Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 22

Tiziyamikira Chuma Chosaoneka Chomwe Tili Nacho

Tiziyamikira Chuma Chosaoneka Chomwe Tili Nacho

“Tikuika maso athu pa zinthu zosaoneka,  . . Pakuti zooneka n’zakanthawi, koma zosaoneka n’zamuyaya.”​—2 AKOR. 4:18.

NYIMBO NA. 45 Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yesu anafotokoza zotani zokhudza chuma chakumwamba?

ZINTHU zomwe ndi zamtengo wapatali kwambiri sizioneka ndi maso. Paulaliki wa paphiri, Yesu anatchula zinthu zakumwamba zomwe ndi zamtengo wapatali kuposa chuma. Anawonjezeranso kuti: “Kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko.” (Mat. 6:19-21) Mtima wathu umatichititsa kuti tizifunafuna zinthu zomwe timaona kuti ndi zofunika kwambiri. Timasunga ‘chuma chathu kumwamba,’ ngati tili ndi mbiri yabwino kwa Mulungu. Ndipo Yesu anafotokoza kuti chuma chimenechi sichingawonongeke kapena kubedwa.

2. (a) Mogwirizana ndi 2 Akorinto 4:17, 18, kodi Paulo anatilimbikitsa kuti tizichita chiyani? (b) Kodi tikambirana chiyani mu nkhaniyi?

2 Mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti ‘tiziika maso athu pa zinthu zosaoneka.’ (Werengani 2 Akorinto 4:17, 18.) Zinthu zosaonekazi ndi zamtengo wapatali kwambiri ndipo zikuphatikizapo madalitso omwe tidzasangalale nawo m’dziko latsopano. Mu nkhaniyi tikambirana zinthu 4 zimene tingati ndi chuma chosaoneka chomwe tingapeze panopa. Zinthuzi ndi monga kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, mphatso ya pemphero, mphatso ya mzimu woyera wa Mulungu komanso thandizo lomwe Yehova, Yesu ndi angelo amatipatsa tikamalalikira. Tikambirananso mmene tingasonyezere kuti timayamikira chuma chosaoneka chimenechi.

KUKHALA PA UBWENZI NDI YEHOVA

3. Kodi chuma cha mtengo wapatali kwambiri kuposa zonse n’chiyani, nanga tingachipeze bwanji?

3 Kukhala pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu ndi chuma cha mtengo wapatali kwambiri kuposa zonse. (Sal. 25:14) Kodi zimatheka bwanji kuti Mulungu akhale pa ubwenzi ndi anthu opanda ungwiro koma iyeyo n’kukhalabe woyera? Zimatheka chifukwa cha nsembe ya Yesu imene ‘imachotsa uchimo wa dziko.’ (Yoh. 1:29) Ngakhale Yesu asanabwere padzikoli, Yehova ankadziwa kuti Mwana wakeyo adzakhala wokhulupirika mpaka imfa yake ndipo adzamugwiritsa ntchito pokwaniritsa cholinga chake chopulumutsa anthu. Ichi n’chifukwa chake Mulungu anatha kukhala pa ubwenzi ndi anthu akale omwe anakhalapo Khristu asanabwere kudzafera anthu.​—Aroma 3:25.

