Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufatsa​—Kodi N’kofunika Bwanji?

Kufatsa​—Kodi N’kofunika Bwanji?

Mlongo wina dzina lake Sara * anati: “Ndine wamanyazi kwambiri komanso ndimadzikayikira. Ndiye zimandivuta ndikakhala ndi anthu ochita zinthu mwaphuma ndiponso osaugwira mtima. Koma ndimamva bwino ndikakhala ndi munthu wofatsa komanso wodzichepetsa. Ndimatha kumasuka kumuuza mavuto anga komanso mmene ndikumvera. Ndi mmene anzanga ambiri alili.”

Zimene Sara ananenazi zikusonyeza kuti munthu akakhala wofatsa, anthu ena amafuna akhale mnzawo. Komanso Yehova amasangalala ndi anthu ofatsa. N’chifukwa chake m’Mawu ake amatilangiza kuti: “Valani . . . kufatsa.” (Akol. 3:12) Ndiye kodi munthu wofatsa amatani? Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wofatsa? Nanga khalidweli lingatithandize bwanji kukhala osangalala?

KODI MUNTHU WOFATSA AMATANI?

Munthu wofatsa ndi amene amatha kuugwira mtima n’kumachita zinthu mwamtendere. Zimenezi zimamuthandiza kuti pochita zinthu ndi ena asamapupulume koma azichita nawo mokoma mtima. Akakumana ndi zinthu zokhumudwitsa amakhala wodekha komanso wodziletsa.

Kufatsa si kupusa. M’chigiriki mawu akuti “kufatsa” amagwiritsidwa ntchito ponena za hatchi yam’tchire imene munthu akuweta. Mphamvu za hatchiyi sizisintha, koma chifukwa chakuti akuiweta imaphunzira kulamulira mphamvu zakezo. Mofanana ndi zimenezi, tikakhala wofatsa timaphunzira kulamulira mtima wathu kuti tizichita zinthu mwamtendere ndi ena.

Mwina tinganene kuti, ‘Mwachibadwa munthune si wofatsa.’ N’zoona kuti m’dzikoli anthu ambiri amachita zinthu mwaphuma komanso saleza mtima ndiye zingakhale zovuta kuti tikhale ofatsa. (Aroma 7:19) Choncho pamafunika khama kuti tikhale ndi khalidweli koma Yehova angatithandize ndi mzimu wake kuti tikwanitse kukhala ofatsa. (Agal. 5:22, 23) Koma kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tikhale ofatsa?

Anthu amakopeka ndi munthu wofatsa. Mofanana ndi Sara yemwe tamutchula uja, tonsefe timamva bwino tikakhala ndi anthu ofatsa. Yesu ndi chitsanzo chabwino cha munthu wofatsa komanso wokoma mtima. (2 Akor. 10:1) Ngakhale ana omwe sankamudziwa n’komwe, ankafuna kucheza naye.​—Maliko 10:13-16.

Kukhala ofatsa kumathandiza ifeyo komanso anthu ena. Tikakhala ofatsa sitikwiya msanga pakachitika zokhumudwitsa. (Miy. 16:32) Zimenezi zimatithandiza kuti tisamadziimbe mlandu chifukwa chokhumudwitsa ena, makamaka anthu amene timawakonda. Kufatsa kumathandizanso anthu ena kuti asavutike chifukwa sitichita zinthu mopupuluma.

CHITSANZO CHABWINO KWAMBIRI PA NKHANI YA KUFATSA

Ngakhale kuti Yesu anali ndi zochita zambiri komanso ankatanganidwa, iye ankachita zinthu mofatsa ndi anthu onse. Anthu ambiri mu nthawi yake ankafunika kutsitsimulidwa chifukwa anali olemedwa komanso ankalimbana ndi zambiri. Ayeneratu kuti anatsitsimulidwa kwambiri pamene Yesu anawauza kuti: “Bwerani kwa ine . . . chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa.”​—Mat. 11:28, 29.

