimene tikuphunzirazo. Timasonyezanso kuyamikira tikamachita zonse zimene tingathe pouza ena uthenga wa m’Baibulo.​—Sal. 1:1-3; Mat. 24:14; werengani Mateyu 28:19, 20.

17. Kodi mu nkhaniyi takambirana mphatso ziti, nanga tidzakambirana chiyani mu nkhani yotsatira?

17 Mu nkhaniyi takambirana mphatso zingapo zimene Mulungu anatipatsa, zomwe ndi dziko lathu lapansili, ubongo wathu komanso Baibulo lomwe ndi Mawu ouziridwa a Mulungu. Koma palinso zinthu zina zomwe Mulungu watipatsa zimene sitingathe kuziona. Mu nkhani yotsatira tidzakambirana zinthu zimenezi.

NYIMBO NA. 12 Yehova Ndi Mulungu Wamkulu

^ ndime 5 Nkhaniyi itithandiza kuti tiziyamikira Yehova chifukwa cha zinthu zomwe anatipatsa. Itithandizanso kudziwa zimene tinganene pokambirana ndi anthu amene amakayikira zoti kuli Mulungu.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo akuphunzira chilankhulo china n’cholinga choti aziphunzitsa anthu ochokera dziko lina choonadi cha m’Mawu a Mulungu.