4. Tchulani zitsanzo za anthu amene anakhalako Chikhristu chisanayambe omwe anali mabwenzi a Mulungu.

4 Taonani zitsanzo za anthu amene anakhalako Chikhristu chisanayambe omwe anali mabwenzi a Mulungu. Abulahamu anali munthu wachikhulupiriro cholimba. Patadutsa zaka zoposa 1,000 Abulahamu atamwalira, Yehova anamutchula kuti “bwenzi langa.” (Yes. 41:8) Zimenezi zikutanthauza kuti ngakhale anthu amwalire, Yehova amawaonabe kuti ndi mabwenzi ake a pamtima. Tingati kwa Yehova, Abulahamu adakali wamoyo. (Luka 20:37, 38) Chitsanzo china ndi Yobu. Pamene angelo anasonkhana kumwamba, Yehova analankhula motsimikiza zokhudza kukhulupirika kwa Yobu. Iye anamutchula kuti anali “munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima, woopa Mulungu ndi wopewa zoipa.” (Yobu 1:6-8) Nayenso Danieli anatumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka pafupifupi 80 ali m’dziko la anthu amene sankalambira Yehova. Ndiye kodi Yehova ankamuona bwanji? Katatu konse angelo anamutsimikizira kuti iye anali “munthu wokondedwa kwambiri” ndi Mulungu. (Dan. 9:23; 10:11, 19) N’zoonekeratu kuti Yehova amachita kulakalaka kuti adzaukitse mabwenzi ake a pamtima omwe anamwalira.​—Yobu 14:15.

Kodi ndi njira zina ziti zomwe tingasonyezere kuti timayamikira chuma chosaoneka? (Onani ndime 5) *

5. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova?

5 Kodi ndi anthu angati masiku ano omwe akusangalala kukhala pa ubwenzi ndi Yehova? Alipo mamiliyoni ambiri. Tikutero chifukwa padziko lonse pali amuna, akazi komanso ana ambiri amene akuchita zinthu zosonyeza kuti ndi mabwenzi a Mulungu. Yehova “amakonda anthu owongoka mtima.” (Miy. 3:32) Anthuwa amakhala pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa amakhulupirira nsembe ya Yesu. Chifukwa cha nsembeyi, timatha kudzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa. Tikachita zinthu zofunika zimenezi, timakhala m’gulu la Akhristu mamiliyoni amene nawonso anadzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa, ndipo akusangalala kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, yemwe ndi wamkulu kuposa wina aliyense.

6. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu?

6 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona ubwenzi wathu ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali? Mofanana ndi Abulahamu komanso Yobu, omwe anakhala okhulupirika kwa Mulungu kwa zaka zoposa 100, nafenso tiyenera kukhalabe okhulupirika ngakhale titamutumikira kwa zaka zambiri m’dziko lakaleli. Mofanana ndi Danieli, nafenso tiziona kuti kukhala pa ubwenzi ndi Yehova n’kofunika kwambiri kuposa moyo wathu. (Dan. 6:7, 10, 16, 22) Yehova angatithandize kuti tipirire mayesero aliwonse amene tingakumane nawo n’kupitirizabe kukhala naye pa ubwenzi wolimba.​—Afil. 4:13.

MPHATSO YA PEMPHERO

7. (a) Mogwirizana ndi Miyambo 15:8, kodi Yehova amamva bwanji tikamapemphera? (b) Kodi Yehova amayankha bwanji mapemphero athu?

7 Chinthu china cha mtengo wapatali chomwe sitingathe kuchiona ndi pemphero. Anthu omwe ndi mabwenzi apamtima amamasukirana kuuzana zakukhosi. Umu ndi mmenenso ziyenera kukhalira pa ubwenzi wathu ndi Yehova. Yehova amatilankhula kudzera m’Mawu ake. Tikamawawerenga timadziwa maganizo ake komanso mmene amamvera. Ifenso timalankhula naye kudzera m’pemphero ndipo tingathe kumufotokozera zimene zili mumtima mwathu komanso mmene tikumvera. Ndipotu Yehova amasangalala kwambiri tikamamuuza maganizo athu. (Werengani Miyambo 15:8) Pokhala iye ndi bwenzi lathu lapamtima, amamvetsera ndi kuyankha mapemphero athu. Nthawi zina angayankhe mapemphero athu mofulumira koma pena tingafunike kupitirizabe kupempherera nkhaniyo. Koma timakhala otsimikiza kuti adzatiyankha pa nthawi yake komanso m’njira yoyenera. Zingathekenso kuti yankho limene Mulungu angatipatse lingakhale losiyana ndi lomwe timayembekezera. Mwachitsanzo, mwina m’malo motithetsera mavuto ena ake, angangotipatsa nzeru komanso mphamvu zoti tithe “kuwapirira.”​—1 Akor. 10:13.

