Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 18

Kodi Mudzakhumudwa N’kusiya Kutsatira Yesu?

Kodi Mudzakhumudwa N’kusiya Kutsatira Yesu?

“Wodala amene sapeza chokhumudwitsa mwa ine.”MAT. 11:6.

NYIMBO NA. 54 “Njira Ndi Iyi”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi mwina chinakudabwitsani n’chiyani mutayamba kuuza ena uthenga wa m’Baibulo?

KODI mukukumbukira mmene munamvera mutazindikira kuti mwapeza choonadi? Munkamvetsa bwino chilichonse chimene munkaphunzira m’Baibulo. Munkaona ngati aliyense avomereza zimene mwayamba kukhulupirirazo. Simunkakayikira kuti uthenga wa m’Baibulo ungawathandize kukhala ndi moyo wosangalala panopa komanso kuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. (Sal. 119:105) Choncho ndi mtima wonse munayamba kuuza anzanu komanso achibale anu mfundo zomwe munkaphunzira. Koma kodi chinachitika n’chiyani? Muyenera kuti munadabwa kuona kuti ambiri anakana zimene munawauza.

2-3. Kodi anthu ambiri ankamuona bwanji Yesu komanso uthenga umene ankalalikira?

2 Sitiyenera kudabwa anthu ena akamakana uthenga umene timalalikira. Mu nthawi ya Yesu, anthu ambiri anamukana ngakhale kuti ankachita zozizwitsa posonyeza kuti anatumidwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, Yesu anaukitsa Lazaro, chomwe chinali chozizwitsa chimene ngakhale anthu amene ankamutsutsawo sakanachikana. Ngakhale zinali choncho, atsogoleri a Chiyuda sanakhulupirire kuti Yesu ndi Mesiya ndipo anayamba kufuna kumupha limodzi ndi Lazaro.​—Yoh. 11:47, 48, 53; 12:9-11.

3 Yesu ankadziwa kuti anthu ambiri sadzavomereza kuti iye ndi Mesiya. (Yoh. 5:39-44) Iye anauza ophunzira a Yohane M’batizi kuti: “Wodala amene sapeza chokhumudwitsa mwa ine.” (Mat. 11:2, 3, 6) Ndiye n’chifukwa chiyani anthu ambiri anakana Yesu?

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Munkhaniyi komanso yotsatira, tikambirana zifukwa zingapo zomwe zinachititsa anthu kuti asakhulupirire Yesu. Tionanso chifukwa chake masiku ano anthu ambiri amakana uthenga wathu. Chofunika kwambiri n’choti tiona chifukwa chake tiyenera kukhulupirira kwambiri Yesu kuti tisakhumudwe n’kusiya kumutsatira.

(1) KUMENE YESU ANAKULIRA

Anthu ambiri anakana Yesu chifukwa’ cha kumene anakulira. Kodi masiku ano zimenezi zingalepheretsenso bwanji ena kutsatira Yesu? (Onani ndime 5) *

5. N’chifukwa chiyani anthu ambiri ankaganiza kuti Yesu sangakhale Mesiya amene ananenedweratu kuti adzabwera?

5 Anthu ambiri anakana kukhulupirira Yesu chifukwa choganizira kumene anakulira. Iwo ankadziwa kuti Yesu anali mphunzitsi waluso komanso ankachita zozizwitsa, koma ankangomuona kuti anali mwana wa kalipentala wosauka. Ndiponso Yesu anali wochokera ku Nazareti, mzinda umene n’kutheka kuti anthu ambiri ankauona kuti ndi wosafunika. Ngakhalenso Natanayeli, yemwe anadzakhala wophunzira wa Yesu, poyamba anati: “Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?” (Yoh. 1:46) N’kutheka kuti Natanayeli sankasangalala ndi mzinda umene Yesu ankakhalawu. Kapenanso ankaganizira ulosi wopezeka pa Mika 5:2, umene unaneneratu kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu, osati ku Nazareti.

