Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafumu Awiri Olimbana M’nthawi ya Mapeto

Mafumu Awiri Olimbana M’nthawi ya Mapeto

Maulosi omwe ali patchatichi akufotokoza zinthu zina zomwe zinachitika pa nthawi yofanana. Maulosiwa amatitsimikizira kuti tikukhala mu “nthawi yamapeto.”​—Dan. 12:4.

  • Malemba Chiv. 11:7; 12:13, 17; 13:1-8, 12

    Ulosi “Chilombo” chakhala chikulamulira kwa zaka zoposa 3,000. Mu nthawi yamapeto, mutu wake wa 7 unavulazidwa. Kenako, unachira ndipo “dziko lonse lapansi” linatsatira chilombocho. Satana anagwiritsa ntchito chilombochi ‘kuchita nkhondo ndi otsala a mbewu’ ya mkazi.

    Kukwaniritsidwa Pambuyo pa Chigumula cha Nowa, maboma otsutsana ndi Yehova anayamba kulamulira anthu. Ndiye patapita zaka zoposa 3,000, pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, boma la Britain linachepa mphamvu kwambiri. Koma linakhalanso ndi mphamvu litagwirizana ndi dziko la United States. Mu nthawi yamapeto, Satana akugwiritsa ntchito maboma onse padziko lapansi kuzunza anthu a Mulungu.

  • Lemba Dan. 11:25-45

    Ulosi Kulimbana kwa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera m’nthawi yamapeto.

    Kukwaniritsidwa Dziko la Germany linamenyana ndi mayiko a Britain ndi America. Mu 1945 boma la Soviet Union ndi mayiko ogwirizana nalo linakhala mfumu ya kumpoto. Mu 1991, ulamuliro wa Soviet Union unatha ndipo m’kupita kwa nthawi dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo ndi amene anakhala mfumu ya kumpoto.

  • Malemba Yes. 61:1; Mal. 3:1; Luka 4:18

    Ulosi Ufumu wa Mesiya usanakhazikitsidwe, Yehova anatumiza “mthenga” wake kuti ‘akakonze njira.’ Mthengayu anayamba kulengeza “uthenga wabwino kwa anthu ofatsa.”

    Kukwaniritsidwa Kuyambira m’ma 1870, M’bale Russell ndi anzake ankaphunzira Baibulo mwakhama kuti azifotokoza bwino mfundo zachoonadi. M’ma 1880, anazindikira kuti n’zofunika kwambiri kuti atumiki a Mulungu azilalikira. Anatulutsa nkhani zokhudza kulalikira monga yakuti “Alaliki 1,000 Akufunika” ndi yakuti “Anadzozedwa Kuti Azilalikira.”

  • Lemba Mat. 13:24-30, 36-43

    Ulosi Mdani anafesa namsongole m’munda wa tirigu. Namsongoleyo anakula n’kufika pophimba tirigu. Nthawi yokolola itakwana namsongole analekanitsidwa ndi tirigu.

    Kukwaniritsidwa Kuyambira chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, kusiyana pakati pa Akhristu oona ndi onyenga kunayamba kuonekera. M’nthawi yamapeto, Akhristu oona anayamba kusonkhanitsidwa mumpingo komanso kulekanitsidwa ndi Akhristu onyenga.

  • Lemba Dan. 2:31-33, 41-43

    Ulosi Mapazi achitsulo chosakanizika ndi dongo a chifaniziro chopangidwa ndi mitundu yosiyanasiyana yazitsulo.

    Kukwaniritsidwa Dongo likuimira anthu wamba mu ulamuliro wa Britain ndi America omwe amatha kuchita zinthu zotsutsana ndi ulamulirowu. Anthu amenewa amalepheretsa ulamuliro wamphamvuwu kusonyeza mphamvu zake zonse.

  • Malemba Mat. 13:30; 24:14, 45; 28:19, 20

    Ulosi “Tirigu” anasonkhanitsidwa n’kumuika “m’nkhokwe” ndipo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anaikidwa kuti aziyang’anira ‘antchito apakhomo.’ Ntchito yolalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ inayamba kufalikira “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”

    Kukwaniritsidwa Mu 1919 kapolo wokhulupirika ndi wanzeru anaikidwa kuti aziyang’anira anthu a Mulungu. Kuyambira nthawiyi, Ophunzira Baibulo akhala akuchita khama pogwira ntchito yolalikira. Masiku ano, a Mboni za Yehova akulalikira m’mayiko oposa 200 ndipo amafalitsa mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa 1,000.