(Onani ndime 8) *

8. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mphatso yapemphero?

8 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mphatso yamtengo wapatali yapemphero? Njira ina ndi kutsatira malangizo akuti ‘tizipemphera mosalekeza.’ (1 Ates. 5:17) Yehova satikakamiza kuti tizipemphera. Koma amalemekeza ufulu wathu ndipo amatilimbikitsa kuti ‘tizilimbikira kupemphera.’ (Aroma 12:12) Choncho tikamapemphera pafupipafupi tsiku lililonse, tidzasonyeza kuti timayamikira mphatsoyi. Popemphera tisamaiwalenso kutamanda ndi kuyamikira Yehova.​—Sal. 145:2, 3.

9. Kodi m’bale wina amaiona bwanji mphatso yapemphero, nanga inuyo mumaiona bwanji?

9 Tikatumikira Yehova kwa zaka zambiri ndi kuona mmene amayankhira mapemphero athu, timayamikira kwambiri mwayi wa pemphero umene anatipatsa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina wotchedwa Chris, yemwe wakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 47. Iye anati: “Ndimakonda kupemphera kwa Yehova m’mawa kwambiri. Zimakhala bwino kuyamba tsiku mwanjira imeneyi chifukwa zimandipatsa mwayi womuthokoza pa mphatso zonse zomwe amandipatsa kuphatikizapo mphatso yapemphero. Ndimapempheranso tsiku likamatha, ndipo ndimasangalala kupita kukagona ndili ndi chikumbumtima chabwino.”

MPHATSO YA MZIMU WOYERA

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira mphatso ya mzimu wa Mulungu?

10 Chinthu chinanso cha mtengo wapatali chomwe sitingathe kuchiona ndi mphatso ya mzimu woyera. Yesu anatilimbikitsa kuti tizipempha mzimuwu. (Luka 11:9, 13) Pogwiritsa ntchito mzimu wake, Yehova amatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akor. 4:7; Mac. 1:8) Mzimu wa Mulungu ungatithandize kuti tithe kupirira mayesero aliwonse amene tingakumane nawo.

(Onani ndime 11) *

11. Kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji?

11 Mzimu woyera umatithandiza kuti tikwanitse kuchita mautumiki osiyanasiyana ndipo ungatithandize kukulitsa luso limene tingakhale nalo. Choncho timadziwa kuti zilizonse zimene timakwanitsa kuchita potumikira Mulungu zimatheka chifukwa iye amatithandiza ndi mzimu wake.

12. Mogwirizana ndi Salimo 139:23, 24, kodi tingapemphe kuti mzimu woyera wa Mulungu uzitithandiza kuchita chiyani?

12 Njira ina imene tingasonyezere kuti timayamikira mphatso ya mzimu woyera ndi kupempha kuti uzitithandiza kudzifufuza kuti tione ngati tayamba kukhala ndi maganizo olakwika mumtima wathu. (Werengani Salimo 139:23, 24.) Tikatero, Yehova angagwiritse ntchito mzimu wake kutithandiza kuzindikira maganizo olakwikawo komanso zomwe tingachite kuti tiwapewe. Tikamachita zimenezi tingasonyeze kuti sitikufuna kuchita chilichonse chomwe chingachititse kuti Yehova asiye kutithandiza ndi mzimu wake woyera.​—Aef. 4:30.

13. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziyamikira kwambiri mphatso ya mzimu woyera?