Kodi tingatani kuti tikhale wofatsa ngati Yesu? Tikamaphunzira Mawu a Mulungu timadziwa mmene Yesu ankachitira zinthu ndi ena komanso zimene ankachita pakakhala zovuta zina. Ndiyeno pakachitika zinthu zofuna kuti tisonyeze kufatsa, timayesetsa kutsanzira Yesu. (1 Pet. 2:21) Tiyeni tione zinthu zitatu zomwe zinathandiza Yesu kuti akhale wofatsa.

Yesu anali wodzichepetsa. Yesu ananena kuti iye anali “wofatsa ndi wodzichepetsa.” (Mat. 11:29) Makhalidwe awiriwa Baibulo limawatchulira pamodzi chifukwa kufatsa kumayendera limodzi ndi kudzichepetsa. (Aef. 4:1-3) N’chifukwa chiyani tikutero?

Kudzichepetsa kumatithandiza kuti tisamakwiye msanga wina akatilankhula kapena kutichitira zinthu zokhumudwitsa. Kodi Yesu anatani anthu atamunena kuti ndi “wosusuka” komanso “wokonda kwambiri vinyo”? Iye analola kuti zochita zake zitsutse zimene ankamunenazo. Komanso ananena mofatsa kuti “nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.”​—Mat. 11:19.

Ngati wina atalankhula mokunyozani chifukwa cha mtundu wanu, chifukwa chakuti ndinu mwamuna kapena mkazi, kapena chifukwa cha kumene munabadwira, mungachite bwino kumuyankha mofatsa. Peter, yemwe ndi mkulu ku South Africa, anati: “Munthu wina akandilankhula zokhumudwitsa, ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi Yesu akanatani pamenepa?’” Ananenanso kuti: “Panopa ndaphunzira kuti ndisamakhumudwe msanga ndi zochita za ena.”

Yesu ankadziwa kuti anthu ndi opanda ungwiro. Ophunzira a Yesu ankafuna kumachita zabwino koma nthawi zina ankalephera kuchita zimene ankafunazo chifukwa cha kupanda ungwiro. Mwachitsanzo, usiku woti Yesu aphedwa mawa lake, Petulo, Yakobo ndi Yohane analephera kukhalabe maso ndi Yesu ngakhale kuti anawapempha kuti asagone. Yesu anawamvetsa ndipo anati: “Mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Mat. 26:40, 41) Kuzindikira zimenezi kunamuthandiza kuti asawakwiyire atumwi akewo.

Poyamba mlongo wina dzina lake Mandy ankakonda kuweruza ena, koma tsopano amayesetsa kukhala wofatsa potsanzira Yesu. Iye anati, “Ndimayesetsa kukumbukira kuti aliyense ndi wopanda ungwiro ndiye ndimaganizira kwambiri zinthu zabwino zimene amachita. Yehovanso amaona zabwino mwa ena.” Yesu ankamvetsa kuti anthu ndi opanda ungwiro. Kutengera chitsanzo chake kungatithandize kuti nafenso tizichita zinthu ndi ena mofatsa.

Yesu ankadalira Mulungu. Yesu ali padziko lapansi anapirira zinthu zopanda chilungamo. Anthu ena sankamumvetsa, ankamunyoza komanso kumuzunza. Ngakhale zinali choncho, iye anakhalabe wofatsa chifukwa ‘anadzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.’ (1 Pet. 2:23) Yesu ankadziwa kuti Atate wake wakumwamba amuthandiza kuti apirire komanso kuti adzathana ndi onse amene amamuzunza.

Winawake akatichitira zopanda chilungamo, ifeyo n’kulephera kuugwira mtima tikhoza kungopangitsa kuti zinthu ziipireipire. N’chifukwa chake Malemba amatikumbutsa kuti: “Mkwiyo wa munthu subala chilungamo cha Mulungu.” (Yak. 1:20) Ngakhale patakhala chifukwa chomveka choti tikwiyire, kupanda ungwiro kungachititse kuti tichite zinthu zosayenera.