6. Kodi n’chiyani chikanathandiza anthu m’nthawi ya Yesu kudziwa kuti iye ndi Mesiya?

6 Kodi Malemba amati chiyani? Mneneri Yesaya ananeneratu kuti adani a Yesu sadzaganizira “tsatanetsane wa mibadwo ya makolo ake [a Mesiya].” (Yes. 53:8) Koma zambiri pa nkhaniyi zinali zitanenedweratu. Anthu amenewa akanafufuza mokwanira, akanadziwa kuti Yesu anabadwira ku Betelehemu, komanso anali wochokera mumzere wa Mfumu Davide. (Luka 2:4-7) Choncho malo omwe Yesu anabadwira ndi amene ananenedweratu mu ulosi wa pa Mika 5:2. Ndiyeno kodi vuto linali pati? Anthuwo ankangofulumira kumuweruza. Popeza kuti sankadziwa zinthu zonse, anakana kukhulupirira Yesu.

7. N’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano amakana kukhulupirira zimene anthu a Yehova amaphunzitsa?

7 Kodi vuto limeneli liliponso masiku ano? Inde lilipo. Anthu a Yehova ambiri ndi osauka moti amaonedwa kuti ndi “osaphunzira ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13) Ena amawaona kuti sangaphunzitse Baibulo chifukwa sanapite kumasukulu azachipembedzo. Enanso amanena kuti Mboni za Yehova ndi “chipembedzo cha ku America.” Koma zoona n’zakuti a Mboni ambiri sakhala kumeneko. Ndiye pali enanso amene anauzidwa kuti a Mboni sakhulupirira Yesu. Kwa zaka zambiri, anthu akhala akunena kuti a Mboni ndi “akazitape a ku America” komanso “anthu oopsa.” Popeza kuti anthu amenewa amauzidwa zinthu zabodzazi, safuna kukhala a Mboni za Yehova.

8. Mogwirizana ndi Machitidwe 17:11, kodi anthu ayenera kuchita chiyani kuti adziwe atumiki a Mulungu masiku ano?

8 Kodi munthu angatani kuti asakhumudwe n’kusiya kutsatira Yesu? Ayenera kufufuza mfundo zoona. Zimenezi ndi zomwe wolemba Uthenga Wabwino Luka anachita. Iye anachita khama pofufuza “zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pa chiyambi.” Ankafuna kuti anthu amene ankawerenga uthenga wake wonena za Yesu adziwe bwinobwino kuti zinthu zimene anaphunzitsidwa “n’zodalirika.” (Luka 1:1-4) Ayuda a ku Bereya nawonso anachita zofanana ndi zimene Luka anachita. Iwo atamva koyamba uthenga wonena za Yesu, anafufuza m’Malemba a Chiheberi kuti atsimikizire kuti zimene anauzidwazo zinali zoona. (Werengani Machitidwe 17:11) Mofanana ndi zimenezi, anthu masiku ano ayenera kufufuza kuti adziwe zoona. Afunika kumayerekezera zimene anthu a Mulungu amaphunzitsa ndi zimene Malemba amanena. Ayeneranso kufufuza zimene anthu a Yehova akuchita masiku ano. Ngati atafufuza bwinobwino, sangasokonezedwe ndi tsankho kapena nkhani zimene anthu ena amangonena, zomwe zilibe umboni.

(2) YESU ANAKANA KUCHITA ZOZIZWITSA PONGOFUNA KUDZIONETSERA

Anthu ambiri anakana Yesu chifukwa’ anakana kuwapatsa zizindikiro pongofuna kudzionetsera. Kodi masiku ano zimenezi zingalepheretsenso bwanji ena kutsatira Yesu? (Onani ndime 9-10) *

9. Kodi chinachitika n’chiyani Yesu atakana kusonyeza chizindikiro chochokera kumwamba?

9 Anthu ena m’nthawi ya Yesu sanakhutire ndi zimene iye ankaphunzitsa moti ankafuna kuti achitenso zinthu zina. Anthuwa anamuuza kuti asonyeze kuti iye ndi Mesiya, powaonetsa “chizindikiro chochokera kumwamba.” (Mat. 16:1) N’kutheka kuti ananena zimenezi chifukwa chosamvetsa zomwe anawerenga pa Danieli 7:13, 14. Komabe, imeneyi sinali nthawi ya Yehova yoti ulosiwu ukwaniritsidwe. Zimene Yesu ankaphunzitsa zinali zokwanira kuwathandiza kudziwa kuti iyeyo anali Mesiya. Koma Yesu atakana kuwasonyeza chizindikiro chomwe ankafunacho, anakhumudwa ndipo anakana kumukhulupirira.​—Mat. 16:4.

10. Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji zimene Yesaya analemba zokhudza Mesiya?

10 Kodi Malemba amati chiyani? Ponena za Mesiya, mneneri Yesaya analemba kuti: “Iye sadzafuula kapena kukweza mawu ake, ndipo mawu ake sadzamvedwa mumsewu.” (Yes. 42:1, 2) Pa utumiki wake, Yesu ankachita zinthu modzichepetsa. Iye sanamange akachisi ogometsa, ndiponso sankavala zovala zapadera zachipembedzo kapena kufuna kuti anthu azimuitana ndi maina aulemu achipembedzo. Pa nthawi imene ankaimbidwa mlandu, Yesu anakana kuchita chozizwitsa pongofuna kusangalatsa Mfumu Herode. (Luka 23:8-11) N’zoona kuti Yesu ankachita zozizwitsa, koma cholinga chake chachikulu chinali kulengeza uthenga wabwino. Iye anauza ophunzira ake kuti chimenechi “ndicho cholinga chimene ndinabwerera.”​—Maliko 1:38.

11. Kodi masiku ano anthu ambiri amakhala ndi maganizo olakwika ati?

11 Kodi vuto limeneli liliponso masiku ano? Inde. Anthu ambiri masiku ano amakopeka ndi matchalitchi amene amakongoletsedwa ndi zinthu zodula, atsogoleri achipembedzo omwe amatchulidwa maina aulemu komanso miyambo imene sadziwa n’komwe kumene inachokera. Koma kodi anthu amene amapita ku matchalitchiwa amaphunzira zilizonse zokhudza Mulungu komanso zolinga zake? Mosiyana ndi zimenezi, anthu amene amapezeka pamisonkhano yathu amaphunzira zimene Yehova amafuna kuti tizichita komanso mmene tingachitire zimenezo. Nyumba zathu za Ufumu zimakhala zaukhondo, koma si kuti zimakongoletsedwa mogometsa. Anthu amene amatsogolera savala zovala zapadera zachipembedzo kapena kutchulidwa maina aulemu. Zonse zomwe timaphunzitsa komanso kukhulupirira zimachokera m’Mawu a Mulungu. Koma ngakhale zili choncho, anthu ambiri amakana uthenga wathu chifukwa amaona kuti zimene timachita polambira Mulungu ndi zosasangalatsa ndiponso zimene timaphunzitsa sizigwirizana ndi zimene amafuna kumva.

12. Mogwirizana ndi Aheberi 11:1, 6, kodi n’chiyani chingatithandize kukhala ndi chikhulupiriro?

12 Kodi tingatani kuti tisakhumudwe n’kusiya kutsatira Yesu? Mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Roma kuti: “Munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva. Ndipo zimene wamvazo zimachokera m’mawu onena za Khristu.” (Aroma 10:17) Choncho timakhala ndi chikhulupiriro chifukwa chophunzira Baibulo, osati pochita nawo miyambo yosemphana ndi Malemba, ngakhale itaoneka kuti ndi yosangalatsa. Tiyenera kuphunzira Malemba kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa “popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.” (Werengani Aheberi 11:1, 6.) Pamenepa zikusonyeza kuti sitikuchita kufunikira kuona chizindikiro chochokera kumwamba kuti tidziwe kuti tapeza choonadi. Kuphunzira mosamala mfundo za m’Baibulo zolimbitsa chikhulupiriro, kungatithandize kuti tisamakaikire ngakhale pang’ono kuti tapeza choonadi.