  • Malemba Dan. 12:11; Chiv. 13:11, 14, 15

    Ulosi Chilombo cha nyanga ziwiri chinatsogolera popanga “chifaniziro cha chilombo” ndipo chinapereka “mpweya ku chifaniziro cha chilombo chija.”

    Kukwaniritsidwa Ulamuliro wa Britain ndi America unatsogolera pokhazikitsa bungwe la League of Nations. M’bungweli munalowanso mayiko ena. Patapita nthawi, mfumu ya kumpoto nayonso inalowamo koma inangokhalamo kuyambira mu 1926 kufika mu 1933. Monga zilili ndi bungwe la United Nations (UN) panopa, anthu ankakhulupiriranso kuti bungweli lingabweretse mtendere, zomwe ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungakwanitse.

  • Lemba Dan. 8:23, 24

    Ulosi Mfumu ya maonekedwe oopsa “idzawononga zinthu zambiri.”

    Kukwaniritsidwa Ulamuliro wa Britain ndi America wapha anthu ambiri komanso kuwononga zinthu zambiri. Mwachitsanzo, pa nthawi yankhondo yachiwiri yapadziko lonse dziko la United States linaponya mabomba awiri m’dziko la adani awo. Mabombawo anawononga kwambiri kuposa mabomba onse m’mbuyomo.

  • Malemba Dan. 11:31; Chiv. 17:3, 7-11

    Ulosi “Chilombo chofiira kwambiri” cha nyanga 10, chomwenso ndi mfumu ya 8, chinatuluka kuphompho. Buku la Danieli limanena kuti mfumuyi ndi “chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko.”

    Kukwaniritsidwa Pa nthawi yankhondo yachiwiri yapadziko lonse bungwe la League of Nations linathetsedwa. Nkhondoyi itatha bungwe la UN, ‘linaikidwa m’malomwake.’ Mofanana ndi la League of Nations, bungwe la UN limapatsidwa ulemerero woyenera Ufumu wa Mulungu.

  • Malemba 1 Ates. 5:3; Chiv. 17:16

    Ulosi Mayiko akulengeza za “bata ndi mtendere” ndipo “nyanga 10” komanso “chilombo” zikuukira “hule” ndi kuliwononga. Kenako mitundu ya anthu ikuwonongedwa.

    Kukwaniritsidwa Mayiko adzanena kuti akwanitsa kubweretsa bata ndi mtendere. Kenako mayiko amene ali m’bungwe la UN adzawononga zipembedzo zonyenga. Kumeneku kudzakhala kuyamba kwa chisautso chachikulu. Chisautsochi chidzafika kumapeto pa Aramagedo, Yesu akadzawononga dziko lonse la Satanali.

  • Malemba Ezek. 38:11, 14-17; Mat. 24:31

    Ulosi Gogi adzaukira anthu a Mulungu. Kenako, angelo adzasonkhanitsa “osankhidwa.”

    Kukwaniritsidwa Mfumu ya kumpoto limodzi ndi maboma onse a padziko lapansi adzaukira anthu a Mulungu. Zimenezi zikadzangoyamba kuchitika, Akhristu odzozedwa omwe adakali padzikoli adzatengedwa kupita kumwamba.

  • Malemba Ezek. 38:18-23; Dan. 2:34, 35, 44, 45; Chiv. 6:2; 16:14, 16; 17:14; 19:20

    Ulosi “Wokwera” pa “hatchi yoyera” “anapambana pa nkhondo yolimbana” ndi Gogi ndi asilikali ake. “Chilombo” “chinaponyedwa m’nyanja ya moto” ndipo mwala unaphwanya chifaniziro chachikulu.

    Kukwaniritsidwa Yesu, amene ndi Mfumu yomwe ikulamulira mu Ufumu wa Mulungu adzapulumutsa anthu a Mulungu. Iye pamodzi ndi anzake 144,000 komanso angelo, adzawononga maboma onse omwe adzaukira anthu a Mulungu. Amenewa adzakhala mapeto a dziko la Satanali.