Mlongo wina wa ku Germany dzina lake Cathy, poyamba ankaganiza kuti, ‘Ngati sungadziteteze wekha, anthu akhoza kumangokutola.’ Koma atayamba kudalira Mulungu, anasintha maganizo ake. Iye anati: “Panopa sindilankhulanso mofuna kudziteteza nthawi zonse. Ndimachita zinthu mofatsa chifukwa ndikudziwa kuti Yehova adzakonza zonse.” Ngati munachitiridwapo zinthu zopanda chilungamo, chitsanzo cha Yesu podalira Mulungu chingakuthandizeni kuti mukhalebe ofatsa.

“ODALA NDI ANTHU AMENE ALI OFATSA”

Kodi kufatsa kungatithandize bwanji pakakhala zovuta zina?

Yesu ananena kuti ngati tikufuna kuti tizisangalala, tiyenera kukhala ofatsa. Iye anati: “Odala ndi anthu amene ali ofatsa.” (Mat. 5:5) Tiyeni tione mmene kufatsa kungatithandizire pazochitika zotsatirazi.

Kufatsa kungachepetse kusamvana m’banja. M’bale wina wa ku Australia, dzina lake Robert, anati: “Ndakhala ndikulankhula mawu ongofuna kumupweteketsa mtima mkazi wanga ngakhale kuti si zomwe ndinkatanthauza. Koma munthu ukalankhula mawu sungathenso kuwabweza. Ndinkamva chisoni kwambiri kuona mmene zinkamukhudzira.”

“Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri” polankhula ndipo kulankhula mosaganiza bwino kungasokoneze mtendere m’banja. (Yak. 3:2) Zikatere, kufatsa kungathandize kuti tiugwire mtima komanso kuti tilankhule mawu abwino.​—Miy. 17:27.

Robert anayesetsa kuti aziugwira mtima komanso kuti azidziletsa. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Iye anati: “Masiku ano, tikasemphana maganizo, ndimayesetsa kumumvetsera bwino, kulankhula mofatsa komanso kudzigwira kuti ndisakwiye kwambiri. Panopa timagwirizana kwambiri ndi mkazi wanga.”

Kufatsa kumatithandiza kuti tizigwirizana ndi ena. Anthu amene amakwiya msanga sakhala ndi anzawo ambiri. Koma kufatsa kungatithandize kukhala “mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa.” (Aef. 4:2, 3) Cathy, yemwe tamutchula kale uja anati, “Kufatsa kwandithandiza kuti ndizicheza bwino ndi aliyense, ngakhalenso anthu amene ndi ovuta kuchita nawo zinthu.”

Kufatsa kumatithandiza kukhala ndi mtendere wamumtima. Baibulo limasonyeza kuti “nzeru yochokera kumwamba” imathandiza munthu kukhala wofatsa komanso wamtendere. (Yak. 3:13, 17) Munthu wofatsa amakhala ndi “mtima wodekha.” (Miy. 14:30) Martin, yemwe anachita khama kuti akhale wofatsa, anati: “Panopa sindikakamiranso maganizo anga, ndili ndi mtendere wamumtima komanso ndine wosangalala.”

N’zoona kuti tingafunike kuchita khama kuti tikhale ofatsa. M’bale wina anati: “Kunena zoona, mpaka pano nthawi zina zimandivutabe kuti ndiugwire mtima.” Koma Yehova amene amatilimbikitsa kuti tikhale ofatsa, angatithandize. (Yes. 41:10; 1 Tim. 6:11) Iye ‘adzamalizitsa kutiphunzitsa,’ komanso ‘adzatipatsa mphamvu.’ (1 Pet. 5:10) Mofanana ndi Paulo, ifenso n’kupita kwa nthawi tidzakwanitsa kutsanzira “kufatsa ndi kukoma mtima kwa Khristu.”​—2 Akor. 10:1.

^ ndime 2 Mayina ena asinthidwa.