(3) YESU SANKACHITA NAWO MIYAMBO YAMBIRI YA CHIYUDA

Anthu ambiri anakana Yesu chifukwa’ anakana kuchita nawo miyambo ina. Kodi masiku ano zimenezi zingalepheretsenso bwanji ena kutsatira Yesu? (Onani ndime 13) *

13. Kodi n’chiyani chinalepheretsa anthu ambiri kutsatira Yesu?

13 Mu nthawi ya Yesu, ophunzira a Yohane M’batizi anadabwa kuti ophunzira a Yesu sankasala kudya. Koma Yesu anawauza kuti panalibe chifukwa choti azisalira kudya iye ali moyo. (Mat. 9:14-17) Ngakhale zinali choncho, Afarisi ndi anthu ena amene ankamutsutsa, anamudzudzula chifukwa choti sankachita nawo miyambo yawo. Iwo ankakwiya akaona kuti Yesu wachiritsa munthu patsiku la Sabata. (Maliko 3:1-6; Yoh. 9:16) Anthu amenewa ankanena kuti amasunga Sabata, koma sankaona vuto kuchita malonda m’kachisi. Ndipo anakwiya Yesu atawadzudzula chifukwa cha zimenezi. (Mat. 21:12, 13, 15) Ndiponso anthu amene Yesu anawalalikira m’sunagoge ku Nazareti, anakhumudwa chifukwa choti iye anawafotokozera nkhani za m’Malemba zimene zinasonyeza kuti iwo anali anthu odzikonda komanso opanda chikhulupiriro. (Luka 4:16, 25-30) Popeza Yesu ankachita zinthu zimene ambiri sankayembekezera, zimenezi zinawakhumudwitsa ndipo ambiri anasiya kumutsatira.​—Mat. 11:16-19.

14. N’chifukwa chiyani Yesu ankadzudzula miyambo ya anthu yosemphana ndi Malemba?

14 Kodi Malemba amati chiyani? Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, Yehova ananena kuti: “Anthu awa ayandikira kwa ine ndi pakamwa pawo pokha, ndipo andilemekeza ndi milomo yawo yokha koma mtima wawo auika kutali ndi ine, ndiponso amangophunzira malamulo a anthu n’kumaganiza kuti kuchita zimenezo ndiye kundiopa.” (Yes. 29:13) Yesu sanalakwitse kudzudzula miyambo ya anthu yomwe sinkagwirizana ndi Malemba. Anthu amene ankaona kuti kutsatira malamulo komanso miyambo ya anthu n’kofunika kwambiri kuposa kutsatira Malemba, anakana Yehova komanso Mesiya amene iye anamutuma.

15. N’chifukwa chiyani masiku ano anthu ambiri sasangalala ndi Mboni za Yehova?

15 Kodi vuto limeneli liliponso masiku ano? Inde. Anthu ambiri amakhumudwa ndi a Mboni za Yehova chifukwa choti sapanga nawo miyambo yosemphana ndi Malemba monga kukumbukira masiku a kubadwa komanso Khirisimasi. Enanso amakwiya chifukwa a Mboni za Yehova sapanga nawo miyambo yosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo komanso ya maliro, yomwe imasemphana ndi Malemba. Anthu amene amakhumudwa ndi zimenezi, amakhulupirira ndi mtima wonse kuti akulambira Mulungu m’njira yovomerezeka. Komatu anthu amenewa sangakondweretse Mulungu ngati amakonda miyambo ya anthu osati mfundo zomveka bwino zopezeka m’Baibulo.​—Maliko 7:7-9.

16. Mogwirizana ndi Salimo 119:97, 113, 163-165, kodi tiyenera kuchita chiyani, nanga tiyenera kupewa chiyani?

16 Kodi tingatani kuti tisakhumudwe n’kusiya kutsatira Yesu? Tiyenera kumakonda kwambiri mfundo komanso malamulo a Yehova. (Werengani Salimo 119:97, 113, 163-165.) Zili choncho chifukwa ngati timakonda Yehova, sitingamachite nawo miyambo iliyonse imene simusangalatsa. Ndipo sitingalole kuti chilichonse chitilepheretse kusonyeza kuti timakonda Yehova.

(4) YESU SANATHANDIZE ANTHU KUSINTHA ULAMULIRO

Anthu ambiri anakana Yesu chifukwa’ sankachita nawo zandale. Kodi masiku ano zimenezi zingalepheretsenso bwanji ena kutsatira Yesu? (Onani ndime 17) *

17. Kodi m’nthawi ya Yesu anthu ambiri ankayembekezera kuti Mesiya achita chiyani?

17 M’nthawi ya Yesu anthu ankafuna ulamuliro utasintha. Iwo ankayembekezera kuti Mesiya adzawapulumutsa ku ulamuliro wopondereza wa Aroma. Koma pamene ankafuna kumuveka Yesu ufumu, iye anakana. (Yoh. 6:14, 15) Anthu enanso kuphatikizapo ansembe, ankada nkhawa kuti Yesu akasintha zinthu pa nkhani ya ulamuliro akwiyitsa Aroma, ndipo izi zichititsa kuti awalande mphamvu zimene anawapatsa. Popeza ankada nkhawa ndi nkhani zandale, Ayuda ambiri anakana Yesu.