13 Timayamikiranso kwambiri mphatso ya mzimu woyera tikamaganizira zimene ukutithandiza kuchita masiku ano. Yesu asanapite kumwamba, anauza ophunzira ake kuti: “Mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Mawu amenewa akukwaniritsidwa masiku ano. Mothandizidwa ndi mzimu woyera, anthu pafupifupi 8.5 miliyoni padziko lonse akulambira Yehova. Komanso monga anthu a Mulungu tikusangalala ndi paradaiso wauzimu chifukwa mzimu wa Mulungu umatithandiza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino. Makhalidwewa ndi monga chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa komanso kudziletsa. Amenewa ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” (Agal. 5:22, 23) Kunena zoona mzimu woyera ndi mphatso yamtengo wapatali.

YEHOVA, YESU KOMANSO ANGELO AMATITHANDIZA TIKAMALALIKIRA

14. Kodi ndi mphatso yosaoneka iti yomwe imatithandiza tikamalalikira?

14 Tilinso ndi mphatso ina yamtengo wapatali yosaoneka yomwe ndi ‘kugwira ntchito limodzi’ ndi Yehova, Yesu komanso angelo. (2 Akor. 6:1) Timagwira nawo ntchito pamene tikulalikira komanso kuphunzitsa anthu. Paulo ananena za anthu onse amene amagwira ntchitoyi kuphatikizapo iyeyo kuti: “Ndife antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Tikamagwira ntchito yolalikirayi timakhalanso antchito anzake a Yesu. Paja iye atauza otsatira ake kuti ‘akaphunzitse anthu a mitundu yonse,’ ananenanso kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu.” (Mat. 28:19, 20) Nanga bwanji za angelo? Ndi mwayi waukulu kutsogoleredwa ndi angelo tikamalalikira “uthenga wabwino wosatha . . . kwa anthu okhala padziko lapansi.”​—Chiv. 14:6.

15. Fotokozani chitsanzo cha m’Baibulo chosonyeza zimene Yehova amachita tikakhala mu utumiki.

15 Kodi takwanitsa kuchita chiyani chifukwa chothandizidwa ndi Yehova, Yesu, komanso angelo? Tikamafesa mbewu za uthenga wa Ufumu, zina zimagwera m’mitima ya anthu omvetsera ndipo zimakula. (Mat. 13:18, 23) Koma kodi ndi ndani amene amachititsa kuti mbewu za choonadi zikule ndi kubereka zipatso? Yesu ananena kuti palibe amene angakhale wotsatira wake akapanda “kukokedwa ndi Atate.” (Yoh. 6:44) Baibulo limatipatsa chitsanzo pa nkhani imeneyi. Limanena zomwe zinachitika pamene Paulo ankalalikira kwa azimayi ena omwe anali kunja kwa mzinda wa Filipi. Timawerenga za mmodzi mwa azimayiwo dzina lake Lidiya, kuti: “Yehova anatsegula kwambiri mtima wake kuti atchere khutu ku zimene Paulo anali kunena.” (Mac. 16:13-15) Mofanana ndi Lidiya, anthu mamiliyoni ambiri akokedwa ndi Yehova.

16. Kodi ndi ndani amene ayenera kutamandidwa zinthu zikamatiyendera bwino pa ntchito yathu yolalikira?

16 Kodi ndi ndani amene ayenera kutamandidwa zinthu zikamatiyendera bwino pa ntchito yathu yolalikira? Paulo anapereka yankho la funsoli mukalata yake yopita ku mpingo wa Akorinto. Iye anati: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathirira, koma Mulungu ndiye anakulitsa. Chotero wobzala kapena wothirira sali kanthu, koma Mulungu amene amakulitsa.” (1 Akor. 3:6, 7) Mofanana ndi Paulo, nafenso tiyenera kutamanda Yehova zinthu zikamatiyendera bwino pa ntchito yathu yolalikira.

17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mwayi umene tili nawo ‘wogwira ntchito limodzi’ ndi Yehova, Khristu komanso angelo?