18. Kodi ndi maulosi ati okhudza Mesiya amene anthu ambiri ankanyalanyaza?

18 Kodi Malemba amati chiyani? Ngakhale kuti maulosi ambiri ananeneratu kuti Mesiya adzapambana pankhondo, panalinso maulosi ena amene anasonyeza kuti choyamba ankafunika kufa chifukwa cha machimo a anthu. (Yes. 53:9, 12) Ndiye n’chifukwa chiyani Ayudawo ankakhala ndi maganizo olakwika okhudza Mesiya? Anthu ambiri ankanyalanyaza maulosi amene sankanena zokhudza kuthetsa mavuto awo pa nthawiyo.​—Yoh. 6:26, 27.

19. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimachititsa anthu kukana uthenga umene timalalikira?

19 Kodi vuto limeneli liliponso masiku ano? Inde. Anthu ambiri amakana uthenga umene timalalikira chifukwa choti sitilowerera zandale. Iwo amafuna kuti tizivota pa nthawi ya zisankho. Komabe, ife timadziwa kuti ngati titasankha munthu kuti azitilamulira, timakhala kuti tikukana Yehova. (1 Sam. 8:4-7) Anthu enanso amaona kuti timayenera kumanga masukulu, zipatala komanso kuchita ntchito zina zachifundo. Iwo amakana uthenga wathu chifukwa choti timaika maganizo athu onse pa ntchito yolalikira, osati kuthetsa mavuto a m’dzikoli.

20. Mogwirizana ndi mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 7:21-23, kodi cholinga chathu chachikulu chiyenera kukhala chiyani?

20 Kodi tingatani kuti tisakhumudwe n’kusiya kutsatira Yesu? (Werengani Mateyu 7:21-23.) Chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu chiyenera kukhala ntchito imene Yesu anatiuza kuti tizigwira. (Mat. 28:19, 20) Sitiyenera kusokonezedwa ndi nkhani zandale komanso kuyesa kuthetsa mavuto a m’dzikoli. N’zoona kuti timakonda anthu komanso timakhudzidwa ndi mavuto amene amakumana nawo, koma timadziwa kuti njira yabwino kwambiri yowathandizira ndi kuwaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu komanso kuwathandiza kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova.

21. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

21 Munkhaniyi, takambirana zinthu 4 zimene zinachititsa anthu kuti akane Yesu m’nthawi yake, zomwenso zingachititse anthu ambiri masiku ano kukana uthenga umene otsatira ake amalalikira. Koma kodi ndi zinthu zokhazi zimene tiyenera kupewa? Ayi. Munkhani yotsatira, tidzakambirana zinthu zinanso 4 zimene zimalepheretsa ena kutsatira Yesu. Tiyeni tikhale otsimikiza kuti tipitirizabe kutsatira Yesu komanso kulimbitsa chikhulupiriro chathu.

NYIMBO NA. 56 Inuyo Panokha Muzikonda Kwambiri Choonadi

^ ndime 5 Ngakhale kuti Yesu anali Mphunzitsi wamkulu kuposa onse amene anakhalako, anthu ambiri m’nthawi yake anamukana. N’chifukwa chiyani? Munkhaniyi, tikambirana zifukwa 4. Tikambirananso chifukwa chake anthu ambiri masiku ano sakhulupirira zimene otsatira enieni a Yesu amanena komanso kuchita. Ndipo tiphunziranso chifukwa chake tiyenera kukhulupirira kwambiri Yesu kuti tisakhumudwe n’kusiya kumutsatira.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Filipo akulimbikitsa Natanayeli kuti akumane ndi Yesu.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yesu akulalikira uthenga wabwino.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yesu akuchiritsa munthu wolumala dzanja pamene anthu otsutsa akuonerera.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yesu akupita kuphiri ali yekhayekha.