17 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mwayi umene tili nawo ‘wogwira ntchito limodzi’ ndi Yehova, Khristu komanso angelo? Tingachite zimenezi tikamachita khama kuuza ena uthenga wabwino. Pali njira zambiri zomwe tingachitire zimenezi monga kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri komanso “kunyumba ndi nyumba.” (Mac. 20:20) Anthu enanso amakonda kulalikira mwamwayi. Iwo akakumana ndi munthu wachilendo amamupatsa moni mwansangala ndipo amayesetsa kuti ayambe kucheza naye. Akaona kuti wayankha mwaulemu, amayamba kukambirana naye uthenga wa Ufumu.

(Onani ndime 18) *

18-19. (a) Kodi tingathirire bwanji mbewu za choonadi? (b) Fotokozani chitsanzo chosonyeza mmene Yehova anathandizira wophunzira Baibulo wina.

18 Monga “antchito anzake a Mulungu,” sitiyenera kumangodzala mbewu za choonadi koma tiyeneranso kumazithirira. Tikapeza munthu amene wasonyeza chidwi, tiziyesetsa kubwererakonso kapena kukonza zoti munthu wina adzapiteko n’cholinga choti akayambe kuphunzira naye Baibulo. Timasangalala tikaona kuti munthu amene tikuphunzira naye, Yehova akumuthandiza kusintha mmene amaganizira komanso zochita zake.

19 Taganizirani chitsanzo cha munthu wina wa ku South Africa, dzina lake Raphalalani, yemwe anali sing’anga. Iye anayamba kuphunzira Baibulo ndipo ankasangalala ndi zimene ankaphunzirazo. Koma zinkamuvuta kuvomereza zimene Mawu a Mulungu amanena pa nkhani yolankhula ndi makolo akufa. (Deut. 18:10-12) Pang’ono ndi pang’ono, analola kuti Mulungu aumbe kaganizidwe kake. Kenako anasiya ntchito yake ya using’anga ngakhale kuti ndi yomwe inkamupezetsa ndalama. Raphalalani, yemwe tsopano ali ndi zaka 60, anati: “Ndimathokoza kwambiri a Mboni za Yehova pondithandiza m’njira zambiri, monga kundithandiza kuti ndipeze ntchito ina. Koposa zonse, ndikuthokoza Yehova pondithandiza kuti ndisinthe moyo wanga. Moti chifukwa cha zimenezi, ndinabatizidwa ndipo ndikugwira nawo ntchito yolalikira.”

20. Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

20 Mu nkhaniyi, takambirana zinthu 4 zimene ndi chuma chosaoneka. Taona kuti chachikulu pa zinthuzi ndi kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Kukhala pa ubwenzi ndi Yehova kungatithandize kuti tizisangalalanso ndi mphatso zina zitatuzo, zomwe ndi kulankhula naye m’pemphero, kuthandizidwa ndi Yehova, Yesu ndiponso angelo tikamalalikira komanso mphatso ya mzimu woyera. Tiyeni tiyesetse kumayamikira kwambiri chuma chosaoneka chimenechi. Komanso tiyeni tipitirize kumathokoza Yehova chifukwa chokhala bwenzi lathu lapamtima.

NYIMBO NA. 145 Mulungu Watilonjeza Paradaiso

^ ndime 5 Mu nkhani yapitayi, tinakambirana zinthu zingapo zomwe Mulungu anatipatsa zimene tingathe kuziona. Koma mu nkhaniyi, tikambirana zinthu zomwe sitingathe kuziona. Tikambirananso zimene tingachite poyamikira zinthu zimenezi komanso poyamikira Yehova Mulungu yemwe amatipatsa zinthuzi.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: (1) Mlongo akuganizira za ubwenzi wake ndi Yehova pamene akuona zinthu zimene Yehova analenga.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: (2) Mlongo yemwe uja akupemphera kwa Yehova kuti amupatse mphamvu kuti athe kulalikira.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: (3) Mzimu woyera wathandiza mlongoyu kukhala wolimba mtima kuti alalikire mwamwayi.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: (4) Mlongoyu akuchita phunziro la Baibulo ndi munthu amene anamulalikira mwamwayi. Iye akugwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu mothandizidwa ndi angelo.